Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitirizani Kuyenda Monga Yesu Kristu Anayendera

Pitirizani Kuyenda Monga Yesu Kristu Anayendera

Pitirizani Kuyenda Monga Yesu Kristu Anayendera

“Iye wakunena kuti akhala mwa [Mulungu], ayeneranso mwini wake kuyenda monga anayenda [Yesu].”​—1 YOHANE 2:6.

1, 2. Kodi kuyang’anitsitsa Yesu kumatanthauza kuchita chiyani?

MTUMWI Paulo analemba kuti: “Tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu.” (Ahebri 12:1, 2) Kuti tiyende m’njira yokhulupirika tiyenera kuyang’anitsitsa Yesu Kristu.

2 Liwu lopezeka m’Malemba Achigiriki Achikristu oyambirira lomwe analimasulira kuti “kupenyerera,” limatanthauza “kuyang’anitsitsa chinthu popanda kudodometsedwa,” “kusiya chinthu chimene ukuyang’ana n’kuyamba kuyang’ana china,” komanso “kuyang’ana chinthu mwachidwi.” Buku lina limati: “Wothamanga wachigiriki amene ali pa mpikisano ankati akangosiya kuyang’ana njira imene akuthamangamo ndiponso kuyang’ana pamene mpikisanowo ukathere n’kucheukira kumene kuli chikhamu choonerera, liwiro lake linkachepa. N’chimodzimodzinso ndi Mkristu.” Zinthu zocheukitsa zingathe kuchepetsa liwiro lathu pamene tikukula mwauzimu. Tiyenera kuyang’anitsitsa Yesu Kristu. Koma kodi timafuna kuona chiyani tikamayang’anitsitsa Woyambira wathuyu? Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “woyambira” amatanthauza kuti “mtsogoleri wamkulu, amene amatsogolera zinthu zonse motero amakhala chitsanzo.” Kuti tiyang’anitsitse Yesu timafunika kutsatira chitsanzo chake.

3, 4. (a) Kodi timafunikira kutani kuti tiziyenda mmene Yesu Kristu ankayendera? (b) Kodi ndi mafunso otani amene tiyenera kuwaganizira?

3 Baibulo limati: “Iye wakunena kuti akhala mwa [Mulungu], ayeneranso mwini wake kuyenda monga anayenda [Yesu].” (1 Yohane 2:6) Tiyenera kukhala mwa Mulungu potsatira malamulo a Yesu monganso iye ankatsatirira malamulo a Atate wake.​—Yohane 15:10.

4 Motero, kuti tiyende monga anayendera Yesu, timafunika kuonetsetsa zochitika za Mtsogoleri Wamkuluyu n’kumazitsanzira mosamala. Mafunso ofunika kuwaganizira pankhaniyi ndi awa: Kodi Kristu amatitsogolera bwanji masiku ano? Kodi kutsanzira mayendedwe ake kuyenera kutithandiza bwanji? Kodi ubwino wotsatira chitsanzo cha Yesu Kristu n’ngotani?

Mmene Kristu Amatsogolerera Otsatira Ake

5. Kodi Yesu asanapite kumwamba anawalonjeza zotani otsatira ake?

5 Yesu Kristu ataukitsidwa koma asanapite kumwamba, anaonekera kwa ophunzira ake n’kuwapatsa ntchito yofunika kwambiri. Iye anati: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse.” Panthawi imeneyi Mtsogoleri Wamkuluyu anawalonjezanso kuti adzakhala nawo pokwaniritsa ntchitoyi ndipo anawauza kuti: “Onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.” (Mateyu 28:19, 20) Kodi Yesu Kristu ali nawo bwanji otsatira ake m’nthawi ino ya chimaliziro cha nthawi ya pansi pano?

6, 7. Kodi Yesu amatitsogolera motani ndi mzimu woyera?

