Chitsanzo cha Makolo Anga Chinandilimbitsa
Mbiri ya Moyo Wanga
Chitsanzo cha Makolo Anga Chinandilimbitsa
YOSIMBIDWA NDI JANEZ REKELJ
M’chaka cha 1958, ine ndi mkazi wanga, Stanka tinali m’mapiri a Karawanken Alps omwe ali m’malire a dziko la Yugoslavia ndi Austria. Timayesa kuthawira ku dziko la Austria. Zimenezi zinali zoopsa, chifukwa asilikali a ku Yugoslavia okhala ndi mfuti olondera malire sanali kulola aliyense kudutsa. Tikuyenda, tinafika pa chiphedi chakuya kwambiri. Ine ndi Stanka tinali tisanaonepo dera la mapirilo la dziko la Austria. Tinalowera chakum’mawa mpaka tinafika pamalo ena omwe anali otsetsereka a miyala ndi mchenga. Titadzimangirira pa lona amene tinali titanyamula tinatsetsereka pa phiripo osadziwa chimene chitichitikire.
NDIFOTOKOZE kaye kuti zinatani kuti zinthu zifike pamenepa ndiponso mmene makolo, chifukwa cha kukhulupirika kwawo, anandilimbikitsira kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova panthawi yovuta.
Ndinakulira ku Slovenia, dziko laling’ono lomwe masiku ano lili m’chigawo cha pakati cha Ulaya. Dzikoli lili m’mapiri a Alps a ku Ulaya, ndipo kumpoto kwake kuli dziko la Austria, kumadzulo kuli Italy, kumwera kuli Croatia komanso kum’mawa kuli Hungary. Koma nthawi imene makolo anga, a Franc ndi a Rozalija Rekelj, anabadwa, dziko la Slovenia linali mbali ya Ufumu wa Austria ndi Hungary. Nkhondo yoyamba yapadziko lonse itatha, dziko la Slovenia linakhala mbali ya dziko latsopano lotchedwa Ufumu wa anthu a ku Serbia, Croatia ndi Slovenia. Mu 1929 dzina la dzikoli linasinthidwa kukhala Yugoslavia, lomwe limatanthauza “Slavia wa Kumwera.” Ndinabadwa pa January 9, m’chaka chimenecho, m’mudzi wa Podhom, pafupi ndi malo okongola kumene kuli nyanja ya Bled.
Amayi analeredwa m’banja lachikatolika. Abambo awo ena aang’ono anali wansembe, ndipo atatu mwa azakhali awo anali avirigo. Amayi ankafuna kwambiri kukhala ndi Baibulo lawo, kuliwerenga ndi kulimvetsa. Koma bambo sanali kukonda zachipembedzo. Iwo anaipidwa kwambiri ndi zimene chipembedzo chinachita pa Nkhondo Yaikulu ya mu 1914 mpaka 1918.
Kuphunzira Kwanga Choonadi
Patapita nthawi nkhondo itatha, mbale wa amayi anga, Janez Brajec ndi mkazi wake Ančka, anakhala Ophunzira Baibulo amene panopa amatchedwa Mboni za Yehova. Panthawi imeneyo ankakhala ku Austria. Kuyambira cha mu 1936 kupita m’tsogolo, nthawi zambiri Ančka ankabwera kudzaona amayi. Iye anapatsa amayi Baibulo, limene iwo analiwerenga mwamsanga limodzi ndi magazini a Nsanja ya Olonda ndi mabuku ena ofotokoza Baibulo a m’Chisiloveniya. Kenako, Hitler analanda dziko la Austria mu 1938, ndipo Janez ndi Ančka anabwereranso ku Slovenia. Ndikukumbukira kuti iwo anali banja lophunzira ndi lanzeru ndiponso lokonda Yehova ndi mtima wonse. Nthawi zambiri ankakambirana choonadi cha m’Baibulo ndi amayi. Zimenezi zinalimbikitsa amayi kudzipereka kwa Yehova moti anabatizidwa mu 1938.
