Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulosi wa Hoseya Umatithandiza Kuyenda ndi Mulungu

Ulosi wa Hoseya Umatithandiza Kuyenda ndi Mulungu

Ulosi wa Hoseya Umatithandiza Kuyenda ndi Mulungu

“Adzatsata Yehova.”​—HOSEYA 11:10.

1. Kodi ndi nkhani iti yophiphiritsa imene imapezeka m’buku la Hoseya?

KODI mumasangalala ndi nkhani zimene anthu ake ndiponso zochitika zake n’zochititsa chidwi? Ndiyetu buku la m’Baibulo la Hoseya lili ndi nkhani yophiphiritsa ngati imeneyo. * Nkhaniyo imafotokoza zochitika za m’banja la Hoseya, mneneri wa Mulungu. Imakhudzanso ukwati wophiphiritsa umene Yehova anachita ndi Israyeli wakale kudzera m’pangano la Chilamulo cha Mose.

2. Kodi n’zotani zimene zikudziwika ponena za Hoseya?

2 Nkhaniyi ikuyambira m’buku la Hoseya chaputala 1. Zikukhala ngati Hoseya anali kukhala m’dera la ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi (umene umadziwikanso ndi dzina la fuko lake lalikulu, Efraimu). Analosera panthawi imene mafumu asanu ndi awiri omaliza a Israyeli anali kulamulira ndiponso panthawi imene Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya​—mafumu a Yuda​—anali kulamulira. (Hoseya 1:1) Choncho Hoseya analosera kwa zaka zosachepera 59. Ngakhale kuti sipanapite nthawi yaitali kuchokera pamene buku lotchedwa ndi dzina lake limeneli linamalizidwa, chitadutsa chaka cha 745 B.C.E., bukuli likugwirabe ntchito masiku ano, pamene anthu mamiliyoni akuchita zofanana ndi zimene analosera m’mawu awa akuti: “Adzatsata Yehova.”​—Hoseya 11:10.

Kupenda Mfundo Zake Mwachidule

3, 4. Fotokozani mwachidule zimene zili m’chaputala 1 mpaka 5 cha Hoseya.

3 Kupenda mwachidule Hoseya chaputala 1 mpaka 5 kutithandiza kulimbikira kuyenda ndi Mulungu mwa kuonetsa chikhulupiriro chathu ndi kuchita zinthu zogwirizana ndi chifuniro chake. Ngakhale kuti nzika za ufumu wa Israyeli zinachita chigololo chauzimu, Mulungu anali kudzawachitira chifundo ngati atalapa. Zimenezi zinasonyezedwa ndi mmene Hoseya anachitira ndi mkazi wake, Gomeri. Mkaziyu atabereka mwana mmodzi wa Hoseya, zikuoneka kuti anaberekanso ana awiri apathengo. Ngakhale kuti mkaziyo anatero, Hoseya anam’tenganso, ngati mmene Yehova analili wokonzeka kuchitira chifundo Aisrayeli olapa.​—Hoseya 1:1–3:5.

4 Yehova anali ndi mlandu ndi Israyeli chifukwa chakuti m’dzikomo munalibe choonadi, chifundo, kapena kudziwa Mulungu. Anali ndi mlandu ndi Israyeli wopembedza mafano ndiponso Yuda, umene unali ufumu wolowerera. Koma anthu a Mulunguwo atakhala “m’masauko mwawo,” anafunafuna Yehova.​—Hoseya 4:1–5:15.

Nkhani Yake

5, 6. (a) Kodi chigololo chinali chofala motani mu ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi? (b) Nanga n’chifukwa chiyani chenjezo loperekedwa kwa Israyeli wakale lili ndi tanthauzo kwa ife?

5 Mulungu anati kwa Hoseya: “Muka, udzitengere mkazi wachigololo ndi ana achigololo; pakuti dziko latsata chigololo chokhachokha kuleka kutsata Yehova.” (Hoseya 1:2) Kodi chigololo chinali chofala motani mu Israyeli? Akutiuza kuti: “Mzimu wachigololo wawalakwitsa [anthu a ufumu wa mafuko khumi], ndipo achita chigololo kuchokera Mulungu wawo. . . . Ana anu akazi achita chitole, ndi apongozi anu achita chigololo. . . . Iwo okha apambukira padera ndi akazi achitole, naphera nsembe pamodzi ndi akazi operekedwa kuchitole.”​—Hoseya 4:12-14.

