Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pewani Maganizo Olakwika

Pewani Maganizo Olakwika

Pewani Maganizo Olakwika

PAMENE Yobu anali pamavuto aakulu, anzake atatu anabwera kudzamuona ndipo mayina awo anali Elifazi, Bilidadi, ndi Zofari. Iwowa anabwera kuti adzakhale naye pamavuto ake komanso kuti adzam’limbikitse. (Yobu 2:11) Pa anzake atatuwa, Elifazi ndiye anali wopatsidwa ulemu ndiponso mwina wamkulu kwambiri. Iyeyu ndiye anayamba kulankhula ndipo ndiye analankhula kwambiri. Kodi pa nthawi zitatu zimene Elifazi analankhulapo, anasonyeza kuti anali munthu wamaganizo otani?

Pokumbukira masomphenya odabwitsa amene anaona nthawi ina, Elifazi anati: “Panapita mzimu pamaso panga; tsitsi la thupi langa lidati nyau nyau.” (Yobu 4:15) Kodi ndi mzimu wotani umene unam’sokoneza maganizo Elifazi? Mawu osalimbikitsa amene ananena pambuyo ponena zimenezi amasonyeza kuti mzimuwo sunali mzimu wochokera kwa Mulungu. (Yobu 4:17, 18) Mzimu umenewu unali chiwanda. N’chifukwa chaketu Yehova anadzudzula Elifazi ndi anzake awiri aja kuti ananena zabodza. (Yobu 42:7) Inde Elifazi anasokonezedwa maganizo ndi ziwanda. Mawu amene ananena anasonyeza kuti maganizo ake sanali maganizo a Mulungu.

Kodi ndi mfundo zotani zimene tingaone m’mawu a Elifazi? N’chifukwa chiyani timafunikira kupewa maganizo olakwika? Ndipo kodi tingachitepo zotani kuti tipewe maganizowa?

“Sakhulupirira Atumiki Ake”

Pa nthawi zonse zitatu zimene analankhula, Elifazi anasonyeza kuti Mulungu n’ngovuta kwambiri kum’sangalatsa moti palibe chilichonse chimene atumiki ake amachita chimene iye amasangalala nacho. Elifazi anamuuza Yobu kuti: “Taona, sakhulupirira atumiki ake; nawanenera amithenga [kapena kuti angelo] ake zopusa.” (Yobu 4:18) Kenakanso Elifazi ananena kuti Mulungu “sakhulupirira opatulika ake; ngakhale m’mwamba simuyera pamaso pake.” (Yobu 15:15) Ndipo anafunsa kuti: “Kodi Wamphamvuyonse akondwera nako kuti iwe ndiwe wolungama?” (Yobu 22:3) Bilidadi anavomerezana nawo maganizo amenewa, chifukwa nayenso anati: “Taonani, ngakhale mwezi ulibe kuwala; ndi nyenyezi siziyera pamaso [pa Mulungu].”​—Yobu 25:5.

Tiyenera kusamala kuti tisayambe kuganiza maganizo otere. Chifukwatu angatipangitse kuona kuti zimene Mulungu amafuna sizoti munthu angakwanitse. Kuganiza motere kungathe kusokoneza ubwenzi wathu weniweniwo ndi Yehova. Komanso, ngati titayamba kuganiza choncho, kodi tingathe kumvera bwinobwino malangizo enaake amene tikupatsidwa? M’malo momvera malangizowo, mtima wathu ungafike “pokwiyira Yehova weniweniyo,” motero tingakhumudwe naye. (Miyambo 19:3, NW) Izitu zingatisokonezere kwambiri ubwenzi wathu ndi Mulungu.

“Kodi Munthu Apindulira Mulungu?”

Maganizo akuti Mulungu n’ngovuta kum’sangalatsa amayendera limodzi ndi maganizo akuti Mulungu saona anthu ngati kanthu. Panthawi yachitatu imene Elifazi analankhula ananenapo mawu akuti: “Kodi munthu apindulira Mulungu? Koma wanzeru angodzipindulira yekha.” (Yobu 22:2) Apatu Elifazi anali kutanthauza kuti munthu sanunkha kanthu kwa Mulungu. Bilidadi anakhudzaponso mfundo yomweyi ponena kuti: “Munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu? Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?” (Yobu 25:4) Tikatengera maganizo amenewa, tingafunse kuti kodi Yobu poti anali munthu, ankadzivutitsiranji kuganiza kuti angathe kukhala wolungama pamaso pa Mulungu?

