Makolo—kodi Ana Anu Mukuwafunira Tsogolo Lotani?
Makolo—kodi Ana Anu Mukuwafunira Tsogolo Lotani?
“Anyamata ndiponso anamwali . . . Alemekeze dzina la Yehova.”—Salmo 148:12, 13.
1. Kodi makolo amakhala ndi nkhawa zotani zokhudza ana awo?
KODI ndi makolo ati amene sakhala ndi nkhawa poganizira za tsogolo la ana awo? Kuyambira nthawi imene khanda labadwa, ngakhale lisanabadwe, makolo amayamba kuda nkhawa za moyo wake. Kodi adzakhala wathanzi? Kodi adzakula bwinobwino? Pamene mwana akukula, pamakhala nkhawa zina zowonjezereka. Makolo ambiri amafunira ana awo zabwino zokhazokha.—1 Samueli 1:11, 27, 28; Salmo 127:3-5.
2. N’chifukwa chiyani makolo ambiri masiku ano amafuna kwambiri kuti ana awo akadzakula adzakhale ndi moyo wabwino?
2 Koma n’zovuta masiku ano kuti makolo apezere ana awo zinthu zabwino. Makolo ambiri akumana ndi mavuto monga nkhondo, mavuto a zandale, mavuto a zachuma, ndipo avulalapo kapena kusautsika mtima, ndiponso akumanapo ndi zinthu zina zambiri. Mwachibadwa, makolo safuna m’pang’ono pomwe kuti zinthu zofanana ndi zimenezi zidzachitikirenso ana awo. M’mayiko olemera, makolo amaona ana a mabwenzi ndi achibale awo akuchita bwino pantchito zaukatswiri ndipo amaoneka kuti akukhala moyo wabwino. Chotero, amakakamizika kuyesetsa kuchita zimene angathe kuti ana awonso akadzakula adzathe kukhala moyo wabwino, wotetezeka, ndi wokhutiritsa.—Mlaliki 3:13.
Kusankha Moyo Wabwino
3. Kodi Akristu asankha kuchita chiyani?
3 Monga otsatira a Yesu Kristu, Akristu asankha kupereka moyo wawo kwa Yehova. Iwo atsatira mawu a Yesu akuti: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine.” (Luka 9:23; 14:27) Ndithudi, moyo wa Mkristu umafuna kudzimana. Koma sikuti moyo wake ndi waumphawi ndi wosasangalatsa. Ndi wosangalatsa ndiponso wokhutiritsa, inde ndi moyo wabwino, chifukwa umafuna kupatsa, ndipo malinga ndi kunena kwa Yesu, “kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
4. Kodi Yesu analimbikitsa otsatira ake kufuna chiyani?
4 Anthu m’nthawi ya Yesu anali kukhala moyo wovuta kwambiri. Kuwonjezera pa kupeza zofunika pamoyo, iwo anali kupirira ulamuliro wankhanza wa Roma ndi miyambo yosautsa yonga chimtolo imene anakhazikitsa anthu otengeka mtima ndi chipembedzo nthawi imeneyo. (Mateyu 23:2-4) Koma anthu ambiri amene anamva za Yesu, anakonda kusiya zofuna zawo, ndi ntchito zomwe, ndipo anakhala otsatira ake. (Mateyu 4:18-22; 9:9; Akolose 4:14) Kodi ophunzira amenewa anali kuika moyo wawo ndi tsogolo lawo pangozi? Tamverani mawu a Yesu awa: “Onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amayi, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha.” (Mateyu 19:29) Yesu anatsimikizira otsatira ake kuti Atate wa kumwamba anali kudziwa zosowa zawo. Chotero, anawalimbikitsa kuti: “Muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mateyu 6:31-33.
5. Kodi makolo ena amaona bwanji mawu a Yesu akuti Mulungu adzasamalira atumiki ake?
5 Zinthu sizikusiyana kwambiri ndi mmene zilili masiku ano. Yehova amadziwa zimene timafuna, ndipo amene amaika zinthu za Ufumu patsogolo m’moyo wawo, makamaka amene akuchita utumiki wanthawi zonse, Yehova akuwatsimikiziranso kuti adzawasamalira. (Malaki 3:6, 16; 1 Petro 5:7) Koma makolo ena amakhala okayikira kwambiri pankhani imeneyi. N’zoona kuti amafuna kuona ana awo akupita patsogolo mu utumiki wa Yehova, mwina m’kupita kwanthawi kuyamba utumiki wanthawi zonse. Koma poganizira mmene kupeza ndalama ndi ntchito kwakhalira kovuta masiku ano, iwo amaona kuti n’kofunika kuti choyamba ana awo apeze maphunziro abwino. Akuchita zimenezi kuti ana awo adzakhale ndi maphunziro a ntchito imene angaifune kapena kuti adzakhale ndi chinachake chimene angadalire zinthu zitavuta. Makolo otero, nthawi zambiri amaona kuti maphunziro abwino ndi maphunziro apamwamba.
