Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Sadzakusiyani Konse

Yehova Sadzakusiyani Konse

Yehova Sadzakusiyani Konse

AKRISTU a ku Yudeya anali kuzunzidwa mwadzaoneni komanso anayenera kuyesetsa kuti asatengere maganizo okonda chuma a anthu a kumeneko. Powalimbikitsa, mtumwi Paulo anawauza mawu amene Yehova anauza Aisrayeli pamene anali kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, akuti: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” (Ahebri 13:5; Deuteronomo 31:6) Mosakayikira, lonjezo limeneli linalimbikitsa Akristu a ku Yudeya omwe analandira kalatayo.

Lonjezo lomweli liyeneranso kutilimbikitsa ifeyo pa nkhawa zimene timakhala nazo ‘m’masiku otsiriza owawitsa’ ano. (2 Timoteo 3:1) Tikamadalira Yehova mumtima mwathu ndi m’zochita zathu zomwe, iye amatithandiza ngakhale titakumana ndi masautso aakulu bwanji. Kuti tione mmene Yehova angathe kukwaniritsira lonjezoli, tiyeni tione chitsanzo cha mmene angatithandizire ngati mwadzidzidzi titapezeka kuti ntchito imene timathandizika nayo pa moyo wathu yatha.

Zinthu Zikasintha Mwadzidzidzi

Anthu amene akusowa ntchito akumka nachuluka padziko lonse. Malingana ndi magazini ina ya ku Poland, kusowa ntchito akuti ndi “limodzi mwa mavuto aakulu kwambiri pa moyo wa anthu ndiponso pa zachuma.” Ngakhale mayiko olemera akukhudzidwa ndi vutoli. Mwachitsanzo, ngakhale m’mayiko amene ali m’bungwe la Organization for Economic Cooperation and Development, anthu amene anali kusowa ntchito pofika chaka cha 2004 “anawonjezeka n’kufika 32 miliyoni, kuposeratu chiwerengero cha anthu amene ankasowa ntchito pa nyengo ya mavuto aakulu a zachuma m’ma 1930.” Ku Poland, bungwe loona za ziwerengero la Central Statistical Office, linati mu December 2003, m’dzikoli munali anthu 3 miliyoni osowa ntchito omwe “anali anthu 18 pa anthu 100 aliwonse a msinkhu wogwira ntchito.” Akutinso m’chaka cha 2002, pafupifupi theka la anthu akuda ku South Africa, anali kusowa ntchito.

Anthu ambiri, kuphatikizapo atumiki a Yehova, amaona kuti angathe kukhala paulova kapenanso kuchotsedwa ntchito mwadzidzidzi. Aliyense amakumana ndi zinthu zogwa mwadzidzidzi. (Mlaliki 9:11) Tonsefe tingathe kupezeka m’mavuto otichititsa kunena mawu a wamasalmo Davide yemwe anati: “Masautso a mtima wanga akula.” (Salmo 25:17) Kodi inuyo mungathane nawo bwinobwino mavuto oterewa ngati atakugwerani? Mavuto otere angathe kusokoneza maganizo anu, moyo wanu wauzimu, ndiponso kukulowetsani mu vuto la zachuma. Ngati tsopano simuli pantchito, kodi mungathe kubwerera mwakale?

Kulimbana ndi Nkhawa

Katswiri wa zamaganizo Janusz Wietrzyński analongosola kuti “ntchito ikatha, amuna ndiwo amavutika mtima kwambiri kuposa akazi,” chifukwa amuna ndiwo nthawi zonse amaonedwa kuti ali ndi udindo wosamalira banja. Katswiriyu ananena kuti kutha kwa ntchito kungachititse mwamuna “kuthedwa nzeru kwabasi,” moti angakhale wokwiya kwambiri kapena angathe kutayiratu mtima. Bambo wochotsedwa ntchito angadzione ngati wolephera ndipo izi zingam’chititse kuyamba “kukangana kawirikawiri ndi anthu a m’banja mwake.”

Adam, yemwe ndi bambo wachikristu wa ana awiri, ananena mawu otsatirawa polongosola mmene anamvera ntchito itam’thera: “Ndinkapsa mtima mwamsanga; ndipo ndinkaipidwa ndi chilichonse. Ngakhale usiku ndinkangolota za ntchito ndi za mmene ndingasamalilire ana komanso mkazi wanga, yemwenso ntchito yake inam’thera mwadzidzidzi.” Ryszard ndi mkazi wake Mariola ali ndi mwana mmodzi. Mmene ntchito yawo inkasokonezeka, n’kuti ali ndi ngongole yaikulu ku banki. Mkaziyo anati: “Nthawi zonse chikumbumtima chinkandipweteka poganizira kuti tinalakwa kutenga ngongoleyo. Ndinkangoona kuti mavuto onsewo anabwera chifukwa cha ine.” Tikakumana ndi mavuto oterewa, tingathe kukhala okwiya, ankhawa, kapena okhumudwa, ndipo maganizo angatichulukire kwambiri. Motero, kodi tingathane nawo bwanji maganizowa?

