Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu a Yehova Akufalikira mu “Dziko la Chiwombankhanga”

Mawu a Yehova Akufalikira mu “Dziko la Chiwombankhanga”

Mawu a Yehova Akufalikira mu “Dziko la Chiwombankhanga”

“DZIKO la Chiwombankhanga.” Umu ndi mmene anthu a ku Albania amatchulira dziko lawo m’chinenero chawo. Dziko limeneli, lomwe lili m’mphepete mwa nyanja ya Adriatic lili m’dera lotchedwa Balkan Peninsula, pakati pa dziko la Greece ndiponso dziko lomwe kale linali Yugoslavia. Ngakhale kuti pali maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya komwe kunachokera anthu a ku Albania, akatswiri ochuluka a mbiri yakale amavomereza kuti anthuwa ndiponso chinenero chawo chinachokera kwa anthu akale a ku Illyria, amene buku la The Encyclopædia Britannica limati chikhalidwe chawo chinayamba kale kwambiri m’ma 2000 B.C.E.

Dziko la Albania lili ndi zinthu zachilengedwe zokongola. Kumpoto kwake kuli mapiri okhala ndi nsonga zambirimbiri ndipo kummwera kwake, ku nyanja ya Adriatic, kuli magombe okhala ndi mchenga woyera mbee. Komabe, dzikoli limakongola kwambiri chifukwa cha anthu ake. Ndi anthu ansangala, ochereza alendo, okonda kuseka ndiponso kucheza, a mitu yogwira zinthu msanga ndipo polankhula amalankhula ndi manja omwe.

Kunafika Mmishonale Wotchuka

N’zosakayikitsa kuti mlendo wina wapadera amene anafika kumeneku zaka zambiri zapitazo anachita chidwi ndi khalidwe losangalatsa la anthuwa ndiponso ndi kukongola kwa dzikoli. Cha m’ma 56 C.E., mtumwi Paulo, yemwe anali atayenda m’madera ambiri, analemba kuti: “Kufikira ku Iluriko, ndinakwanitsa [kulalikira] Uthenga Wabwino wa Kristu.” (Aroma 15:19) Kummwera kwa Iluriko n’kumene panopo kuli dera la pakati ndi la kumpoto kwa dziko la Albania. Paulo ankalemba zimenezi ali mu mzinda wa Korinto ku Girisi, kummwera kwa Iluriko. Mawu akuti anakwanitsa kulalikira mpaka “kufikira ku Iluriko” akusonyeza kuti mwina Paulo anafika kumalire a Iluriko kapena kuti anafika mpaka m’kati mwa chigawochi. Mulimonsemo, iyeyu ayenera kuti analalikira m’dera limene panopo lili kummwera kwa dziko la Albania. Motero, Paulo ndiye munthu wakale kwambiri amene akudziwika kuti analalikira za Ufumu ku Albania.

Kenaka panatha zaka zambiri. Maufumu anakhazikitsidwa ku Albania mpaka kuthetsedwa. Mayiko ena analamulira kadziko ka ku Ulayaka mpaka pamene ulamuliro wawo unafika pakutha, ndipo mapeto ake kadzikoka kanalandira ufulu wodzilamulira mu 1912. Patatha zaka pafupifupi teni, mawu a Ufumu wa Yehova anayambanso kumveka ku Albania.

Anayambanso Kufalikira Mochititsa Chidwi

M’ma 1920, anthu owerengeka a ku Albania omwe anasamukira ku United States n’kuyamba kumasonkhana ndi a Mboni za Yehova, omwe panthawiyo ankadziwika ndi dzina loti Ophunzira Baibulo a Padziko Lonse, anabwerera ku Albania kuti akauze ena zimene anaphunzirazo. Mmodzi wa anthu amenewa anali Nasho Idrizi. Anthu ena anamvera zonena zawo ndipo anayamba kumachuluka. Motero pofuna kuthandiza anthu achidwiwa, mu 1924 ofesi ya nthambi ya ku Romania inapatsidwa udindo woyang’anira ntchito yolalikira ku Albania.