Kukonza Tsogolo
6. Kodi mawu akuti “maphunziro apamwamba” agwiritsidwa ntchito motani m’nkhani ino?
6 Maphunziro amasiyanasiyana mogwirizana ndi dziko. Mwachitsanzo, ku United States, masukulu a boma amapereka maphunziro ofunika kwa zaka 12. Zikatero, ophunzira angasankhe kupita ku yunivesite kapena ku koleji kwa zaka zinayi kapena kuposapo. Amachita zimenezi kuti akhale ndi digiri kapena kuti apitirizebe maphunziro a payunivesite ngakhale ali kale ndi digiri. Cholinga chimakhala chakuti adziwe ntchito ya udokotala, zamalamulo, uinjiniya ndi zina zotero. Maphunziro otero a payunivesite ndi amene tikutanthauza m’nkhani ino tikamati “maphunziro apamwamba.” Koma palinso masukulu ophunzitsa ntchito zamanja. Masukulu amenewa amaphunzitsa anthu m’nthawi yochepa kuti akhale ndi setifiketi kapena dipuloma paluso lina kapena ntchito ina yake.
7. Kodi ophunzira m’sukulu za sekondale akuwakakamiza kuchita chiyani?
7 Masiku ano sukulu za sekondale zambiri zikukonzekeretsa ophunzira awo kuti adzakhale ndi maphunziro apamwamba. Kuti akwaniritse zimenezi, sukulu za sekondale zambiri zimangophunzitsa zinthu zimene zingawathandize kukhoza bwino mayeso opitira ku yunivesite m’malo mowaphunzitsa zinthu zimene zingawathandize kupeza ntchito. Ophunzira m’sukulu za sekondale masiku ano akukakamizidwa kwambiri ndi aphunzitsi, alangizi, ndi ophunzira anzawo kuti akhale ndi cholinga chopita ku mayunivesite otchuka kwambiri. Kumayunivesite amenewa n’kumene amaganiza kuti mwina angapeze digiri imene ingawathandize kupeza ntchito zabwino ndiponso za malipiro ambiri.
8. Kodi ndi nkhani zotani zimene makolo achikristu afunika kusankhapo?
8 Chotero, kodi makolo achikristu angachite chiyani? N’zoona kuti iwo akufuna ana awo kuchita bwino kusukulu ndi kuphunzira luso lofunika loti lidzawathandize m’tsogolo. (Miyambo 22:29) Koma, kodi makolo adzangolekerera ana awo kutengeka ndi mzimu wopikisana wokhala ndi zinthu zambiri zakuthupi ndiponso moyo wopeza bwino? Kodi zolankhula ndi zochita zawo, zimalimbikitsa ana awo kukhala ndi zolinga zotani? Makolo ena amagwira ntchito mwakhama ndi kusunga ndalama kuti adzathe kutumiza ana awo ku mayunivesite ndi makoleji nthawi ikadzakwana. Ena amalolera kukongola ndalama kuti adzathandize ana awo. Koma posankha zoti achite m’pofunika kuonanso mbali zina osati ndalama zokha. Kodi maphunziro apamwamba masiku ano amafunanso zotani?—Luka 14:28-33.
Zimene Maphunziro Apamwamba Amafuna
9. Kodi masiku ano tinganene chiyani pankhani ya ndalama zolipirira maphunziro apamwamba?
9 Nthawi zambiri tikaganiza zimene maphunziro apamwamba amafuna, timangoganiza za ndalama. M’mayiko ena, boma ndi limene limalipira ndalama za maphunziro apamwamba ndipo ophunzira amene ali ndi zowayenereza salipira kalikonse. Koma m’mayiko ambiri, maphunziro apamwamba ndi odula kwambiri ndipo akukwerabe mtengo. Nkhani ina mu nyuzipepala ya New York Times Op-Ed inati: “Maphunziro apamwamba ankaonedwa monga njira yoti aliyense apezere mwayi wa ntchito zosiyanasiyana. Koma masiku ano, maphunziro apamwamba akusonyeza kusiyana kumene kuli pakati pa olemera ndi osauka.” M’mawu ena, maphunziro abwino kwambiri ndiponso apamwamba akukhala a anthu achuma ndi otchuka. Amenewa amaphunzitsa ana awo n’cholinga choti anawonso adzakhale anthu achuma ndiponso otchuka m’dzikoli. Kodi makolo achikristu ayenera kusankhira ana awo zimenezi?—Afilipi 3:7, 8; Yakobo 4:4.
