Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukuchiona Chizindikiro cha Kukhalapo kwa Yesu?

Kodi Mukuchiona Chizindikiro cha Kukhalapo kwa Yesu?

Kodi Mukuchiona Chizindikiro cha Kukhalapo kwa Yesu?

PALIBE amene amafuna kudwala kwambiri kapena kuti tsoka lim’chitikire. Kuti apewe masoka otero, munthu wanzeru amaona zizindikiro zosonyeza ngozi ndipo amachita mogwirizana ndi zomwe waonazo. Yesu Kristu anafotokoza chizindikiro chinachake chimene tifunika kuchiona. Chizindikiro chimene ankanenacho chikukhudza anthu padziko lonse, kuphatikizapo inuyo ndi banja lanu.

Yesu ananena za Ufumu wa Mulungu umene udzachotsa kuipa ndi kupanga dziko lapansi kukhala paradaiso. Ophunzira ake anali ndi chidwi pankhani imeneyi ndipo ankafuna kudziwa nthawi imene Ufumuwo uti udzabwere. Iwo anafunsa kuti: “Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika [“kukhalapo,” NW] kwanu n’chiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano?”​—Mateyu 24:3.

Yesu anadziwa kuti ataphedwa ndi kuukitsidwa, padzapita zaka zambiri iye asanaikidwe kukhala Mfumu ya Umesiya kumwamba kuti alamulire anthu. Popeza kuti anthu sakamuona akuvekedwa Ufumu, Yesu anapereka chizindikiro chothandiza otsatira ake kudziwa za “kukhalapo” kwake ndiponso “mathedwe a nthawi ya pansi pano.” Chizindikiro chimenechi chili ndi mbali zingapo, zimene zonse pamodzi zimadziwikitsa nthawi ya kukhalapo kwa Yesu.

Mateyu, Marko ndi Luka amene analemba Mauthenga Abwino, aliyense payekha analemba mosamala bwino yankho la Yesu. (Mateyu, machaputala 24 ndi 25; Marko, chaputala 13; Luka chaputala 21) Olemba Baibulo ena anawonjezera mfundo zina pa chizindikirochi. (2 Timoteo 3:1-5; 2 Petro 3:3, 4; Chivumbulutso 6:1-8; 11:18) M’nkhani ino malo oti n’kulembapo mfundo zonse sangakwanire koma tifotokoza mfundo zisanu zofunika zimene zimapanga chizindikiro chimene Yesu anatchula. Muona kuti zimenezi n’zofunika kwambiri kwa inu. Onani bokosi patsamba 6

Kusintha Kumene Kunayambitsa Nyengo Yatsopano

“Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Magazini ya ku Germany (Der Spiegel) inanena kuti chaka cha 1914 chisanafike, anthu “ankakhulupirira kuti tsogolo lawo lidzakhala labwino kwambiri ndipo adzakhala ndi ufulu wambiri, chitukuko ndiponso kuti adzakhala olemera.” Kenaka zinthu zonse zinasinthiratu. Magazini ya GEO inati: “Nkhondo yomwe inayamba mu August 1914 ndi kutha mu November 1918 anthu anadabwa nayo kwambiri. Nkhondoyi inasintha mbiri ya anthu mwadzidzidzi, kulekanitsa zakale ndi zatsopano.” Asilikali oposa 60 miliyoni ochokera m’makontineti asanu anachita nawo nkhondoyi imene inapulula anthu. Asilikali pafupifupi 6000 ankaphedwa tsiku lililonse. Kuchokera nthawi imeneyo, akatswiri olemba mbiri mu mbadwo uliwonse ndiponso okhala ndi maganizo osiyanasiyana pa ndale, anena kuti “zaka za 1914 mpaka 1918 zinasintha zinthu n’kuyambitsa nyengo yatsopano.”

Nkhondo yoyamba yapadziko lonse inasinthiratu moyo wa anthu ndipo anthu anayamba kukhala m’masiku otsiriza a dongosolo lino la zinthu. Zaka zonse za m’ma 1900 kunali nkhondo zambiri ndi uchigawenga kuposa zaka zonse m’mbuyomo. M’zaka zoyambirira za m’ma 2000 muno, zinthu sizinawongokere. Kupatulapo nkhondo, pali mbali zina za chizindikiro zimene zikuoneka.