Amayi atasiya kuchita miyambo yosemphana ndi Malemba, monga kukondwerera Khirisimasi; atasiyanso kudya masoseji ophatikiza ndi magazi, ndiponso atatentha mafano onse omwe tinali nawo, anthu a m’dera lomwe tinkakhala sanasangalale. Posapita nthawi anayamba kuwatsutsa. Azakhali a amayi anga omwe anali avirigo, analemba kalata n’cholinga choti amayi asinthe maganizo awo kuti abwerera kwa Mariya ndi ku tchalitchi. Koma pamene amayi analembera azakhaliwa ndi kuwapempha kuti ayankhe mafunso ena a m’Baibulo, sanawayankhe. Agogo anga aamuna nawonso ankawatsutsa kwambiri amayi. Agogo sanali munthu wankhanza, koma achibale athu ndiponso anthu a m’dera lomwe tinkakhala anali kuwakakamiza kwambiri. Chifukwa cha zimenezi, nthawi zambiri iwo ankawononga mabuku ofotokoza Baibulo a mayi anga koma Baibulo la amayi sanalikhudze. Agogo anachita kugwada pochonderera amayi kuti abwerere ku tchalitchi. Iwo anafika mpaka powaopseza ndi mpeni. Koma bambo anga anauza agogo mwamphamvu kuti salola kuti iwo azichita zimenezo.
Bambo anapitiriza kuchirikiza amayi paufulu wawo wa kuwerenga Baibulo ndi kusankha zomwe ankafuna kukhulupirira. Kenako iwonso anabatizidwa mu 1946. Nditaona mmene Yehova analimbitsira amayi kukhala opanda mantha pochirikiza choonadi ngakhale anali kutsutsidwa, ndiponso mmene Yehova anawadalitsira chifukwa cha chikhulupiriro chawo, zinandilimbikitsa kuti
ndikhale paubwenzi ndi Mulungu. Ndinapindulanso kwambiri ndi chizolowezi cha amayi chondiwerengera mofuula Baibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo.Amayi ankakambirananso nthawi yaitali ndi mng’ono wawo, Marija Repe. M’kupita kwa nthawi ine ndi azakhali anga a Marija tinabatizidwa tsiku limodzi pakati pa mwezi wa July mu 1942. Mbale anabwera kudzakamba nkhani mwachidule ndipo tinabatizidwa panyumba yathu m’bafa yaikulu yamatabwa.
Ntchito Yakalavulagaga Panthawi ya Nkhondo Yachiwiri Yapadziko Lonse
Mu 1942, nkhondo yachiwiri yapadziko lonse ili m’kati, mayiko a Germany ndi Italy analanda dziko la Slovenia ndipo mayiko awiriwa kuphatikizapo dziko la Hungary anagawana dzikoli. Makolo anga anakana kulowa chipani cha Volksbund cha Anazi. Kusukulu ndinakana kunena kuti “Hitler Mpulumutsi Wathu.” Zikukhala ngati aphunzitsi anga anadziwitsa akuluakulu zimenezi.
Anatikweza sitima ya pamtunda kupita ku nyumba ya malinga yomwe inali ku Bavaria pafupi ndi mudzi wa Hüttenbach. Malo amenewa ankawagwiritsa ntchito monga ndende yolangirako anthu. Abambo anakonza zoti ndizikhala ndi banja la munthu amene ankaphika buledi ndiponso kuti ndizigwira naye ntchito limodzi. Panthawi imeneyi, ndinaphunzira ntchito yophika buledi, ndipo m’tsogolo ntchito imeneyi inandithandiza kwambiri. M’kupita kwa nthawi, banja lathu lonse (kuphatikizapo azakhali anga a Marija ndi banja lawo) anatisamutsira kundende ina ku Gunzenhausen.
Nkhondo itatha, ndinafuna kutsagana ndi gulu lina kupita komwe kunali makolo anga. Usiku ndisanachoke, bambo anafika mwadzidzidzi. Sindikudziwa kuti zikanandithera bwanji ndikanapita ndi gululi, chifukwa linali lokayikitsa. Apanso ndinaona kuti Yehova amandikonda chifukwa anagwiritsa ntchito makolo anga kunditeteza ndi kundiphunzitsa. Ine ndi bambo tinayenda kwa maola atatu kuti tikakumane ndi banja lathu. Mu June 1945, tonse tinabwerera ku nyumba.
