Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Mkristu angakhale ndi chikumbumtima choyera ngati walowa ntchito yofunika kuti azinyamula mfuti kapena zida zina?

Mboni za Yehova padziko lonse sizinyalanyaza m’pang’ono pomwe udindo womwe Mulungu anazipatsa wosamalira mabanja awo. (1 Timoteo 5:8) Komabe, pali ntchito zina zosemphaniranatu ndi mfundo za m’Baibulo ndipo si bwino kugwira ntchito zotero. Zina mwa izo ndi ntchito zokhudzana ndi kutchova juga, kugwiritsa ntchito molakwa magazi, ndiponso ntchito zolimbikitsa anthu kusuta fodya. (Yesaya 65:11; Machitidwe 15:29; 2 Akorinto 7:1; Akolose 3:5) Ntchito zina, ngakhale kuti siziletsedwa m’Baibulo, zingavutitse chikumbumtima cha munthu wogwira ntchitoyo kapena cha anthu ena.

Zili kwa munthu kuvomera kapena kukana ntchito yomwe imafuna kuti munthu azinyamula mfuti kapena chida china chilichonse. Komabe, ntchito yofunika kunyamula chida imaika munthu pangozi yokhala ndi mlandu wa mwazi ngati patafunika kugwiritsa ntchito chidacho. Motero Mkristu afunika kupemphera ndi kulingalira bwino kuti aone ngati akufuna kulandira udindo wosankha mwadzidzidzi zoti achite ndi chida chake, zomwe zingakhudze moyo wa munthu. Kunyamula chida kumaikanso munthu pangozi yoti akhoza kuvulazidwa kapena kuphedwa kumene ngati ataukiridwa ndi adani kapena anthu ena ofuna kum’bwezera zomwe anawachitira.

Enanso angakhudzidwe ndi zimene munthu wasankha kuchita. Mwachitsanzo, udindo waukulu wa Mkristu ndiwo kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Kodi zingatheke kuti munthu aziphunzitsa anthu ‘kukhala mwamtendere ndi anthu onse,’ pamene iyeyo amagwira ntchito yofunika kunyamula chida? (Aroma 12:18) Nanga bwanji za ana ndi anthu ena a m’banja mwake? Kodi miyoyo yawo ingakhale pangozi chifukwa chosunga mfuti m’nyumba? Komanso, kodi anthu angakhumudwe ndi zimene iye wasankha kuchita pankhaniyi?​—Aroma 14:21.

‘M’masiku otsiriza’ ano, anthu ‘aukali, osakonda abwino’ akuchulukirachulukira. (2 Timoteo 3:1, 3) Poganizira zimenezi, kodi zingatheke munthu ‘kukhala wopanda chifukwa’ ngati wasankha ntchito yofunika kunyamula chida imene ingapangitse kuti azilimbana ndi anthu oterowo? (1 Timoteo 3:10) N’zosatheka. Chifukwa cha zimenezi, mpingo sungaone munthu woteroyo kuti ndi “wopanda chirema” ngati akupitiriza kunyamula chida pambuyo poti anthu ena am’patsa mokoma mtima malangizo a m’Baibulo. (1 Timoteo 3:2; Tito 1:5, 6) Motero, bambo kapena mayi woteroyo sangayenerere kupatsidwa mwayi wa utumiki wapadera mu mpingo.

Yesu anatsimikizira ophunzira ake kuti ngati aika zinthu za Ufumu patsogolo m’miyoyo yawo, sayenera kuda nkhawa kwambiri ndi nkhani yopeza zofunika pamoyo. (Mateyu 6:25, 33) Inde, ngati tidalira Yehova ndi mtima wonse, ‘Iye adzatigwiriziza: Nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.’​—Salmo 55:22.