6 Yesu anati: “Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzam’tuma m’dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.” (Yohane 14:26) Mzimu woyera umatumizidwa m’dzina la Yesu n’kumatitsogolera ndi kutilimbikitsa masiku ano. Umatitsegula maso mwauzimu ndipo umatithandiza kumvetsa ngakhale zinthu “zakuya za Mulungu.” (1 Akorinto 2:10) Komanso, makhalidwe a Mulungu monga “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso” ndiwo “chipatso cha mzimu” umenewu. (Agalatiya 5:22, 23) Tingathe kukhala ndi makhalidwe amenewa mothandizidwa ndi mzimu woyera.

7 Tikamaphunzira Malemba n’kumayesetsa kutsatira zimene tikuphunzira, mzimu wa Yehova umatithandiza kukula mu nzeru, kuzindikira, kudziwa zinthu, kuweruza, ndiponso kuganiza mozama. (Miyambo 2:1-11) Mzimu woyera umatithandizanso kupirira mayesero. (1 Akorinto 10:13; 2 Akorinto 4:7; Afilipi 4:13) Akristu amalimbikitsidwa kuti ‘adzikonzere okha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero.’ (2 Akorinto 7:1) Kodi mopanda kuthandizidwa ndi mzimu woyera tingathedi kukhala moyo wogwirizana ndi malamulo a Mulungu okhudza kukhala oyera? Njira imodzi imene Yesu amatitsogolera masiku ano ndiyo kudzera mwa mzimu woyera, umene Yehova Mulungu anavomereza Mwana wakeyu kuugwiritsa ntchito.​—Mateyu 28:18.

8, 9. Kodi Kristu amatitsogolera motani kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”?

8 Taganizirani njira ina imene Kristu amatsogolera mpingo masiku ano. Ponena za kukhalapo kwake ndiponso za mapeto a dongosolo lino la zinthu, Yesu anati: “Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anam’khazika woyang’anira banja lake, kuwapatsa zakudya panthawi yake? Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzam’peza iye alikuchita chotero. Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzam’khazika iye woyang’anira zinthu zake zonse.”​—Mateyu 24:3, 45-47.

9 “Mbuye” wotchulidwa mlembali ndi Yesu Kristu. “Kapolo” ndi gulu la Akristu odzozedwa omwe ali padziko lapansi. Gulu la kapololi linapatsidwa ntchito yosamalira zinthu zonse za Yesu za padziko lapansi ndiponso yopereka chakudya chauzimu panthawi yake. Kagulu kakang’ono ka oyang’anira odziwa bwino ntchito yawo kamene kali m’gulu la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kamatchedwa Bungwe Lolamulira, ndipo ndiko kamaimira gulu lonse la kapolo. Bungweli limayang’anira ntchito ya padziko lonse yolalikira Ufumu ndiponso limaonetsetsa kuti chakudya chauzimu chikuperekedwa panthawi yake. Motero Kristu amatsogolera mpingo kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” wodzozedwa ndi mzimu, komanso kudzera mwa Bungwe Lolamulira la kapoloyu.

10. Kodi akulu tiyenera kumawaona motani ndipo n’chifukwa chiyani?

10 Kristu amatitsogoleranso kudzera mwa “mphatso mwa amuna,” kapena kuti akulu a mumpingo, kapenanso kuti oyang’anira. Iwowa anaperekedwa “kuti akonzere oyera mtima ku ntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Kristu.” (Aefeso 4:8, 11, 12, NW) Ponena za anthu amenewa lemba la Ahebri 13:7 limati: “Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mawu a Mulungu; ndipo poyang’anira chitsiriziro cha mayendedwe awo mutsanze chikhulupiriro chawo.” Akulu amatsogolera mumpingo. Pakuti amatsanzira Kristu Yesu, chikhulupiriro chawo n’chofunika kuchitsanzira. (1 Akorinto 11:1) Tingasonyeze kuti timayamikira kuti panakonzedwa zoti pakhale akulu pomawamvera akuluwa omwe ali “mphatso mwa amuna.”​—Ahebri 13:17.