Nkhondo itatha, achipani cha Chikomyunizimu omwe anali kutsogoleredwa ndi Pulezidenti Josip Broz Tito anayamba kulamulira Yugoslavia. Chifukwa cha zimenezi, zinthu zinakhalabe zovuta kwa Mboni za Yehova.
Mu 1948 mbale anabwera kuchokera ku Austria ndipo anadzadyera kwathu. Kulikonse kumene anapita, apolisi anali kum’tsatira ndipo anagwira abale omwe anali kucheza naye. Abambo nawonso anawagwira chifukwa chomulandira ndi kulephera kuuza apolisi za iye, ndipo anakhala kundende zaka ziwiri. Imeneyi inali nthawi yovuta kwambiri kwa amayi. Inali yovuta chifukwa chakuti bambo panalibe, komanso chifukwa chakuti amayiwo ankadziwa kuti nthawi ina iliyonse ineyo ndi mng’ono wanga tidzayesedwa pa nkhani yolowa usilikali.
Nthawi Imene Ndinakhala M’ndende ku Macedonia
Mu November 1949, anandiitana kuti ndikalowe usilikali. Ndinapita kukaonekera ndi kufotokoza chimene ndinakanira kulowa usilikali malinga ndi zimene ndimakhulupirira. Akuluakulu a boma sanandimvere ndipo anandikweza sitima ya pamtunda yomwe inali ndi anthu olembedwa kumene usilikali yopita ku Macedonia, mbali ina ya dziko la Yugoslavia.
Kwa zaka zitatu, sindinalankhule ndi a m’banja mwathu kapena abale ndipo ndinalibe buku lililonse ngakhale Baibulo. Zinali zovuta kwambiri. Kusinkhasinkha za Yehova ndi chitsanzo cha Mwana wake, Yesu Kristu, n’kumene kunandithandiza ndiponso chitsanzo cha makolo anga chinandilimbitsa. Ndipo, kupempherera nyonga nthawi zonse kunandithandiza kuti ndisataye mtima.
M’kupita kwa nthawi, ananditumiza kundende ya ku Idrizovo, pafupi ndi Skopje. Mu ndende imeneyi, akaidi ankagwira ntchito zosiyanasiyana. Poyamba, ndinkagwira ntchito yoyeretsa ndiponso ya umesenjala m’maofesi. Ngakhale kuti nthawi zambiri mkaidi wina amene poyamba anali wa polisi ankandizunza kwambiri, ndinkagwira bwino ntchito ndi wina aliyense kuphatikizapo alonda, akaidi ngakhale mkulu wa ndende.
Nthawi ina, ndinamva kuti m’ndendemo ankafuna munthu wophika buledi. Patapita masiku ochepa, mkulu wa ndende anabwera kudzaitana mayina. Iye anayenda kutsata mzera n’kudzaima patsogolo panga, ndipo anandifunsa kuti: “Kodi umadziwa kuphika buledi?” Ndinayankha kuti: “Inde bwana.” Iye anati: “Mawa nthawi ya kum’mawa ubwere kumene timaphikira buledi.” Mkaidi amene ankandizunza uja nthawi zambiri anali kudutsa kumene tinali kuphikira buledi koma palibe chimene akanachita. Ndinagwira ntchito kumeneku kuyambira mu February mpaka July mu 1950.
Ndiyeno anandisamutsira kundende yotchedwa Volkoderi, kumwera kwa Macedonia, pafupi ndi nyanja ya Prespa. Popeza mzinda wa Otešovo unali pafupi ndi kunyumba, ndinkatha kulembera a kunyumba makalata. Ndinkagwira ntchito yopanga msewu ndi gulu la akaidi, koma nthawi zambiri ndinkagwira yophika buledi, imene inali kundipeputsira zinthu. Anandimasula mu November chaka cha 1952.
