Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinalandira ‘Zokhumba Mtima Wanga’

Ndinalandira ‘Zokhumba Mtima Wanga’

Mbiri ya Moyo Wanga

Ndinalandira ‘Zokhumba Mtima Wanga’

YOSIMBIDWA NDI DOMINIQUE MORGOU

Pambuyo podikirira kwa nthawi yaitali, mu December 1998, ndinafika ku Africa. Kumeneku kunali kukwaniritsidwa kwa cholinga chomwe ndinakhala nacho kuyambira ndili mwana. Ndinkachita chidwi nthawi zonse ndi madera akuluakulu atchire lokhalokha a ku Africa ndiponso nyama zake zakuthengo zokongola kwambiri. Apa, maloto anga anakwaniritsidwa! Ukunso kunali kukwaniritsidwa kwa chinthu china chomwe ndinkachifunitsitsa kwambiri, chomwe chinali kupita kudziko lina monga mlaliki wa nthawi zonse. N’kutheka kuti kwa ambiri izi zinkaoneka ngati zosatheka. Maso anga saona bwinobwino, ndipo m’misewu yafumbi ya m’midzi ya ku Africa ndinkayenda motsogoleredwa ndi galu amene anaphunzitsidwa kuyenda m’misewu ya m’mizinda ya ku Ulaya. N’takufotokozerani mmene zinachitikira kuti ndithe kukatumikira ku Africa ndiponso mmene Yehova wandipatsira ‘zokhumba mtima wanga.’​—Salmo 37:4.

NDINABADWIRA kum’mwera kwa dziko la France, pa June 9, 1966. Ndinali chimalizira m’banja mwathu mwa ana asanu ndi awiri, amuna awiri ndi akazi asanu. Tonsefe makolo athu ankatikonda ndi kutisamalira bwino. Koma ndili mwana panachitika chinthu chimodzi chomvetsa chisoni. Mofanana ndi agogo anga aakazi, amayi anga, ndiponso mmodzi mwa azichemwali anga, ineyo ndili ndi matenda otengera kwa makolo omwe pang’ono ndi pang’ono amachititsa munthu khungu.

Ndili mtsikana anthu ankandisala, ndiponso kundichitira zachinyengo moti zinapangitsa kuti ndizidana ndi anthu. Panthawi yovutayi m’pamene tinasamukira ku dera lotchedwa Hérault. Tili kumeneko panachitika chinthu china chosangalatsa.

Lamlungu lina m’mawa, pakhomo pa nyumba yathu panafika azimayi awiri a Mboni za Yehova. Amayi anali kuwadziwa alendowo ndipo anawalowetsa m’nyumba. Mmodzi wa iwo anakumbutsa amayi lonjezo lawo loti tsiku lina adzavomera kuphunzira nawo Baibulo. Amayi anakumbukira zimenezo n’kuwafunsa kuti, “Ndiye tingayambe liti?” Anagwirizana kuti azikumana Lamlungu lililonse m’mawa, ndipo mwa njira imeneyi amayi anayamba kuphunzira “choonadi cha Uthenga Wabwino.”​—Agalatiya 2:14.

Kuzindikira Zinthu

Amayi anachita khama kwambiri kuti azimvetsa ndi kukumbukira zimene aphunzira. Poti anali akhungu, ankafunika kuloweza pamtima chilichonse. Mboni zija zinaleza nawo mtima kwambiri. Koma ine, nthawi iliyonse Amboniwo akabwera, ndinkakabisala kuchipinda kwanga n’kusokolokako iwo akapita. Koma tsiku lina masana, Eugénie, mmodzi wa Mboni zija, anakumana nane ndi kundilankhula. Anandiuza kuti Ufumu wa Mulungu udzathetseratu chinyengo, udani ndiponso kusalana padzikoli. Anati: “Mulungu yekha ndiye amene angathetse mavuto amenewa.” Kenako anandifunsa ngati ndimafuna kudziwa zambiri. Tsiku lotsatira, ndinayamba kuphunzira Baibulo.