11. Kodi Kristu amatsogolera otsatira ake masiku ano m’njira zotani, ndipo kodi timafunika kutani kuti tiyende monga iye anayendera?

11 Inde, Yesu Kristu amatsogolera otsatira ake masiku ano kudzera mwa mzimu woyera, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ndiponso akulu mumpingo. Kuti tiyende mmene Kristu anayendera timafunika kumvetsa njira imene iye amatitsogolera kenaka n’kumamvera utsogoleriwu. Timafunikanso kutsanzira mayendedwe ake. Mtumwi Petro analemba kuti: “Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Kristu anamva zowawa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake.” (1 Petro 2:21) Kodi kutsatira chitsanzo changwiro cha Yesu kuyenera kutithandiza motani?

Gwiritsirani Ntchito Mphamvu Zanu Mosamala

12. Kodi ndi mbali zotani za chitsanzo cha Kristu zimene makamaka akulu mumpingo ayenera kuziganizira?

12 Ngakhale kuti Yesu anapatsidwa mphamvu zoposa za wina aliyense kuchokera kwa Atate wake, iye ankazigwiritsa ntchito mosamala. Anthu onse mumpingo, makamaka oyang’anira, ayenera kuyesetsa kuti ‘kulolera kwawo kudziwike kwa anthu onse.’ (Afilipi 4:5; 1 Timoteo 3:2, 3, NW) Popeza kuti akulu ali ndi mphamvu pa zinthu zina mumpingo, amafunika kutsatira mapazi a Kristu pogwiritsira ntchito mphamvuzi.

13, 14. Kodi akulu angatsanzire bwanji Kristu akamalimbikitsa ena kutumikira Mulungu?

13 Yesu ankawamvetsa ophunzira ake pa zofooka zawo. Iye sankawauza kuchita zinthu zimene iwo sakanakwanitsa. (Yohane 16:12) Yesu anawalimbikitsa otsatira ake mosawaopseza kuti ‘ayesetse’ kuchita chifuniro cha Mulungu. (Luka 13:24) Anatero powatsogolera ndiponso powalimbikitsa kuchita zinthu mwamtima wonse. Nawonso akulu mumpingo masiku ano saopseza anthu kuti azitumikira Mulungu chifukwa cha manyazi. Koma amawalimbikitsa kuti azitumikira Yehova chifukwa chokonda Yehovayo, Yesu, ndiponso anthu anzawo.​—Mateyu 22:37-39.

14 Yesu sanatengerepo mwayi pa mphamvu zimene Mulungu anam’patsa n’kumangolamulira ena pa zochita zawo zonse. Sankakhwimitsa zinthu kapena kuchulukitsa malamulo. Ankangolimbikitsa anthuwo kuchita zinthu mochoka pansi pamtima, powathandiza kumvetsa mfundo zofunikira za m’malamulo amene anaperekedwa kudzera mwa Mose. (Mateyu 5:27, 28) Potsanzira Yesu Kristu, akulu amayesetsa kupewa kukhazikitsa malamulo opanga okha kapena kukakamira maganizo awo. Pankhani ya zovala, kudzikongoletsa ndiponso zosangalatsa, akulu amayesetsa kuwafika ena pamtima ndi mfundo za m’Baibulo, monga zimene zili pa Mika 6:8; 1 Akorinto 10:31-33; ndi 1 Timoteo 2:9, 10.

