Yendani ndi Mulungu, Kuti Mukolole Zabwino
Yendani ndi Mulungu, Kuti Mukolole Zabwino
“Abzala mphepo, nadzakolola kavumvulu.”—HOSEYA 8:7.
1. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tiyende ndi Yehova?
ULENDO wodutsa dera loopsa ungakhale wabwino ngati tili ndi munthu wina wodziwa deralo, amene akutiperekeza. Kungakhale kwanzeru kuyenda ndi munthu wotiperekezayo kusiyana ndi kungoyamba ulendowo tokhatokha. Penapake, fanizo limeneli likusonyeza mmene zinthu zilili ndi ifeyo. Tingati Yehova wadzipereka kuti atiperekeze kudutsa m’dziko loipali longa chipululu chachikulu. Choncho ndi nzeru kuyenda ndi iye kusiyana ndi kuyesa kutsogolera tokha mapazi athu. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tiyende ndi Mulungu? Tiyenera kutsatira malangizo amene iye wapereka m’Mawu ake.
2. Kodi m’nkhani ino tikambirana chiyani?
2 Nkhani yapita ija inafotokoza nkhani yophiphiritsa imene ikupezeka m’chaputala 1 mpaka 5 cha Hoseya. Malinga ndi zimene tinaona, nkhaniyo ili ndi mfundo zimene tingaphunzirepo, zimene zingatithandize kuyenda ndi Mulungu. Tsopano tiyeni tikambirane mfundo zina zazikulu zimene zili m’chaputala 6 mpaka 9. Kuti zitithandize, tiyeni tione kaye mwachidule zimene zili m’machaputala anayi amenewa.
Chidule Chake
3. Fotokozani mwachidule zimene zili m’chaputala 6 mpaka 9 cha Hoseya.
3 Yehova anatumiza Hoseya makamaka kukalosera ku ufumu wa Israyeli wa kumpoto wa mafuko khumi. Mtundu umenewo, umene unali kudziwikanso kuti Efraimu, kutengera dzina la fuko lake lalikulu, unali utam’siya Yehovayo. M’chaputala 6 mpaka 9, Hoseya akusonyeza kuti anthu anakhala osakhulupirika mwa kuswa pangano la Yehova ndi kuchita zoipa. (Hoseya 6:7) Iwo anakhulupirira mapangano ndi mayiko ena m’malo mobwerera kwa Yehova. Chifukwa chakuti iwo anapitiriza kubzala zoipa, anali kudzakolola zoipa. Kunena kwina, chiweruzo chawo chinali pafupi. Koma ulosi wa Hoseya ulinso ndi uthenga wabwino wolimbikitsa kwambiri. Anthuwo anawatsimikizira kuti angabwerere kwa Yehova ndi kuchitiridwa chifundo akapereka umboni wakuti analapa kuchokera pansi pa mtima.
4. Kodi tikambirana mfundo ziti zothandiza zimene tiphunzire mu ulosi wa Hoseya?
4 M’machaputala anayi amenewa a ulosi wa Hoseya, tingapezemo malangizo ena amene adzatithandiza kuyenda ndi Mulungu. Tiyeni tikambirane mfundo zothandiza zinayi zimene tiphunziremo: (1) Kulapa kwenikweni kumaoneka ndi ntchito za munthu, osati mawu ake okha; (2) nsembe pa zokha Mulungu sakondwera nazo; (3) Yehova zimam’pweteka anthu amene amam’lambira akam’siya; ndipo (4) kuti tikolole zabwino, tiyenera kubzala zabwino.
Mmene Tingasonyezere Kulapa Kwenikweni
5. Tanenani mbali yofunika kwambiri ya zimene zanenedwa pa Hoseya 6:1-3.
5 Ulosi wa Hoseya umatiphunzitsa zambiri zokhudza kulapa ndi chifundo. Pa Hoseya 6:1-3, timawerenga kuti: “Tiyeni, tibwerere kumka kwa Yehova; pakuti wang’amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga. Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lachitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pake. Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kutuluka kwake kwakonzekeratu ngati matandakucha; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.”
6-8. Kodi chinalakwika n’chiyani ndi kulapa kwa Israyeli?
