Pindulani ndi Maphunziro Abwino Koposa
Pindulani ndi Maphunziro Abwino Koposa
BAIBULO limati Yehova Mulungu ndiye Mlengi wa zinthu zonse, kuphatikizaponso anthu. (Genesis 1:27; Chivumbulutso 4:11) Pakuti iyeyo ndi Mlangizi Wamkulu, anaphunzitsa mkazi ndi mwamuna woyamba, Adamu ndi Hava, n’kuwakonzekeretsa zokhala m’munda wokongola wa Edene. Cholinga chake chinali choti apitirize kuwaphunzitsa ndi kuwasamalira kwamuyaya. (Genesis 1:28, 29; 2:15-17; Yesaya 30:20, 21) Iwowatu anali ndi tsogolo labwino kwambiri.
Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthuwa anataya zonsezi. Kusakhulupirika kwawo kunalowetsa makhalidwe oipa ndiponso mavuto pa moyo wa anthu onse. (Genesis 3:17-19; Aroma 5:12) Pofotokoza makhalidwe a anthu amene anakhalako mibadwo yochepa chabe pambuyo pa kulengedwa kwa anthu oyambirirawa, Baibulo limanena mawu otsatirawa: “Anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha.”—Genesis 6:5.
Tsopano patha zaka pafupifupi 4,500 Yehova ataona kuti zolingalira za anthu zimangokhala zoipa nthawi zonse, ndipotu panopo moyo wa anthu wafika poipa kwambiri kuposa n’kale lonse. Anthu ambiri amanama popanda kuchita manyazi, amaba, kapenanso kuvulaza anzawo. Tsiku lililonse mavuto akumka nawonjezeka, ndipo kuganizirana kukumka kuchepa. Komansotu anthu ambiri sakugwirizana, ngakhale m’banja mmene. Koma Mulungu si amene akuchititsa mavuto amenewa, ndipo iye sanasiye kuganizira mavuto amene tikukumana nawo panopo. Yehova sanasiyepo kuganizira anthu, ndipo iye n’ngokonzeka kuphunzitsa onse amene amadalira kuti iyeyo ndiye angawatsogolere kuti akhale wosangalala pa moyo. Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, iye anatumiza Mwana wake, Yesu Kristu, kuti abwere padziko lapansi ndipo potero Yehovayo anasonyeza kuti n’ngofunitsitsa kuphunzitsa anthu omwe akufuna kuti moyo wawo ukhale wabwino. Yesu anapereka chitsanzo cha maphunziro ambambande chifukwa choti iye anaphunzitsidwa ndi Mlangizi Wamkulu kwa zaka zosawerengeka.
Chikristu Choona Chili Maphunziro
Yesu Kristu anayambitsa Chikristu choona, chomwe ndi moyo wozikidwa pa chikondi. Pa moyo umenewu, maganizo ndiponso zochita zonse za munthu zimayenera kugwirizana ndi chifuniro cha Mulungu n’cholinga choti dzina la Mulungu lilemekezeke. (Mateyu 22:37-39; Ahebri 10:7) Ziphunzitso zonse za Yesu zokhudza moyo umenewu zinali zochokera kwa Atate wake, Yehova. Pa Yohane 8:29 timawerenga motere za thandizo limene Yesu analandira kwa Yehova: ‘Wondituma Ine ali ndi Ine; sanandisiya Ine pandekha; chifukwa ndichita Ine zimene zim’kondweretsa Iye nthawi zonse.’ Inde, Yesu anathandizidwa ndiponso anatsogoleredwa ndi Atate wake pa utumiki wake wonse. Nawonso otsatira oyambirira a Yesu sanalimbane ndi mavuto a m’moyowa popanda kutsogoleredwa. Yehova anawaphunzitsa kudzera mwa Mwana wake. Iwowa anakhala anthu abwino potsatira ziphunzitso ndiponso chitsanzo cha Yesu. Zilinso chimodzimodzi ndi otsatira a Yesu masiku ano.—Onani bokosi lakuti “Mmene Yesu ndi Ziphunzitso Zake Amakhudzira Anthu,” patsamba 6.
Chinthu chapadera chokhudza Chikristu choona n’chakuti maphunziro ake amakhudza maganizo ndiponso mtima, motero anthu amasintha kuchokera mumtima. (Aefeso 4:23, 24) Tiyeni tionepo chitsanzo chimodzi chokha cha zimene Yesu anaphunzitsa anthu zokhudza kukhala okhulupirika m’banja. Iye anati: “Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo; koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang’ana mkazi kum’khumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:27, 28) Ponena mawu amenewa, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti mtima uyenera kukhala woyera ndiponso kuti ngakhale munthu atapanda kutsatira maganizo ndiponso zilakolako zake zoipa, zinthu zimenezi zingamuike m’mavuto aakulu. Kodi sizoona kuti maganizo oipa angathe kutichititsa zinthu zokhumudwitsa Mulungu ndiponso zopweteka anthu anzathu?