Muzimvetsa Ena Ndiponso Muziwakhululukira

15. Kodi Yesu anatani nawo ophunzira ake pa zolephera zawo?

15 Kristu anatisiyira chitsanzo cha zimene iyeyo ankachita pa zolakwa ndi zophophonya za ophunzira ake. Taganizirani nkhani ziwiri izi zomwe zinachitika usiku pa tsiku lomaliza Yesu ali padziko lapansi monga munthu. Atafika ku Getsemane, Yesu “anatenga pamodzi ndi Iye Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane” n’kuwauza kuti ‘adikire.’ Kenaka, “anapita m’tsogolo pang’ono, nagwa pansi, napemphera.” Atabwerera ‘anawapeza iwo ali m’tulo.’ Kodi Yesu anatani? Iye anati: “Mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.” (Marko 14:32-38) M’malo mowakalipira kwambiri ophunzira ake atatuwo, iye anawamvetsa. Usiku womwewu, Petro anakana Yesu katatu. (Marko 14:66-72) Kodi pambuyo pake Yesu anam’chitira zotani Petro? “Ambuye anauka ndithu, naonekera kwa Simoni [Petro].” (Luka 24:34) Baibulo limati: “Anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo.” (1 Akorinto 15:5) M’malo momukwiyira mtumwi wake wolapayo, Yesu anam’khululukira n’kumulimbikitsa. Pambuyo pake Yesu anam’patsa Petro maudindo aakulu kwambiri kusonyeza kumukhulupirira.​—Machitidwe 2:14; 8:14-17; 10:44, 45.

16. Kodi tingayende bwanji monga anayendera Yesu pamene Akristu anzathu atikhumudwitsa kapena kutilakwira m’njira inayake?

16 Okhulupirira anzathu akamatikhumudwitsa kapena kutilakwira m’njira inayake chifukwa cha kupanda ungwiro kwawo, kodi ifenso sitiyenera kuwamvetsa ndiponso kuwakhululukira monga ankachitira Yesu? Petro analimbikitsa okhulupirira anzake kuti: “Khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa; osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso.” (1 Petro 3:8, 9) Komano tingatani ngati munthu wina akuchita zinthu zimene Yesu sakanatichitira, ndipo sakufuna kutimvetsa ndi kutikhululukira? Ngakhale zitatero ifeyo tiyenera kuyesetsa kutsanzira Yesu ndi kuchita zinthu zimene Yesu akanachita.​—1 Yohane 3:16.

Ikani Zinthu Zauzimu Patsogolo

17. N’chiyani chimasonyeza kuti Yesu ankaona kuti kuchita chifuniro cha Mulungu ndiko chinthu chofunika kuposa chilichonse pa moyo wake?

17 Pali njira inanso imene tiyenera kuyenda monga anayendera Yesu Kristu. Yesu ankaona kuti kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kunali chinthu chofunika kuposa china chilichonse pa moyo wake. Atalalikira kwa mkazi wachisamariya pafupi ndi mzinda wa Sukari ku Samariya, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yohane 4:34) Kuchita chifuniro cha Atate wake kunam’limbikitsa Yesu; kunkam’sangalatsa ndiponso kumupatsa mphamvu ngati chakudya. N’zachidziwikire kuti ngati titatsanzira Yesu polimbikira kuchita chifuniro cha Mulungu nafenso tingakhale osangalala.

18. Kodi ndi madalitso otani amene amabwera chifukwa cholimbikitsa ana kuchita utumiki wa nthawi zonse?

18 Makolo akamalimbikitsa ana awo kuchita utumiki wa nthawi zonse, iwowo ndi anawo amadalitsidwa kwambiri. Bambo wina wa ana aamuna awiri amapasa ankawalimbikitsa anawo, kuyambira adakali ana, kuti adzachite upainiya. Atamaliza sukulu, anawo anakhaladi apainiya. Poganizira chisangalalo chimene bamboyu wakhala nacho, iye analemba kuti: “Ana athu sanatikhumudwitse ayi. Tingathe kunena moyamikira kuti, “ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova.” (Salmo 127:3) Ndipo kodi ana amapindula motani pochita utumiki wa nthawi zonse? Mayi wina wa ana asanu anati: “Upainiya wathandiza ana anga onse kukonda kwambiri Yehova, kutha kuphunzira paokha nthawi zonse, kulinganiza bwino nthawi yawo, ndiponso kutsogoza zinthu zauzimu pa zochita zawo zonse. Ngakhale kuti onsewo anayenera kusintha khalidwe lawo m’njira zosiyanasiyana kuti afike pokhala anthu otere, palibe amene amanong’oneza bondo posankha kuyenda m’njira imeneyi.”