6 Kodi analankhula mawu olembedwa m’mavesi amenewa ndani? Ena amati amene analankhula Hoseya 6:4) Zimenezitu ndi umboni womvetsa chisoni wakuti moyo wauzimu wa anthu a Mulunguwa unali woipa kwambiri! Tingati kukoma mtima, kapena kuti chikondi chokhulupirika, chinali chitatheratu—ngati mame a m’mamawa amene amazimiririka msanga dzuwa likatuluka. Ngakhale kuti anthuwa anadzionetsera ngati kuti alapa, Yehova sanapeze chifukwa chowachitira chifundo. Kodi vuto linali chiyani?
mawu amenewa anali Aisrayeli osakhulupirika ndipo amati anthu amphulupuluwo anali kunamizira kulapa ndipo anali kudyerera chifundo cha Mulungu. Koma ena amati mneneri Hoseya ndiye anali kulankhula mawuwa, kuchonderera anthuwo kuti abwerere kwa Yehova. Kaya ananena mawu amenewa ndani, koma funso lofunika kwambiri n’lakuti, Kodi anthu onse a ufumu wa Israyeli wa mafuko khumiwo anabwerera kwa Yehova, n’kusonyeza kulapa kwenikweni? Yankho lake n’lakuti ayi. Kudzera mwa Hoseya, Yehova anati: “Efraimu iwe, ndidzakuchitira chiyani? Yuda iwe, ndikuchitire chiyani? Pakuti kukoma mtima kwako kukunga mtambo wa m’mawa ndi ngati mame akuphwa mamawa.” (7 Vuto linali lakuti kulapa kwa Israyeli sikunali kochokeradi pansi pa mtima. Lemba la Hoseya 7:14, likufotokoza kusakondwa kwa Yehova ndi anthu ake kuti: “Sanafuulira kwa Ine ndi mtima wawo, koma alira pakama pawo.” Vesi 16 ikuwonjeza kuti: ‘Anabwerera, koma si kwa Wam’mwambamwambayo,’—kunena kwina, osati pa kupembedza kokwezeka. Anthuwo sanafune kubwerera pa kupembedza kokwezeka kwa Yehova mwa kusintha zofunikira kusintha kuti akonze unansi wawo ndi iye. Eyadi, kwenikweni iwo sanafune kuyenda ndi Mulungu!
8 Panalinso vuto lina ndi kulapa kwa Israyeli. Anthuwo anali kuchitabe tchimo—ndipotu, anali machimo ambiri osiyanasiyana, kuphatikizapo chinyengo, umbanda, kuba, kupembedza mafano, ndi kuchita mapangano opanda nzeru ndi mitundu ina. Pa Hoseya 7:4, anthuwo anawayerekeza ndi “ng’anjo,” kapena uvuni ya wophika mkate, mwachionekere chifukwa cha zilakolako zoipa zimene zinali kuyaka ngati moto mwa iwo. Chifukwa cha moyo wauzimu woipa kwambiri choncho, kodi iwo anayenera kuwachitira chifundo? Kutalitali! Hoseya anauza anthu opandukawo kuti Yehova “adzakumbukira mphulupulu yawo” ndipo “adzalanga zochimwa zawo.” (Hoseya 9:9) Panalibenso zowachitira chifundo!
9. Kodi mawu a Hoseya akutiphunzitsa chiyani za kulapa ndi chifundo?
9 Kodi tikamawerenga mawu a Hoseya, akutiphunzitsa chiyani za kulapa ndi chifundo? Chitsanzo chotichenjeza cha Aisrayeli opanda chikhulupiriro chikutiphunzitsa kuti tiyenera kuonetsa kulapa kochokera pansi pa mtima kuti tipindule ndi chifundo cha Yehova. Kodi kulapa koteroko kumaoneka motani? Yehova sanyengeka ndi mawu kapena misozi ayi. Kulapa kwenikweni kumaoneka ndi ntchito za munthu. Kuti munthu wolakwa achitidwe chifundo, ayenera
kusiyiratu njira yake ya uchimo ndi kugwirizanitsa moyo wake ndi miyezo yapamwamba ya kupembedza kokwezeka kwa Yehova.Nsembe pa Zokha Yehova Sakondwera Nazo
10, 11. Malinga ndi zimene nkhani ya Israyeli ikusonyeza, n’chifukwa chiyani nsembe pa zokha Yehova sakondwera nazo?
