Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Chikondano cha Inu Nonse Chikukula’

‘Chikondano cha Inu Nonse Chikukula’

‘Chikondano cha Inu Nonse Chikukula’

MU 2004, ku Japan kunachitika masoka achilengedwe ambirimbiri. Ena mwa masoka achilengedwe amenewa anali mphepo zamkuntho, kusefukira kwa madzi, ndiponso zivomezi. Masokawa anakhudza anthu ambiri kuphatikizapo Mboni za Yehova. (Mlaliki 9:11) Komabe, masokawa anapereka mwayi woti Mboni zisonyeze chikondi chaubale kwa wina ndi mnzake.​—1 Petro 1:22.

Mwachitsanzo, mtsinje umene uli m’chigawo chapakati cha dziko limeneli la Japan, unasefukira chifukwa cha mvula yamphamvu imene inagwa mwezi wa July. Madzi osefukirawo anawononga nyumba za Mboni za Yehova zoposa 20. Ndipo madzi anadzaza m’kati mwa Nyumba ya Ufumu ina, pafupifupi mita imodzi kuchokera pansi. Posakhalitsa zimenezi zitachitika, Mboni za mipingo ya pafupi ndi Nyumba ya Ufumuyo, zinabwera kudzathandiza. Anthu ambirimbiri odzipereka anayeretsa nyumba zonse zomwe zinali ndi matope. Pa milungu iwiri yokha, Nyumba ya Ufumuyo anali ataimaliza kuikonzanso bwinobwino.

Pa October 23, m’dera lomweli, munachitika chivomezi chimene atachiyeza pa sikelo yoyezera kuopsa kwa chivomezi yotchedwa Richter, chinakwana 6.8. Chivomezichi chinapha anthu pafupifupi 40 ndipo anthu opitirira 100,000 anasamuka m’nyumba zawo. Zinthu monga madzi, mafuta, ndiponso magetsi kunalibe. Nyumba ya Ufumu imene anali atangoikonza kumene ija, sinawonongeke ngakhale kuti panali chabe mtunda wokwana makilomita 50, kuchokera pa malo amene panachitikira chivomeziwo. Ndipo posakhalitsa, Nyumba ya Ufumuyo inakhala malo ogawirako thandizo. Oyang’anira achikristu anafufuza mwamsanga kuti adziwe ngati okhulupirira anzawo anali bwino, ndipo atamva kuti palibe amene anavulala kapena kuphedwa, mitima yawo inakhala pansi. M’mamawa wa tsiku lotsatira, Mboni zokwana sikisi zimene zinakhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi kumene kunachitika mu July kuja, zinadzipereka kukasiya chakudya ndi madzi kudera limene linawonongeka ndi chivomezili. M’maola ochepa chabe chivomezichi chitachitika, anthu analandira katundu wachitandizo.

Woyang’anira wina wa mpingo anati: “Anthu amene anavutika nthawi imene kunasefukira madzi ija, anaona ntchito yothandiza anthu omwe agweredwa tsoka la chivomezichi kukhala mwayi wawo woti athokozere thandizo limene analandira. Anagwira ntchito molimbika kuyambira m’mamawa mpaka usiku. Ndipo nkhope zawo zimasonyeza kuti anali kusangalala.”

Kaya n’kusefukira kwa madzi kapena zivomezi, palibe chimene chingasokoneze chomangira cha chikondi chimene chimalimbitsa ubale wachikristu wa Mboni za Yehova. M’malo mwake, pakagwa tsoka, Akristu amaona zimene mtumwi Paulo anauza okhulupirira anzake ku Tesalonika kuti: “Chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake.”​—2 Atesalonika 1:3.