Thanas Duli (kapena kuti Athan Doulis) anali mmodzi wa anthu amene anaphunzira za Yehova ku Albania pa zaka zimenezo. Iye amakumbukira kuti: “Mu 1925 ku Albania kunali mipingo itatu, ndipo m’madera osiyanasiyana m’dziko lonseli munali Ophunzira Baibulo ochepa komanso ochita chidwi owerengeka. Mosiyana kwambiri ndi anzawo ena onse m’dzikoli . . . anthuwa ankakondana.” *

Kuyenda m’dzikoli kunali kovuta kwambiri chifukwa cha misewu yake. Komabe, ofalitsa akhama analimba nazo. Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Areti Pina, yemwe amakhala kugombe la kummwera la Vlorë, anabatizidwa mu 1928 ali ndi zaka 18. Iye anayenda ulendo wodutsa m’zitunda ndi m’mitsetse ya mapiri, n’kumalalikira atatenga Baibulo lake m’manja. Mlongoyu anali mmodzi wa anthu a mumpingo winawake wolimba wa ku Vlorë cha kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1930.

Mmene chimafika chaka cha 1930, ntchito yolalikira ku Albania inali m’manja mwa ofesi ya nthambi ku Athens, m’dziko la Greece. Mu 1932 woyang’anira woyendayenda wochokera ku Greece anafika ku Albania kuti akalimbikitse abale. Anthu ambiri amene anali kuphunzira choonadi cha m’Baibulo panthawiyo anali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba. Anali anthu odziwika chifukwa cha udongo ndiponso kuwongoka mtima kwawo motero kulikonseko anthu ankawapatsa ulemu kwambiri. Ntchito ya abale okhulupirika amenewa inabala zipatso zambiri. M’chaka chilichonse, pa zaka za 1935 ndi 1936, ku Albania anagawira zowerenga pafupifupi 6,500 zofotokoza Baibulo.

Tsiku lina, m’chigawo cha pakati pa mzinda wa Vlorë, Nasho Idrizi anaika nkhani ina ya Mbale J. F. Rutherford pa galamafoni kuti anthu amvere. Anthu anatseka mabizinesi awo kudzamvetsera Mbale Idrizi akumasulira nkhaniyo mu Chialubaniya. Khama la anthu akale ophunzitsa Baibulo mosatopawa linapindula. Pofika chaka cha 1940 ku Albania kunali Mboni 50.

Dziko Losakhulupirira Kuti Kuli Mulungu

M’chaka cha 1939, boma la ndale za chifasizimu la ku Italy linalanda dzikoli. Aboma analetsa Mboni za Yehova pamodzi ndi ntchito yawo yolalikira. Kenaka posakhalitsa, asilikali a dziko la Germany analanda dzikoli. Mmene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inkatha panabwera mtsogoleri wina wa asilikali wodziwa kukopa anthu, dzina lake Enver Hoxha. Chipani chake cha Communist Party chinapambana pa chisankho cha mu 1946, ndipo iyeyu anakhala nduna yaikulu ya dzikolo. Zaka zotsatirapo zinadzatchedwa kuti nthawi ya ufulu, koma kwa anthu a Yehova imeneyi siinali nthawi yaufulu ayi.

Pang’ono ndi pang’ono, bomalo linayamba kusagwirizana ndi zopembedza. Mogwirizana ndi chikhulupiriro chawo chosalowerera m’ndale pokhala Akristu, a Mboni za Yehova ku Albania anakana kumenya nawo nkhondo ndi kuchita nawo ndale. (Yesaya 2:2-4; Yohane 15:17-19) Ambiri anatsekeredwa m’ndende, osapatsidwa chakudya kapena zinthu zina zofunika pamoyo. Nthawi zambiri, alongo awo auzimu amene sanali m’ndende ankawachapira zovala ndi kuwaphikira.