10 Tsopano tiyeni tikambirane mfundo yachiwiri imene tikuphunzirapo imene ingatithandize kuyenda ndi Yehova. Mfundo yake ndi iyi: Nsembe pa zokha Mulungu sakondwera nazo. Lemba la Hoseya 6:6 limati: “[Ine, Yehova] ndikondwera nacho chifundo, si nsembe ayi; ndi kum’dziwa Mulungu koposa nsembe zopsereza.” Onani kuti Yehova amakondwera ndi chifundo, kapena kuti chikondi chokhulupirika—khalidwe la mu mtima wa munthu—ndi kum’dziwa iye. N’kutheka kuti mukudabwa kuti: ‘N’chifukwa chiyani vesi imeneyi ikunena kuti Yehova sakondwera ndi “nsembe” komanso “nsembe zopsereza”? Kodi Chilamulo cha Mose sichinali kufuna zimenezo?’
11 Inde, Chilamulo chinalidi kufuna nsembe komanso nsembe zopsereza. Komabe, anthu masiku a Hoseya anali ndi vuto lalikulu kwambiri. Zikuoneka kuti panali Aisrayeli amene anangogonjera n’kumapereka nsembe zimenezo pofuna kudzionetsera kuti anali anthu opembedza. Komano panthawi yofananayo, anthuwo anali kuchitabe uchimo. Kuchimwa kwawoko kunasonyeza kuti mu mtima mwawo munalibe chikondi chokhulupirika. Kunasonyezanso kuti iwo anakana kum’dziwa Mulungu, pakuti iwo sanatsatire m’pang’ono pomwe zimene anali kudziwa za Mulunguyo. Ngati anthuwo mtima wawo ndiponso moyo wawo unali woipa, nsembe zawo zikanakhala bwanji zaphindu? Nsembe zawo zinali zonyansa kwa Yehova Mulungu.
12. Kodi pa Hoseya 6:6 pali chenjezo lotani kwa anthu masiku ano?
12 Mawu a Hoseya akupereka chenjezo limene tingaphunzirepo kwa anthu ambiri amene amapita kutchalitchi masiku ano. Iwo amapereka nsembe kwa Mulungu mwa kuchita ntchito zachipembedzo ndi miyambo yake. Koma kupembedza kwawoko sikukhudza khalidwe lawo la masiku onse, ndipo ngati kumatero, m’pang’ono chabe. Kodi anthu amenewo amakondweretsadi Mulungu ngati mitima yawo siwalimbikitsa kum’dziwa iye molondola ndi kutsatira zimene akudziwazo mwa kupewa ntchito zauchimo? Munthu aliyense asaganize kuti Mulungu amakondwera ndi ntchito zachipembedzo pa zokha. Yehova sakondwera ndi anthu amene amayesa kupeza chiyanjo chake mwa kupembedza kwamwambo chabe m’malo motsatiradi Mawu ake ndi mtima wonse.—2 Timoteo 3:5.
13. Kodi timapereka nsembe zotani, koma m’pofunika kukumbukira chiyani chimene chimapangitsa kuti nsembezo zikhale zaphindu?
13 Ifenso Akristu oona timakumbukira kuti nsembe pa zokha Mulungu sakondwera nazo. N’zoona kuti sitipereka nsembe za nyama kwa Yehova. Komabe, ‘timapereka nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.’ (Ahebri 13:15) M’pofunika kusamala kuti tisakhale ngati Aisrayeli ochimwa a m’masiku a Hoseya, mwa kuganiza kuti titha kulipira machimo athu mwa kupereka nsembe zotero zauzimu kwa Mulungu. Tamverani chitsanzo ichi cha mtsikana wina amene anachita chiwerewere n’kubisa. Pambuyo pake anaulula kuti: “Ndinawonjezera utumiki wanga wa kumunda, ndikumaganiza kuti kuchita zimenezi kudzafufuta tchimo langa.” Zimenezi zikufanana ndi zimene Aisrayeli amphulupulu aja anayesa kuchita. Koma Yehova amalandira nsembe yathu ya kuyamika kokha ngati poipereka tili ndi mtima wabwino ndi khalidwe labwino.