Anthu ena masiku ano amavutika ndi maganizo olakwika okhudza moyo wawo. N’kutheka kuti amaganiza choncho chifukwa cha mmene analeredwera, mavuto amene akumana nawo pa moyo wawo, mwinanso kusankhidwa mtundu kapena fuko. Koma Satana ndi ziwanda zake amasangalalanso kwambiri kuvutitsa anthu. Amadziwa kuti akangochititsa munthu kuyamba kumva kuti palibe chimene angachite choti Mulungu Wamphamvuyonse n’kusangalala nacho, m’posavuta kuti munthuyo asowe kolowera. Kenaka mwapang’onopang’ono munthuyo angathe kuyamba kutalikirana ndi Mulungu wamoyo mwinanso kufika polekana naye kumene.​—Ahebri 2:1; 3:12.

Kukalamba ndiponso matenda amatilepheretsa kuchita zinthu zina. Tingaone kuti tikulephera kuchita zambiri mu utumiki wa Ufumu poyerekezera ndi zimene tinkachita tili aang’ono, tili athanzi, ndiponso tili amphamvu. M’pofunika kwambiri kuzindikira kuti Satana ndi ziwanda zake amafuna kuti tiziganiza kuti zimene tikuchita panopa si zoti Mulungu n’kusangalala nazo ayi. Tiyeni tiyesetse kupewa maganizo oterewa.

Mmene Tingapewere Maganizo Olakwika

Ngakhale kuti Satana Mdyerekezi anam’bweretsera Yobu mavuto adzaoneni, Yobuyo ananena kuti: “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.” (Yobu 27:5) Popeza kuti ankakonda Mulungu, Yobu anafunitsitsa kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu zivute zitani, ndipo sanalole kuti china chilichonse chimusunthe pa mfundo imeneyi. Apatu m’pamene pagona chinsinsi chopewera maganizo olakwika. Tiyenera kudziwa bwino chikondi cha Mulungu n’kulola kuti chitifike pamtima. Komanso tiyenera kuyamba kum’konda kwambiri Mulungu. Tingatero powerenga Mawu a Mulungu nthawi zonse ndi kusinkhasinkha zimene akutiphunzitsa.

Mwachitsanzo, lemba la Yohane 3:16 limati: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha.” (Yohane 3:16) Yehova amakonda kwambiri anthu padziko lapansi, ndipo timaona chikondi chimenechi poganizira za mmene wakhala akuchitira zinthu ndi anthu m’mbuyo monsemu. Posinkhasinkha zitsanzo zakale tingathe kufika pomumvetsadi Yehova ndiponso kuyamba kum’konda kwambiri, ndipo zimenezi zingatithandize kupewa maganizo olakwika kapena ofoola.

Taganizirani zimene Yehova anam’chitira Abrahamu, atangotsala pang’ono kuwononga Sodomu ndi Gomora. Abrahamu anafunsa Yehova nthawi eyiti za mmene Yehovayo aweruzire mizindayi. Nthawi zonsezi Yehova sanasonyezepo kuti watopa nawo mafunso a Abrahamu kapena kuti wanyong’onyeka nawo. Koma mayankho ake onse anali om’khazika mtima m’malo ndi kum’limbikitsa. (Genesis 18:22-33) Pambuyo pake, Mulungu atapulumutsa Loti ndi banja lake ku Sodomu, Loti anapempha Mulungu kuti athawire ku mzinda wina wapafupi, m’malo mothawira ku mapiri. Yehova anam’yankha kuti: “Taona, ndikuvomereza iwe pamenepanso kuti sindidzawononga mudzi uwu umene wandiuza.” (Genesis 19:18-22) Kodi nkhani zimenezi zikusonyeza kuti Yehova ndi wolamulira wovuta kum’sangalatsa, wopanda chikondi, komanso wochulukitsa malamulo? Ayi. Zimasonyeza kuti iye kwenikweni ndi Wolamulira wachikondi, wokoma mtima, wachifundo, ndiponso womvetsa zinthu.

