Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Dikirani” Chifukwa Nthawi ya Chiweruzo Yafika

“Dikirani” Chifukwa Nthawi ya Chiweruzo Yafika

“Dikirani” Chifukwa Nthawi ya Chiweruzo Yafika

Mfundo zimene zili m’nkhani yophunzira ino zachokera m’bulosha lakuti Dikirani! Bulosha limeneli linatulutsidwa pamisonkhano yachigawo imene inachitika padziko lonse mu 2004 ndi 2005.

“Dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.”​—MATEYU 24:42.

1, 2. Kodi Yesu moyenerera anayerekezera kubwera kwake ndi chiyani?

KODI mungachite chiyani mutadziwa kuti mbala ikuyendayenda mwakachetechete m’dera lanu kufunafuna nyumba yoti ithyole? Kuti muteteze okondedwa anu ndi katundu wanu, mudzakhala tcheru. Ndipo mudzachita zimenezi chifukwa chakuti mbala situmiza kalata yonena nthawi imene iti ibwere. Koma imabwera mwakachetechete ndiponso modzidzimutsa.

2 Nthawi zingapo, Yesu anagwiritsa ntchito mmene mbala imachitira monga fanizo. (Luka 10:30; Yohane 10:10) Ponena za zinthu zimene zidzachitika nthawi ya mapeto ndiponso zimene zidzachitika iye asanabwere kupereka chiweruzo, Yesu anapereka chenjezo ili: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake lakufika Ambuye wanu. Koma dziwani ichi, kuti mwininyumba akadadziwa nthawi iti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe.” (Mateyu 24:42, 43) Chotero, Yesu anayerekezera kubwera kwake ndi kubwera kodzidzimutsa kwa mbala.

3, 4. (a) Kodi tifunika kuchita chiyani kuti timvere chenjezo la Yesu lonena za kubwera kwake? (b) Kodi pakubuka mafunso otani?

3 Fanizoli linali loyenera, chifukwa tsiku lenileni la kubwera kwa Yesu silikudziwika. Poyamba, mu ulosi umenewu, Yesu anati: “Koma za tsiku ilo ndi nthawi yake sadziwa munthu aliyense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyu 24:36) N’chifukwa chake, Yesu analangiza omvera ake kuti: “Khalani inunso okonzekeratu.” (Mateyu 24:44) Amene adzamvera chenjezo la Yesu adzakhala okonzekera, akhalidwe labwino, mosasamala kanthu kuti adzabwera nthawi iti kupereka chiweruzo cha Yehova.

4 Ndiyeno pakubuka mafunso ena ofunika akuti: Kodi chenjezo la Yesu likukhudza anthu akudziko okha, kapena kodi Akristu oona iwonso afunika ‘kudikira’? N’chifukwa chiyani ‘kudikira’ kuli kofunika, ndipo tingachite bwanji zimenezi?

Chenjezo, kwa Ndani?

5. Kodi tikudziwa bwanji kuti mawu akuti “dikirani” akugwira ntchito kwa Akristu oona?

5 N’zoona kuti kubwera kwa Ambuye kudzakhala kodzidzimutsa, monga mbala, kwa anthu akudziko, amene amanyalanyaza chenjezo la chiwonongeko chikubwerachi. (2 Petro 3:3-7) Nanga bwanji kwa Akristu oona? Mtumwi Paulo analembera okhulupirira anzake kuti: “Inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku.” (1 Atesalonika 5:2) Sitikukayikira kuti “tsiku la Ambuye lidzadza.” Kodi zimenezi zimachepetsa kufunika koti tikhale odikira? Taonani kuti anali ophunzira ake amene Yesu anauza kuti: “Pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzabwera.” (Mateyu 24:44) Poyamba, pamene anali kuuza ophunzira ake kupitirizabe kufunafuna Ufumu, Yesu anachenjeza kuti: “Khalani okonzeka . . . chifukwa nthawi imene simulingirira, Mwana wa munthu akudza.” (Luka 12:31, 40) Kodi si zoonekeratu kuti Yesu anali kuganizira otsatira ake pamene anachenjeza kuti: “Dikirani”?

