Kodi Chikumbumtima Chanu Ndi Chophunzitsidwa Bwino?
Kodi Chikumbumtima Chanu Ndi Chophunzitsidwa Bwino?
KODI munayamba mwanenapo kuti, “M’mtima mwangamu ndikudziwa kuti zimenezi si zabwino,” kapena “Chinachake m’mtima mwangamu chikundiletsa ndiye sindingachite zimene mukufuna kuti ndichitezo”? Chimenecho ndicho chikumbumtima chanu, mtima wozindikira chabwino ndi choipa, umene umakuimbani mlandu kapena kukuuzani kuti zimene mwachita n’zabwino. Inde, chikumbumtima timachita kubadwa nacho.
Ngakhale kuti anthu ndi otalikirana ndi Mulungu, amathabe kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Izi zili choncho chifukwa anapangidwa m’chifanizo cha Mulungu, ndipo amatha kusonyezako makhalidwe a Mulungu monga nzeru ndi chilungamo. (Genesis 1:26, 27) Ponena za nkhaniyi, mtumwi Paulo mouziridwa ndi Mulungu analemba kuti: ‘Pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo; popeza iwo aonetsa ntchito ya lamulo yolembedwa m’mitima yawo, ndipo chikumbumtima chawo chichitiranso umboni pamodzi nawo, ndipo maganizo awo wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana.’ *—Aroma 2:14, 15.
Chibadwa chozindikira khalidwe labwino chimene tinalandira kwa munthu woyamba, Adamu, chili ngati “lamulo” kapena mfundo yolamulira khalidwe la anthu a mafuko ndi mayiko. Chifukwa cha khalidwe limeneli timatha kudzipenda ndi kudziweruza tokha. (Aroma 9:1) Adamu ndi Hava anasonyeza khalidwe limeneli atangophwanya lamulo la Mulungu mwa kubisala. (Genesis 3:7, 8) Chitsanzo china choonetsa mmene chikumbumtima chimagwirira ntchito ndi chija chimene chimasonyeza mmene Mfumu Davide anachitira atadziwa kuti wachimwa chifukwa cha kuwerenga anthu. Baibulo limanena kuti, “mtima wa Davide unam’tsutsa.”—2 Samueli 24:1-10.
Kutha kuona zimene tachita ndi kuweruza khalidwe lathu kungatithandize kuchita mbali yofunika kwambiri yosonyeza kulapa kumene Mulungu amavomereza. Davide analemba kuti: “Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse. Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.” (Salmo 32:3, 5) Chotero chikumbumtima chamoyo chingabweze munthu wochimwa kwa Mulungu. Chingam’thandize kuzindikira kuti akufunika akhululukidwe ndi Mulungu ndi kuti atsatire njira Zake.—Salmo 51:1-4, 9, 13-15.
Chikumbumtima chimatichenjezanso kapena kutitsogolera pamene tikufuna kusankha zochita kapena kuchita zinthu zokhudza khalidwe lathu. Inali mbali imeneyi ya chikumbumtima yomwe iyenera kuti inathandiza Yosefe kuzindikira pasadakhale kuti kuchita chigololo n’kulakwa, n’koipa ndipo n’kuchimwira Mulungu. Patapita nthawi lamulo loletsa chigololo linaikidwa pa Malamulo Khumi amene anapatsidwa Genesis 39:1-9; Eksodo 20:14) Mwachionekere, tingapindule kwambiri ngati chikumbumtima chathu n’chophunzitsidwa kutitsogolera m’malo moti chizingotiweruza. Kodi chikumbumtima chanu chimagwira ntchito mwa njira imeneyi?
kwa Israyeli. (Kuphunzitsa Chikumbumtima Kupanga Zosankha Zoyenera
Ngakhale timabadwa ndi mphamvu ya chikumbumtima, n’zomvetsa chisoni kuti mphatso imeneyi ndi yopanda ungwiro. Ngakhale kuti anthu poyamba anali angwiro, “onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Chifukwa chodetsedwa ndi uchimo ndiponso kupanda ungwiro, chikumbumtima chathu chingakhale chopotoka. Ndipo sichingagwire bwino ntchito monga mmene Yehova ankafunira poyamba. (Aroma 7:18-23) Ndiponso, zinthu zina zingasokoneze chikumbumtima chathu. Chingamatsatire mmene tinaleredwera kapena miyambo ya kwathuko, zikhulupiriro ndiponso kumene tikukhala. Ndithudi, makhalidwe oipa ndiponso miyezo ya dziko yomwe ikuipiraipirabe siingatsogolere chikumbumtima chabwino.