Nthawi imene ndinachoka ku Podhom, mpingo unapangidwa m’deralo. Poyamba, mpingowu unkasonkhanira m’nyumba ya alendo mu mzinda wa Spodnje Gorje. Patapita nthawi, bambo anapereka chipinda cha nyumba yathu kuti mpingo uzichitiramo misonkhano. Ndinali wosangalala kusonkhana nawo nditachoka ku Macedonia. Ndinayambitsanso chibwenzi changa ndi Stanka, amene ndinakumana naye ndisanapite kundende. Pa April 24, 1954, tinakwatirana. Koma sipanapite nthawi yaitali kuti andimangenso.
Nthawi Imene Ndinakhala M’ndende ku Maribor
Mu September 1954, anandiitananso kuti ndikalowe usilikali. Panthawiyi, anandilamula kukakhala kundende zaka zoposa zitatu ndi theka. Ndende imeneyi inali ku Maribor, mzinda womwe uli kum’mawa kwa Slovenia. Nditangopeza mpata, ndinagula mapepala ndi mapensulo. Ndinalemba zonse zimene ndinakumbukira monga malemba, mfundo zochokera mu Nsanja ya Olonda ndi m’mabuku ena achikristu. Ndinkawerenga mfundo zomwe ndinalembazo ndipo ndinkawonjezera zina zomwe ndinkakumbukira. Mapeto ake, buku lonse linadzaza ndipo zimenezi zinandithandiza kuika maganizo anga pa choonadi ndi kukhalabe wolimba mwauzimu. Pemphero ndi kusinkhasinkha zinandithandizanso kwambiri kukhala wolimba mwauzimu moti ndinakhala wolimba mtima kwambiri pouza ena choonadi.
Panthawi imeneyi, ankadilola kulandira kalata imodzi pa mwezi ndiponso kucheza ndi odzandiona kwa mphindi 15 kamodzi pa mwezi. Stanka ankayenda usiku wonse pa sitima yapamtunda kuti afike kundende m’mawa kudzandiona. Ndipo anali kubwerera tsiku lomwelo. Maulendo amenewa anandilimbikitsa kwambiri. Ndiyeno ndinaganizira njira yopezera Baibulo. Ine ndi Stanka tinakhala moyang’anana pa thebulo, tili ndi mlonda wotiyang’anira. Pamene mlonda anayang’ana kumbali, ndinalowetsa kalata m’chikwama cha Stanka. Ndipo m’kalatayo ndinam’pempha kuika Baibulo m’chikwama chake ulendo womwe adzabwerenso kudzandiona.
Stanka ndi makolo anga poona kuti zimenezi zinali zoopsa kwambiri, anathothola Baibulo la Malemba Achigiriki Achikristu ndi kutenga masamba ake n’kuwaika m’mabanzi. Mwa njira imeneyi ndinalandira Baibulo lomwe ndinkafuna. Ndipo mwa
njira imodzimodziyi, ndinalandiranso magazini a Nsanja ya Olonda olembedwa pamanja ndi Stanka. Ndikangolandira ndinkalembanso kope lina ndi kuwononga loyambalo kotero kuti munthu aliyense amene angadzapeze nkhanizo asadziwe kumene ndinazichotsa.Chifukwa cha kulimbikira kulalikira, akaidi anzanga ankanena kuti zimenezi zindibweretsera mavuto. Panthawi ina, ndinali kukambirana mwamphamvu za m’Baibulo ndi mkaidi mnzanga. Kenako, tinangomva mlonda akutsegula chitseko ndi kiyi, ndipo analowa. Nthawi yomweyo ndinaganiza kuti andiika mu chipinda chandekha. Koma cholinga cha mlondayo sichinali chimenecho. Iye anali atatimva tikukambirana ndipo anafuna kukhala nawo pa kukambiranako. Atakhutira ndi mayankho a mafunso ake, anachoka ndi kukhoma chitseko.
