Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Samalani Kuti Musakhale ndi Mtima Wodzikuza

Samalani Kuti Musakhale ndi Mtima Wodzikuza

Samalani Kuti Musakhale ndi Mtima Wodzikuza

“Mulungu akaniza odzikuza.”​—YAKOBO 4:6.

1. Perekani zitsanzo za zinthu zabwino zimene anthu amanyadira.

KODI munayamba mwanyadirapo kwambiri mumtima mwanu chifukwa cha zochitika zinazake? Munthu amamva bwino kwambiri panthawi yotereyi ndipo ambirife zimenezi zatichitikirapo. Kunyadira zinthu zinazake si kulakwa. Mwachitsanzo, makolo achikristu akalandira lipoti la kusukulu lonena kuti mwana wawo ali ndi khalidwe labwino ndiponso amalimbikira sukulu, amanyadira kwambiri ndi zochita za mwana wawoyo. Mtumwi Paulo ndi anzake ananyadira mpingo watsopano umene iwowo anathandiza kukhazikitsa, popeza kuti abale a kumeneko anakhalabe okhulupirika ngakhale pozunzidwa.​—1 Atesalonika 1:1, 6; 2:19, 20; 2 Atesalonika 1:1, 4.

2. N’chifukwa chiyani kunyada kuli koipa?

2 Pa zitsanzo tatchulazi, tingathe kuona kuti kunyadira kumasonyeza kusangalala chifukwa cha zochita kapena zinthu zinazake zimene tili nazo. Komano kunyada nthawi zambiri kumasonyeza kudzimva kuti ndiwe woposa ena chifukwa cha luso lako, maonekedwe ako, ndalama zako, kapena udindo wako. Nthawi zambiri munthu wonyada amaonekera pa kudzitukumula kwake. Ndithu, kunyada ndi khalidwe limene ifeyo Akristu tiyenera kulipewa kwambiri. Chifukwa chiyani? Chifukwa choti mwachibadwa, anthufe tili ndi mtima wodzikonda umene tinatengera kwa Adamu, kholo lathu lakale. (Genesis 8:21) Motero, mitima yathu ingatinyenge mosavuta n’kutichititsa kuti tizinyada. Mwachitsanzo, Akristu ayenera kupewa kunyadira fuko lawo, chuma chawo, maphunziro awo, luso lawo lachibadwa, kapena kunyadira zoti amaposa ena pa kagwiridwe ka ntchito. Ngati munthu akunyadira zimenezi, Yehova sasangalala naye.​—Yeremiya 9:23; Machitidwe 10:34, 35; 1 Akorinto 4:7; Agalatiya 5:26; 6:3, 4.

3. Kodi kudzikuza n’kutani ndipo kodi Yesu ananenapo chiyani za kudzikuza?

3 Palinso chifukwa china chopewera kunyada. Tikalola kuti mtima umenewu ukule, mapeto ake ungafike poipa zedi n’kukhala mtima wodzikuza. Kodi kudzikuza n’kutani? Munthu wodzikuza amadziona kuti n’ngoposa ena, ndipo anthu amene amawaona ngati a pansi pake sawawerengera n’komwe. (Luka 18:9; Yohane 7:47-49) Yesu anatchula “kudzikuza” pa gulu la makhalidwe ena oipa amene ‘amatuluka mumtima’ ndipo ‘amadetsa’ munthu. (Marko 7:20-23) Choncho, Akristu amaona kuti m’pofunika kwambiri kupewa mtima wodzikuza.

4. Kodi kuona zitsanzo za m’Baibulo za anthu odzikuza kungakuthandizeni motani?

4 M’Baibulo muli nkhani zina za anthu odzikuza zimene zingakuthandizeni kupewa khalidweli. Nkhanizi zingakuthandizeni kudziwa mosavuta maganizo aliwonse osonyeza kunyada amene muli nawo panopo kapena amene angakubwerereni m’tsogolo. Zimenezi zingakuthandizeni kupewa maganizo aliwonse amene angakuyambitseni mtima wodzikuza. Choncho simungadzawonongedwe nawo Mulungu akamadzakwaniritsa mawu ake akuti: “Ndidzachotsa pakati pako amene akondwera ndi kudzikuza kwako, ndipo sudzachita kudzikuzanso m’phiri langa lopatulika.”​—Zefaniya 3:11.

Mulungu Amathana ndi Anthu Odzikuza

5, 6. Kodi Farao anasonyeza bwanji kudzikuza ndipo zinamuthera bwanji?