Baibulo limatipatsa malangizo otithandiza kusataya mtima. Mtumwi Paulo anati: “Musadere nkhawa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Kupemphera kwa Yehova kumatipatsa “mtendere wa Mulungu.” Mtendere umenewu ndi kukhazikika pansi kwa maganizo chifukwa chokhulupirira Mulungu. Mkazi wa Adam, Irena, anati: “Tikamapemphera, tinkamuuza Yehova za vuto lathu ndipo tinkamuuzanso kuti tiyesetsa kuti moyo wathu usakhale wolira zambiri. Mwamuna wanga, yemwe m’mbuyomo ankakonda kuda nkhawa ndi zinthu, anayamba kuona kuti n’zotheka kuthana ndi vutoli.”

Ngati ntchito yanu ingakuthereni mwadzidzidzi, dziwani kuti umenewo ndi mwayi wanu wogwiritsira ntchito mawu olimbikitsa amene Yesu Kristu ananena pa ulaliki wa pa phiri, akuti: “Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. . . . Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:25, 33) Ryszard ndi Mariola anatsatira malangizo amenewa pothana ndi maganizo awo. Mariola anati: “Mwamuna wanga ankandilimbikitsa nthawi zonse ndipo ankakonda kunena kuti Yehova sangatisiye ayi.” Mwamuna wakeyo anatinso: “Popemphera limodzi mosalekeza, tayandikira kwambiri kwa Mulungu, ndiponso ifeyo patokha tayamba kukondana kwabasi, ndipo zimenezi zatilimbikitsa zedi.”

Mzimu woyera wa Mulungu ungatithandizenso kuthana ndi maganizo osautsa. Khalidwe la kudziletsa, limene mzimuwu ungatipangitse kukhala nalo, lingatithandize kukhazika mtima m’malo. (Agalatiya 5:22, 23) Zingakhale zovuta, koma n’zotheka chifukwa Yesu analonjeza kuti “Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akum’pempha Iye.”​—Luka 11:13; 1 Yohane 5:14, 15.

Musanyalanyaze Zosowa Zanu Zauzimu

Munthu akachotsedwa ntchito mwadzidzidzi, ngakhale atakhala Mkristu wochita zinthu mosamala zedi, poyamba amakhala ndi nkhawa kwambiri, koma sibwino kunyalanyaza zosowa zathu zauzimu. Taganizirani za Mose, yemwe ali ndi zaka 40 moyo wake unasintha kwambiri atachotsedwa pa udindo wapamwamba n’kuyamba ntchito ya ubusa, yomwe inali ntchito yonyozeka kwa Aigupto. (Genesis 46:34) Mose anayenera kusintha mogwirizana ndi mmene zinthu zinasinthira pa moyo wake. Kwa zaka 40 zotsatira, iye analola kuti Yehova amuumbe n’kumukonzekeretsa kuchita ntchito zimene zinali kubwera m’tsogolo. (Eksodo 2:11-22; Machitidwe 7:29, 30; Ahebri 11:24-26) Ngakhale kuti anakumana ndi zovuta, Mose anaika maganizo ake onse pa zinthu zauzimu, ndipo anali wofunitsitsa kuphunzitsidwa ndi Yehova. Ifenso tisalole ngakhale pang’ono kuti mavuto atiiwalitse zinthu zauzimu.

Ntchito yathu ikatha mwadzidzidzi tingasokonezeke maganizo kwambiri, komabe imeneyi ndi nthawi yabwino yolimbikitsa ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu ndiponso ndi anthu ake. Adam, amene tam’tchulapo kale m’nkhani ino, anaona zinthu m’njira imeneyi. Iye anati: “Ineyo ndi mkazi wanga ntchito zathu zitatithera, sitinaganizeko n’komwe zosiya kupita ku misonkhano yachikristu kapena kuchepetsako ntchito yolengeza uthenga wabwino. Zimenezi zinatithandiza kuti tisamade nkhawa kwambiri tikamaganizira za mawa.” Ryszard naye ali ndi maganizo ofanana ndi amenewa, ndipo anati: “Pakanapanda misonkhano ndiponso utumiki, zinthu zikanativuta kwambiri; tikanadwala ndi maganizo. Tikamacheza nkhani zauzimu ndi ena timalimbikitsidwa, chifukwa timasiya kuganizira kwambiri zofuna zathu zokha n’kuyamba kuganizira zofuna za iwowo.”​—Afilipi 2:4.

Inde, m’malo momangokhalira kudandaula kuti simuli pantchito, yesetsani kuti panthawi imene simukugwira ntchitoyo muzichita zinthu zauzimu, kuphunzira Baibulo panokha, kuchita nawo zinthu mumpingo, kapena kuwonjezera zinthu zina pa utumiki wanu. M’malo momangokhala poti ndinu lova mungathe kukhala “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye,” ndipo zimenezi zingabweretse chimwemwe kwa inuyo ngakhalenso kwa anthu onse oona mtima amene angamvere uthenga wa Ufumu umene mukulalikira.​—1 Akorinto 15:58.