Motero, Baibulo limapereka malangizo awa: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Koma mwina mungafunse kuti: ‘Kodi n’zothekadi kuti maphunziro athe kukonzanso mtima wa munthu?’ Kukonzanso mtima kumatanthauza kuuchititsa kukonda zinthu zosiyana ndi zimene ukukonda panthawiyo poudzadza ndi mfundo ndiponso malangizo opezeka m’Mawu a Mulungu. Zimenezi zingatheke polola kuphunzira zimene Mulungu amaphunzitsa m’Mawu ake.
Analimbikitsidwa Kusintha
“Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita.” (Ahebri 4:12) Mpaka panopo Mawu a Mulungu akusintha kwambiri anthu, ndipo zimenezi zikutsimikizira kuti mawuwa safika potha ntchito. Angathe kumulimbikitsa munthu kuti asinthe moyo wake, avomereze Chikristu choona, ndi kuti akhale munthu wabwino. Zitsanzo zotsatirazi zikusonyeza mmene kuphunzira Baibulo kumathandizira.
Emilia, amene tam’tchula m’nkhani yoyamba ija, anati: “Pandekha ndinalephera kusintha zinthu pakhomo panga. Koma nditayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndinaona kuti sindiyenera kutaya mtima moti ndinayamba kusintha. Ndinaphunzira kuleza mtima ndiponso kusiya mtima wansontho. Patsogolo pake, nayenso mwamuna wanga anayamba kuphunzira Baibulo pamodzi nane. Iyeyu zinamuvuta kwambiri kusiya mowa, koma anayesetsa, mpaka anafika posiya. Zimenezi zinatithandiza kuti tikonze banja lathu. Tikunena pano tonse ndife Akristu osangalala ndipo tikuphunzitsa ana athu mfundo zabwino kwambiri za m’Baibulo.”—Deuteronomo 6:7.
Maphunziro amene Chikristu choona chimapereka angam’thandize munthu kusiya moyo wachabechabe komanso khalidwe loipa. Izi n’zimene zinam’chitikira Manuel. * Pamene anali ndi zaka 13, iyeyu anathawa kunyumba kwawo n’kuyamba kusuta chamba. Patsogolo pake anayamba kugwiritsira ntchito mankhwala oopsa osokoneza bongo. Ankachita zachiwerewere ndi amuna anzake komanso akazi kuti apeze malo ogona ndiponso ndalama. Nthawi zina Manuel ankapeza ndalama pofwamba anthu. Komanso nthawi zonse ankagwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ndipo chifukwa cha khalidwe lake lachiwawa, iyeyu anali kabwerebwere ku ndende. Nthawi ina anakhala m’ndende kwa zaka zinayi, ndipo kumeneko anayamba kuchita malonda ozembetsa zida. Atakwatira, Manuel anapitirizabe kulowa m’mavuto adzaoneni chifukwa cha zochita zake. Iye anati: “Tinafika pomakhala m’kanyumba kosungiramo nkhuku. Sindiiwala mpaka pano kuti mkazi wanga ankaphika pa moto wa mafuwa a njerwa. Moyo wathu unali wokayikitsa kwambiri moti azibale anga anafika polangiza mkazi wanga kuti andisiye.”
Kodi n’chiyani chinasintha moyo wa Manuel? Iye anayankha kuti: “Munthu wina amene timadziwana naye anabwera kunyumba kwathu n’kudzatiuza za Baibulo. Ndinavomera kuti azitiyendera pofuna kungomusonyeza kuti kulibe Mulungu amene amaganizira anthu. Ndinkadziona kuti ndine chitsanzo chotsimikizira mfundo imeneyo. Ndinadabwa kuti wa Mboniyo analeza mtima ndiponso anali waulemu, motero ndinavomera kukakhala nawo pamisonkhano yawo ku Nyumba ya Ufumu. Ngakhale kuti anthu ena kumeneko ankadziwa khalidwe langa, iwo anandilonjera mwansangala. Anandilandira bwino kwambiri moti sindinachite chilendo. Zimenezi zinandilimbikitsa kwambiri. Ndinakhudzidwa mtima kwambiri moti ndinaganiza zosiya mankhwala osokoneza bongo kuti ndipeze ntchito yolongosoka. Patatha miyezi inayi chiyambireni kuphunzira Baibulo, ndinayamba kuchita nawo ntchito yolalikira, ndipo patatha miyezi ina inayi, ndinabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova.”
Kodi Chikristu choona chathandiza bwanji Manuel ndi banja lake? Iye anati: “Ndikanapanda kuphunzira Baibulo bwenzi nditafa kalekale. Moyo umene Yesu anaphunzitsa ndi umene wandipulumutsira banja langa. Motero ana anga awiri sadzakumana ndi mikwingwirima yofanana ndi imene ndakumana nayo ine. Ndimanyadira ndiponso ndimathokoza kwambiri Yehova kuti tsopano ndimagwirizana kwambiri ndi mkazi wanga. Anzanga ena akale andiyamikirapo ndipo amandiuza kuti akuona kuti ndayamba moyo wabwino kwambiri.”