Yehova Zimam’pweteka Anthu Amene Amam’lambira Akam’siya
14. Kodi ulosi wa Hoseya ukutiuza chiyani za mtima wa Mulungu?
14 Mfundo yachitatu imene tikuphunzira m’chaputala 6 mpaka 9 cha Hoseya ikukhudza mmene Yehova amamvera anthu amene amam’lambira akam’siya. Mulungu ndi wolimba mtima komanso amakhudzika mtima. Mtima wake umasangalala kwambiri anthu akalapa machimo awo ndipo amawachitira chifundo. Koma ngati anthu akewo salapa, iye amachitapo kanthu mwamphamvu. Chifukwa chakuti Mulungu amatifunira zabwino kwambiri, amakondwera tikamayenda ndi iye mokhulupirika. Lemba la Salmo 149:4 limati: “Yehova akondwera nawo anthu ake.” Nanga kodi Mulungu amamva bwanji ngati atumiki ake ali osakhulupirika?
15. Malinga ndi Hoseya 6:7, kodi Aisrayeli ena anali kuchita zotani?
15 Za Aisrayeli osakhulupirika, Yehova anati: “Iwo analakwira chipangano ngati Adamu, mmene anandichitira monyenga.” (Hoseya 6:7) Liwu la Chihebri limene analimasulira kuti ‘chitira monyenga’ limatanthauzanso “kuchenjeretsa, (kuchita) mosakhulupirika.” Pa Malaki 2:10-16, liwu la Chihebri lomwelo lagwiritsidwa ntchito kufotokoza khalidwe losakhulupirika la Aisrayeli amene anali osakhulupirika kwa anzawo m’banja. Ponena za mmene liwu limeneli limene aligwiritsa ntchito pa Hoseya 6:7, buku lina la umboni limanena kuti ndi “fanizo lonena za ukwati losonyeza maganizo amene munthu amakhala nawo pa ubwenzi umenewo . . . Apa m’poti zinthu zam’vuta chifukwa chakuti chikondi chasokonezeka.”
16, 17. (a) Kodi Israyeli anachita zotani pa pangano la Mulungu ndi mtunduwo? (b) Kodi tiyenera kukumbukira zotani pa zimene timachita?
16 Yehova anaona Israyeli monga mkazi wake wophiphiritsa chifukwa chakuti iyeyo analowa m’pangano ndi mtunduwo. Ndiye pamene anthu ake anaswa mfundo za panganolo, iwo anakhala ngati akuchita chigololo. Mulungu anali ngati mwamuna wokhulupirika, koma anthu ake anam’siya!
17 Nanga bwanji ifeyo? Mulungu zimam’khudza ngati ife tiyenda naye kapena sitiyenda naye. 1 Yohane 4:16) Choncho ngati tilondola njira yoipa, timam’pweteka kwambiri Yehova ndipo sitimusangalatsa ayi. Kukumbukira zimenezi kudzakhala ngati chitetezo chathu champhamvu kuti tisagonje poyesedwa.
Ndi bwino kumakumbukira kuti “Mulungu ndiye chikondi” ndi kuti zimene timachita zimakhudza mtima wake. (Zimene Tiyenera Kuchita Kuti Tikolole Zabwino
18, 19. Kodi pa Hoseya 8:7 tikupezapo mfundo yotani, ndipo mfundo imeneyi inagwira ntchito motani pa Aisrayeli?
18 Tiyeni tsopano tikambirane mfundo yachinayi imene ulosi wa Hoseya ukutiphunzitsa—zimene tiyenera kuchita kuti tikolole zabwino. Ponena za Aisrayeli ndi kupusa kwawo komanso kupanda pake kwa njira yosakhulupirika imene iwo anatsatira, Hoseya analemba kuti: “Abzala mphepo, nadzakolola kavumvulu.” (Hoseya 8:7) Pamenepa pali mfundo imene tingachite bwino kumaikumbukira. Mfundoyo n’njakuti: Pali kugwirizana kwambiri pakati pa zimene tikuchita panopa ndi zimene zidzatichitikire m’tsogolo muno. Kodi mfundo imeneyi inakhala yoona motani pa Aisrayeli osakhulupirikawo?
