Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za M’buku Loyamba la Mbiri

Mfundo Zazikulu za M’buku Loyamba la Mbiri

Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za M’buku Loyamba la Mbiri

PAPITA zaka 77 tsopano chichokereni Ayuda mu ukapolo wa ku Babulo kubwerera kwawo. Kachisi amene anamangidwanso ndi Kazembe Zerubabele wakhalapo zaka 55. Chifukwa chachikulu chimene Ayuda anabwerera ku Yerusalemu ndicho kuyambitsanso kulambira koona. Koma anthu alibe changu cha kupembedza Yehova. Akufunika kuwalimbikitsa kwambiri, ndipo zimenezi n’zomwe buku Loyamba la Mbiri la m’Baibulo likuchita.

Kupatulapo kulembedwa kwa mibadwo, buku Loyamba la Mbiri limafotokoza zinthu zomwe zinachitika pafupifupi zaka 40, kuchokera pa imfa ya Mfumu Sauli mpaka pa imfa ya Mfumu Davide. Wansembe Ezara ndi amene analemba buku ili m’chaka cha 460 B.C.E. Buku Loyamba la Mbiri ndi lofunika kwa ife chifukwa limafotokoza za kulambira kwa pakachisi ndipo limasonyeza mfundo zonena za mzera wobadwira wa Mesiya. Monga mbali ya Mawu a Mulungu ouziridwa, uthenga wake umalimbitsa chikhulupiriro chathu ndipo umatithandiza kulimvetsa bwino Baibulo.​—Ahebri 4:12.

MNDANDANDA WOFUNIKA WA MAYINA

(1 Mbiri 1:1–9:44)

Mndandanda watsatanetsatane wa mayina a mibadwo umene Ezara analemba ndi wofunika pa zifukwa zitatu: kutsimikizira kuti anthu ovomerezeka okha ndi amene anatumikira monga ansembe, kuthandiza kusonyeza anthu oyenera kulandira cholowa cha fuko, ndi kusunga zolemba za mbadwo wa makolo wofika kwa Mesiya. Mayina a mibadwo amagwirizanitsa Ayuda ndi mbiri yawo yakale mpaka kufika pa munthu woyamba, Adamu. Pali mibadwo khumi kuchoka pa Adamu kufika pa Nowa, ndipo palinso mibadwo khumi kufika pa Abrahamu. Pambuyo pondandalitsa ana a Ismayeli, ana a Ketura, mdzakazi wa Abrahamu, ndi ana a Esau, nkhaniyi ikufotokozanso za mzera wobadwira wa ana 12 a Israyeli.​—1 Mbiri 2:1.

Ezara akufotokoza kwambiri za mbadwa za Yuda chifukwa ndiwo mzera umene Mfumu Davide anabadwira. Pali mibadwo 14 kuchoka pa Abrahamu kufika pa Davide ndiponso mibadwo ina 14 kufika nthawi imene anatengedwa kupita ku Babulo. (1 Mbiri 1:27, 34; 2:1-15; 3:1-17; Mateyu 1:17) Ndiyeno Ezara akutchula mbadwa za mafuko a kum’mawa kwa Yordano, kenako mbadwo wa ana a Levi. (1 Mbiri 5:1-24; 6:1) Ndiye akufotokoza mwachidule mafuko ena a kumadzulo kwa mtsinje wa Yordano ndipo akufotokoza mwatsatanetsatane mbadwa za Benjamini. (1 Mbiri 8:1) Palinso mayina a anthu omwe anali oyamba kukakhala ku Yerusalemu atamasulidwa mu ukapolo ku Babulo.​—1 Mbiri 9:1-16.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

1:18—Kodi anali bambo a Sela ndani​—Kainane kapena Aripakasadi? (Luka 3:35, 36) Aripakasadi ndiye anali bambo ake a Sela. (Genesis 10:24; 11:12) Dzina loti “Kainane” pa Luka 3:36 liyenera kuti linali kulakwitsa kwa dzina loti “Kaldayo.” Ngati zili choncho, ndiye kuti malemba oyambirira ankanena za “mwana wa Aripakasadi wa ku Kaldayo.” Kapena n’kutheka kuti mayinawa Kainane ndi Aripakasadi amanena munthu mmodzi. Koma sitiyenera kunyalanyaza mfundo yakuti mawu akuti “mwana wa Kainane” sapezeka m’malemba ena a pamanja.​—Luka 3:36.