6 Chigololo chauzimu ndi chakuthupi chinali ponseponse mu Israyeli. N’chifukwa chake Yehova ‘anawabwezera,’ kapena kuti kuwalanga, Aisrayeli. (Hoseya 1:4; 4:9) Chenjezo limeneli lili ndi tanthauzo kwa ife chifukwa Yehova adzalanga anthu amene amachita chiwerewere ndiponso amene amatsata kupembedza kodetsa masiku ano. Koma amene akuyenda ndi Mulungu amatsatira miyezo yake ya kupembedza koyera ndipo amadziwa kuti “wadama yense . . . alibe cholowa m’ufumu wa Kristu ndi Mulungu.”​—Aefeso 5:5; Yakobo 1:27.

7. Kodi ukwati wa Hoseya ndi Gomeri unaimira chiyani?

7 Pamene Hoseya anakwatira Gomeri, ayenera kuti Gomeriyo anali namwali, ndipo anali mkazi wokhulupirika nthawi imene ‘anam’balira mwana wamwamuna.’ (Hoseya 1:3) Mogwirizana ndi nkhani yophiphiritsa imeneyi, Mulungu atangomasula Aisrayeli ku ukapolo wa ku Igupto mu 1513 B.C.E., iyenso anachita nawo pangano limene linali ngati pangano la ukwati woyera. Povomereza panganolo, Israyeli analonjeza kuti adzakhala wokhulupirika kwa ‘mwamuna wake,’ Yehova. (Yesaya 54:5) Inde, ukwati wophiphiritsa umenewu pakati pa Israyeli ndi Mulungu ndi umene unaimiridwa ndi ukwati woyera wa Hoseya ndi Gomeri. Koma ndiye zinthu zinadzasinthatu!

8. Kodi chinachitika n’chiyani kuti pakhale ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi, nanga munganenepo zotani pankhani ya kupembedza kwake?

8 Mkazi wa Hoseya “anaimanso, nabala mwana wamkazi.” Mwana wamkazi ameneyo, ndiponso mwana wina amene Gomeri anabala pambuyo pake, ayenera kuti anali ana achigololo. (Hoseya 1:6, 8) Popeza kuti Gomeri ankaimira Israyeli, mungafunse kuti, ‘Kodi Israyeli anakhala bwanji mkazi wachigololo?’ Mu 997 B.C.E., mafuko khumi a Israyeli anapatukana ndi mafuko a kumwera a Yuda ndi Benjamini. Mu ufumu wa Israyeli wakumpoto wa mafuko khumi, anayamba kupembedza mwana wa ng’ombe kuti anthu ake asamapite ku Yuda kukapembedza Yehova m’kachisi wake ku Yerusalemu. Kupembedza Baala mulungu wonyenga, limodzi ndi mapwando ake a kugonana, zinazika mizu kwambiri mu Israyeli.

9. Malinga ndi ulosi wa pa Hoseya 1:6, kodi n’chiyani chinachitikira Israyeli?

9 Panthawi imene mwana wachiwiri wa Gomeri anabadwa amene ayenera kuti anali wapathengo, Mulungu anauza Hoseya kuti: “Umutche dzina lake Wosachitidwachifundo [kapena kuti “Lo-ruhama”]; pakuti sindidzachitiranso chifundo nyumba ya Israyeli, kuti ndiwakhululukire konse [“chifukwa ndidzawatenga ndithu,” NW].” (Hoseya 1:6) Yehova ‘anawatenga’ pamene Asuri anatenga Aisrayeli kupita nawo ku ukapolo mu 740 B.C.E. Komabe, Mulungu anachitira chifundo ufumu wa Yuda wa mafuko awiri ndipo anaupulumutsa. Sanaupulumutse ndi uta, lupanga, nkhondo, akavalo, kapena apakavalo ayi. (Hoseya 1:7) Tsiku lina usiku mu 732 B.C.E., mngelo mmodzi yekha anapha asilikali 185,000 a Asuri amene anali kufuna kuwononga Yerusalemu, likulu la Yuda.​—2 Mafumu 19:35.