6. N’chifukwa chiyani tifunika ‘kudikira’?

6 Kodi n’chifukwa chiyani tifunika “kudikira” ndiponso ‘kukhala okonzeka’? Yesu anafotokoza kuti: “Adzakhala awiri m’munda; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa: awiri adzakhala opera pamphero; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.” (Mateyu 24:40, 41) Amene akhala okonzeka “adzatengedwa,” kapena kupulumutsidwa, nthawi imene dziko losapembedza Mulungu lidzawonongedwa. Ena “adzasiyidwa” kuti awonongedwe chifukwa akhala akuchita zofuna zawo zadyera pamoyo. Amenewa angaphatikizepo anthu amene poyamba ankadziwa choonadi koma sanadikire.

7. Kodi kusadziwa nthawi imene mapeto adzafika, kumatilola kuchita chiyani?

7 Kusadziwa tsiku lenileni la mapeto a dongosolo lino kumatipatsa mwayi wosonyeza kuti timatumikira Mulungu ndi zolinga zabwino. N’chifukwa chiyani tikunena zimenezi? Mwina mapeto a dzikoli angaoneke kuti akuchedwa kufika. N’zomvetsa chisoni kuti Akristu ena amene amaona choncho alola changu chawo chotumikira Yehova kuzilala. Koma podzipereka kwa Yehova, tinadzikhutula kuti tim’tumikire. Anthu odziwa Yehova amazindikira kuti sangam’sangalatse ngati asonyeza changu nthawi itatha kale. Iye amaona zimene zili mu mtima.​—1 Samueli 16:7.

8. Kodi kukonda Yehova kumatilimbikitsa bwanji kudikira?

8 Chifukwa chakuti timakondadi Yehova, timasangalala kwambiri pochita chifuniro chake. (Salmo 40:8; Mateyu 26:39) Ndipo tikufuna kutumikira Yehova kosatha. Sikuti chifukwa chakuti tifunika kudikira kwa nthawi yotalikirapo kuposa mmene tikuganizira, ndiye kuti lonjezo limeneli n’losafunika. Koposa zonse, timadikira chifukwa tikuyembekeza mwachidwi zimene tsiku la Yehova lidzachita pokwaniritsa chifuno chake. Kufunitsitsa kwathu kusangalatsa Mulungu kumatilimbikitsa kugwiritsa ntchito malangizo a m’Mawu ake ndi kuika zinthu za Ufumu wake patsogolo m’moyo wathu. (Mateyu 6:33; 1 Yohane 5:3) Tiyeni tione mmene kudikira kuyenera kukhudzira zosankha zathu ndiponso mmene timakhalira tsiku ndi tsiku.

Kodi Moyo Wanu Ukulowera Kuti?

9. Kodi n’chifukwa chiyani anthu m’dziko afunika kuzindikira mwamsanga tanthauzo la zimene zikuchitika nthawi yathu ino?

9 Anthu ambiri masiku ano akudziwa kuti mavuto aakulu ndi zinthu zina zoimitsa mutu zikuchitika kawirikawiri. Ndipo sakusangalala ndi kumene moyo wawo ukulowera. Koma kodi akudziwa tanthauzo lenileni la zimene zikuchitika m’dzikoli? Kodi akudziwa kuti tikukhala mu nthawi ya “mathedwe a nthawi ya pansi pano?” (Mateyu 24:3) Kodi iwo akudziwa kuti kuchuluka kwa dyera, chiwawa, ngakhale maganizo oipa, zimadziwikitsa masiku ano kukhala “masiku otsiriza”? (2 Timoteo 3:1-5) Iwo afunika kuzindikira mwamsanga tanthauzo la zinthuzi ndi kuganizira za kumene moyo wawo ukulowera.