Analimba Mtima Pozunzidwa

Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1940, Frosina Xheka, amene panthawiyi anali ndi zaka zosakwana 20 ndipo ankakhala m’tauni ina ya kufupi ndi Përmet, anamva zimene azichimwene ake ankaphunzitsidwa ndi wa Mboni wina wosoka nsapato dzina lake Nasho Dori. * Akuluakulu aboma anali atayamba kukhwimitsira zinthu Mboni za Yehova, komabe chikhulupiriro cha Frosina chinakula, ndipo izi zinakhumudwitsa makolo ake. Frosina anati: “Iwo ankandibisira nsapato ndipo ndikapita kumisonkhano yachikristu ankandimenya. Anayesa kukonza zoti ndikwatiwe ndi munthu wosakhulupirira. Nditakana, anandithamangitsa kunyumba. Tsiku limenelo kunazizira kwambiri. Nasho Dori anapempha mbale Gole Flloko ku Gjirokastër kuti andithandize. Iwowa anakonza zoti ndizikakhala ndi banja lawo. Azichimwene anga anakhala m’ndende kwa zaka ziwiri chifukwa chokana kulowerera m’ndale. Atamasulidwa, ndinasamukira ku Vlorë n’kumakakhala nawo.

“Apolisi anayesa kundikakamiza kuti ndizichita nawo zandale koma ndinakana. Anandimanga, n’kundipititsa m’chipinda chinachake, n’kundizungulira. Mmodzi wa apolisiwo anandiopseza mwa kundifunsa kuti: ‘Kodi ukudziwa kuti tingathe kukuonetsa zoopsa?’ Ndiyeno ndinamuyankha kuti: ‘Zimene mungandichite ndi zokhazo zimene Yehova wakulolani kuti muchite.’ Ndiye anati: ‘Iwe mutu wakowu sukuyenda bwino ayi. Tiye, tuluka!’”

Mzimu wokhulupirika woterewu ndi umene abale a ku Albania anasonyeza m’zaka zonsezo. Pofika chaka cha 1957 ofalitsa Ufumu anafika mpaka 75. Kumayambiriro kwa m’ma 1960, likulu la Mboni za Yehova linakonza zoti John Marks, yemwe anasamukira ku United States kuchokera ku Albania, apite ku Tiranë kukathandiza kulinganiza ntchito yachikristu. * Koma posakhalitsa Luçi Xheka, Mihal Sveci, Leonidha Pope, ndi abale ena a maudindo anatumizidwa ku ndende zozunzirako anthu.

Chiyembekezo Chakuti Vutolo Lidzatha

Chisanafike chaka cha 1967 ku Albania boma silinkasangalala ndi zopembedza. Kenaka linaletseratu chipembedzo china chilichonse. Sankalola Akatolika, a Orthodox, kapena Asilamu kuchititsa mwambo uliwonse. Matchalitchi ndi mizikiti zinatsekedwa ndipo ena anawasintha kukhala nyumba zochitiramo masewera olimbitsa thupi, zosungiramo zinthu zakale zochititsa chidwi, kapena zogulitsiramo zinthu. Sankalola munthu aliyense kukhala ndi Baibulo. Ankaletsa ngakhale kungonena chabe kuti umakhulupirira Mulungu.

Kulalikira ndiponso kusonkhana kunali kovuta kwambiri. Mboni pazokhapazokha zinkayesetsa kutumikira Yehova, ngakhale kuti zinkavutika kuchita ntchitoyi pazokha. Kuchokera m’zaka za m’ma 1960 mpaka m’ma 1980 Mboni za Yehova zinachepa kwambiri. Komabe zinali zolimba kwambiri mwauzimu.

Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1980, ku Albania ndale zinayamba kusintha pang’onopang’ono. Chakudya ndi zovala zinali zovuta kupeza. Anthu sanali osangalala. Kusintha kwa ndale kummawa kwa Ulaya kunafika ku Albania kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1990. Pambuyo pa zaka 45 za ulamuliro wankhanza, ku Albania kunabwera boma latsopano lomwe linavomerezanso ufulu wopembedza.

Motsogoleredwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, ofesi za nthambi za ku Austria ndi ku Greece zinayamba mwamsanga kupeza abale a ku Albania. Abale a ku Greece amene ankadziwa Chialubaniya anatenga mabuku ongomasuliridwa kumene ofotokoza za m’Baibulo n’kupita nawo ku Tiranë ndi ku Berat. Abale amene poyamba anabalalitsidwa aja anasangalala kwambiri kukumananso ndi Mboni zochokera kunja patatha zaka zambiri.