19 Chifukwa chopitiriza kuchimwa, Aisrayeli amenewo anali kubzala zoipa. Kodi akanapitiriza kutero popanda kukolola zoipa? Iwo sakanapewa chiweruzo chowawa. Lemba la Hoseya 8:13 limati: “Tsopano [Yehova] adzakumbukira mphulupulu yawo, nadzalanga zochimwa zawo.” Ndipo pa Hoseya 9:17, timawerenga kuti: “Mulungu wanga adzawataya, pakuti sanam’mvera Iye; ndipo adzakhala othawathawa mwa amitundu.” Inde, Yehova anali kudzawalanga Aisrayeli chifukwa cha zochimwa zawo. Chifukwa chakuti iwo anabzala zoipa, anadzakolola zoipa. Chiweruzo cha Mulungu pa iwo chinafika mu 740 B.C.E., pamene Asuri anagonjetsa ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi ndi kutenga anthu ake ukapolo.
20. Kodi zimene zinachitikira Aisrayeli zikutiphunzitsa chiyani?
20 Zimene zinachitikira Aisrayeli amenewo zikutiphunzitsa mfundo yosatsutsika yakuti: Timatuta zimene tafesa. Mawu a Mulungu amatichenjeza kuti: “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” (Agalatiya 6:7) Chotero, ngati tifesa zoipa, tidzatuta zoipa. Mwachitsanzo, aja amene ali ndi moyo wachiwerewere amatuta zoipa zopweteka. Munthu wochimwa koma wosalapa amakumana ndi zopweteka.
21. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikolole zabwino?
21 Ndiye tiyenera kuchita chiyani kuti tikolole zabwino? Tiyankhe funso limeneli ndi fanizo losavuta ili: Ngati mlimi akufuna kuti adzakolole chimanga, amabzala chiyani? Tirigu? Iyayi! Mlimi amabzala zimene akufuna kuti adzakolole. Chimodzimodzinso ife. Ngati tikufuna kukolola zabwino, tiyenera kubzala zabwino. Kodi mukufuna kuti muzikololabe zabwino—moyo wosangalatsa panopa ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu? Ngati ndi choncho, ndiyetu mupitirize kubzala zabwino mwa kuyenda ndi Mulungu ndi kutsatira miyezo yake yolungama.
22. Kodi ndi mfundo ziti zimene taphunzira m’chaputala 6 mpaka 9 cha Hoseya?
22 Kuchokera m’chaputala 6 mpaka 9 cha Hoseya, taphunziramo mfundo zinayi zimene zingatithandize kuyenda ndi Mulungu: (1) Kulapa kwenikweni kumaoneka ndi ntchito za munthu; (2) nsembe pa zokha Mulungu sakondwera nazo; (3) Yehova zimam’pweteka anthu amene amam’lambira akam’siya; ndipo (4) kuti tikolole zabwino, tiyenera kubzala zabwino. Nanga kodi machaputala omaliza asanu a buku limeneli la m’Baibulo angatithandize bwanji kuyenda ndi Mulungu?
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi kulapa kwenikweni kumaoneka bwanji?
• Kodi n’chifukwa chiyani nsembe pa zokha Atate wathu wa kumwamba sakondwera nazo?
• Kodi Mulungu amamva bwanji anthu amene amam’lambira akam’siya?
• Kodi tiyenera kubzala chiyani ngati tikufuna kukolola zabwino?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 23]
Monga mtambo wa m’mawa, chikondi chokhulupirika cha Israyeli chinazimiririka
[Chithunzi patsamba 23]
Zilakolako zoipa za Israyeli zinatentha ngati ng’anjo
[Chithunzi patsamba 24]
Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anakana nsembe za anthu ake?
[Chithunzi patsamba 25]
Kuti tikolole zabwino, tiyenera kubzala zabwino