10. Kodi tifunika kuchita chiyani kutsimikizira kuti tikudikira?

10 Kodi ifeyo tikuziona bwanji zinthu zimenezi? Tsiku lililonse timafunika kusankha zochita pankhani za ntchito, thanzi lathu, banja lathu ndiponso kulambira kwathu. Timadziwa zimene Baibulo limanena, ndipo timayesa kuzigwiritsa ntchito. N’chifukwa chake, tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndalola nkhawa za moyo kundiiwalitsa zinthu zauzimu? Kodi ndimayendera nzeru za dziko popanga zosankha zanga?’ (Luka 21:34-36; Akolose 2:8) Tifunika kupitiriza kusonyeza kuti timakhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse ndipo sitikhulupirira luntha lathu. (Miyambo 3:5) Mwa njira imeneyi, ‘tidzagwira moyo weniweniwo,’ moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu.​—1 Timoteo 6:12, 19.

11-13. Kodi tikuphunzira chiyani pa zitsanzo zosonyeza zimene zinachitika (a) m’masiku a Nowa? (b) m’masiku a Loti?

11 Baibulo lili ndi zitsanzo zochenjeza zambiri zimene zingatithandize kudikira. Taganizirani zimene zinachitika m’nthawi ya Nowa. Padakali nthawi yochuluka, Mulungu anaonetsetsa kuti chenjezo laperekedwa. Koma anthu sanadziwe kanthu kusiyapo Nowa ndi a m’banja lake. (2 Petro 2:5) Pankhani imeneyi, Yesu anati: “Monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu. Pakuti monga m’masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa, ndipo iwo sanadziwa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.” (Mateyu 24:37-39) Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimenezi? Ngati aliyense wa ife alola zinthu za m’dziko ngakhale ntchito zathu za masiku onse, kulowa m’malo mwa zinthu zauzimu zimene Mulungu watiuza kuika patsogolo, ayenera kuganizira kwambiri mmene moyo wake ulili.​—Aroma 14:17.

12 Ganiziraninso za masiku a Loti. Mzinda wa Sodomu, kumene Loti ndi banja lake ankakhala, unali wolemera kwambiri koma unalibe makhalidwe abwino. Yehova anatumiza angelo ake kuti akawononge mzindawo. Angelo anauza Loti ndi banja lake kuthawa kuchoka m’Sodomu ndiponso kuti asayang’ane kumbuyo. Chifukwa cholimbikitsidwa ndi angelo, anachoka mu mzindawo. Koma mkazi wa Loti akuoneka kuti zinam’vuta kuiwala nyumba yake ku Sodomu. Iye anayang’ana kumbuyo, zomwe zinasonyeza kusamvera kwake. Ndipo chifukwa cha zimenezi anataya moyo wake. (Genesis 19:15-26) Ponena za m’tsogolo, Yesu anachenjeza kuti: “Kumbukirani mkazi wa Loti.” Kodi tikulabadira chenjezo limeneli?​—Luka 17:32.

13 Anthu amene anamvera machenjezo a Mulungu anapulumuka. Ndi mmene zinalili kwa Nowa ndi banja lake ndiponso Loti ndi ana ake aakazi. (2 Petro 2:9) Pamene tiganizira za chenjezo la zitsanzo zimenezi, ifenso timalimbikitsidwa ndi uthenga wa chipulumutso wa anthu okonda chilungamo womwe uli m’machenjezo amenewa. Chifukwa cha zimenezi, timayembekezera ndi chidaliro chonse kuti Mulungu adzakwaniritsa lonjezo lakuti kudzakhala ‘miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmene mukhalitsa chilungamo.’​—2 Petro 3:13.

‘Nthawi ya Chiweruzo Yafika’!

14, 15. (a) Kodi “nthawi” ya chiweruzo imaphatikizapo chiyani? (b) Kodi ‘kuopa Mulungu ndi kum’patsa ulemerero’ kumafuna kuti tichite chiyani?