Zonse zomwe ndinkaphunzira zinali zachilendo kwa ine. Tsopano ndinayamba kumvetsa kuti Mulungu ali ndi chifukwa chomveka chololera kuti kwanthawi yochepa padzikoli pakhale kuipa. (Genesis 3:15; Yohane 3:16; Aroma 9:17) Komanso, ndinaphunzira kuti Yehova satisiya opanda chiyembekezo chilichonse. Watilonjeza moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi pano, lomwe ndi lonjezo losangalatsa kwambiri. (Salmo 37:29; 96:11, 12; Yesaya 35:1, 2; 45:18) Ndinaphunziranso kuti m’Paradaiso ameneyo, ndidzayambiranso kuona bwinobwino, komwe panthawiyi ndimachita kuvutikira kwambiri.​—Yesaya 35:5.

Kuyamba Utumiki wa Nthawi Zonse

Pa December 12, 1985, ndinasonyeza kuti ndadzipereka kwa Yehova pobatizidwa m’madzi. Apa, ndinafanana ndi mchemwali wanga Marie-Claire, yemwe anali atabatizidwa kale. Posakhalitsa, nayenso mlongo wanga Jean-Pierre anabatizidwa, chimodzimodzinso ndi amayi.

Kumpingo womwe ndinkapita kunali anthu angapo omwe anali apainiya okhazikika kapena kuti alaliki a nthawi zonse. Changu chawo ndiponso mmene anali kusangalalira ndi utumiki zinandilimbikitsa nanenso. Ngakhale Marie-Claire, amene anali ndi vuto la maso ndiponso anali wolumala mwendo moti ankachita kuvala chitsulo kumwendo, anayamba utumiki wa nthawi zonse. Mpaka pano, Marie-Claire amandilimbikitsabe mwauzimu. Pokhala ndi apainiya kumpingo ndi m’banja mwathu momwe, ndinayamba kukhala ndi chidwi choti nanenso ndichite utumiki wa nthawi zonse. Motero, mu November 1990, ndinayamba kutumikira monga mpainiya mu mzinda wa Béziers.​—Salmo 94:17-19.

Kupirira Zofooketsa

Mu utumiki, ndinali kusamalidwa bwino kwambiri ndi apainiya anzanga. Izo zili apo, ndinkakhumudwa nthawi ndi nthawi ndikaganizira za zinthu zina zimene sindingathe kuchita ndipo ndinkalakalaka n’tamachita zinthu zambiri. Komabe Yehova ankakhala nane panthawi zimene ndinafookazo. Ndinafufuza mu Watch Tower Publications Index, kuyang’ana nkhani za apainiya omwe nawonso anali ndi vuto la maso ngati ineyo. Ndinadabwa kuona kuti analipo ambirimbiri. Nkhani zothandiza ndi zolimbikitsa zimenezi zinandiphunzitsa kuti ndizikhala woyamikira pa zimene ndimatha kuchita ndiponso kuti ndizivomereza kuti pali zinthu zina zimene sindingathe kuchita.

Kuti ndizitha kupeza zosowa pamoyo wanga, ndinkagwira ntchito yokonza m’masitolo limodzi ndi Mboni zina. Tsiku lina ndinazindikira kuti anzanga omwe ndinkagwira nawo ntchitoyi akubwerezanso kukonza pamene ine ndinali n’tangokonza kumene. Mosakayikira, ndiye kuti sindimakonza bwino. Ndinakalankhula ndi Valérie, mpainiya amene amayang’anira gulu lathu lokonza m’masitolo, ndi kumuuza kuti asamangike, andiuze ngati ndimavutitsa anzanga ena pagululo. Mokoma mtima, anasiya nkhaniyo m’manja mwanga kuti ndidzasiye ndekha pamene ndikuona kuti sindingathenso kugwira ntchitoyo. Mu March 1994, ndinasiya kugwira nawo ntchito yokonza m’masitoloyo.

Zitachitika izi, ndinadzionanso kuti ndine wopanda pake. Ndinapemphera zolimba kwa Yehova, ndipo ndikudziwa kuti anamva zopempha zanga. Ulendo uwunso, ndinathandizidwa kwambiri chifukwa chophunzira Baibulo ndi mabuku achikristu. Komabe, maganizo ofuna kutumikira Yehova anapitiriza kukula, ngakhale kuti vuto langa la maso lija limamka likula. Ndiye ndikanatani?