19. Kodi achinyamata ayenera kukhala ndi zolinga zanzeru zotani zokhudza tsogolo lawo?

19 Kodi ananu, zolinga zanu za m’tsogolo n’zotani? Kodi mukulimbana ndi zofuna kuchita maphunziro enaake apamwamba? Kapena mukuyesetsa kuchita zotheka kuti ntchito yanu idzakhale ya utumiki wa nthawi zonse? Paulo analimbikitsa kuti: “Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.” Ndipo anawonjezera kunena kuti: “Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye n’chiyani.”​—Aefeso 5:15-17.

Khalani Okhulupirika

20, 21. Kodi Yesu anali wokhulupirika m’njira yotani, ndipo kodi tingatsanzire motani kukhulupirika kwake?

20 Kuti tiyende monga mmene Yesu anayendera timafunika kutsanzira kukhulupirika kwake. Ponena za kukhulupirika kwa Yesu Baibulo limati: “Pokhala nawo maonekedwe a Mulungu, sanachiyesa cholanda kukhala wofana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa m’maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa” ya pamtengo wozunzirapo. Mokhulupirika, Yesu anachita zinthu zotsimikizira kuti Yehova ndiye ayenera kulamulira ndipo anatero pochita chifuniro cha Mulungu chokhudza iyeyo. Yesu anakhulupirika mpaka kufa imfa ya pa mtengo wozunzirapo. Ifenso tiyenera ‘kukhala ndi mtima womwewo’ pokhulupirika kuchita chifuniro cha Mulungu.​—Afilipi 2:5-8.

21 Yesu anasonyezanso kukhulupirika kwa atumwi ake okhulupirika. Ngakhale kuti iwo anali ndi zofooka ndiponso anali opanda ungwiro, Yesu “anawakonda kufikira chimaliziro.” (Yohane 13:1) Ifenso tisalole kuti kupanda ungwiro kwa abale athu kutipatse mtima wokonda kuwatola zifukwa.

Pitirizani Kutsatira Chitsanzo cha Yesu

22, 23. Kodi ubwino wotsatira chitsanzo cha Yesu n’ngotani?

22 Poti ndife anthu opanda ungwiro, inde sitingathe kutsatira ndendende mapazi a Yesu, yemwe ali Chitsanzo chathu changwiro. Komabe, tingayesetse kutsatira mapazi ake mosamala. Kuti titero timafunikira kuzindikira ndiponso kumvera ulamuliro wa Kristu ndi kupitirizabe kutsatira chitsanzo chake.

23 Kutsanzira Kristu kumabweretsa madalitso ambiri. Moyo wathu umakhala n’cholinga komanso umakhala wosangalatsa chifukwa choganizira kwambiri kuchita zofuna za Mulungu osati zathu. (Yohane 5:30; 6:38) Timakhala ndi chikumbumtima chabwino ndipo mayendedwe athu amapereka chitsanzo kwa ena. Yesu anaitana anthu onse olema ndi othodwa kuti apite kwa iye kukapeza mpumulo pa miyoyo yawo. (Mateyu 11:28-30) Tikamatsatira chitsanzo chake, nafenso tingathe kupatsa ena mpumulo pocheza nawo. Motero, tiyeni tipitirize kuyenda monga Yesu anayendera.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi Kristu amatsogolera bwanji otsatira ake masiku ano?

• Kodi akulu angatsatire bwanji utsogoleri wa Kristu pogwiritsira ntchito mphamvu zimene Mulungu wawapatsa?

• Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pankhani ya zolephera za ena?

• Kodi achinyamata angatsogoze bwanji zinthu za Ufumu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Akulu mumpingo amatithandiza kutsatira utsogoleri wa Kristu

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Kodi achinyamata, mukupanga zolinga zotani kuti mudzakhale ndi moyo wachikristu wosangalatsa?