10. Kodi maphunziro apamwamba amagwirizana motani ndi kupititsa patsogolo dongosolo lino?
10 Ngakhale kumene maphunziro apamwamba ndi aulere, pamakhala maudindo ena obisika oti mudzakwaniritse. Mwachitsanzo, magazini ya The Wall Street Journal inanena kuti m’dziko lina la kumwera cha kum’mawa kwa Asia, boma lili ndi “dongosolo la maphunziro limene limalimbikitsa dala ophunzira ochita bwino koposa kuti azipeza malo apamwamba.” M’kupita kwa nthawi, “malo apamwamba” amenewa amatanthauza kupita ku mayunivesite otchuka kwambiri pa dziko lapansi monga Oxford ndi Cambridge ku England, makoleji ndi mayunivesite a Ivy League ku United States, ndi ena otero. N’chifukwa chiyani bomali limapereka maphunziro otero? Magaziniyo inati: “Kuti alimbikitse chuma cha dzikolo.” Maphunziro angakhale aulere, koma zotsatira zake zimakhala zoti ophunzirawo amangokhalira kupititsa patsogolo dongosolo lino. Ngakhale kuti moyo wotero ndi umene anthu ambiri amaufuna m’dzikoli, kodi ndi umene makolo achikristu akufunira ana awo?—Yohane 15:19; 1 Yohane 2:15-17.
11. Kodi malipoti akusonyeza chiyani pankhani ya kumwetsa mowa ndi chiwerewere pakati pa ophunzira a kuyunivesite?
11 Chinthu china chofunika kuganizira ndicho zochitika za kumalo ophunzirirako. Kumayunivesite ndi makoleji kumapezeka makhalidwe oipa monga kumwa mankhwala osokoneza bongo, kumwetsa mowa, chiwerewere, chinyengo, kuzunza ophunzira atsopano, ndi makhalidwe ena ambiri ofanana ndi amenewa. Taganizirani za kumwetsa mowa. Pofotokoza za kumwetsa mowa n’cholinga choledzera magazini ya New Scientist inati: “Pa ophunzira 100 alionse [pa mayunivesite a ku United States] pafupifupi ophunzira 44 amamwetsa mowa kamodzi pamilungu iwiri iliyonse.” Vutoli limapezekanso kwambiri pakati pa achinyamata ku Australia, Britain, Russia ndi mayiko ena. Pankhani ya chiwerewere, ophunzira a kuyunivesite ali ndi mawu awo okuluwika amene amalankhula akamanena za kugonana. Malinga ndi kunena kwa magazini ya Newsweek, mawu amene amalankhulawo “amanena za chizolowezi chochita zachiwerewere kamodzi, monga kupsopsonana mpaka kugonana kumene. Amene amachita zimenezi ndi anthu osadziwana bwinobwino oti angokumana kumene ndipo saganizanso zoti akambirana akamaliza 1 Akorinto 5:11; 6:9, 10.
zachiwerewerezo.” Kafukufuku akusonyeza kuti ophunzira pakati pa 60 ndi 80 mwa ophunzira 100 alionse amachita chiwerewere cha mtundu umenewu. Mkazi wina wochita kafukufuku anati: “Ngati ndiwe wophunzira wabwinobwino wa pakoleji uyenera kuchita zimenezi.”—12. Kodi ophunzira a kukoleji amakumana ndi zotani?
12 Kuwonjezera pa kuipa kwa malo, ophunzira amapanikizika ndi za kusukulu ndiponso mayeso. Kuti ophunzira akhoze mayeso, amafunikira kuwerenga ndi kulemba homuweki. Ophunzira ena angafune kugwira ntchito ya ganyu pamene ali pasukulu. Zonsezi zimatenga nthawi yawo yambiri ndiponso nyonga. Kodi mudzatsala ndi nthawi ndiponso nyonga iliyonse yochitira zinthu zauzimu? Zochita zikachuluka, kodi n’ziti zimene mudzasiya kaye kuchita? Kodi zinthu za Ufumu zidzakhalabe patsogolo, kapena mudzaziika kaye pambali? (Mateyu 6:33) Baibulo limalimbikitsa Akristu kuti: “Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.” (Aefeso 5:15, 16) N’zomvetsa chisoni kuti ena ataya chikhulupiriro ali kukoleji chifukwa cha zinthu zina zofuna nthawi ndi nyonga yawo kapena chifukwa cha khalidwe losemphana ndi malemba.