Mlandu Pakati pa Yehova ndi Israyeli

10. Kodi chigololo cha Gomeri chinaimira chiyani?

10 Gomeri anasiya Hoseya n’kukhala “mkazi wachigololo,” ndipo anayamba kuchita chigololo ndi mwamuna wina. Izi zinaimira zimene ufumu wa Israyeli unachita polowa m’mapangano andale ndi mitundu ina yopembedza mafano n’kuyamba kumaidalira. M’malo monena kuti analemera chifukwa cha Yehova, Israyeli ananena kuti analemera chifukwa cha milungu ya mitundu imeneyo ndipo anaphwanya pangano lake la ukwati ndi Mulungu mwa kupembedza milungu yawo yonyenga. M’pake kuti Yehova anali ndi mlandu ndi mtundu umenewu umene unali kuchita chigololo chauzimu!​—Hoseya 1:2; 2:2, 12, 13.

11. Kodi n’chiyani chinachitika ndi pangano la Chilamulo pamene Yehova analola Israyeli ndi Yuda kupita ku ukapolo?

11 Kodi Israyeli analandira chilango chotani chifukwa chosiya Mwamuna wake? Mulungu anachititsa kuti ‘amke kuchipululu’ ku Babulo, mtundu umene unagonjetsa Asuri, amene anatenga Aisrayeli ukapolo mu 740 B.C.E. (Hoseya 2:14) Pamene Yehova anathetsa ufumu wa mafuko 10, sanathetse pangano la ukwati ndi mtundu woyambirira wa mafuko 12 wa Israyeli. Ndipotu pamene Mulungu analola Ababulo kuwononga Yerusalemu mu 607 B.C.E., n’kulola anthu a ku Yuda kukhala akapolo, sanathetse pangano la Chilamulo cha Mose limene mafuko 12 a Israyeli analowa nalo mu ukwati ndi iye. Unansi umenewo unatha pamene atsogoleri achiyuda anakana Yesu Kristu ndi kumupha mu 33 C.E.​—Akolose 2:14.

Yehova Alangiza Israyeli

12, 13. Kodi mfundo ya pa Hoseya 2:6-8 n’njotani, ndipo kodi mawu amenewo anagwira bwanji ntchito pa Israyeli?

12 Mulungu analangiza Israyeli kuti “achotse zadama zake,” koma Israyeli anafuna kutsata aja amene anali kum’konda. (Hoseya 2:2, 5) “Chifukwa chake,” anatero Yehova, “taonani, ndidzatchinga njira yako ndi minga, ndipo ndidzam’mangira mpanda, kuti asapeze mabande ake. Ndipo adzatsata om’konda koma osawakumika, adzawafunafuna koma osawapeza; pamenepo adzati, Ndidzamuka ndi kubwererana ndi mwamuna wanga woyamba, popeza pamenepo panandikomera koposa tsopano. Pakuti sanadziwa kuti ndine ndinam’patsa tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi kum’chulukitsira siliva ndi golidi, zimene anapanga nazo Baala.”​—Hoseya 2:6-8.

13 Ngakhale kuti Israyeli anafuna thandizo ku mitundu imene inali ‘kum’konda,’ sipanapezeke ndi mtundu umodzi womwe unam’thandiza. Anali ngati watchingidwa ndi mpanda wosatheka kulowamo, moti iwo sakanatha kum’patsa thandizo. Asuri atazinga mzinda wa Samariya, likulu lake, kwa zaka zitatu, mzindawo unagwa mu 740 B.C.E., ndipo ufumu wa mafuko khumiwo sunakhazikitsidwenso kachiwiri. Anthu ena mwa Aisrayeli amene anali akapolo, ndi okhawo amene anazindikira kuti zinthu zinali bwino pamene makolo awo anali kutumikira Yehova. Otsalira amenewo anasiya kupembedza Baala ndipo anafuna kuyambiranso unansi wawo umene anapanga ndi Yehova.

Kuonanso Mbali Ina ya Nkhaniyo

14. Kodi zinachitika bwanji kuti Hoseya ayambirenso ukwati wake ndi Gomeri?

14 Kuti timvetsetse mgwirizano umene unalipo pakati pa zochitika m’banja la Hoseya ndi unansi wa Israyeli ndi Yehova, tione mawu awa: “Yehova anati kwa ine, Mukanso, konda mkazi wokondedwa ndi bwenzi lake, koma wakuchita chigololo.” (Hoseya 3:1) Hoseya anamvera lamulolo mwa kugula Gomeri kwa mwamuna amene anali kukhala naye. Atatero, Hoseya analamula mkazi wake mwamphamvu kuti: “Uzikhala ndi ine masiku ambiri, usachita chigololo, usakhala mkazi wa mwamuna aliyense.” (Hoseya 3:2, 3) Gomeri analabadira chilangocho, ndipo Hoseya anayambiranso naye ukwati. Kodi zimenezi zinagwirizana bwanji ndi zimene Yehova anachita ndi anthu a Israyeli ndi Yuda?