Apainiya Achangu Ochokera M’mayiko Ena Anatsogolera Ntchitoyo

Kumayambiriro kwa chaka cha 1992, Bungwe Lolamulira linakonza zoti Michael DiGregorio ndi mkazi wake Linda, omwe ndi amishonale ochokera ku Albania, asamuke n’kubwerera ku dziko lakwawoli. Kumeneko anakapezana ndi abale achikulire okhulupirika ndipo anathandiza abalewa kuti akhalenso mbali ya banja lauzimu la padziko lonse. Mu November kunafika gulu la anthu 16 akhama a ku Italy, omwe anali apainiya apadera, kapena kuti anthu olalikira uthenga wabwino nthawi zonse, ndipo kunafikanso apainiya anayi a ku Greece. Pofuna kuwathandiza kuphunzira chinenero cham’dzikoli anakhazikitsa kalasi yophunzitsa chinenero.

Moyo wa tsiku ndi tsiku unali wovuta kwa apainiya ochokera kunjawa. Magetsi ankazimazima. M’nyengo yachisanu kunkazizira kwambiri. Anthu ankakhala pa mizera kwa nthawi yaitali kuti apeze chakudya kapena zinthu zina zofunika pamoyo. Koma vuto lalikulu kwambiri kwa abalewa linali lopeza nyumba yaikulu bwino yoti anthu ambirimbiri ochita chidwi ndi uthenga wabwino azitha kukwanamo akasonkhana.

Apainiya amene ankalimbana ndi kuphunzira Chialubaniya anazindikira kuti kudziwa chinenero m’poyambira chabe. Mbale wina wodziwa kuphunzitsa Baibulo anawauza kuti: “Tingathe kuwasonyeza abale athu chikondi poseka nawo ndiponso powakumbatira ngakhale titapanda kufika podziwa bwinobwino chinenero chawo. Chikondi chanu chochokera pansi pamtima ndicho chingakhudze mtima anthu a kuno, osati kulankhula chinenero chawo mosalakwitsa. Motero, musadandaule ayi, anthuwa azikumvetsani ndithu.”

Kosi yoyamba ya chinenerochi itatha, apainiyawo anayamba kuchita ntchito yawo ku Berat, Durres, Gjirokastër, Shkodër, Tiranë, ndi ku Vlorë. Posakhalitsa, m’mizinda yonseyi munayambika mipingo. Apa n’kuti Areti Pina adakali ku Vlorë. Panthawiyo iye anali ndi zaka 80 ndiponso anali wofooka. Apainiya apadera awiri anatumizidwa kumeneko kuti azikalalikira pamodzi ndi Areti. Anthu anadabwa kwambiri kuona alendo akunja akulankhula Chialubaniya. Motero ankanena kuti: “Ifeyo tikafuna kuphunzira zinthu, amishonale a zipembedzo zina amatikakamiza kuphunzira Chingelezi kapena Chitaliyana. Anthu inu muyenera kuti mumatikondadi ndipo muli ndi uthenga wofunikadi. Ndithu inu kulolera kuphunzira Chialubaniya!” Areti anamaliza moyo wake wa padziko lapansi mokhulupirika mu January 1994, ndipo ankalalikirabe mpaka mwezi umene anamwalira. Khama limene iyeyu ndiponso apainiya ena aja anasonyeza linapindula. Mpingo unakhazikitsidwanso ku Vlorë mu 1995. Panopa, kumeneku kuli mipingo itatu yamphamvu, yomwe ikulalikira m’doko limeneli.

M’dziko lonselo, anthu anali ndi njala yauzimu ndipo analibe tsankho kwenikweni pankhani ya zipembedzo. Motero ankawerenga mofunitsitsa mabuku kapena zowerenga zina zilizonse zofotokoza za m’Baibulo zimene alandira kwa Mbonizo. Achinyamata ambiri anayamba kuphunzira ndi kupita patsogolo mwamsanga.