13. Kodi makolo achikristu afunika kuganizira mafunso otani?
13 Koma chiwerewere, makhalidwe ena oipa, ndi Miyambo 22:3; 2 Timoteo 2:22) Kodi phindu limene ana angapeze n’lofunika kwambiri moti zilibe kanthu kuti akakumana ndi ngozi yotani? Ndipo funso lofunika kwambiri n’loti, kodi ana akuphunzitsidwa chiyani pa zinthu zimene ayenera kuika patsogolo m’moyo? * (Afilipi 1:10; 1 Atesalonika 5:21) Makolo afunika kupemphera kwambiri ndi kuganizira mofatsa za mafunso amenewa ndiponso za ngozi imene ingakhalepo chifukwa chotumiza ana awo kusukulu yomwe ili mu mzinda wina kapena dziko lina.
kupanikizika sizimangopezeka kukoleji ndi kuyunivesite kokha. Koma achinyamata ambiri akudziko amangoona zinthu zimenezi kukhala mbali ya maphunziro, ndipo amaganiza kuti palibe cholakwika ndi zinthu zimenezi. Kodi makolo achikristu angalole dala ana awo kupezeka kumalo otero kwa zaka zinayi kapena mwina zoposa pamenepa? (Kodi Pali Maphunziro Ena M’malo mwa Maphunziro Apamwamba?
14, 15. (a) Mosasamala kanthu za zimene ambiri amaganiza, kodi ndi uphungu uti wa m’Baibulo umene umagwira ntchito masiku ano? (b) Kodi ndi mafunso otani amene achinyamata afunika kudzifunsa?
14 Masiku ano, maganizo a anthu ambiri ndi akuti, kuti achinyamata zinthu ziwayendere bwino afunika maphunziro a kuyunivesite basi. Koma m’malo motsatira maganizo amene anthu ambiri ali nawo, Akristu amamvera langizo la Baibulo lakuti: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:2) M’mbali yomaliza ya nthawi ya mapetoyi, kodi chifuniro cha Mulungu kwa anthu ake, akulu ndi ana n’chotani? Paulo analimbikitsa Timoteo kuti: “Khala maso m’zonse, imva zowawa, chita ntchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako.” Mawu amenewa amagwiranso ntchito kwa tonsefe masiku ano.—2 Timoteo 4:5.
15 M’malo motengeka ndi mzimu wa dziko wokonda kwambiri zinthu za kuthupi, tonsefe tifunika ‘kukhala maso,’ kuikabe maso athu pa zinthu zauzimu. Ngati ndinu wachinyamata, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikuyesetsa kwambiri kuti “ndikwaniritse utumiki wanga,” kuti ndikhale mtumiki woyenerera wa Mawu a Mulungu? Kodi ndakonza zotani kuti ndichite utumiki wanga mokwanira? Kodi ndaganizapo zochita utumiki wanthawi zonse monga ntchito yanga?’ Mafunso amenewa ndi ovuta, makamaka ngati mukuona achinyamata ena akuchita zinthu zokonda iwowo basi, ‘kufunafuna zinthu zazikulu’ zimene akuganiza kuti zidzawathandiza kukhala ndi tsogolo labwino. (Yeremiya 45:5) Chotero, makolo achikristu mwanzeru amaonetsetsa kuti pabanja pakuchitika zinthu zosonyeza kuti amakonda zinthu zauzimu ndipo amaphunzitsa ana awo zimenezi kuyambira ali akhanda.—Miyambo 22:6; Mlaliki 12:1; 2 Timoteo 3:14, 15.