15, 16. (a) Kuti mtundu wolangidwa wa Mulungu auchitire chifundo, kodi unayenera kuchita chiyani? (b) Kodi lemba la Hoseya 2:18 lakwaniritsidwa motani?

15 Pamene anthu a ku Israyeli ndi Yuda anali akapolo ku Babulo, Mulungu anagwiritsa ntchito aneneri ake ‘kuwalankhula mowakonda mtima,’ kapena kuti mowafika pamtima. Kuti Mulungu awachitire chifundo, anthu akewo anafunika kuonetsa kulapa ndi kubwerera kwa Mwamuna wawo, ngati mmene Gomeri anachitira kubwerera kwa mwamuna wake. Kenako Yehova adzatenga mtundu wakewo wonga mkazi woti walangidwa kuuchotsa “kuchipululu” cha Babulo ndi kuubweretsa ku Yuda ndi ku Yerusalemu. (Hoseya 2:14, 15) Anakwaniritsa lonjezo limenelo mu 537 B.C.E.

16 Mulungu anakwaniritsanso lonjezo ili: “Ndidzawachitira pangano ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo ndidzathyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zichoke m’dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.” (Hoseya 2:18) Ayuda otsalira amene anabwerera ku dziko lawo anakhala mosatekeseka, osaopa nyama zilizonse. Ulosi umenewu unakwaniritsidwanso mu 1919 C.E., pamene otsalira a Israyeli wauzimu anamasulidwa ku ‘Babulo Wamkulu,’ ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga. Tsopano akukhala mosatekeseka ndipo akusangalala ndi moyo m’paradaiso wauzimu limodzi ndi mabwenzi awo, amene akuyembekeza kukhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Pakati pa Akristu oona amenewa sipapezeka anthu amene ali ndi makhalidwe auchinyama.​—Chivumbulutso 14:8; Yesaya 11:6-9; Agalatiya 6:16.

Zimene Tikuphunzirapo

17-19. (a) Kodi ndi makhalidwe ati a Mulungu amene akutilimbikitsa kutsanzira? (b) Kodi chifundo ndi kukoma mtima kwa Yehova ziyenera kutikhudza motani?

17 Mulungu ali wachifundo ndi wokoma mtima, ndipo ifenso tiyenera kukhala otero. Imeneyi ndi mfundo imodzi imene machaputala oyambirira a Hoseya akutiphunzitsa. (Hoseya 1:6, 7; 2:23) Mtima wa Mulungu wofuna kuchitira chifundo Aisrayeli olapa ukugwirizana ndi mwambi uwu wouziridwa wakuti: “Wobisa machimo ake sadzaona mwayi; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.” (Miyambo 28:13) Ndiponso mawu a wamasalmo ndi otonthoza kwambiri kwa anthu ochimwa amene alapa. Iye anati: “Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.”​—Salmo 51:17.

18 Ulosi wa Hoseya umasonyeza kukoma mtima ndi chifundo zimene Mulungu amene timam’pembedza ali nazo. Ngakhale ena atapatuka pa njira zake zolungama, n’zotheka kuti angalape ndi kubwerera. Ndipo iwo akatero, Yehova amawalandira. Anachitira chifundo anthu olapa a mtundu wa Israyeli, umene analowa nawo mu ukwati wophiphiritsa. Ngakhale kuti iwo sanamvere Yehova ndipo ‘anapweteka Woyerayo wa Israyeli, iye anawachitira chifundo ndipo anakumbukira kuti iwo ndiwo anthu.’ (Salmo 78:38-41) Chifundo choterocho chiyenera kutilimbikitsa kuyendabe ndi Mulungu wathu wokoma mtimayo Yehova.