Kudikirira Kenako N’kuganiza Zochita Mwamsangamsanga

Ndinapempha kukaphunzira ku sukulu ya akhungu ya Rehabilitation Center for the Blind and Visually Impaired ku Nîmes, ndipo patapita kanthawi anandilola kukaphunzirako miyezi itatu. Nthawi imeneyi sinapite pachabe. Ndinayamba kumvetsa bwino chilema changachi ndipo ndinaphunzira kukhala mogwirizana nacho. Kukhala ndi anthu a zilema zosiyanasiyana kunandithandiza kuzindikira ubwino wa chiyembekezo chimene ndili nacho monga Mkristu. Ine ndinaliko bwino popeza ndinali ndi cholinga pamoyo ndiponso ndinkatha kuchita zinthu zaphindu. Ndinaphunziranso kuwerenga zilembo za akhungu za Chifalansa.

Nditabwerera kunyumba, banja langa linazindikira kuti sukulu ija inandithandiza kwambiri. Komabe, chinthu chimodzi chimene sindinasangalale nacho m’pang’ono pomwe ndi ndodo yoyendera akhungu yomwe anandipatsa. Ndinavutika kwambiri kuti ndiizolowere. Kukanakhala bwino kupeza njira ina, mwina kumatsogoleredwa ndi galu.

Motero ndinapempha galu koma ndinauzidwa kuti panali anthu ambiri omwe anali kuyembekezera agalu. Komanso bungwe lomwe ndinalipemphalo linafunika kudzafufuza kaye mmene ndizidzakhalira naye. Sapereka agalu chisawawa kwa anthu. Tsiku lina, mayi wina amene ankathandiza kuyendetsa bungwe lina la anthu akhungu anandiuza kuti gulu lina la osewera mpira wa tenesi linakonza zopereka galu kwa munthu wakhungu kapena amene ali ndi vuto la maso m’dera lathu. Anandiuza kuti iye atamva zimenezi, anaganizira za ineyo. Anandifunsa ngati ndingalandire galuyo. Ndinaona kuti Yehova ndiye anali kuchititsa zimenezi ndipo ndinavomera thandizolo. Komabe, ndinafunika kudikirira galuyo.

Ndinali Kuganizirabe Zopita ku Africa

Ndili m’kati modikirira, ndinayamba kuika mtima pa zinthu zina. Monga ndanenera kumayambiriro kuja, ndinkachita chidwi kwambiri ndi Africa kungoyambira ndili mwana. Ngakhale kuti vuto langa la maso linafika poipa, chidwi chimenecho chinakula kwambiri, makamaka nditamva kuti anthu ambiri ku Africa amachita chidwi ndi Baibulo ndipo ali ndi mtima wofuna kutumikira Yehova. Nthawi inayake m’mbuyomo, ndinatchulirapo Valérie mocheza, kuti ndikufuna kukacheza ku Africa. Ndinamufunsa ngati angakonde kutsagana nane. Anavomera, ndipo tinalembera kalata ku nthambi zingapo za Mboni za Yehova za m’mayiko a ku Africa olankhula Chifalansa.

Tinalandira yankho kuchokera ku Togo. Mtima uli m’malere, ndinapempha Valérie kuti andiwerengere kalatayo. Munali nkhani yabwino, motero Valérie anati: “Ngati ndi choncho, tilekeranji kupitako?’ Titalemberana kalata ndi abale ku nthambi, ndinauzidwa kuti ndilankhulane ndi Sandra, mpainiya wa mu mzinda wa Lomé, womwe ndi likulu la dzikolo. Tinakonza zoti tidzanyamuke pa December 1, 1998.

Titafika, tinaona kuti zinthu zinali zosiyana kwambiri ndi kwathu, koma tinali ndi chimwemwe chodzadza tsaya. Ndege yathu itatera ku Lomé, ife n’kutsikamo tinaombedwa mphepo yotentha ya ku Africa. Kenako tinakumana ndi Sandra. Tinali tisanakumanepo, koma titangokumana tinakhala ngati tinayamba kalekale kugwirizana. Ulendo wathuwu utayandikira, Sandra ndi mnzake wina, dzina lake Christine, anaikidwa kukakhala apainiya apadera ku Tabligbo, mzinda waung’ono womwe uli m’katikati mwa dziko la Togo. Apa, tinali ndi mwayi wopita nawo limodzi ku ntchito yawo yatsopanoyi. Tinakhalako pafupifupi miyezi iwiri, ndipo titabwerera kwathu, ndinkadziwa kuti ndidzapitakonso.