M’dziko lonselo, mipingo ndi magulu oposa 90 akupitiriza ‘kulimbikitsidwa m’chikhulupiriro, nachuluka m’chiwerengo chawo tsiku ndi tsiku.’ (Machitidwe 16:5) Mboni 3,513 zomwe zili ku Albania zidakali ndi ntchito yambiri yoti zichite. M’March 2005, pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu panafika anthu 10,144. Anthu a ku Albania amene amalandira bwino alendo akhala akucheza ndi Mboni za Yehova moti tsopano kumeneko kuli anthu 6,000 amene akuphunzira Baibulo. N’zoonekeratu kuti anthu ambiri apindula nalo Baibulo la New World Translation, limene langotulutsidwa kumene m’Chialubaniya. Ndithudi, mawu a Yehova akufalikira mu “Dziko la Chiwombankhanga” moti Yehova akutamandidwa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Nkhani ya mbiri ya moyo wa Thanas Duli ili mu Nsanja ya Olonda, ya Chingelezi ya December 1, 1968.

^ ndime 17 Nkhani ya mbiri ya moyo wa Nasho Dori ili mu Nsanja ya Olonda, ya January 1, 1996.

^ ndime 19 Nkhani ya mbiri ya moyo wa Helen, yemwe anali mkazi wa mbale John Marks, ili mu Nsanja ya Olonda, ya January 1, 2002.

[Bokosi patsamba 20]

KUDANA CHIFUKWA CHA MAFUKO KUTHA KU KOSOVO

M’zaka za m’ma 1990 dzina la Kosovo linkamveka kawirikawiri. Panthawiyi, anthu a kumeneko ankalimbirana malo ndiponso ankadana kwambiri chifukwa chosiyana mafuko moti m’derali munabuka nkhondo imene inachititsa kuti mayiko ena alowererepo.

Panthawi ya nkhondo ya m’mayiko a chigawo chotchedwa Balkan, anthu ambiri a Mboni anathawira m’mayiko oyandikana nawo. Nkhondoyo itazilala, ochepa mwa anthuwa anabwerera ku Kosovo, ali okonzeka kuchita ntchito yolalikira. Apainiya apadera a ku Albania ndi ku Italy anadzipereka kuti asamukire ku Kosovo kukathandiza anthu 2,350,000 a kumeneko. M’gawoli muli ofalitsa pafupifupi 130 omwe akutumikira Yehova m’mipingo inayi ndi magulu sikisi.

M’chaka cha 2003, anachita tsiku la msonkhano wapadera ku Priština, ndipo kunasonkhana anthu 252. Ena mwa anthuwa anali anthu a Chialubaniya, Chijeremani, Chijipisi, Chisebiya, Chitaliyana. Pamapeto a nkhani ya ubatizo, wokamba nkhaniyo anafunsa mafunso awiri. Anthu atatu anaimirira n’kuyankha mafunsowa ponena kuti inde, aliyense m’chinenero chake. Mmodzi anali Mwalubaniya, wina Mjipisi, ndi winayo Msebiya.

Panamveka phokoso lowomba m’manja anthu atatu okabatizidwawo atayankha nthawi imodzi komanso mokweza kuti: “Va!,” “Da!,” “Po!” Kenaka anakumbatirana. Iwowa anali atathetsa mumtima mwawo chidani chachikulu chimene chilipo pakati pa mafuko awo m’derali.

[Mapu patsamba 17]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Nyanja ya Mediterranean

ITALY

ALBANIA

GREECE

[Chithunzi patsamba 18]

Achinyamata a Mboni amatsanzira khama la Mboni zachikulire

[Chithunzi patsamba 18]

Areti Pina anatumikira Yehova mokhulupirika kuchokera mu 1928 mpaka mu 1994 pamene anamwalira

[Chithunzi patsamba 19]

Gulu loyamba la apainiya ochokera kunja likuphunzira chinenero

[Mawu a Chithunzi patsamba 16]

Eagle: © Brian K. Wheeler/​VIREO