2:15—Kodi Davide anali mwana wachisanu ndi chiwiri wa Jese? Ayi. Jese anali ndi ana aamuna asanu ndi atatu, ndipo Davide anali wamng’ono pa onse. (1 Samueli 16:10, 11; 17:12) Zikuoneka kuti mwana mmodzi wa Jese anamwalira asanakhale ndi ana. Popeza kumuika mwanayo pa mndandanda wa mayina a mibadwo sikukanathandiza, Ezara analumpha dzina lake.

3:17—N’chifukwa chiyani lemba la Luka 3:27 limanena za Salatieli mwana wa Yekoniya kukhala mwana wa Neri? Yekoniya anali bambo wa Salatieli. Komabe, zikuoneka kuti Neri anapereka mwana wake wa mkazi kwa Salatieli kukhala mkazi wake. Luka anali kunena za mkamwini wa Neri kukhala Mwana wa Neri monga mmene anachitira kwa Yosefe. Iye anatcha Yosefe kukhala mwana wa Heli, bambo ake a Mariya.​—Luka 3:23.

3:17-19—Kodi ubale wa Zerubabeli, Pedaya, ndi Salatieli unali wotani? Zerubabeli anali mwana wa Pedaya, amene anali mchimwene wake wa Salatieli. Koma nthawi zina Baibulo limatcha Zerubabeli kukhala mwana wa Salatieli. (Mateyu 1:12; Luka 3:27) Izi zili choncho mwina chifukwa chakuti Pedaya atamwalira, Salatieli ndi amene analera Zerubabeli. Mwinanso chifukwa chakuti Salatieli anamwalira asanakhale ndi mwana, Pedaya anakwatira mkazi wa mchimwene wakeyo, ndipo atakwatirana Zerubabeli anali mwana wawo woyamba.​—Deuteronomo 25:5-10.

5:1, 2—Kodi kulandira zoyenera woyamba kubadwa kunatanthauzanji kwa Yosefe? Kunatanthauza kuti Yosefe analandira magawo awiri a cholowa. (Deuteronomo 21:17) Chotero, iye anakhala bambo wa mafuko awiri, la Efraimu ndi la Manase. Ana aamuna ena a Israyeli aliyense anakhala kholo la fuko limodzi.

Zimene Tikuphunzirapo:

1:1–9:44. Mndandanda wa mayina a anthu amene anakhalakodi uli umboni wosonyeza kuti dongosolo lonse la kulambira koona ndi lozikidwa pa zinthu zenizeni osati nthano.

4:9, 10. Yehova anayankha pemphero lochokera pansi pa mtima la Yabezi lofuna kukulitsa malire a gawo lake mwamtendere. Anapempha zimenezi kuti pamalo pakepo padzakhale anthu ambiri oopa Mulungu. Ifenso tifunika kupemphera mochokera pansi pa mtima kuti Mulungu awonjezere anthu pamene tichita nawo mwachangu ntchito yopanga ophunzira.

5:10, 18-22. M’masiku a Mfumu Sauli, mafuko amene anali kum’mawa kwa Yordano anagonjetsa Ahagiri ngakhale kuti chiwerengero cha Ahagiri chinali chochuluka kuwirikiza kawiri pochiyerekeza ndi cha mafukowa. Izi zinali choncho chifukwa chakuti amuna amphamvu a mafuko amenewa anadalira Yehova kuwathandiza. Tiyeni tidalire Yehova ndi mtima wonse pamene tikupitiriza kumenya nkhondo yauzimu ndi adani omwe ali ochuluka kutiposa.​—Aefeso 6:10-17.