Ndinasangalala Kwambiri Kubwereranso ku Togo

Ndili ku France, sipanapite nthawi yaitali, ndinayamba kukonzekera ulendo wanga wachiwiri wa ku Togo. Banja langa linandithandiza, ndipo ndinatha kukonza zoti ndikakhaleko miyezi isanu ndi umodzi. Motero, mu September 1999, ndinakweranso ndege ulendo wa ku Togo. Koma paulendo uwu ndinali ndekha. Mukhoza kuona nokha kuti banja langa linali ndi nkhawa kundiona ndikunyamuka ndekha, chikhalirecho ndili wolumala. Koma panalibe chifukwa chodera nkhawa. Ndinatsimikizira makolo anga kuti anzanga, omwe ndinali n’tayamba kale kuwaona ngati azibale anga, andichingamira ku Lomé.

Zinali zosangalatsa kwambiri kubwerera kudera limene anthu ambiri amachita chidwi ndi Baibulo. Sizachilendo kuona anthu akuwerenga Baibulo mumsewu. Ku Tabligbo anthu amatha kukuitana kuti mungokambirana za m’Baibulo basi. Ndipo unalitu mwayi wapadera kukhala m’nyumba yaing’ono ndi alongo awiri, ochita upainiya wapadera. Ndinaphunzira chikhalidwe china, zomwe zinandithandiza kuti ndiziona zinthu mosiyana kwambiri ndi mmene ndinkazionera kale. Choyambirira, ndinaona kuti abale ndi alongo athu ku Africa amaika zinthu za Ufumu patsogolo m’miyoyo yawo. Mwachitsanzo, salephera kufika pamisonkhano ngakhale kuti amafunika kuyenda mitunda italiitali kuti akafike pa Nyumba ya Ufumu. Ndinaphunziranso zambiri mwa kuona chikondi chawo ndiponso mmene amacherezera alendo.

Tsiku lina tikuchokera mu utumiki wa kumunda, ndinauza Sandra kuti ndinali kuopa ndikaganizira zobwerera ku France. Vuto langa la maso lija linali litamkiramkira. Ndinkaganizira za misewu yodzadza ndi anthu ndiponso yaphokoso ya ku Béziers, za masitepe a nyumba za nsanjika, ndiponso zinthu zina zambiri zimene zimachititsa kuti munthu wosaonetsetsa azivutika. Mosiyana ndi zimenezi, misewu ya ku Tabligbo, ngakhale kuti inali yafumbi, inali yabata, yopanda anthu ndi galimoto zambiri. Popeza ndinali n’tazolowera kukhala ku Tabligbo, ndinkadzifunsa kuti kodi zinthu zikandiyendera motani ku France?

Patatha masiku awiri, amayi anaimba telefoni kundidziwitsa kuti a sukulu ya agalu otsogolera akhungu akundiyembekezera. Galu wina, dzina lake Océane, anali chire kuti azikayenda nane monga “maso” anga. Apanso, zofuna zanga zinakwaniritsidwa ndipo mtima wanga unakhala m’malo. Patatha miyezi isanu ndi umodzi yotumikira mosangalala ku Tabligbo, ndinanyamuka kubwerera ku France kukakumana ndi Océane.

Pambuyo pa maphunziro a miyezi ingapo, anandipatsa Océane. Poyambirira, inali ntchito. Tinafunika kuphunzirana kuti tizimvana bwino. Komabe, pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kuzindikira kuti Océane ndi wofunikira pamoyo wanga. Kunena zoona, panopo ndimadalira kwambiri Océane pamoyo wanga. Kodi anthu ku Béziers ankatani akandiona ndikufika pakhomo pawo ndi galu? Ankandipatsa ulemu kwambiri ndiponso ankachita nane zinthu mokoma mtima. Océane anatchuka kwambiri m’dera lomwe tinali kukhalalo. Popeza kuti anthu satakasuka akakhala pafupi ndi munthu wolumala, kuyenda ndi galuyu kunandithandiza kulankhula momasuka za chilema changa. Anthu ankamasuka ndi kutchera khutu. Ndithudi, Océane ankandithandiza kwambiri kuti ndiyambe kucheza ndi anthu.

