Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu “a Manenedwe Onse” Akumva Uthenga Wabwino

Anthu “a Manenedwe Onse” Akumva Uthenga Wabwino

Anthu “a Manenedwe Onse” Akumva Uthenga Wabwino

“Amuna khumi . . . a manenedwe onse a amitundu [adzati], Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”​—ZEKARIYA 8:23.

1. Kodi Yehova anapereka nthawi yabwino yotani yokhazikitsira ntchito yachikristu m’zinenero ndiponso m’mayiko ambiri?

NTHAWI yake inali yabwino kwambiri. Munali mu 33 C.E., ndipo ili linali tsiku la Pentekoste. Milungu ingapo tsikuli lisanafike, Ayuda limodzi ndi anthu otembenukira ku Chiyuda ochokera m’zigawo zosachepera 15 za ufumu waukulu kwambiri wa Roma ndiponso ochokera m’madera ena anasonkhana ku Yerusalemu kudzachita mwambo wa Paskha. Patsiku la Pentekosteli, anthu masauzande ambiri mwa anthu amenewo anamva anthu wamba odzazidwa ndi mzimu woyera, akulengeza uthenga wabwino m’zinenero zambiri za mu ufumuwo. Sikuti anthuwa anasokonezeka ngati mmene zinachitikira kale pa Babele ayi, koma ankamva bwinobwino zomwe zinkalankhulidwazo. (Machitidwe 2:1-12) Chimenechi chinali chizindikiro cha kubadwa kwa mpingo wachikristu ndiponso kuyambika kwa ntchito yapadziko lonse yomwe ikuchitikabe mpaka lerolino, yophunzitsa anthu m’zinenero zambiri.

2. Kodi ophunzira a Yesu ‘anadabwitsa’ motani anthu osiyanasiyana omwe ankawamvetsera pa Pentekoste wa mu 33 C.E.?

2 N’kutheka kuti ophunzira a Yesu ankalankhula Chigiriki cha anthu wamba, chomwe chinali chofala panthawiyo. Ankalankhulanso Chihebri, chomwe chinkagwiritsidwa ntchito pa kachisi. Koma patsiku la Pentekosteli, ophunzirawo ‘anadabwitsa’ anthu osiyanasiyana omwe ankawamvetsera, mwa kulankhula zinenero za anthuwo. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Anthu owamvetserawo anakhudzidwa mitima ndi mfundo za choonadi zofunika kwambiri zomwe anamva m’chinenero chawo. Patsikuli, gulu laling’ono la ophunzira linakula kwambiri kufika pa anthu oposa 3,000!​—Machitidwe 2:37-42.

3, 4. Kodi ntchito yolalikira inafutukuka motani pamene ophunzira anali kusamuka ku Yerusalemu, Yudeya, ndi Galileya?

3 Patangotha nthawi yochepa chichitikireni zinthu zofunika kwambirizi, ku Yerusalemu kunayamba chizunzo, ndipo “iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mawuwo.” (Machitidwe 8:1-4) Mwachitsanzo, m’chaputala 8 cha buku la Machitidwe, timapezamo nkhani ya Filipo, yemwe zikuoneka kuti anali mlaliki wolankhula Chigiriki. Filipo analalikira Asamariya. Analalikiranso nduna ya ku Itiopiya imene inalabadira uthenga wonena za Kristu.​—Machitidwe 6:1-5; 8:5-13, 26-40; 21:8, 9.

4 Pamene Akristuwo anali kuyendayenda ndi kufufuza malo oti akhalepo kunja kwa Yerusalemu, Yudeya, ndi Galileya, iwo anali kukumana ndi mavuto atsopano a chikhalidwe ndi chinenero. N’kutheka kuti ena mwa iwo ankangolalikira Ayuda okha. Koma pofotokoza zomwe zinachitika, wophunzira Luka anati: “Panali ena mwa iwo, amuna a ku Kupro, ndi Kurene, amenewo, mmene adafika ku Antiokeya, analankhula ndi Ahelene, ndi kulalikira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu.”​—Machitidwe 11:19-21.

