Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Tingachepetsere Maganizo

Mmene Tingachepetsere Maganizo

Mmene Tingachepetsere Maganizo

KODI nthawi zina maganizo amakuchulukirani? Kodi simuchedwa kukhumudwa ndiponso kupsa mtima? Kodi mumangokhala a nkhawa chifukwa cha mavuto? Ngati ndi choncho, kodi n’chiyani chingakuthandizeni?

Munthu salephera kukhala ndi maganizo. Ndipotu akamathana nawo bwinobwino maganizowa moyo wake umakoma. Koma Baibulo limanena kuti “nsautso iyalutsa wanzeru.” (Mlaliki 7:7) Tikukhala m’dziko limene zachiwawa ndiponso ngozi zili ponseponse, motero palibe amene angakhale wopanda maganizo. Komabe, Malemba amanenanso kuti: “Kulibe kanthu kabwino kopambana . . . kuti munthu akondwere ndi ntchito zake.” (Mlaliki 3:22) Choncho, kuti moyo tiziumva kukoma, tiyenera kuphunzira kukhala osangalala poyesetsa kukhala ndi maganizo abwino. Kodi tingatani kuti tikhale ndi maganizo abwino n’kuthetsa maganizo oipa?

Kuti tichepetse maganizo oipa, nthawi zambiri pamafunika kuchita zinazake zothandiza. Mwachitsanzo, tikamada nkhawa ndi zinthu zimene sitingathe kuzikonza mwa njira ina iliyonse, kodi m’malo momangoganizira nkhaniyo, sibwino kungosintha maganizo athu pa nkhaniyo kapenanso kungochokapo? Kuyenda mowongola miyendo, kumvetsera nyimbo zokhazika mtima pansi, kuchita zinthu zolimbitsa thupi, kapenanso kuthandiza munthu wina m’njira inayake, kungatikhazike pansi maganizo ndiponso kungatithandize kukhala osangalala.​—Machitidwe 20:35.

Komabe, njira yabwino kwambiri yothetsera maganizo ndiyo kudalira Mlengi. Maganizo akatichulukira, tiyenera ‘kutaya nkhawa zathu zonse kwa Mulungu’ popemphera kwa iye. (1 Petro 5:6, 7) Baibulo limatitsimikizira kuti: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka . . . Masautso a wolungama mtima achuluka: koma Yehova am’landitsa mwa onsewa.” (Salmo 34:18, 19) Kodi tingatsimikize bwanji kuti Mulungu angathe kukhala ‘mthandizi wathu, ndi mpulumutsi wathu’? (Salmo 40:17) Tingatero powerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha pa zitsanzo zake zomveka bwino zosonyeza kuti Mulungu amaganizira ndiponso kusamalira kwambiri atumiki ake.