Kusamalira Banja Lanu

Zinthu zauzimu zili apo, dziwani kuti munthu wanjala sangakhute zinthu zauzimu. Tisaiwale mfundo yotsatirayi: “Ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.” (1 Timoteo 5:8) Adam anati: “Ngakhale kuti abale mumpingo amasangalala kutipatsako thandizo, ifeyo monga Akristu tili ndi udindo wofunafuna ntchito.” Inde, sitikayika kuti Yehova ndiponso anthu ake azitithandiza, koma tisaiwale kuti tiyenera kuyesetsa kupeza ntchito.

Kodi tingayesetse m’njira yotani? Adam anati: “Osangokhala pansi n’kupinda manja, n’kumadikirira kuti Mulungu achite zozizwitsa kuti akuthandizeni. Mukamafunafuna ntchito, osazengereza kutchula kuti ndinu wa Mboni za Yehova. Nthawi zambiri mabwana amafuna anthu a Mboni.” Ryszard anapereka malangizo awa: “Muzifunsa mnzanu wina aliyense ngati wamvapo za ntchito kwinakwake, muzikafunsa ku ofesi yoona za anthu ofuna ntchito, muziwerenga zinthu zofalitsidwa zokhudza anthu ofuna antchito, monga zonena kuti: ‘Tikufuna mayi woti adzasamalire munthu wolumala’; kapena zonena kuti ‘Pano pali ganyu yokolola.’ Musatope n’kufunafuna ntchito ayi. Musamakhale ndi mtima wongofuna ntchito inayake yokha basi, ngakhale mutapeza ntchito yonyozeka kapena ntchito yomwe si ya kumtima kwanu, ndi ntchitobe basi.”

Inde, “Mthandizi [wanu] ndiye Ambuye.” ‘Sadzakusiyani konse, kungakhale kukutayani.’ (Ahebri 13:5, 6) Palibe chifukwa choti muzidera nkhawa kwambiri. Wamasalmo Davide analemba kuti: “Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita.” (Salmo 37:5) ‘Kupereka njira yathu kwa Yehova’ kumatanthauza kuti, ngakhale pamene zinthu sizikutiyendera bwino, tizimudalira ndi kuchita zinthu mmene iyeyo amafunira.

Adam ndi Irena anapeza njira yodzisamalirira pa moyo wawo pomatsuka mawindo ndi kukolopa m’masitepesi ndiponso pogwiritsira ntchito ndalama zawo mosamala. Komanso nthawi zambiri ankapita ku ofesi yoona za anthu ofuna ntchito. Irena anati: “Nthawi zonse thandizo linkapezeka nthawi yeniyeni imene tikulifunayo.” Mwamuna wa Irena anawonjezerapo kuti: “Panopo tinazindikira kuti zinthu zimene tinkapempha Mulungu sikuti kwenikweni zinali zogwirizana ndi chifuniro chake. Zimenezi zatiphunzitsa kudalira kwambiri nzeru za Mulungu ndi kusachita zinthu mwanzeru zathu. Ndi bwino kudikirira moleza mtima kuti Mulungu akupatseni njira yokuthandizirani.”​—Yakobo 1:4.

Ryszard ndi Mariola ankagwira ntchito zosiyanasiyana zimene zapezeka koma panthawi yomweyo ankalalikira m’magawo amene munalibe olalikira okwanira. Ryszard anati: “Panthawi zimene tinalibiretu chakudya ntchito inkapezeka. Tinkakana kugwira ntchito za malipiro ambiri zimene zikanasokoneza maudindo athu okhudza zinthu zauzimu. Tinaona kuti ndi bwino kudikirira kuti Yehova atithandize.” Iwowa amakhulupirira kuti Yehova ndiye anawathandiza kuti apeze nyumba ya lenti yotsika mtengo ndipo patsogolo pake Ryszard anadzapeza ntchito.

Kutha kwa ntchito n’kopweteka kwambiri, komatu ndi bwino kuona vutoli monga mwayi woti muone nokha kuti Yehova sadzakusiyani. Yehovatu amakuyang’anirani. (1 Petro 5:6, 7) Iye analonjeza kudzera mwa mneneri Yesaya kuti: “Usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata.” (Yesaya 41:10) Osalola kuti zinthu zamwadzidzidzi, kuphatikizapo kutha kwa ntchito, zikusokonezeni. Chitani mbali yanu ndi mphamvu zanu zonse, ndipo mukatero siyani zonse m’manja mwa Yehova. Dikirirani Yehova “modekha.” (Maliro 3:26) Mukatero adzakudalitsani kwambiri.​—Yeremiya 17:7.

[Chithunzi patsamba 9]

M’malo mongokhala muzichita zinthu zauzimu

[Zithunzi patsamba 10]

Phunzirani kugwiritsira ntchito ndalama zanu mosamala, ndipo pofunafuna ntchito osakhala ndi mtima wongofuna ntchito inayake yokha basi