16. Kodi makolo achikristu angachite bwanji mwanzeru kuti banja lawo likhale lolimbikitsa mwauzimu kwa ana awo?
16 M’banja lina la ana aamuna atatu, mwana wamkulu anati: “Amayi anali kusamala kwambiri ndi anthu amene tinali kucheza nawo.” M’banja limeneli, mayi wakhala mtumiki wanthawi zonse kwa zaka zambiri. Mwanayu anapitiriza kuti: “Sitinali kucheza ndi anthu omwe tinali kuphunzira nawo kusukulu koma tinali kucheza ndi anthu okhawo a mu mpingo amene anali ndi makhalidwe abwino auzimu. Amayi nthawi zonse analinso kuitanira kunyumba kwathu anthu amene ali mu utumiki wanthawi zonse monga amishonale, oyang’anira oyendayenda, a pa Beteli, ndi apainiya kuti tizicheza nawo. Kumvetsera zokumana nazo zawo ndi kuona mmene analili osangalala zinatithandiza kukhala ndi chikhumbo chofuna kuchita utumiki wanthawi zonse.” Masiku ano, n’zosangalatsa kwambiri kuona ana onse atatu ali mu utumiki wanthawi zonse. Wina akutumikira pa Beteli, wina anachita nawo Sukulu Yophunzitsa Utumiki ndipo wina akuchita upainiya.
17. Kodi makolo angatsogolere bwanji ana awo posankha maphunziro a kusukulu ndi ntchito zimene afuna kudzagwira? (Onani bokosi patsamba 29.)
17 Kuwonjezera pa kuonetsetsa kuti banja lawo ndi lolimba mwauzimu, makolo afunikanso kuyamba mwamsanga kutsogolera bwino ana awo posankha *
maphunziro a kusukulu ndiponso ntchito. Mnyamata wina, amene tsopano akutumikira pa Beteli, anati: “Makolo anga onse awiri anachita upainiya asanakwatirane ndiponso atakwatirana. Ndipo anayesetsa kwambiri kuti tonse m’banjamo tikhale ndi mzimu wa upainiya. Nthawi zonse pamene tinali kusankha maphunziro kusukulu kapena kusankha zochita zimene zingakhudze tsogolo lathu, iwo anali kutilimbikitsa kusankha zinthu zimene zidzatipatsa mpata wabwino wopeza ntchito ya ganyu kwinaku tikuchita upainiya.” M’malo mosankha maphunziro amene cholinga chake ndi kuwathandiza kupita ku yunivesite, makolo ndi ana afunika kuona maphunziro amene ali othandiza pochita utumiki wa Mulungu.18. Kodi ndi ntchito zotani zimene achinyamata angaziganizire?
18 Kafukufuku akusonyeza kuti m’mayiko ambiri, muli kusowa kwa anthu ogwira ntchito zamanja ndi ntchito zina osati kusowa kokhala ndi anthu omaliza maphunziro a payunivesite. Nyuzipepala ya USA Today inanena kuti “anthu 70 ogwira ntchito pa anthu 100 alionse, m’zaka zikubwerazi sadzafunika kukhala ndi digiri ya zaka zinayi kukoleji. Koma m’malo mwake, azifunika kukhala ndi digiri ya zaka ziwiri kukoleji kapena kukhala ndi setifiketi yosonyeza kuti akudziwa ntchito yamanja.” Sukulu zambiri zotero zimaphunzitsa kwa nthawi yochepa ntchito za mu ofesi, kukonza galimoto, makompyuta, mipope, kukonza tsitsi, ndi ntchito zina zambiri. Kodi ntchitozi anthu amazikonda? Inde amazikonda. Mwina ntchito zoterozo si zosangalatsa kwambiri monga momwe ena amaganizira. Komatu zimawathandiza kupeza zofunika pamoyo ndiponso zimawapatsa mpata wochita zinthu zina ngati akufuna. Izi n’zimene amafunikira anthu omwe ntchito yawo yeniyeni ndi kutumikira Yehova.—2 Atesalonika 3:8.
19. Kodi njira yodalirika kwambiri yokhalira ndi moyo wosangalatsa ndi wokhutiritsa ndi yotani?
19 Baibulo limalimbikitsa kuti: “Anyamata ndiponso anamwali . . . alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo.” (Salmo 148:12, 13) Mosakayikira, ntchito yotumikira Yehova nthawi zonse ndiyo njira yodalirika kwambiri yokhalira ndi moyo wosangalatsa ndiponso wokhutiritsa poyerekeza ndi malo kapenanso zinthu zimene wina angakhale nazo m’dzikoli. Kumbukirani mawu a m’Baibulo akuti: “Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”—Miyambo 10:22.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 13 Kuti mupeze nkhani za amene anaona maphunziro auzimu kukhala ofunika kuposa maphunziro a kuyunivesite, onani Nsanja ya Olonda, yachingelezi ya May 1, 1982, masamba 3-6; April 15, 1979, masamba 5-10; Galamukani! yachingelezi ya June 8, 1978, tsamba 15; ndi ya August 8, 1974, masamba 3-7.