Pa moyo wachikristu, anthu amayenera kukhala a makhalidwe oyera komanso amayenera kukhala anthu audongo. John, amene akukhala 1 Petro 1:16, omwe amatilimbikitsa kuti tikhale oyera poti Yehova Mulungu n’ngoyera, amandigwira mtima. Motero, ngakhale kuti siife olemera, panopo timayesetsa kuti pakhomo pathu pazioneka bwino.”
m’dera lina losauka ku South Africa, anafika pozindikira zimenezi. Iye analongosola kuti: “Mwana wathu wamkazi nthawi zina sankasamba kwa mlungu wathunthu, ndipo ifeyo tinalibe nazo ntchito zimenezi.” Mkazi wake anavomerezanso kuti pakhomo pawo panali posasamalika ngakhale pang’ono. Koma iwowa atayamba kuphunzira Chikristu, zinthu zinasintha. John anachoka m’gulu la mbava zoba magalimoto n’kuyamba kusamalira kwambiri banja lake. Iye anati: “Tinaphunzira kuti poti ndife Akristu, tiyenera kukhala audongo posamba ndiponso kuchapa zovala zathu. Mawu a lemba laMungathe Kupeza Maphunziro Abwino Koposa
Nkhani zimene tazilongosolazi si zokhazi ayi, palinso zina. Chifukwa cha maphunziro ozikidwa m’Baibulo, anthu ochuluka zedi aphunzira kukhala moyo wabwino. Mabwana awo kuntchito amawakonda chifukwa chokhala oona mtima ndiponso akhama. Akhala anthu othandiza m’madera awo komanso kwa anzawo, chifukwa amaganizira zofuna za anthu anzawo. Iwo amayesetsa kupewa makhalidwe oipa ndiponso zizolowezi za umunthu, motero amasamalira bwino thanzi lawo ndiponso maganizo awo. Iwo sawonongera zinthu zawo zofunika pa makhalidwe oipa, koma amagwiritsira ntchito zinthuzo m’njira yowapindulitsa ndiponso yopindulitsa mabanja awo. (1 Akorinto 6:9-11; Akolose 3:18-23) Mosakayikira, kusintha kwa anthu chifukwa chotsatira zimene Yehova amanena m’Baibulo kumatsimikizira kuti moyo wabwino kwambiri ndiwo moyo wa Chikristu choona, ndipo amenewa ndiwo maphunziro abwino kuposa ena aliwonse. Ponena za munthu amene amatsatira malamulo a Mulungu, Baibulo limati: “Zonse azichita apindula nazo.”—Salmo 1:3.
N’zolimbikitsa kudziwa kuti Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova, amafuna kutiphunzitsa. Iye amanena kuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.” (Yesaya 48:17) Inde, Yehova anasonyeza njira imeneyi kudzera mwa chitsanzo ndiponso ziphunzitso za Mwana wake, Yesu Kristu. Ziphunzitso zake zinapindulitsa kwambiri anthu ochuluka amene anamudziwa pamene iye anali padziko lapansi, ndipo zilinso chimodzimodzi ndi anthu ena ambiri amene amatsatira ziphunzitsozi masiku ano. Bwanji osapeza nthawi kuti muphunzire zinthu zinanso zokhudza ziphunzitso zimenezi? Mboni za Yehova za kumene mukukhalako zingasangalale kukuthandizani kupeza maphunziro ofunikawa.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 12 Mayina ena tawasintha.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]
Mmene Yesu ndi Ziphunzitso Zake Amakhudzira Anthu
Pa udindo wake monga mkulu wa amisonkho, Zakeyu anapezerapo mwayi wolemera mwa kulanda anthu ndalama ndiponso kubera anthu wamba. Koma iyeyu anasintha moyo wake potsatira ziphunzitso za Yesu.—Luka 19:1-10.
Saulo wa ku Tariso anasiya kuzunza Akristu ndipo anayamba Chikristu, n’kukhala mtumwi Paulo.—Machitidwe 22:6-21; Afilipi 3:4-9.
Akristu ena ku Korinto anali ‘adama, opembedza mafano, achigololo, akudziipsa ndi amuna, ambala, osirira, oledzera, olalatira, ndi olanda.’ Koma, ataphunzira Chikristu choona, iwo ‘anasambitsidwa, kuyeretsedwa, n’kuyesedwa olungama, m’dzina la Ambuye wawo Yesu Kristu.’—1 Akorinto 6:9-11.
[Chithunzi patsamba 7]
Baibulo lingakusonyezeni mmene mungakhalire ndi moyo wabwino