Chotero, Mkristu afunika kukhala ndi thandizo lina lomutsogolera la miyezo yosasintha ndiponso yolungama yopezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Miyezo imeneyi ingatsogolere chikumbumtima chathu kupenda zinthu bwinobwino ndi kuzikonza. (2 Timoteo 3:16) Ngati chikumbumtima chathu chiphunzitsidwa miyezo ya Mulungu, chingatithandize kupewa makhalidwe amene angatiwononge. Ndiponso chingatithandize “kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” (Ahebri 5:14) Popanda miyezo ya Mulungu, chikumbumtima chathu sichingatichenjeze pamene tasochera kulowera ku njira yoipa. Baibulo limati: “Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka, koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.”—Miyambo 16:25; 17:20.
M’mbali zina za moyo, Mawu a Mulungu amapereka malangizo osapita m’mbali otitsogolera, ndipo ndi bwino kuwatsatira. Komabe, pali zochitika zambiri zimene zilibe malangizo achindunji m’Baibulo. Zimenezi zingaphatikizepo kusankha ntchito, chithandizo cha mankhwala, zosangalatsa, zovala ndi kudzikongoletsa ndiponso zinthu zina. Si zophweka kudziwa chochita ndi kusankha bwino pa zinthu zonsezi. N’chifukwa chake tiyenera kukhala ndi maganizo a Davide amene anapemphera kuti: “Mundidziwitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m’choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa.” (Salmo 25:4, 5) Tikamvetsa bwino mmene Mulungu amaonera zinthu ndi njira zake, m’pamene tidzatha kuona bwino zochita zathu ndi kupanga zosankha ndi chikumbumtima chabwino.
Chotero, tikakhala ndi funso kapena tikafuna kusankha zochita, tiganizire kaye za mfundo za Akolose 3:18, 20); kukhala oona mtima m’zinthu zonse (Ahebri 13:18); kudana ndi choipa (Salmo 97:10); kulondola mtendere (Aroma 14:19); kumvera maulamuliro omwe alipo (Mateyu 22:21; Aroma 13:1-7); kulambira Mulungu yekha (Mateyu 4:10); kusakhala mbali ya dziko (Yohane 17:14); kupewa mayanjano oipa (1 Akorinto 15:33); kuvala kwaulemu ndi kudzikongoletsa bwino (1 Timoteo 2:9, 10); ndi kusakhumudwitsa ena (Afilipi 1:10). Chotero, kudziwa mfundo yoyenerera ya m’Baibulo kungalimbitse chikumbumtima chathu ndi kutithandiza kusankha bwino.
m’Baibulo zimene zingakhudze nkhani imeneyo. Zina mwa mfundo zimenezi zingakhale: kulemekeza mutu (Mverani Chikumbumtima Chanu
Kuti chikumbumtima chathu chitithandize tifunika kuchimvera. Pokhapokha ngati timvera zimene chikumbumtima chathu chophunzitsidwa Baibulo chikutiuza m’pamenenso chingatipindulitse. Chikumbumtima chophunzitsidwa tingachiyerekeze ndi timagetsi ta m’galimoto tochenjeza dalaivala. Bwanji ngati getsi lotichenjeza kuti mafuta ndi ochepa liyaka. Kodi chingachitike n’chiyani ngati sitichitapo kanthu mwamsangamsanga, ndipo tikungopitirizabe kuyendetsa galimotoyo? Tingawononge kwambiri injini ya galimoto. Mofananamo, chikumbumtima chathu chingatichenjeze kuti zimene tikufuna kuchita n’zolakwika. Poyerekeza miyezo ndi makhalidwe abwino a m’Malemba amene ife timatsatira ndi zimene tikuchita kapena zimene tikuganizira kuchita, chikumbumtima chimatichenjeza, monga mmene getsi la m’galimoto limachenjezera dalaivala. Ngati timvera chenjezolo, tidzapewa mavuto amene amabwera chifukwa cha khalidwe loipa ndiponso chikumbumtima chathu chidzapitirizabe kugwira bwino ntchito.
