Dipo Limasonyeza Bwino Chilungamo cha Mulungu
Dipo Limasonyeza Bwino Chilungamo cha Mulungu
ADAMU ndi Hava atagalukira Yehova, iye anafotokoza cholinga chake chodzaukitsa Mbewu yomwe idzazunzundidwe chitende. (Genesis 3:15) Izi zinakwaniritsidwa pamene adani a Mulungu anachititsa kuti Yesu Kristu aphedwe pamtengo wozunzirapo. (Agalatiya 3:13, 16) Yesu anali wopanda tchimo, chifukwa chakuti mayi wake womwe anali namwali anatenga pathupi mozizwitsa ndi mphamvu ya mzimu woyera. Motero, mwazi wake womwe unakhetsedwa ukanatha kugwiritsidwa ntchito monga dipo loombolera anthu, amene anatengera uchimo ndi imfa kwa Adamu.—Aroma 5:12, 19.
Palibe chimene chingalepheretse Mulungu wamphamvuyonse, Yehova, kuchita zolinga zake. Motero, anthu atachimwa, kwa Yehova zinali ngati kuti dipo laperekedwa kale, ndipo akanatha kuchita zinthu ndi anthu amene anakhulupirira kuti malonjezo ake adzakwaniritsidwa. Izi zinachititsa kuti mbadwa zochimwa za Adamu, monga Enoke, Nowa, ndi Abrahamu, zithe kuyenda ndi Mulungu ndiponso kukhala naye pa ubwenzi popanda kuipitsa chiyero chake.—Genesis 5:24; 6:9; Yakobo 2:23.
Anthu ena amene anakhulupirira Yehova anachita machimo akuluakulu. Chitsanzo cha anthu oterewa ndi Mfumu Davide. Mwina mungafunse kuti, ‘Zinatheka bwanji kuti Yehova apitirize kudalitsa Mfumu Davide pambuyo poti iye wachita chigololo ndi Bateseba ndipo kenako waphetsa mwamuna wake, Uriya?’ Chifukwa chachikulu chomwe chinachititsa zimenezi chinali chakuti Davide analapa mochokera pansi pamtima ndiponso anali ndi chikhulupiriro. (2 Samueli 11:1-17; 12:1-14) Chifukwa cha nsembe ya Yesu Kristu ya m’tsogolo, Mulungu anatha kukhululukira machimo a Davide iye atalapa, ndipo Mulungu anakhalabe wolungama. (Salmo 32:1, 2) Potsimikizira zimenezi, Baibulo limafotokoza kuti chinthu chapatali kwambiri chimene dipo la Yesu linakwaniritsa chinali ‘kuonetsa chilungamo chake [cha Mulungu], popeza Mulungu m’kulekerera kwake analekerera machimo ochitidwa kale lomwe’ ndiponso a “m’nyengo yatsopano.”—Aroma 3:25, 26.
Zoonadi, anthu akudalitsidwa kwambiri chifukwa cha mtengo wa mwazi wa Yesu. Chifukwa cha dipo, anthu ochimwa amene alapa angathe kukhala ndi unansi wabwino ndi Mulungu. Komanso, dipo lidzachititsa kuti anthu akufa adzauke n’kukhala m’dziko latsopano la Mulungu. Machitidwe 24:15) Panthawi imeneyo, chifukwa cha dipo, Yehova adzapereka moyo wosatha kwa anthu onse omvera. (Yohane 3:36) Yesu mwiniyo anafotokoza kuti: ‘Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.’ (Yohane 3:16) Anthu adzapeza madalitso onsewa chifukwa cha zimene Mulungu anakonza zoti paperekedwe nsembe ya dipo.
Anthu amenewa adzaphatikizapo atumiki okhulupirika a Mulungu amene anamwalira Yesu asanapereke dipo, ngakhalenso anthu ambiri amene anafera mu umbuli ndipo sankalambira Mulungu. Baibulo limati: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Chinthu chapadera kwambiri chokhudza dipo sikuti ndi phindu limene ifeyo timapezapo. M’malo mwake, chinthu chachikulu kwambiri ndi mmene dipo la Kristu limakhudzira dzina la Yehova. Limatsimikizira kuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo kwambiri amene angathe kuchita zinthu ndi anthu ochimwa, iye n’kupitirizabe kukhala woyera ndiponso wosadetsedwa. Mulungu akanapanda kukonza za dipo, palibe mbadwa iliyonse ya Adamu, ngakhale Enoke, Nowa, kapenanso Abrahamu, imene ikanayenda ndi Yehova kapena kukhala naye paubwenzi. Wamasalmo anazindikira mfundo imeneyi ndipo analemba kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chiriri ndani, Ambuye?” (Salmo 130:3) Ndiyetu tizimuyamikira kwambiri Yehova chifukwa chotumiza kudziko lapansi Mwana wake wokondedwa ndipo tizimuyamikiranso Yesu chifukwa cholola mosanyinyirika kutiperekera moyo wake monga dipo.—Marko 10:45.