‘Iwo Akutsikira Kunyanja M’zombo’
‘Iwo Akutsikira Kunyanja M’zombo’
MUMZINDA wa Gloucester, ku Massachusetts, m’dziko la United States, muli chiboliboli cha mwala wa mkuwa cha munthu wowongolera chombo cha m’madzi, yemwe akuyesetsa kuwongolera chombocho panyanja patachita mafunde. Chibolibolicho anachiika kuti chikhale chikumbukiro cha asodzi ambirimbiri a ku Gloucester amene anafera panyanja. M’munsi mwa chibolibolichi ndiponso cha pafupi ndi chibolibolipo pali mawu opezeka pa Salmo 107:23, 24, akuti: “Iwo akutsikira kunyanja nalowa m’zombo, akuchita ntchito zawo pa madzi akulu; iwowa apenya ntchito za Yehova, ndi zodabwiza zake m’madzi ozama.”
Kusodza m’nyanja ya Atlantic, yomwe ili ndi nsomba zambiri, n’koopsa. Akuti kufika panopo, anthu aamuna okwana 5,368 a mumzinda wa Gloucester, womwe tsopano uli ndi anthu pafupifupi 30,000, afera m’nyanja posodza. Chikumbukirocho chimati: “Ena anafa chifukwa cha mphepo yamkuntho yochokera kumpoto chakummawa yomwe imapangitsa chimphepo ndiponso mafunde aatali. Ena anafa ali okhaokha atasochera m’kabwato chifukwa chosiyana ndi chombo chomwe chinapita nawo ku dera losodzeralo. Zombo zina zinawombana chifukwa cha chimphepo ndipo mwatsoka zinamira. Ena anawombedwa ndi sitima zam’madzi zomwe anakumanizana nazo mwangozi.”
Chikumbukirochi chimaikira umboni nkhani zomvetsa chisoni zokhudza chintchito chimene asodzi akhala akugwira ndiponso zoopsa zimene asodzi akumana nazo kwa zaka zambiri m’mbuyo monsemu. Tangoganizirani chisoni chosaneneka ndiponso kulira kwa anthu oferedwa amuna awo, abambo awo, azichimwene kapena azing’ono awo komanso ana awo. Komatu, Yehova Mulungu saiwala akazi ndi ana amasiye, ngakhalenso anthu amene anafera pamadziwo. Mtumwi Yohane ananenapo za zomwe zidzachitike m’tsogolo pamene anati: “Nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali mmenemo.” (Chivumbulutso 20:13) Panthawi yodzawaukitsa, anthu amene ‘anatsikira kunyanja m’zombo’ adzapenyadi “ntchito za Ambuye” zodabwitsa.