9:26, 27. Alevi oyang’anira zipata anali ndi udindo wofunika kwambiri. Iwo anapatsidwa makiyi otsegulira malo opatulika osiyanasiyana a pakachisi. Anali okhulupirika potsegula zipata tsiku lililonse. Tapatsidwa udindo wofikira anthu m’gawo lathu ndi kuwathandiza kuyamba kupembedza Yehova. Kodi sitiyenera kukhala odalirika ndi okhulupirika monga mmene Alevi oyang’anira zipata anachitira?

DAVIDE ALAMULIRA MONGA MFUMU

(1 Mbiri 10:1–29:30)

Nkhaniyi imayamba ndi kufotokoza kumwalira kwa Mfumu Sauli ndi ana ake atatu pa nkhondo yomenyana ndi Afilisiti pa phiri la Giliboa. Davide, mwana wa Jese anaikidwa kukhala mfumu ya fuko la Ayuda. Amuna a m’mafuko onse anabwera ku Hebroni ndipo anamuika kukhala mfumu yolamulira Israyeli yense. (1 Mbiri 11:1-3) Patapita nthawi yochepa, anagonjetsa Yerusalemu. Kenako, Aisrayeli anabweretsa likasa la chipangano ku Yerusalemu “ndi kufuula, ndi kumveka kwa lipenga . . . ndi zisakasa, ndi azeze.”​—1 Mbiri 15:28.

Davide anafuna kumangira Mulungu woona nyumba. Yehova anasungira Solomo mwayi umenewu ndipo anachita pangano la Ufumu ndi Davide. Pamene Davide anapitiriza kulimbana ndi adani a Israyeli, Yehova anam’thandiza kugonjetsa adaniwo nthawi zambiri. Ntchito yowerenga anthu mosavomerezeka inachititsa kuti anthu 70,000 aphedwe. Atalandira malangizo kwa mngelo omanga guwa la nsembe la Yehova, Davide anagula malo kwa Orinani Myebusi. Davide anayamba ‘kukonzekeratu mochuluka’ kumanga nyumba “yaikulu yopambana” ya Yehova pamalopo. (1 Mbiri 22:5) Davide anakonza dongosolo la ntchito za Alevi, zimene azifotokoza mwatsatanetsatane kwambiri m’buku lino Loyamba la Mbiri kuposa kwina kulikonse m’Malemba. Mfumu ndi anthu anapereka za kachisi mowolowa manja. Atalamulira kwa zaka 40, Davide anamwalira “wochuluka masiku, zolemera, ndi ulemerero; ndi Solomo mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.”​—1 Mbiri 29:28.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

11:20, 21—Kodi Abisai anali ndi udindo wotani poyerekeza ndi amuna atatu amphamvu a Davide? Abisai sanali mmodzi wa amuna atatu amphamvu koposa amene anatumikira Davide. Koma malinga n’kunena kwa 2 Samueli 23:18, 19, iye anali mkulu wa ankhondo 30 ndipo anali kulemekezedwa kwambiri kuposa aliyense wa iwo. Abisai anatchuka mofanana ndi amuna atatu amphamvu chifukwa anachita zamphamvu mofanana ndi Yasobeamu.

12:8—Kodi nkhope za gulu lankhondo la Agadi zinafanana bwanji ndi “nkhope za mikango”? Amuna olimba mtima amenewa anali kukhala ndi Davide m’chipululu. Tsitsi lawo linali litatalika. Chifukwa chokhala ndi tsitsi lalitali anali kuoneka oopsa, monga mkango.