14 Pamene tikudikira, kodi tingayembekezere chiyani kuchitika? Buku la Chivumbulutso limasonyeza mmene chifuno cha Mulungu chidzakwaniritsidwira mwatsatanetsatane. Tifunika kumvera zimene bukuli limanena kuti tisonyeze kuti ndife okonzeka. Ulosiwo umafotokoza bwino kwambiri zinthu zimene zidzachitika “tsiku la Ambuye,” limene linayamba nthawi imene Kristu anaikidwa pampando wachifumu kumwamba mu 1914. (Chivumbulutso 1:10) Buku la Chivumbulutso likutisonyeza mngelo amene wapatsidwa “Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire.” Iye akulengeza ndi mawu aakulu kuti: “Opani Mulungu, m’patseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake.” (Chivumbulutso 14:6, 7) “Nthawi” ya chiweruzo imeneyi ndi yaifupi, ndipo imaphatikizapo kulengeza ziweruzo ndiponso kupereka ziweruzo zimene zasonyezedwa mu ulosi umenewu. Tsopano tili m’nthawi imeneyo.

15 Panopa, nthawi ya chiweruzo isanathe, tikulangizidwa kuti: “Opani Mulungu, m patseni ulemerero.” Kodi zimenezi zimafuna kuti tichite chiyani? Chifukwa choopa Mulungu, tiyenera kupewa zoipa. (Miyambo 8:13) Ngati tilemekeza Mulungu, tidzam’mvera ndi kum’patsa ulemu waukulu. Sitidzakhala otanganidwa kwambiri moti n’kulephera kuwerenga Mawu ake, Baibulo, nthawi zonse. Sitidzaona malangizo ake onena kuti tizifika pamisonkhano yachikristu monga osafunika. (Ahebri 10:24, 25) Tidzayamikira kwambiri mwayi wa kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu wolamulidwa ndi Mesiya ndipo tidzachita zimenezi mwachangu. Tidzakhulupirira Yehova nthawi zonse ndi mtima wathu wonse. (Salmo 62:8) Chifukwa timazindikira kuti Yehova ndiye Mfumu ya Chilengedwe Chonse, timam’lemekeza mwa kum’gonjera ndi mtima wonse monga Wolamulira moyo wathu. Kodi mumaopadi Mulungu ndi kum’patsa ulemerero m’njira zonsezo?

16. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chiweruzo cha Babulo Wamkulu chopezeka pa Chivumbulutso 14:8 chachitika kale?

16 Buku la Chivumbulutso chaputala 14 likupitiriza kufotokoza zinthu zina zimene ziyenera kuchitika nthawi ya chiweruzo. Babulo Wamkulu, ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga, akutchulidwa choyamba kuti: “Anatsata mngelo wina mnzake ndi kunena, Wagwa, wagwa, Babulo waukulu.” (Chivumbulutso 14:8) Inde, pamaso pa Mulungu, Babulo Wamkulu anagwa kale. Mu 1919 atumiki a Yehova odzozedwa anamasulidwa ku ukapolo wa ziphunzitso za Babulo ndi miyambo yake, zimene anthu ndi mayiko atsatira kwa zaka zambiri. (Chivumbulutso 17:1, 15) Kuyambira nthawi imeneyo anadzipereka kuchirikiza kulambira koona. Ndipo ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse yakhala ikuchitika.​—Mateyu 24:14.

17. Kodi kutuluka m’Babulo Wamkulu kumafuna chiyani?

17 Palinso mbali zina za chiweruzo cha Mulungu pa Babulo Wamkulu. Chiwonongeko chake chomaliza chili pafupi. (Chivumbulutso 18:21) Pachifukwa chabwino, Baibulo limalangiza anthu kulikonse kuti: “Tulukani m’menemo [m’Babulo Wamkulu] . . . kuti mungayanjane ndi machimo ake.” (Chivumbulutso 18:4, 5) Kodi timatulukamo bwanji m’Babulo Wamkulu? Zimenezi sizitanthauza kungochoka m’chipembedzo chonyenga basi. Izi zili choncho chifukwa chakuti mzimu wachibabulo umapezekanso m’zikondwerero ndi miyambo yotchuka, m’khalidwe lotayirira la dzikoli pa zachiwerewere, m’zosangalatsa zolimbikitsa kukhulupirira mizimu ndi zina zambiri. Choncho, kuti tikhale odikira, m’pofunika kuti, mwa zochita zathu ndi zokhumba zathu, tisonyeze kuti tinachokeratu m’Babulo Wamkulu n’kusiyiratu zonse.