Mulungu Wopanda Tsankho Ali ndi Uthenga wa Onse

5. Kodi umboni woti Yehova alibe tsankho umaonekera motani mogwirizana ndi uthenga wabwino?

5 Nkhani zimenezi n’zogwirizana ndi zochita za Mulungu; iye alibe tsankho. Mtumwi Petro atathandizidwa ndi Yehova kusintha maganizo amene anali nawo pa anthu amitundu, iye analankhula moyamikira kuti: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35; Salmo 145:9) Nayenso mtumwi Paulo, yemwe poyamba ankazunza Akristu, anavomereza mfundoyi pamene anati Mulungu “afuna anthu onse apulumuke.” (1 Timoteo 2:4) Timaona umboni wakuti Mlengi alibe tsankho tikaganizira kuti munthu aliyense, mwamuna kapena mkazi, wafuko lililonse, dziko lililonse, kapena wa chinenero chilichonse, ali ndi mwayi wodzalowa mu Ufumu wa Mulungu.

6, 7. Kodi ndi maulosi ati a m’Baibulo amene ananena kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino idzakula kufika padziko lonse ndiponso idzachitika m’zinenero zambiri?

6 Kale kwambiri panaperekedwa maulosi osonyeza kuti ntchitoyi idzakula kufika padziko lonse. Malinga ndi ulosi wa Danieli, Yesu “anam’patsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, am’tumikire.” (Danieli 7:14) Umboni wakuti ulosi wa m’Baibulo umenewu wakwaniritsidwa ndiwo wakuti magazini ino imasindikizidwa m’zinenero 151 ndipo imafalitsidwa padziko lonse, zomwe zakupatsani mwayi wowerenga za Ufumu wa Yehova.

7 Baibulo linalosera za nthawi ina pamene anthu a zinenero zosiyanasiyana adzamve uthenga wake wopatsa moyo. Pofotokoza mmene ambiri adzachitire chidwi ndi kulambira koona, Zekariya analosera kuti: ‘Kudzachitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda [Mkristu wodzozedwa ndi mzimu, yemwe ndi mmodzi wa anthu a “Israyeli wa Mulungu”], ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’ (Zekariya 8:23; Agalatiya 6:16) Ndipo pofotokoza zimene anaona m’masomphenya, mtumwi Yohane anati: ‘Taonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliwerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.’ (Chivumbulutso 7:9) Taona maulosi amenewa akukwaniritsidwa.

Kulalikira Anthu Onse

8. Kodi masiku ano kukuchitika zotani zomwe zikupangitsa kuti tisinthe zina ndi zina pantchito yathu yolalikira?

8 Masiku ano, anthu akuyendayenda kwambiri. Chifukwa cha mwayi womwe ulipo woyenda mosavuta padziko lonse, anthu ambiri akusamukasamuka. Ambiri asamuka m’madera a nkhondo ndi osauka n’kupita kumadera abata, pofuna kukakhala moyo wabwino. M’mayiko ambiri, kuchuluka kwa anthu osamukirako ndiponso othawa kwawo kwachititsa kuti mukhale madera a anthu a chinenero cha dziko lina. Mwachitsanzo, ku Finland kuli zinenero zoposa 120; ku Australia zilipo zoposa 200. Ku United States, mumzinda wina umodzi wokha, wa San Diego, muli zinenero zoposa 100!