Kodi chingachitike n’chiyani ngati tasankha kunyalanyaza chenjezo? M’kupita kwa nthawi, chikumbumtima chingasiye kugwira ntchito. Zimene zingachitike ngati nthawi zonse tinyalanyaza kapena kupondereza chikumbumtima tingazifanizire ndi kutenga chitsulo chotentha n’kusindikiza pakhungu. Chipsera chake sichimva kukhudza kulikonse. (1 Timoteo 4:2) Chikumbumtima chotero sichitiweruza tikachimwa ndipo sichitichenjeza kuti tisabwerezenso tchimo. Chikumbumtima chopimbidzala chimanyalanyaza miyezo ya Baibulo ya chabwino ndi choipa ndipo n’chikumbumtima choipa. Chimakhala chodetsedwa, munthu wake amakhala wopandiratu khalidwe labwino ndipo amakhala wotalikirana ndi Mulungu. (Aefeso 4:17-19; Tito 1:15) Zimenezitu n’zotsatirapo zoipa kwambiri.
‘Khalani ndi Chikumbumtima Chabwino’
Kuti tikhale ndi chikumbumtima chabwino tifunika kuyesetsa nthawi zonse. Mtumwi Paulo Machitidwe 24:16) Monga Mkristu, Paulo nthawi zonse ankapenda ndi kuwongolera zochita zake. Ankachita zimenezi n’cholinga choti asalakwire Mulungu. Paulo ankadziwa kuti pomaliza pake, ndi Mulungu amene adzanena ubwino ndi kuipa kwa zimene timachita. (Aroma 14:10-12; 1 Akorinto 4:4) Paulo anati: “Zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.”—Ahebri 4:13.
anati: “Ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbumtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.” (Paulo anatchulanso za kusalakwira anthu. Chitsanzo chabwino kwambiri ndi uphungu umene anapereka kwa Akristu a ku Korinto wonena za “kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano.” Mfundo yake inali yakuti, ngakhale kuti chinthu china n’chosaletsedwa ndi Mawu a Mulungu, ndi bwino kuganizira chikumbumtima cha ena. Kulephera kuchita zimenezi kungapangitse ‘abale amene Kristu anawafera kutayika’ mwauzimu. Tingawonongenso ubwenzi wathu ndi Mulungu.—1 Akorinto 8:4, 11-13; 10:23, 24.
Chotero, pitirizani kuphunzitsa ndi kusunga chikumbumtima chabwino. Posankha zochita, pemphani Mulungu kukutsogolerani. (Yakobo 1:5) Phunzirani Mawu a Mulungu, ndipo lolani mfundo zake kuumba maganizo ndi mtima wanu. (Miyambo 2:3-5) Pakabuka nkhani zazikulu, funsirani kwa Akristu okhwima kuti mutsimikizire ngati mwamva molondola mfundo za m’Baibulo zimene zikukhudza nkhaniyo. (Miyambo 12:15; Aroma 14:1; Agalatiya 6:5) Ganizirani mmene zosankha zanu zidzakhudzira chikumbumtima chanu, anthu ena ndiponso koposa zonse, mmene zidzakhudzira ubwenzi wanu ndi Yehova.—1 Timoteo 1:5, 18, 19.
Chikumbumtima chathu ndi mphatso yabwino kwambiri yochokera kwa Atate wathu wachikondi wa kumwamba, Yehova Mulungu. Mwa kuchigwiritsa ntchito mogwirizana ndi chifuniro cha amene anatipatsa, tidzayandikira kwambiri kwa Mlengi wathu. Pamene tikuyesetsa “kukhala nacho chikumbumtima chabwino” m’zonse zimene tikuchita, timasonyeza bwino kwambiri kuti tinapangidwa m’chifanizo cha Mulungu.—1 Petro 3:16; Akolose 3:10.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Mawu achigiriki akuti chikumbumtima amene agwiritsidwa ntchito palembali amatanthauza “mphamvu ya m’mtima yozindikira khalidwe labwino” (The Analytical Greek Lexicon Revised, yolembedwa ndi Harold K. Moulton); “kusiyanitsa khalidwe labwino ndi loipa.”—Greek-English Lexicon, yolembedwa ndi J. H. Thayer.
[Zithunzi patsamba 13]
Kodi chikumbumtima chanu n’chophunzitsidwa kukutsogolerani m’malo moti chizingokuweruzani?
[Chithunzi patsamba 14]
Timakhala ndi chikumbumtima chophunzitsidwa bwino ngati tiphunzira ndi kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo
[Zithunzi patsamba 15]
Chikumbumtima chikamakuchenjezani, musanyalanyaze