19 Ngakhale kuti machimo monga umbanda, kuba, ndi kuchita chigololo anali ofala kwambiri mu Israyeli, Yehova ‘analankhula naye mom’konda mtima,’ kapena kuti mom’fika pamtima. (Hoseya 2:14; 4:2) Mitima yathu iyenera kulimbikitsidwa ndipo chikondi chathu pa Yehova chiyenera kulimba tikamaganizira za chifundo chake ndi kukoma mtima kwake. Ndiye tidzifunse kuti: ‘Kodi ndingachite chiyani kuti nditsanzire bwino chifundo ndi kukoma mtima kwa Yehova pochita zinthu ndi ena? Ngati mbale kapena mlongo amene wandilakwira wandipempha kuti ndikhululuke, kodi ndine wokonzeka kukhululuka ngati mmene Mulungu alili?’​—Salmo 86:5.

20. Perekani chitsanzo kusonyeza kuti tiyenera kukhala ndi chidaliro pa chiyembekezo chimene Mulungu wapereka.

20 Mulungu amapatsa chiyembekezo. Mwachitsanzo, analonjeza kuti: “Ndidzam’patsa . . . chigwa cha Akori chikhale khomo la chiyembekezo.” (Hoseya 2:15) Gulu lakale la Yehova longa mkazi wake linali ndi chiyembekezo chodalirika chakuti lidzabwerera kudziko lawo, kumene kunali “chigwa cha Akori.” Popeza kuti lonjezo limenelo linakwaniritsidwa mu 537 B.C.E., tili ndi chifukwa chabwino chosangalalira ndi chiyembekezo chodalirika chimene Yehova waika patsogolo pathu.

21. Kodi kudziwa Mulungu kungatithandize bwanji kuyenda naye?

21 Kuti tipitirize kuyenda ndi Mulungu, tifunika kupitiriza kuphunzira kuti tim’dziwe iye ndi kugwiritsa ntchito zimene tikuphunzirazo. Mu Israyeli anthu ambiri sanali kum’dziwa Yehova. (Hoseya 4:1, 6) Ngakhale zinali tero, ena anayamikira kwambiri chiphunzitso cha Mulungu, anachitsatira, ndipo anadalitsidwa kwambiri. Mmodzi wa iwo anali Hoseya. Enanso anali anthu 7,000 amene sanagwadire Baala masiku a Eliya. (1 Mafumu 19:18; Aroma 11:1-4) Ngati tiyamikira malangizo a Mulungu, zidzatithandiza kupitiriza kuyenda naye.​—Salmo 119:66; Yesaya 30:20, 21.

22. Kodi mpatuko n’ngofunika kuuona bwanji?

22 Yehova amafuna kuti amuna amene akutsogolera anthu ake adane ndi mpatuko. Koma taonani zimene lemba la Hoseya 5:1 likunena: “Imvani ichi, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israyeli; tcherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti chiweruzochi chinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabora.” Atsogoleri ampatuko anali msampha ndi ukonde kwa Aisrayeli, ndipo anawakopa kuti azipembedza mafano. Phiri la Tabora ndiponso malo otchedwa Mizipa ayenera kuti anali malo amene kumachitikira kupembedza konyenga kumeneko.

23. Kodi mwapindula zotani mwa kuphunzira machaputala 1 mpaka 5 a Hoseya?

23 Zokha zimene takambirana kuchokera mu ulosi wa Hoseyazi zatisonyeza kuti Yehova ali Mulungu wachifundo amene amapatsa chiyembekezo ndipo amadalitsa anthu amene amatsatira malangizo ake ndi kudana ndi mpatuko. Mofanana ndi Aisrayeli olapa akale, tiyeni tifunefune Yehova ndi kuyesetsa nthawi zonse kum’kondweretsa. (Hoseya 5:15) Tikatero, tidzatuta zabwino ndi kupeza chisangalalo ndi mtendere zosaneneka, zimene anthu amene amayenda ndi Mulungu mokhulupirika amakhala nazo.​—Salmo 100:2; Afilipi 4:6, 7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Lemba la Agalatiya 4:21-26 limafotokoza nkhani ina yophiphiritsa. Kuti mumve za nkhani imeneyi, onani mu Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, tsamba 693 ndi 694, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ukwati wa Hoseya kwa Gomeri unaimira chiyani?

• Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anali ndi mlandu ndi Israyeli?

• Kodi ndi mfundo iti imene mwachita nayo chidwi kuchokera m’chaputala 1 mpaka 5 cha buku la Hoseya?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi mukudziwa kuti mkazi wa Hoseya akuimira ndani?

[Chithunzi patsamba 19]

Asuri anagonjetsa nzika za Samariya mu 740 B.C.E.

[Chithunzi patsamba 20]

Anthu osangalala akubwerera kudziko lawo