5 Mungathenso kuona mmene Yehova amaonera anthu odzikuza poganizira mmene iye anathanirana ndi olamulira amphamvu monga Farao, wolamulira wa Aigupto. N’zosachita kufunsa kuti Farao anali ndi mtima wodzikuza. Farao ankadziona ngati mulungu woti anthu azimulambira motero ankanyoza akapolo ake, Aisrayeli. Taganizirani yankho lake atapemphedwa kuti alole Aisrayeli kupita kuchipululu ‘kukachita madyerero’ popembedza Yehova. Farao anayankha modzikuza, amvekere: “Yehova ndani, kuti ndimvere mawu ake ndi kulola Israyeli apite?”​—Eksodo 5:1, 2.

6 Farao atakhaulitsidwa ndi miliri sikisi, Yehova anauza Mose kuti akamufunse funso lakuti: “Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke?” (Eksodo 9:17) Ndiyeno apa Mose ananena kuti kubwera mliri wa nambala seveni, womwe unali chimvula cha matalala chomwe chinawononga kwambiri dzikolo. Pambuyo pa mliri wachikhumi, Aisrayeli atangololedwa kuti azipita, Farao anasintha maganizo n’kuyamba kuwathamangira. Mapeto ake, Farao ndi gulu lake lankhondo anapezeka m’Nyanja Yofiira, akusowa kothawira chifukwa choti madzi anawazungulira. Tangoganizirani zimene zinkayenda m’maganizo mwawo pamene amaona madziwo akubwera poteropo mwamkokomo. Kodi kudzikuza kwa Farao kunamubweretsera zotani? Asilikali ake, omwe anali odziwa kwambiri nkhondo, ananena kuti: “Tithawe pamaso pa Israyeli; pakuti Yehova alikuwagwirira nkhondo pa Aaigupto.”​—Eksodo 14:25.

7. Kodi olamulira a Babulo anasonyeza motani mtima wodzikuza?

7 Pali olamulira enanso odzikuza amene Yehova anawathetsa makani. Mmodzi wa iwo anali Sanakeribu, mfumu ya Asuri. (Yesaya 36:1-4, 20; 37:36-38) Patapita nthawi, dziko la Asuri linalandidwa ndi Ababulo, koma patsogolo pake Yehova anathetsanso makani mafumu awiri odzikuza a Babulo. Kumbukirani phwando limene Mfumu Belisazara anachita. Paphwando limenelo iyeyo ndi alendo ake olemekezeka anatenga ziwiya za m’kachisi wa Yehova n’kumamweramo vinyo, n’kumatamanda milungu ya ku Babulo. Mwadzidzidzi, anangoona zala za munthu zikulemba uthenga winawake pakhoma. Ndiyeno atafunsa mneneri Danieli kuti alongosole tanthauzo la zilembo zosadziwikazo, Danieli anakumbutsa Belisazara kuti: “Mulungu Wam’mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu . . . Koma pokwezeka mtima wake . . . kuchita modzikuza, anam’tsitsa pa mpando wa ufumu wake, nam’chotsera ulemerero wake; . . . ndipo inu mwana wake, Belisazara inu, simunadzichepetsa m’mtima mwanu, chinkana munazidziwa izi zonse.” (Danieli 5:3, 18, 20, 22) Usiku womwewo, ankhondo a Amedi ndi Aperisi anagonjetsa Babulo, ndipo Belisazara anaphedwa.​—Danieli 5:30, 31.

8. Kodi Yehova anatani nawo anthu osiyanasiyana odzikuza?

8 Ganiziraninso za anthu ena odzikuza amene ananyoza anthu a Yehova. Pali anthu monga Goliati, yemwe anali chimphona cha Afilisti; Hamani, yemwe anali Nduna Yaikulu ya ku Perisiya; ndi Mfumu Herode Agripa, yemwe anali wolamulira wa chigawo cha Yudeya. Chifukwa cha kudzikuza kwawo, anthu atatuwa anafa imfa zamanyazi kwambiri polangidwa ndi Mulungu. (1 Samueli 17:42-51; Estere 3:5, 6; 7:10; Machitidwe 12:1-3, 21-23) Zimene Yehova anachita ndi anthu odzikuzawa zimagogomezera mfundo yakuti: “Kunyada kutsogolera kuwonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.” (Miyambo 16:18) Ndithu, “Mulungu akaniza odzikuza.”​—Yakobo 4:6.