18. Poona zimene zafotokozedwa pa Chivumbulutso 14:9, 10, kodi Akristu atcheru safuna kuchita chiyani?

18 Mbali ina yokhudza ‘nthawi ya chiweruzo’ ikufotokozedwa pa Chivumbulutso 14:9, 10. Mngelo wina akuti: “Ngati wina alambira chirombocho, ndi fano lake, nalandira lemba pamphumi pake, kapena pa dzanja lake, iyenso adzamwako ku vinyo wa mkwiyo wa Mulungu.” Chifukwa chiyani? “Chirombocho, ndi fano lake” zikuimira ulamuliro wa anthu, umene suvomereza ulamuliro wa Yehova. Akristu atcheru safuna kuti, mwa maganizo kapena zochita zawo, akhale akapolo a anthu amene amakana ulamuliro wapamwamba wa Mulungu woona, Yehova. Safunanso kuti, mwa maganizo ndi zochita zawo, alandire nawo chizindikiro chimenecho. Akristu amadziwa kuti Ufumu wa Mulungu wakhazikitsidwa kale kumwamba. Amadziwanso kuti udzathetsa maulamuliro onse a anthu, ndipo udzakhala chikhalire.​—Danieli 2:44.

Tisasiye Kukhala Maso!

19, 20. (a) Pamene tikufika kumapeto a masiku otsiriza, kodi tili otsimikiza za chiyani chimene Satana adzayesa kuchita? (b) Kodi tiyenera kukhala otsimikiza kuchita chiyani?

19 Pamene tikuyandikira mapeto a masiku otsiriza, mavuto ndi ziyeso zizingowonjezereka. Malinga ngati tikukhala m’dongosolo lakale lino ndipo tili opanda ungwiro, tidzakhudzidwabe ndi zinthu monga matenda, ukalamba, imfa ya wachibale, kukhumudwa ndiponso kugwa ulesi pamene anthu ena sakulabadira tikamawalalikira Mawu a Mulungu ndi zina zambiri. Musaiwale kuti chimene Satana akufuna si china ayi koma kuti tisiye kulalikira uthenga wabwino kapena kutsatira miyezo ya Mulungu chifukwa cha mavuto amene tikukumana nawo. (Aefeso 6:11-13) Ino si nthawi yosiya kukhala maso malinga ndi mmene zinthu zilili masiku ano.

20 Yesu anadziwa kuti tidzakhala opanikizidwa kwambiri moti n’kufuna kusiya, n’chifukwa chake anatilangiza kuti: “Dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.” (Mateyu 24:42) Chotero, tiyeni nthawi zonse tikhale maso ndi mmene nthawi ikuyendera. Tiyeni tikhale maso ndi machenjera a Satana amene angatibwezere m’mbuyo kapena kutisiyitsa choonadi. Tiyenitu nthawi zonse tikhale otsimikiza kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu mwachangu ndiponso molimbika kwambiri. Ndithudi, tiyeni tikhale tcheru pamene tikulabadira chenjezo la Yesu lakuti: “Dikirani.” Mwa kuchita zimenezi, tidzalemekeza Yehova ndipo tidzakhala pakati pa anthu oyembekezera madalitso ake osatha.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi timadziwa bwanji kuti chenjezo la Yesu la ‘kudikira’ limagwira ntchito kwa Akristu oona?

• Kodi ndi zitsanzo zochenjeza ziti za m’Baibulo zomwe zingatithandize ‘kudikira’?

• Kodi nthawi ya chiweruzo n’chiyani, ndipo tikulangizidwa kuchita chiyani nthawiyi isanathe?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Yesu anayerekezera kubwera kwake ndi kubwera kwa mbala

[Chithunzi patsamba 24]

Kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu kuli pafupi

[Zithunzi patsamba 25]

Tiyeni tikhale otsimikiza kulalikira mwachangu ndiponso molimbika kwambiri nthawi zonse