9. Kodi tiyenera kuwaona motani anthu a zinenero zina m’gawo lathu?

9 Kodi ifeyo monga atumiki achikristu timaona kuti kupezeka kwa anthu a zinenero zosiyanasiyana amenewa kukusokoneza utumiki wathu? Ayi. M’malo mwake, timasangalala nazo, ndipo timaona kuti zikuthandiza kukulitsa gawo la utumiki wathu. Timaona gawo limeneli monga za m’munda zimene zacha ndipo zikufunika kukolola. (Yohane 4:35) Timayesetsa kuthandiza anthu ozindikira kusowa kwawo kwauzimu, ndipo sitiganizira za dziko limene akuchokera, kapena chinenero chawo. (Mateyu 5:3) Izi zikuchititsa kuti chaka ndi chaka anthu ambiri a ‘manenedwe onse’ azikhala ophunzira a Kristu. (Chivumbulutso 14:6) Mwachitsanzo, mu August 2004, ku Germany ntchito yolalikira inali kuchitika m’zinenero pafupifupi 40. Panthawiyi, ku Australia uthenga wabwino unalalikidwa m’zinenero pafupifupi 30, kuchoka pa zinenero 18 zaka khumi zokha zapitazo. Ku Greece, Mboni za Yehova zinali kulalikira anthu m’zinenero pafupifupi 20. Padziko lonse, Mboni za Yehova pafupifupi 80 pa Mboni 100 zilizonse sizilankhula Chingelezi, chomwe ndi chinenero chachikulu cholankhulidwa padziko lonse.

10. Kodi wofalitsa aliyense payekha ali ndi udindo wotani pantchito yophunzitsa anthu a “mitundu yonse”?

10 Zoonadi, lamulo la Yesu ‘lophunzitsa anthu a mitundu yonse’ likukwaniritsidwa. (Mateyu 28:19) Pokhala ndi chidwi chokwaniritsa lamulo limeneli, Mboni za Yehova zikugwira ntchito yawo m’mayiko 235, ndipo zikugawa mabuku m’zinenero zoposa 400. Ngakhale kuti gulu la Yehova limatipatsa zipangizo zofunika polalikira, wofalitsa Ufumu aliyense payekha ayenera kuchitapo kanthu kuti afotokozere anthu “onse” uthenga wa m’Baibulo m’chinenero chomwe anthuwo angamve bwinobwino. (Yohane 1:7) Khama lomwe tonsefe tikuchita likuthandiza kuti anthu ambiri a zinenero zosiyanasiyana apindule ndi uthenga wabwino. (Aroma 10:14, 15) Inde, aliyense wa ife amachita mbali yofunika kwambiri!

Kuthandiza Anthu a Zinenero Zina

11, 12. (a) Kodi tikuyenera kuchita chiyani kuti tithandize anthu a zinenero zina, ndipo mzimu woyera umatithandiza motani? (b) N’chifukwa chiyani zimathandiza kawirikawiri kulalikira anthu m’chinenero chawo?

11 Masiku ano, ofalitsa Ufumu ambiri angakonde kuphunzira chinenero china, koma sangadalire kapena kuyembekezera mphatso yodabwitsa ya mzimu wa Mulungu. (1 Akorinto 13:8) Kuphunzira chinenero chatsopano si ntchito yamasewera. Ngakhalenso anthu amene akudziwa kale chinenero china angafunikire kusintha maganizo ndi njira yolalikirira n’cholinga choti anthu a chinenerocho, omwe n’ngosiyana nawo kochokera ndiponso chikhalidwe, achite chidwi ndi uthenga wa m’Baibulo. Komanso, anthu amene angosamuka kumene amakhala amantha; ndipo pamafunika khama kuti timvetse maganizo awo.

12 Komabe, mzimu woyera ukupitiriza kuthandiza atumiki a Yehova pantchito yawo yothandiza anthu a zinenero zina. (Luka 11:13) M’malo motipatsa luso lolankhula zinenero zina mozizwitsa, mzimuwu ungalimbikitse mtima wathu wofuna kulankhula ndi anthu amene salankhula chinenero chathu. (Salmo 143:10) Anthu angamve ndithu uthenga wa m’Baibulo m’chinenero chimene iwo sachidziwa bwino, koma kuti tiwafike pamtima penipeni, nthawi zambiri zimakhala bwino kuwafotokozera uthengawu m’chinenero chawochawo.​—Luka 24:32.