13:5—Kodi “Sihori wa ku Aigupto” anali chiyani? Popeza kuti “Sihori” kwenikweni amatanthauza “mtsinje” m’Chihebri, anthu ena amaganiza kuti mawuwa amatanthauza nthambi ya mtsinje wa Nile. Amaganizanso kuti “mtsinje wa Aigupto” wotchulidwa pa Numeri 34:5 ndi “mtsinje” womwewo. Koma pa Numeri 34:5 anagwiritsa ntchito liwu lina lachihebri limene lingamasulidwe molondola kwambiri kukhala “chigwa.” Chotero, “Sihori wa ku Aigupto” anthu ambiri amanena kuti ndi “chigwa cha Aigupto,” chigwa chakuya ndiponso chachitali chimene chachita malire kumwera chakumadzulo kwa Dziko Lolonjezedwa.​—Numeri 34:2, 5; Genesis 15:18.

16:30—Kodi ‘kunjenjemera’ chifukwa cha Yehova kukutanthauzanji? Mawu akuti ‘kunjenjemera’ pa lembali agwiritsidwa ntchito mophiphiritsa kutanthauza kuopa Yehova chifukwa chomupatsa ulemu kwambiri.

16:1, 37-40; 21:29, 30; 22:19—Kodi ndi dongosolo lotani la kulambira lomwe linali kuchitika m’Israyeli kuyambira nthawi imene Likasa linabwera ku Yerusalemu kufikira nthawi imene kachisi anamangidwa? Davide atabweretsa Likasa ku Yerusalemu ndi kuliika m’hema amene anamanga, panali patapita zaka zambiri Likasalo lisanakhale m’chihema. Atalisamutsira ku Yerusalemu, Likasalo linakhalabe m’hema. Chihema chinali ku Gibeoni, kumene Mkulu wa Ansembe Zadoki ndi abale ake anali kuwotchera nsembe zimene Chilamulo chinanena. Dongosolo limeneli linapitiriza mpaka nthawi imene kachisi anamalizidwa ku Yerusalemu. Atamaliza kachisi, anasamutsira chihema ku Yerusalemu kuchoka ku Gibeoni. Ndipo Likasa linaikidwa m’Malo Opatulikitsa a kachisi.​—1 Mafumu 8:4, 6.

Zimene Tikuphunzirapo:

13:11. M’malo mokwiya ndi kuimba Yehova mlandu pamene zoyesayesa zathu zilephera, tiyenera kupenda zochitikazo ndi kuyesa kuona chimene chapangitsa kuti tilephere. Mosakayikira, Davide anachita zimenezo. Iye anatengerapo phunziro pa zolakwa zake ndipo m’kupita kwa nthawi anatha bwinobwino kubweretsa Likasa ku Yerusalemu mogwiritsa ntchito njira yoyenera. *

14:10, 13-16; 22:17-19. Nthawi zonse tiyenera kupemphera kwa Yehova ndi kuyang’ana kwa iye kuti atitsogolere tisanachite chilichonse chimene chidzatikhudza mwauzimu.

16:23-29. Kupembedza Yehova kuzikhala patsogolo m’moyo.

18:3. Yehova amakwaniritsa zimene amalonjeza. Kudzera mwa Davide, anakwaniritsa lonjezo lake lakuti adzapatsa mbewu ya Abrahamu dziko lonse la Kanani, “kuyambira pa nyanja ya Aigupto kufikira pa nyanja yaikulu, nyanja ya Firate.”​—Genesis 15:18; 1 Mbiri 13:5.

21:13-15. Yehova analamula mngelo kuletsa mliri chifukwa chakuti Iye amakhudzidwa kwambiri anthu Ake akamavutika. Ndithudi, “zifundo zake zichulukadi.” *

22:5, 9; 29:3-5, 14-16. Ngakhale kuti sanauzidwe kumanga kachisi wa Yehova, Davide anasonyeza mzimu wa kuwolowa manja. Chifukwa chiyani? Chifukwa anadziwa kuti zinthu zonse zimene anali nazo anazipeza chifukwa cha ubwino wa Yehova. Mtima woyamikira wofanana ndi wa Davide uyenera kutilimbikitsa kukhala ndi mzimu wowolowa manja.