Zitsanzo za Aroni, Davide ndiponso Manase, omwe anali anthu a ku Israyeli wakale, zimasonyezeratu poyera kuti sizoona kuti Mulungu amakonda kutola ena zifukwa ndiponso kuti palibe angam’sangalatse. Aroni anachimwa milandu itatu ikuluikulu. Iye anapanga fano la mwana wang’ombe, anagwirizana ndi mlongo wake Miriamu pom’tsutsa Mose, ndipo sanalemekeze Mulungu pa Meriba. Komabe, Yehova anaona kuti Aroni anali ndi makhalidwe ena abwino motero anam’lola kukhalabe mkulu wa ansembe mpaka pamene anamwalira.​—Eksodo 32:3, 4; Numeri 12:1, 2; 20:9-13.

Mfumu Davide anachita machimo aakulu muulamuliro wake. Machimo ake anali chigololo, kukonza chiwembu chopha munthu wosalakwa, ndiponso anawerenga anthu pamene sanayenere kutero. Komabe, Yehova anaona kuti Davide walapa ndipo Iye anasungabe pangano lake la Ufumu pomulola kukhala mfumu mpaka imfa yake.​—2 Samueli 12:9; 1 Mbiri 21:1-7.

Manase, mfumu ya Yuda, anapanga maguwa operekera nsembe kwa Baala, anapititsa ana ake pamoto wansembe, analimbikitsa zokhulupirira mizimu, ndiponso anamanga maguwa a chipembedzo chonyenga m’mabwalo a kachisi. Komabe atasonyeza kulapa kochoka pansi pamtima, Yehova anamukhululukira, anam’masula kuukaidi, n’kumupatsanso ufumu. (2 Mbiri 33:1-13) Kodi tinganene kuti Mulungu amene anachita zoterezi ndi woti palibe munthu angakwanitse kum’sangalatsa? Ayi ndithu, sitingatero.

Wonamizira Anzakeyo Ndiye Wolakwa

Sitiyenera kudabwa kuti Satana ndiye chimake cha makhalidwe onse oipa amene iye amanamizira Yehova. Satana ndi wovuta mapeto ndipo si woti n’kumusangalatsa. Umboni wooneka bwino wotsimikizira zimenezi n’ngwakuti kale iye ankachititsa olambira onyenga kumapereka tiana monga nsembe. Aisrayeli opanduka ankaotcha ana awo aamuna ndi aakazi, ndipotu izi ndi zinthu zoti Yehova sanaziganizepo n’komwe.​—Yeremiya 7:31.

Si Yehova ayi koma Satana, amene amatola ena zifukwa. Lemba la Chivumbulutso 12:10 limanena kuti Satana ndi “wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.” Koma wamasalmo anaimba ponena za Yehova kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye? Koma kwa Inu kuli chikhululukiro.”​—Salmo 130:3, 4.

Nthawi Imene Sikudzakhalanso Maganizo Olakwika

Angelo ayenera kuti mitima inakhala pansi pamene Satana Mdyerekezi ndi ziwanda zake anachotsedwa kumwamba. (Chivumbulutso 12:7-9) Atawachotsa kumwamba anthu oipa auzimuwa analibenso mphamvu iliyonse pa zochitika za banja la kumwamba la Yehova la angelo.​—Danieli 10:13.

M’tsogolo muno, anthu onse padziko lapansi adzasangalala. Posachedwapa kudzabwera mngelo wochoka kumwamba, m’manja mwake muli chifungulo, kapena kuti kiyi wa kuphompho ndi unyolo waukulu ndipo adzamanga Satana ndi ziwanda zake n’kuwaponyera kuphomphoko kuti asakhalenso ndi mphamvu zochita china chilichonse. (Chivumbulutso 20:1-3) Akadzatero, anthufe mitima idzakhala pansi kwambiri.

Pakali pano, tiyenera kuyesetsa kupewa maganizo olakwika. Tikangoona kuti maganizo olakwika ayamba kutibwerera, tiyenera kuwapewa poganizira za chikondi cha Yehova. Tikatero ndiye kuti ‘mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yathu ndi maganizo athu mwa Kristu Yesu.’​—Afilipi 4:6, 7.

[Chithunzi patsamba 26]

Yobu anapewa maganizo olakwika

[Chithunzi patsamba 28]

Loti anafika pozindikira kuti Yehova ndi Wolamulira womvetsa zinthu