Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziko Lopanda Chilungamo

Dziko Lopanda Chilungamo

Dziko Lopanda Chilungamo

KODI mungavomereze kuti tikukhala m’dziko lopanda chilungamo? Mosakayikira mungatero. Ndipotu ngakhale tikhale aluso chotani ndiponso zoganiza zathu zikhale zanzeru chotani, sitikhala otsimikiza kuti tidzapeza chuma, tidzakhala moyo wabwino, ngakhalenso kudzapeza chakudya. Nthawi zambiri zimachitika ngati mmene mfumu yanzeru Solomo inanenera kalekale kuti: “Anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima.” N’chifukwa chiyani zimakhala choncho? Solomo anapitiriza kuti, chifukwa chakuti “yense angoona zom’gwera m’nthawi mwake.”​—Mlaliki 9:11.

‘Zoopsa Zikagwa Mwadzidzidzi’

Inde, ‘zakugwa m’nthawi mwake,’ zomwe nthawi zambiri ndi mavuto otigwera mwadzidzidzi, zimasokoneza zoganiza zathu ndiponso zinthu zimene tinali kuyembekezera. Malinga n’kunena kwa Solomo, timakhala ‘monga nsomba zokodwa mu ukonde ndi mbalame mu msampha, . . . pakagwa zoopsa mwadzidzidzi.’ (Mlaliki 9:12, Malembo Oyera) Mwachitsanzo, anthu ambirimbiri amalima mwakhama m’minda mwawo n’cholinga choti mabanja awo adzakhale ndi chakudya. Koma mosayembekezeka amakumana ndi “zoopsa” mvula ikapanda kugwa, mbewu zawo n’kuwonongeka ndi dzuwa.

Ena amayesa kuthandiza, koma chithandizo chimene mayiko amapereka kwa anthu owonekedwa “zoopsa,” nachonso kawirikawiri chimaoneka kuti sichiperekedwa mwachilungamo. Mwachitsanzo, bungwe lina lalikulu lothandiza pa mavuto ogwa mwadzidzidzi linafotokoza zotsatirazi zomwe zinachitika polimbana ndi chilala chaka china posachedwapa: “Chithandizo chomwe [Africa] yense analandira chinali cha ndalama zochepa kwambiri poyerekeza ndi ndalama zomwe zinagwiritsidwa ntchito pankhondo ya ku Gulf, zomwe zinali zowirikiza kasanu.” Kodi chinali chilungamo kuti pankhondo ya m’dziko limodzi lokha, mayiko opereka chithandizo awononge ndalama zowirikiza kasanu kuposa ndalama zogwiritsa ntchito pochepetsa mavuto amene Africa yense anakumana nawo chifukwa cha chilala? Ndipo kodi ndi chilungamo kuti m’nthawi yathu ino, pamene anthu ambiri ali ndi chuma, munthu mmodzi pa anthu anayi alionse padziko lonse adakali paumphawi wadzaoneni? Kapena, kodi n’chilungamo kuti chaka ndi chaka ana mamiliyoni ambiri azifa ndi matenda oti adakatha kupewedwa? Kunena zoona, chimenechi sichilungamo ayi.

N’zoona kuti ‘zoopsa za mwadzidzidzi’ sizimadza chifukwa cha ‘zakugwa m’nthawi mwake’ zokha ayi. Nawonso anthu amene ali ndi mphamvu amatha kulamulira miyoyo yathu ndiponso ndiwo amachititsa zinthu zina zomwe zimatigwera. Izi ndi zomwe zinachitika m’chilimwe cha chaka cha 2004 mumzinda wa Beslan, ku Alania, pamene anthu ochuluka omwe ambiri mwa iwo anali ana ongoyamba kumene sukulu tsiku limenelo, anaphedwa pa mkangano waukulu wa pakati pa zigawenga ndi asilikali limodzi ndi apolisi. Kunena zoona, amene anaphedwa kapena kupulumuka pamkanganowo linali tsoka kapena mwayi chabe, koma chochititsa chachikulu cha ‘zoopsazi’ unali mkangano wa anthu.

Kodi Zidzakhala Chonchi Mpaka Kalekale?

“Komatu umu ndi mmene moyo wakhalira,” ena amatero pankhani ya kupanda chilungamo. Amati, “Ndi mmene zakhala zikuchitikira m’mbuyo monsemu ndipo zidzapitiriza kukhala chonchi mpaka kalekale.” Kwa iwowo, anthu amphamvu aziponderezabe anthu opanda mphamvu, ndipo olemera aziwadyerabe masuku pamutu anthu osauka. Iwo amati, malinga ngati padziko lapansili pali anthu, tidzapitiriza kuvutika ndi zimenezi pamodzi ndi ‘zotigwera m’nthawi mwake.’

Koma kodi zikufunikadi kukhala chonchi? Kodi zidzatheka kuti anthu amene amayesetsa kuchita zinthu mwanzeru athe kupindula mwachilungamo ndi khama lomwe achita? Kodi pali aliyense amene angasinthe zinthu kwamuyaya padziko lopanda chilungamoli? Taonani zimene nkhani yotsatirayi ikunena za zimenezi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

COVER: Man with a child: UN PHOTO 148426/​McCurry/​Stockbower

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

MAXIM MARMUR/​AFP/​Getty Images