Njala, Miliri, ndi Zivomezi

“Kudzakhala njala.” (Mateyu 24:7) Ku Ulaya kunali njala panthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse ndipo kuyambira nthawi imeneyo njala yavutitsa anthu. Wolemba mbiri, Alan Bullock, analemba kuti, mu 1933, ku Russia ndi Ukraine, “magulu a anthu ovutika ndi njala anali kuyendayenda m’mayikowo . . . Mitembo anaiunjika m’mbali mwa msewu.” Mu 1943 mtolankhani T. H. White anaona anthu akuvutika ndi njala ku China m’chigawo chotchedwa Henan. Iye analemba kuti: “Nthawi yanjala munthu angadye chilichonse. Atha kuchikonza mpaka chitafika podyeka. Kenako akachidya thupi limapeza mphamvu. Koma munthu angaganize zodya chinthu chimene poyamba sankaganiza kuti angadye poona kuti ngati satero amwalira.” N’zomvetsa chisoni kuti m’zaka zinozi njala ku Africa kuno ikupezeka pafupifupi malo alionse. Ngakhale kuti chakudya chimene amalima padziko chingakwanire munthu aliyense, bungwe la United Nation lotchedwa Food and Agriculture Organisation linanena kuti pafupifupi anthu 840 miliyoni padziko lonse ali ndi chakudya chochepa kwambiri.

“Miliri m’malo akutiakuti.” (Luka 21:11) Nyuzipepala ya Süddeutsche Zeitung inati: “Fuluwenza ya ku Spain akuti inapha anthu pakati pa 20 mpaka 50 miliyoni mu 1918. Anthu ophedwawa anaposa amene anaphedwa ndi mliri wa makoswe kapena nkhondo yoyamba yapadziko lonse.” Kuyambira nthawi imeneyo, anthu ambiri amadwala matenda a malungo, nthomba, chifuwa chachikulu, poliyo ndi kolera. Ndipo anthu akusowa chochita poona mmene matenda a Edzi akufalikira mosaletseka. Tsopano zinthu n’zodabwitsa kwambiri chifukwa matenda osatha alipobe ngakhale kuti anthu apita patsogolo kwambiri pankhani ya zamankhwala. Vuto ngati limeneli, limene anthu kale sanalionepo, likusonyeza kuti nthawi imene tikukhalamo n’njapadera kwambiri.

“Zivomezi.” (Mateyu 24:7) Zaka 100 zapitazi, zivomezi zapha anthu masauzande ambiri. Malinga ndi kunena kwa lipoti lina, kuyambira mu 1914, chaka chilichonse pachitika zivomezi zokwana 18, zokhala ndi mphamvu yotha kuwononga nyumba ndi kung’amba nthaka. Zivomezi zowononga kwambiri zotha kugwetseratu nyumba, zachitika kamodzi pa chaka. Ngakhale kuti sayansi yapita patsogolo kwambiri, anthu ophedwa amakhalabe ambiri. Izi zili choncho chifukwa mizinda yambiri imene ikufulumira kukula ili m’madera amene mumachitika zivomezi kawirikawiri.

Uthenga Wosangalatsa!

Mbali zambiri za chizindikiro cha masiku otsiriza n’zodetsa nkhawa. Koma Yesu ananenanso za uthenga wosangalatsa.

“Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 24:14) Ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu, imene Yesu iyemwini anayambitsa, inali kudzafika pachimake m’masiku otsiriza. Ndipo zachitikadi choncho. Mboni za Yehova zikulalikira uthenga wa m’Baibulo ndipo, anthu amene akufuna, zikuwaphunzitsa njira imene angagwiritsire ntchito zimene akuphunzira pamoyo wawo tsiku ndi tsiku. Pakalipano, Mboni zoposa sikisi miliyoni zikulalikira m’mayiko okwana 235 ndipo m’zinenero zoposa 400.

Taonani kuti Yesu sananene kuti anthu adzasiya kuchita zinthu zonse pamoyo wawo chifukwa cha kuvuta kwa zinthu m’dziko. Iye sananenenso kuti dziko lonse lapansi lidzakhala ndi mbali imodzi yokha ya chizindikiro. Koma analosera zinthu zambiri zimene zonse pamodzi zidzapanga chizindikiro chimene chidzadziwika kulikonse padziko lapansi.

M’malo moyang’ana chochitika chimodzi, kodi mukuona mbali zosiyanasiyana za chizindikirocho zikuchitika padziko lonse lapansi? Zimene zikuchitika padziko lapansi zikukhudza inuyo ndi banja lanu. Komano tingafunse kuti, nanga n’chifukwa chiyani ndi anthu ochepa kwambiri amene akuchiona chizindikiro?

Munthu Amaona Zimene Amakonda Kukhala Zofunika

“Osasambira pano,” “Chenjerani ndi galu,” “Chepetsani Liwiro.” Izi ndi zina mwa zizindikiro zochenjeza zimene timaona, koma nthawi zambiri anthu amazinyalanyaza. Chifukwa chiyani? Timatengeka mosavuta ndi zinthu zimene tikuona kuti timazikonda. Mwachitsanzo, tingafune kuyendetsa galimoto mothamanga kwambiri kuposa mmene lamulo likunenera, kapena tingafune kwambiri kusambira kumalo amene si ololedwa. Koma si nzeru yabwino kunyalanyaza zizindikiro.