Ndili ku Africa ndi Océane

Sindinaiwale za ku Africa, ndipo ndinayamba kukonzekera ulendo wachitatu. Ulendo uwu tinatsagana ndi Océane. Ndinatsagananso ndi Anthony ndi mkazi wake Aurore, omwe anali achinyamata, ndiponso mnzanga wina dzina lake Caroline, ndipo onsewa anali apainiya ngati ine ndemwe. Pa September 10, 2000, tinafika ku Lomé.

Poyamba, anthu ambiri ankachita mantha ndi Océane. Ku Lomé kunali anthu ochepa omwe anali ataonapo galu wamkulu ngati Océane, popeza agalu ambiri a ku Togo ndi ang’onoang’ono matupi. Akaona chingwe chake, ena ankaganiza kuti ndi chigalu choopsa chofunika kuchimangirira nthawi zonse. Naye Océane ankakhala chire kuti anditeteze ku chilichonse chomwe waona kuti ndi choopsa. Koma, posakhalitsa Océane anayamba kuzolowera dziko lachilendoli. Akakhala pachingwe, ndiye kuti ali pantchito; amakhala galu wosunga mwambo ndi wodziwa ntchito yake, ndipo sasiyana nane. Ngati sali pachingwe, amakonda kusewera, ndipo amapulupudza nthawi zina. Timasangalala kwambiri tikakhala limodzi.

Tonsefe tinapemphedwa kukakhala ndi Sandra ndi Christine ku Tabligbo. Pofuna kuthandiza abale ndi alongo a kumeneko kuti azolowerane ndi Océane, tinkawaitana kuti adzatichezere ndipo tinkawafotokozera ntchito ya galu ngati Océane, chifukwa chimene ndinkayendera naye, ndiponso zimene iwo ayenera kuchita akakhala naye pafupi. Akulu anavomera kuti ndizipita ndi Océane ku Nyumba ya Ufumu. Popeza izi zinali zachilendo kwambiri ku Togo, kumpingo kunaperekedwa chilengezo cha nkhaniyi. Ku utumiki ndinkapita ndi Océane pa maulendo obwereza ndi ku maphunziro a Baibulo basi. Nthawi zimenezi ndi pamene anthu sankavutika kumvetsa chifukwa chake ndikuyenda naye.

Kulalikira m’gawo limeneli n’kosangalatsabe kwambiri. Ndinakhudzidwanso mtima chifukwa cha zinthu zosiyanasiyana zomwe anthu ankachita zondiganizira. Iwo ankandiganizira pondichitira zinthu mokoma mtima, monga kundipatsa mpando mosanyinyirika. Mu October 2001, amayi anga anapita nane limodzi paulendo wanga wachinayi wa ku Togo. Atakhalako milungu itatu anabwerera ku France, ali osangalala ndi okhutira kuti ndili bwino.

Ndimamuyamikira kwambiri Yehova chifukwa choti ndinakhala ndi mwayi wokatumikira ku Togo. Sindikayikira m’pang’ono pomwe kuti Yehova apitiriza kundipatsa ‘zokhumba mtima wanga’ pamene ndikupitiriza kugwiritsa ntchito zinthu zonse zimene ndili nazo pomutumikira. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 37 Mlongo Morgou anabwerera ku France ndipo anatha kukonza ulendo wachisanu wa ku Togo, womwe anapita pa October 6, 2003, n’kubwerera kwawo pa February 6, 2004. N’zomvetsa chisoni kuti chifukwa cha thanzi lake, n’kutheka kuti umenewu unali ulendo wake wotsiriza wa ku Togo m’dongosolo lino la zinthu. Komabe, cholinga chake chachikulu chidakali chotumikira Yehova.

[Zithunzi patsamba 10]

Ndinkachita chidwi nthawi zonse ndi madera akuluakulu atchire lokhalokha a ku Africa ndiponso nyama zake zakuthengo zokongola kwambiri

[Chithunzi patsamba 10]

Océane ndinkapita naye pamaulendo obwereza

[Chithunzi patsamba 11]

Akulu anavomera kuti ndizipita ndi Océane ku misonkhano