24:7-18. Dongosolo la magulu 24 a ansembe limene Davide anakhazikitsa linali kugwirabe ntchito nthawi imene mngelo wa Yehova anaonekera kwa Zakariya, bambo a Yohane Mbatizi. Ndipo mngeloyo analengeza kuti kudzabadwa mwana dzina lake Yohane. Popeza Zakariya anali wa “gulu la ansembe la Abiya,” inali nthawi yake kutumikira pa kachisi. (Luka 1:5, 8, 9) Kuyambira kale anthu amene atsata kulambira koona ndi enieni, si anthu opeka. Timadalitsidwa tikamagwirizana mokhulupirika ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” pankhani ya kupembedza Yehova mwadongosolo masiku ano.​—Mateyu 24:45.

Tumikirani Yehova Mosangalala

Buku Loyamba la Mbiri silifotokoza chabe za mndandanda wa mayina a mibadwo. Limafotokozanso ntchito imene Davide anachita yosamutsira likasa la chipangano ku Yerusalemu ndi nkhondo zimene anapambana. Limanenanso zimene anachita pokonzekera ntchito yomanga kachisi, ndiponso za kukhazikitsa kwake magulu a ansembe a fuko la Levi otumikira pakachisi. Zonse zimene Ezara anafotokoza m’buku Loyamba la Mbiri ziyenera kuti zinapindulitsa Aisrayeli. Zinawathandiza kukhalanso achangu polambira Yehova pakachisi.

Davide anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri poika kulambira Yehova patsogolo m’moyo wake. M’malo modzipezera maudindo apadera, Davide anafuna kuchita chifuniro cha Mulungu. Tikulimbikitsidwa kugwiritsa ntchito malangizo ake kuti titumikire Yehova “ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu.”​—1 Mbiri 28:9.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Kuti muphunzire zina pankhani ya Davide yofuna kusamutsira Likasa ku Yerusalemu, onani Nsanja ya Olonda ya May 15, 2005, masamba 16 mpaka 19.

^ ndime 6 Kuti muphunzire zina zokhudza ntchito yowerenga anthu mosavomerezeka imene Davide anachita, onani Nsanja ya Olonda ya May 15, 2005, masamba 16 mpaka 19.

[Tchati/​Zithunzi pamasamba 8-11]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Mibadwo kuchokera pa Adamu kufika pa Noah (zaka 1,056)

4026 B.C.E. Adamu

Zaka 130 ⇩

Seti

105 ⇩

Enoki

90 ⇩

Kenani

70 ⇩

Mahalaheli

65 ⇩

Yaredi

162 ⇩

Enoki

65 ⇩

Metusela

187 ⇩

Lameki

182 ⇩

2970 B.C.E. NOWA abadwa

Mibadwo kuchokera pa Nowa kufika pa Abrahamu(zaka 952)

2970 B.C.E. Nowa

Zaka 502 ⇩

Semu

100 ⇩

CHIGUMULA 2370 B.C.E.

Aripakasadi

35 ⇩

Sela

30 ⇩

Ebere

34 ⇩

Pelege

30 ⇩

Reu

32 ⇩

Reu

30 ⇩

Nahori

29 ⇩

Tera

130 ⇩

2018 B.C.E. ABRAHAMU abadwa

Kuchoka pa Abrahamu mpaka pa Davide: mibadwo 14 (zaka 911)

2018 B.C.E. Abrahamu

Zaka 100.

Isake

60 ⇩

Yakobo

mwina.88 ⇩

Yuda

Perezi

Hezroni

Ramu

Amminadab

Nasoni

Salimoni

Boazi

Obedi

Jese

1107 B.C.E. DAVIDE abadwa