9. Kodi mafumu a ku Turo anasintha n’kuchita zinthu zachinyengo zotani?

9 Mosiyana ndi olamulira odzikuza a ku Aigupto, Asuri, ndi Babulo, mfumu ya ku Turo panthawi ina inathandizapo anthu a Mulungu. Panthawi yaulamuliro wa Mfumu Davide komanso Mfumu Solomo, mfumu ya ku Turoyi inapereka anthu aluso ndiponso inapereka zinthu zofunika pa ntchito yomanga nyumba zachifumu ndiponso kachisi wa Mulungu. (2 Samueli 5:11; 2 Mbiri 2:11-16) N’zomvetsa chisoni kuti pambuyo pake, Aturo anaukira anthu a Yehova. Kodi n’chifukwa chiyani anatero?​—Salmo 83:3-7; Yoweli 3:4-6; Amosi 1:9, 10.

“Unadzikuza Mtima”

10, 11. (a) Kodi ndani amene tingamuyerekezere ndi mafumu a Turo? (b) N’chiyani chinachititsa kuti Aturo asinthe n’kuyamba kupondereza Aisrayeli?

10 Yehova anauzira mneneri wake Ezekieli kuti abweretse poyera zochita za mafumu onse amene analamulira Turo ndi kuti awadzudzule. Uthenga umenewo, womwe unali wopita kwa “mfumu ya Turo,” uli ndi mawu ofotokoza mafumu onse amene analamulira Turo komanso ofotokoza wachinyengo woyamba, Satana, amene “sanaima m’choonadi.” (Ezekieli 28:12; Yohane 8:44) Poyamba Satana anali munthu wauzimu wokhulupirika mu gulu la Yehova la ana ake a kumwamba. Kudzera mwa Ezekieli, Yehova Mulungu anasonyeza chifukwa chachikulu chimene chinachititsa kuti mafumu a Turo ndiponso Satana apanduke.

11 “Unali m’Edene, munda wa Mulungu, mwala uli wonse wa mtengo wake unali chofunda chako . . . Unali kerubi wodzozedwa wakuphimba . . . Unali wangwiro m’njira zako chilengedwere iwe, mpaka chinapezeka mwa iwe chosalungama. Mwa kuchuluka kwa malonda ako anakudzaza mkati mwako ndi chiwawa, ndipo unachimwa; chifukwa chake . . . ndinakuwononga, kerubi wakuphimba iwe . . . Unadzikuza mtima chifukwa cha kukongola kwako, waipsa nzeru zako; chifukwa cha kuwala kwako.” (Ezekieli 28:13-17) Inde, kudzikuza n’kumene kunapangitsa kuti mafumu a Turo achitire zachiwawa anthu a Yehova. Ufumu wa Turo unali likulu la zamalonda ndipo unalemera kwambiri komanso unatchuka chifukwa cha zinthu zokongola zimene unkagulitsa. (Yesaya 23:8, 9) Mafumu a Turo anayamba kudzikuza n’kumapondereza anthu a Mulungu.

12. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Satana ayambe zachinyengo, ndipo kodi iyeyu akupitirizabe kuchita zotani?

12 N’chimodzimodzinso ndi mngelo amene anasanduka Satana. Iyeyu poyamba anali ndi nzeru zochitira ntchito iliyonse imene Mulungu ankamupatsa. Koma m’malo mothokoza, iyeyu anayamba ‘kudzitukumula’ n’kumanyoza malamuliridwe a Mulungu. (1 Timoteo 3:6) Anadziona kuti ndi wapamwamba kwambiri moti anayamba kufuna kuti Adamu ndi Hava azilambira iyeyo. Chikhumbo choipa chimenechi chinam’kulira ndipo chinabala uchimo. (Yakobo 1:14, 15) Satana ananyenga Hava kuti adye chipatso cha mtengo wokhawo umene Mulungu anamuletsa. Kenaka, Satana anagwiritsira ntchito Havayo kum’chititsa Adamu kudya chipatso choletsedwacho. (Genesis 3:1-6) Motero anthu awiri oyambawa anakana ufulu umene Mulungu ali nawo wowalamulira, ndipo potero iwowa kwenikweni anakhala olambira a Satana. Satana ndi wodzikuza mapeto. Iyeyu anayesapo kunyenga angelo onse kumwamba ndiponso anthu onse padziko lapansi, ngakhalenso Yesu Kristu, pofuna kuti iwowa azilambira iyeyo pokana kulamuliridwa ndi Yehova.​—Mateyu 4:8-10; Chivumbulutso 12:3, 4, 9.