Mwachitsanzo, zigumukire za mu mapiri a Alps a ku Austria, France, Italy ndi Switzerland nthawi zina zapha alendo odzaona malo. Amenewa aphedwa chifukwa chonyalanyaza machenjezo owauza kuti afunika azitsata njira zotetezeka zokha potsetsereka paphiri. Malinga ndi kunena kwa nyuzipepala ya Süddeutsche Zeitung, alendo oona malo ambiri amene amanyalanyaza machenjezo otero amayendera mfundo yoti, Sungasalale popanda kuika moyo pangozi. Tsoka lake n’loti kunyalanyaza machenjezo kungabweretse mavuto aakulu ngakhale imfa.

Kodi anthu ali ndi zifukwa zotani zonyalanyazira chizindikiro chimene Yesu anafotokoza? Anthuwo sachiona chizindikiro chimenecho chifukwa cha dyera lawo, mphwayi, kukayikira, kuzolowera, kapena safuna kukhala otsalira. Kodi inu mungakhale mukunyalanyaza chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu chifukwa cha chimodzi mwa zinthu zimene tatchulazi? Kodi si nzeru yabwino kuchitapo kanthu mutaona chizindikiro?

Mmene Moyo Udzakhalira M’Paradiso Padziko Lapansi

Anthu ambiri akulabadira chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu. Kristian, mwamuna wachinyamata wokwatira ku Germany, analemba kuti: “Ino ndi nthawi yovuta. Mosakayikira, tikukhala ‘m’masiku otsiriza.’” Iye ndi mkazi wake amagwiritsa ntchito nthawi yochuluka kulankhula kwa ena za Ufumu wa Mesiya. Frank, nayenso akukhala m’dziko la Germany. Iye ndi mkazi wake amalimbikitsa anthu ena ndi uthenga wabwino wa m’Baibulo. Frank anati: “Chifukwa cha mmene zinthu zili m’dzikoli, anthu ambiri masiku ano akudera nkhawa za tsogolo lawo. Timayesa kuwalimbikitsa ndi maulosi a m’Baibulo onena za dziko lapansi la paradaiso.” Motero, Kristian ndi Frank amathandiza kukwaniritsa mbali imodzi ya chizindikiro cha Yesu. Mbali imeneyi ndiyo kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu.​—Mateyu 24:14.

Pamene masiku otsiriza akufika pachimake, Yesu adzawononga dongosolo lakale lino limodzi ndi anthu amene amalichirikiza. Nthawi imeneyo, Ufumu wa Mesiya ndi umene udzayendetse zinthu padziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lidzakhala Paradaiso malinga ndi kunena kwa ulosi. Anthu sadzadwalanso ndipo sadzamwaliranso, ndiponso akufa adzaukitsidwa kuti akhale ndi moyo padziko lapansi. Izitu ndi zinthu zosangalatsa zimene anthu amene akuona chizindikiro cha nthawi ino akuyembekezera. Kodi si nzeru yabwino kuphunzira zambiri za chizindikiro ndiponso zimene wina afunika kuchita kuti apulumuke mapeto a dongosolo lino? Ndithudi, imeneyi iyenera kukhala nkhani yofunika kwambiri kwa aliyense.​—Yohane 17:3.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

Yesu analosera za zinthu zambiri zimene pamodzi zidzapanga chizindikiro chimene chidzadziwika kulikonse padziko lapansi

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Kodi mukuona mbali zosiyanasiyana za chizindikirocho zikuchitika padziko lonse lapansi?

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 6]

ZIZINDIKIRO ZA MASIKU OTSIRIZA

Nkhondo zomwe sizinachitikepo n’kale lonse.​—Mateyu 24:7; Chivumbulutso 6:4

Njala.​—Mateyu 24:7; Chivumbulutso 6:5, 6, 8

Miliri.​—Luka 21:11; Chivumbulutso 6:8

Kuchuluka kwa kusaweruzika.​—Mateyu 24:12

Zivomezi.​—Mateyu 24:7

Nthawi zowawitsa.​—2 Timoteo 3:1

Kukonda kwambiri ndalama.​—2 Timoteo 3:2

Kusamvera makolo.​—2 Timoteo 3:2

Kupanda chikondi chachibadwidwe.​—2 Timoteo 3:3

Kukonda zokondweretsa munthu, osati Mulungu.​—2 Timoteo 3:4

Kusadziletsa.​—2 Timoteo 3:3

Kusakonda chabwino.​—2 Timoteo 3:3

Kusafuna kudziwa za ngozi yobwera m’tsogolo.​—Mateyu 24:39

Onyoza omwe amakana umboni wa masiku otsiriza.​—2 Petro 3:3, 4

Kulalikira Ufumu wa Mulungu padziko lonse lapansi.​—Mateyu 24:14

[Mawu a Chithunzi patsamba 5]

WWI soldiers: From the book The World War​—A Pictorial History, 1919; poor family: AP Photo/​Aijaz Rahi; polio victim: © WHO/​P. Virot