M’mwezi womaliza wokhala kundende, mkulu yemwe ankayang’anira ntchito yosintha akaidi anandithokoza kwambiri chifukwa cha kulimbika kwanga pa choonadi. Ndinaona kuti imeneyi inali mphoto yanga yabwino kwambiri chifukwa cha khama langa podziwitsa ena dzina la Yehova. Mu May 1958, ananditulutsanso m’ndende.
Tinathawira ku Austria, Kenako ku Australia
Mu August 1958, amayi anga anamwalira. Iwo anali atadwala kwa nthawi yaitali. Ndiyeno, mu September 1958, ndinaitanidwanso kachitatu kulowa usilikali. Usiku womwewo ineyo ndi Stanka tinapanga chosankha chachikulu, ndipo n’chifukwa chake tinadutsa malire mwa njira yomwe ndaifotokoza koyambirira ija. Sitinauze munthu aliyense, tinalongedza zikwama ziwiri ndi lona ndipo tinatulukira pawindo. Tinapita ku malire a dziko la Austria omwe anali kumwera kwa phiri la Stol. Nthawi imeneyo tinaona kuti Yehova akutitsogolera ataona kuti tikufunikiradi mpumulo.
Akuluakulu a boma la Austria anatitumiza ku msasa wa anthu othawa kwawo pafupi ndi Salzburg. Miyezi isanu ndi umodzi yomwe tinali kumeneko, tinali kukhala mu msasa nthawi yochepa chifukwa chakuti nthawi zambiri tinali kukhala ndi Mboni zakomweko. Anthu ena mu msasa anadabwa kwambiri kuona mmene tinakhalira ndi mabwenzi mofulumira. Panthawi imeneyi m’pamene tinakapezekako ku msonkhano wathu woyamba. Ndiponso kwa nthawi yoyamba tinatha kulalikira nyumba ndi nyumba momasuka. Nthawi yochoka itakwana tinavutika kwambiri kusiyana ndi mabwenzi okondedwa amenewa.
Akuluakulu a boma la Austria anatipatsa mwayi woti tisamukire ku Australia. Tinali tisanaganizeko zoti tingadzapite kutali choncho. Tinayenda pasitima ya pamtunda kupita ku Genoa m’dziko la Italy. Kenako tinakwera sitima ya pamadzi yopita ku Australia. Pomalizira tinakhazikika mu mzinda wa Wollongong, ku New South Wales. Tili kumeneku, mwana wathu Philip anabadwa pa March 30, 1965.
Kukhala kwathu ku Australia kwatsegula mipata yambiri ya utumiki. Zimenezi zaphatikizapo mwayi wolalikira kwa anthu ena amene anachokera ku madera omwe poyamba ankatchedwa Yugoslavia. Timayamikira kwambiri madalitso a Yehova, kuphatikizapo mwayi woti tikum’tumikira monga banja logwirizana. Philip ndi mkazi wake Susie, ali ndi mwayi wotumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Australia. Ndipo analinso ndi mwayi wokhala zaka ziwiri pa ofesi ya nthambi ku Slovenia.
Mosasamala kanthu za mavuto obwera chifukwa cha ukalamba ndi kudwaladwala, ine ndi mkazi wanga tikupitirizabe kutumikira Yehova mosangalala. Ndikuyamikira kwambiri chitsanzo chabwino cha makolo anga. Chitsanzo chimenechi chimandilimbitsabe ndi kundithandiza kuchita zimene mtumwi Paulo ananena. Iye anati: “Kondwerani m’chiyembekezo, pirirani m’masautso; limbikani chilimbikire m’kupemphera.”—Aroma 12:12.
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Makolo anga cha ku mapeto kwa zaka za m’ma 1920
[Chithunzi patsamba 17]
Mayi anga, ali kumanja, ndi Ančka, amene anawaphunzitsa choonadi
[Chithunzi patsamba 18]
Ine ndi mkazi wanga, Stanka, titangokwatirana kumene
[Chithunzi patsamba 19]
Mpingo umene unkasonkhana m’nyumba yathu mu 1955
[Chithunzi patsamba 20]
Ine ndi mkazi wanga, mwana wathu Philip ndi mkazi wake, Susie