13. Kodi kudzikuza kwabala zipatso zotani?

13 Motero mungathe kuona kuti kudzikuza kunayamba ndi Satana, ndipo kudzikuza n’kumene makamaka kunayambitsa uchimo, kuvutika, ndi makhalidwe oipa amene alipo masiku anowa. Pakuti Satana ndiye “mulungu wa nthawi ino ya pansi pano” iye akupitirizabe kulimbikitsa anthu kukhala onyada ndiponso odzikuza. (2 Akorinto 4:4) Satana akudziwa kuti nthawi yatsala pang’ono kum’thera, motero amalimbana ndi Akristu oona. Cholinga chake n’chakuti awachititse kuti am’tembenukire Mulungu, n’kuyamba kudzikonda, kudzitamandira, ndi kudzikuza. Baibulo linaneneratu kuti makhalidwe oterewa adzafala mu “masiku otsiriza” ano.​—2 Timoteo 3:1, 2; Chivumbulutso 12:12, 17.

14. Kodi Yehova amayendera lamulo lotani pochita zinthu ndi anthu?

14 Yesu Kristu molimba mtima anavumbula poyera zipatso zowola zimene kudzikuza kwa Satana kwabala. Panthawi zosachepera zitatu, ali pamaso pa adani ake odziona ngati anthu olungama, Yesu anatchula lamulo limene Yehova amayendera pochita zinthu ndi anthu. Iye anati: “Munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.”​—Luka 14:11; 18:14; Mateyu 23:12.

Tetezani Mtima Wanu Kuti Usakhale Wodzikuza

15, 16. Kodi n’chiyani chinachititsa Hagara kukhala ndi mtima wodzikuza?

15 Mwina mwaona kuti zitsanzo za kudzikuza zimene tatchulazi ndi zitsanzo zokhudza anthu amene anali apamwamba. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti anthu wamba sangakhale ndi vuto lodzikuza? Ayi sizikusonyeza choncho. Taganizirani zimene zinachitika pabanja la Abrahamu. Iyeyu analibe mwana aliyense wodzalowa m’malo mwake, ndipo mkazi wake Sara, anali atadutsa msinkhu wobereka. Pachikhalidwe chawo, mwamuna amene wapezeka m’vuto langati la Abrahamu ankakwatira mkazi wachiwiri n’kubereka ana. Mulungu ankalola maukwati otere chifukwa choti nthawi inali isanakwane yoti akhazikitsenso lamulo lake loyamba la mmene ukwati uyenera kukhalira pakati pa olambira ake oona.​—Mateyu 19:3-9.

16 Chifukwa cholimbikitsidwa ndi mkazi wake, Abrahamu anavomera kukwatira mdzakazi wa Sara wa ku Aigupto, dzina lake Hagara. Hagara anakhala mkazi wachiwiri wa Abrahamu ndipo anatenga pakati. Hagara akanakhala wina, bwenzi atayamikira kwambiri kuti anapatsidwa ulemu waukulu woterewu. Koma m’malo moyamikira, iye anayamba kukhala ndi mtima wodzikuza. Baibulo limati: “Pamene anaona kuti anatenga pakati, anapeputsa wakuka wake [kapena kuti mbuye wake wamkazi] m’maso mwake.” Mtima umenewu unabweretsa mavuto aakulu pabanja la Abrahamu moti mpaka Sara anathamangitsa Hagara pakhomopo. Koma njira yothetsera vutoli inalipo. Mngelo wa Mulungu analangiza Hagara kuti: “Bwera kwa wakuka wako, udzichepetse wekha pamanja pake.” (Genesis 16:4, 9) Zikuoneka kuti Hagara anamvera zimenezi, anasintha khalidwe lake n’kuyamba kum’lemekeza Sara, motero Hagara anadzakhala kholo la anthu amene anachulukana kwambiri.

17, 18. N’chifukwa chiyani tonsefe tiyenera kusamala ndi mtima wodzikuza?

17 Nkhani ya Hagara imasonyeza kuti zinthu zikayamba kumuyendera bwino munthu, amatha kuyamba kudzikuza. Motero tikuphunzirapo kuti ngakhale Mkristu amene wakhala akutumikira Mulungu modzichepetsa angathe kuyamba mtima wodzikuza akapeza chuma kapena udindo. Mtima umenewu ungayambenso ngati anzake akumutama chifukwa chotha kuyendetsa bwino zinthu, chifukwa cha nzeru zake, kapena luso lake. Inde, Mkristu ayenera kusamala kuti asakhale wodzikuza mumtima mwake. Zimenezi n’zofunikira makamaka ngati zinthu zamuyendera bwino kapena ngati walandira maudindo ena.

