Kodi Muli “Nacho Chuma cha kwa Mulungu”?
Kodi Muli “Nacho Chuma cha kwa Mulungu”?
PA Mafanizo ambiri ochititsa chidwi a Yesu Kristu, pali lina lomwe limanena za mwinimunda wachuma. Pofuna kudzikonzera tsogolo labwino, mwinimunda anakonza zomanga nkhokwe zazikulu. Koma m’fanizo la Yesu, munthuyu anatchedwa “wopusa.” (Luka 12:16-21) Kodi n’chifukwa chiyani anaonedwa choncho?
N’zoonekeratu kuti munthu wachumayu sanaganizire Mulungu pa zimene amafuna kuchita. Ndipo sanayamikire Mulungu chifukwa cha kukolola zochuluka. (Mateyu 5:45) M’malo mwake, anadzitama kuti: “Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere.” Iye anaganiza kuti zimene anakolola chifukwa cha khama lake zidzakhala ngati “khoma lalitali.”—Miyambo 18:11.
Pochenjeza za mzimu wotero wodzikuza, Yakobo amene anali wophunzira analemba kuti: “Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa ku mudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nawo; inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.”—Yakobo 4:13, 14.
Mogwirizanadi ndi mawu amenewo, munthu wachuma m’fanizo la Yesu anauzidwa kuti: “Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?” Monga utsi wokanganuka, munthu wachumayu adzamwalira asanaone zimene ankafuna kuti zichitike. Kodi tikupezapo phunziro pamenepa? Yesu anati: “Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.” Kodi muli “nacho chuma cha kwa Mulungu”?