Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi kusewera masewera achiwawa a pakompyuta kungam’sokonezere munthu ubwenzi wake ndi Yehova?

Mfumu Davide ya Israyeli wakale inati: “Yehova ayesa wolungama mtima: koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.” (Salmo 11:5) Mawu a Chihebri otanthauza ‘kuda’ amatanthauzanso “kukhala mdani.” Motero munthu aliyense amene amakonda zachiwawa akudzipangitsa yekha kukhala mdani wa Mulungu. Choncho funso limene tiyenera kuliganizira ndi ili: Kodi kuchita masewera enaake pakompyuta kungayambitse munthu kukonda zachiwawa?

Masewera achiwawa a pakompyuta amalimbikitsa wosewerayo kugwiritsira ntchito zida zankhondo. Nthawi zambiri masewerawa amaphunzitsa munthuyo nkhondo. Magazini yotchedwa The Economist inanena kuti: “Gulu la asilikali a dziko la United States layamba kudalira kwambiri masewera a pakompyuta pophunzitsa asilikali ake nkhondo. Masewera ena amene asilikaliwa amagwiritsira ntchito amawagula m’masitolo a anthu wamba.”

N’zoona kuti anthu amene amachita masewera achiwawa a pakompyuta sikuti amakhala akuvulazadi anthu enieni. Komabe, kodi kukonda masewera oterewa kumasonyeza kuti mtima wawo ndi wotani? (Mateyu 5:21, 22; Luka 6:45) Kodi munthu wokonda kubaya, kuwombera, kupundula, ndiponso kupha anthu osakhala enieni, mungati ndi wotani? Nanga mungam’ganizire chiyani munthuyu ngati nthawi zambiri mlungu uliwonse amakhala akusangalala pochita masewera achiwawa oterewa, mpaka kufika pomulowerera kwambiri? Ndithu sikulakwa kuganiza kuti munthuyu wayamba kukonda zachiwawa, monga mmene mungadziwire kuti munthu wayamba kukonda zadama ngati akukonda kuona zithunzi zolaula.​—Mateyu 5:27-29.

Kodi Yehova amamuona motani munthu wokonda zachiwawa? Mawu a Davide aja amasonyeza kuti Yehova amadana kwambiri ndi anthu otero. M’masiku a Nowa, Yehova anasonyeza kuti amadana kwambiri ndi anthu okonda zachiwawa. Iye anauza Nowa kuti: “Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; taonani, ndidzawononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi.” (Genesis 6:13) Mulungu woona anawononga dziko lonse la anthu la panthawiyo chifukwa cha zochita zawo zachiwawa. Iye anasiyako Nowa yekha ndi am’banja mwake, ndipo onse pamodzi analipo anthu eyiti okha amene sankakonda zachiwawa.​—2 Petro 2:5.

Anthu ofuna kukhala mabwenzi a Yehova ‘amasula malupanga awo akhale zolimira.’ M’malo mophunzira kukonda zachiwawa, iwo ‘saphunziranso nkhondo.’ (Yesaya 2:4) Kuti tizigwirizanabe ndi Mulungu, osadana naye, tiyenera ‘kupatuka pazoipa, n’kumachita zabwino.’ Tiyenera ‘kufunafuna mtendere ndi kuulondola.’​—1 Petro 3:11.

Nanga tingatani ngati tinazolowera kale masewerawa? Poti Yehova amadana nawo, tiyesetse kupewa masewerawa kuti tim’sangalatse. Ndithu, tiyenera kupemphera kuti mzimu woyera wa Mulungu utithandize kusiya khalidwe limeneli, lomwe limasokoneza munthu mwauzimu. Tingathe kulisiya pokhala anthu abwino, amtendere, ndiponso odziletsa, n’cholinga chakuti moyo wathu ukhale wogwirizana ndi malamulo a Mulungu.​—Luka 11:13; Agalatiya 5:22, 23.