^ ndime 17 Onani Galamukani! ya October 8, 1998, “Kufunafuna Moyo Wotetezereka,” masamba 4-6, ndi yachingelezi ya May 8, 1989, “Kodi Ndingasankhe Ntchito Yotani?” masamba 12-14.
Kodi Mungafotokoze?
• Kodi Akristu amadalira chiyani kuti akhale ndi tsogolo labwino?
• Kodi ndi mavuto otani amene makolo achikristu amakumana nawo ponena za tsogolo la ana awo?
• Kodi mufunika kuganizira chiyani poona ubwino ndi kuipa kochita maphunziro apamwamba?
• Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kusankha ntchito yotumikira Yehova?
[Mafunso]
[Bokosi patsamba 29]
Kodi Maphunziro Apamwamba Ali Ndi Phindu Lanji?
Anthu ambiri amene amapita ku yunivesite amafuna kukhala ndi digiri imene idzawathandiza kupeza ntchito yolandira ndalama zambiri ndiponso yotetezeka. Koma malipoti a boma amasonyeza kuti pa anthu 100 alionse opita ku koleji, ndi anthu 25 okha amene amakhala ndi digiri pa zaka sikisi. Zimenezi zikusonyeza kuti ambiri sachita bwino. Komano ngakhale munthu atakhala ndi digiri, kodi ndiye kuti basi adzapeza ntchito yabwino? Taonani zimene apeza posachedwapa atachita kafukufuku.
“Ngati munthu wapita ku [yunivesite ya] Harvard kapena ku Duke, sindiye kuti basi adzapeza ntchito yabwino ndiponso yolandira ndalama zambiri . . . Makampani sadziwa zambiri zokhudza achinyamata ofuna ntchito. Digiri yapamwamba kwambiri (ya ku Ivy League) ingakhale yosangalatsa. Koma m’kupita kwa nthawi, zomwe olemba ntchito amayang’ana ndi zinthu zimene anthu angathe kuchita kapena zimene sangathe.”—Newsweek, November 1, 1999.
“Ngakhale kuti ntchito masiku ano zimafuna kuti munthu akhale ndi luso kwambiri poyerekeza ndi kale . . . , luso lofunika pantchito zimenezi ndi luso la kusekondale monga masamu, kuwerenga ndiponso kulemba limene munthu amakhala nalo ali m’chaka cha chisanu ndi chinayi pasukulu . . . , osati luso limene amaliphunzira ali kukoleji. . . . Ophunzira safunikira kuchita kupita ku koleji kuti apeze ntchito yabwino, koma afunika kukhala ndi luso limene anaphunzira kusukulu ya sekondale.”—American Educator, Spring 2004.
“Makoleji ambiri saphunzitsa zinthu zothandiza ophunzira kupeza ntchito mogwirizana ndi mmene zinthu zilili m’dziko. Sukulu zophunzitsa ntchito zamanja . . . zikuchuluka kwambiri. Anthu opita ku sukulu zimenezi awonjezereka [pafupifupi ndi theka] kuchoka mu 1996 kufika mu 2000. . . . Komabe, madipuloma odula ndi otenga nthawi yaitali a kukoleji akhala osathandiza kwenikweni poyerekeza ndi kale.”—Time, January 24, 2005.
“Kafukufuku wochokera ku bungwe la U.S. Department of Labor wa chaka cha 2005 akusonyeza zinthu zomvetsa chisoni kwambiri. Wophunzira mmodzi mwa ophunzira atatu alionse omaliza maphunziro azaka zinayi pakoleji sadzapeza ntchito yogwirizana ndi madigiri awo.”—The Futurist, July/August 2000.
Chifukwa cha zonsezi, anthu ambiri odziwa za maphunziro akukayikira kwambiri phindu la maphunziro apamwamba masiku ano. Magazini yotchedwa The Futurist inati: “Tikuphunzitsa anthu ndi zolinga zolakwika.” Mosiyana ndi zimenezi, taonani zimene Baibulo limanena za Mulungu: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”—Yesaya 48:17, 18.
[Chithunzi patsamba 26]
Anasiya ntchito zawo ndi kutsatira Yesu
[Chithunzi patsamba 31]
Makolo achikristu mwanzeru amaonetsetsa kuti pabanja pakuchitika zinthu zolimbikitsa mwauzimu kuyambira ana ali akhanda