18 Chifukwa chachikulu kwambiri chopewera kudzikuza n’chakuti Mulungu sasangalala nako. Mawu ake amati: “Maso akunyada, ndi mtima wodzikuza, ndi nyali ya oipa, zili tchimo.” (Miyambo 21:4) N’zochititsa chidwi kuti Baibulo limachita kutchula Akristu “achuma m’nthawi ino ya pansi pano” n’kuwachenjeza kuti “asadzikuze.” (1 Timoteo 6:17; Deuteronomo 8:11-17) Akristu amene sali olemera ayenera kupewa “diso loipa,” kapena kuti losirira ndipo ayenera kukumbukira kuti munthu aliyense, kaya ndi wolemera kapena wosauka, angathe kuyamba mtima wodzikuza.​—Marko 7:21-23; Yakobo 4:5.

19. Kodi Uziya anadziwonongera bwanji mbiri yake yabwino?

19 Mtima wodzikuza ndiponso makhalidwe ena otere angathe kutiwonongera ubwenzi wathu ndi Yehova. Mwachitsanzo, taganizirani mbali yoyamba ya ulamuliro wa Mfumu Uziya. Iyeyu anachita “zoongoka pamaso pa Yehova . . . Ndipo iye anali munthu wakufuna Mulungu . . . ; ndipo masiku akufunira Yehova iye, Mulungu anam’lemereza.” (2 Mbiri 26:4, 5) Komabe n’zomvetsa chisoni kuti Mfumu Uziya anadziwonongera mbiri yake yabwino, popeza kuti “mtima wake unakwezeka momuwononga.” Uziya anayamba kudzitama kwambiri mumtima mwake moti mpaka analowa m’kachisi kuti apereke nsembe. Ansembe anamuchenjeza kuti asachite zinthu modzikuza choncho, koma “Uziya anapsa mtima.” Motero Yehova anam’chititsa khate, ndipo anafa Mulungu atasiya kumuyanja.​—2 Mbiri 26:16-21.

20. (a) Kodi mbiri yabwino ya Mfumu Hezekiya ikanawonongeka motani? (b) Kodi nkhani yotsatirayi ilongosola chiyani?

20 Mungathe kusiyanitsa zimenezi ndi chitsanzo cha Mfumu Hezekiya. Panthawi ina, mbiri yabwino ya mfumu imeneyi ikanawonongeka chifukwa choti “mtima wake unakwezeka.” Koma n’zosangalatsa kuti “Hezekiya anadzichepetsa m’kudzikuza kwa mtima wake” ndipo Mulungu anayambanso kumuyanja. (2 Mbiri 32:25, 26) Apatu mungathe kuona kuti kudzichepetsa n’kumene kunam’thandiza Hezekiya kuti asiye kudzikuza mtima. Inde, kudzichepetsa ndi khalidwe losiyana kwambiri ndi kudzikuza. Motero, m’nkhani yotsatirayi tilongosola mmene tingayambire kukhala odzichepetsa mwachikristu ndi kupitiriza kusonyeza khalidweli.

21. Kodi Akristu odzichepetsa angayembekezere chiyani?

21 Komabe, tisaiwale zipatso zonse zoipa zimene kudzikuza kwabala. Popeza kuti “Mulungu akaniza odzikuza,” tiyeni titsimikize mtima kukankhira kutali maganizo aliwonse osonyeza kunyada. Tikamayesetsa kukhala Akristu odzichepetsa, tingakhale ndi chiyembekezo chodzapulumuka pa tsiku lalikulu la Mulungu, pamene anthu odzikuza ndiponso zipatso zawo zidzachotsedwe padziko lapansi. Panthawi imeneyi, “kudzikweza kwa munthu kudzaweramitsidwa pansi, kudzikuza kwa munthu kudzatsitsidwa; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.”​—Yesaya 2:17.

Mfundo Zofunika Kuzisinkhasinkha

• Kodi munthu wodzikuza amakhala wotani?

• Kodi kudzikuza kunayamba bwanji?

• N’chiyani chingachititse munthu kuyamba kudzikuza?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala ndi mtima wodzikuza?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Farao, yemwe anali wodzikuza, anathetsedwa makani

[Chithunzi patsamba 24]

Hagara anayamba kudzikuza chifukwa choti zinthu zinayamba kumuyendera bwino

[Chithunzi patsamba 25]

Hezekiya anadzichepetsa ndipo Mulungu anayambanso kumuyanja