13, 14. (a) Kodi n’chiyani chimene chimalimbikitsa ena kuyamba utumiki m’chinenero china? (b) Kodi mtima wodzipereka umaonekera motani?

13 Ofalitsa Ufumu ambiri amayamba kulalikira m’madera a zinenero zina akaona kuti anthu akulabadira kwambiri choonadi cha m’Baibulo. Ena amalimbikitsidwa kwambiri utumiki wawo ukakhala wofuna khama ndiponso wosangalatsa kwambiri. Ofesi ina ya nthambi ya Mboni za Yehova kum’mwera kwa Ulaya inati: “Ambiri mwa anthu ochokera kum’mawa kwa Ulaya ali ndi ludzu la choonadi.” Zimasangalatsa kwambiri kuthandiza anthu olabadira choonadi ngati amenewa!​—Yesaya 55:1, 2.

14 Komabe, kuti tipindule pantchitoyi, tikufunika kuikirapo mtima ndiponso kukhala odzipereka. (Salmo 110:3) Mwachitsanzo, mabanja ambiri ndithu a Mboni ku Japan asiya nyumba zabwino m’mizinda ikuluikulu n’kusamukira kumadera akutali ndi tauni n’cholinga chokaphunzitsa Baibulo nzika za ku China zomwe zasamukira m’maderawo. Kudera lakumadzulo kwa dziko la United States, nthawi zambiri ofalitsa amayenda pagalimoto kwa ola limodzi kapena awiri kuti akachititse maphunziro a Baibulo ndi anthu olankhula Chifilipino. Ku Norway, mwamuna wina ndi mkazi wake amaphunzira ndi banja lina lomwe linachokera ku Afghanistan. Banja la Mbonilo limagwiritsa ntchito bulosha la Chingelezi ndi la Chinorowe la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? * Banja limene akuphunzira nalolo limawerenga ndime m’Chiperisiya, chinenero chofanana kwambiri ndi chinenero chawo cha Chidari. Amakambirana m’Chingelezi ndi Chinorowe. Anthu a mtima wodzipereka ndiponso wotha kusintha ngati umenewu amafupidwa kwambiri anthu osamukawo akalabadira uthenga wabwino. *

15. Kodi tonsefe tingatani kuti tichite nawo ntchito yolalikira m’zinenero zambiri?

15 Kodi inu mungachite nawo ntchito ya m’zinenero zambiriyi? Bwanji osayamba ndi kufufuza zinenero za kumayiko ena zomwe anthu ambiri amalankhula m’gawo lanu? Kenako mungamayende ndi mathirakiti kapena mabulosha a zinenero zimenezo. Tikunena pano, kabuku kakuti Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse, komwe kanatulutsidwa mu 2004, kathandiza kwambiri pofalitsa chiyembekezo cha Ufumu chifukwa cha uthenga wake wosavuta ndi wolimbikitsa womwe uli m’zinenero zambiri.​—Onani nkhani yakuti “Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse,” patsamba 32.

‘Kukonda Mlendo’

16. Kodi abale amaudindo angasonyeze motani kusadzikonda pothandiza anthu a zinenero za kumayiko ena?

16 Kaya tiphunzire chinenero china kapena ayi, tonsefe tingathandize nawo pantchito yophunzitsa zinthu zauzimu anthu ochokera m’mayiko ena amene ali m’dera lathu. Yehova analangiza anthu ake kuti ‘akondane naye mlendo.’ (Deuteronomo 10:18, 19) Mwachitsanzo, mumzinda wina waukulu ku North America, mipingo isanu imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi. Monga momwe zimachitikira m’Nyumba za Ufumu zambiri, mipingoyo imasinthana nthawi za misonkhano chaka ndi chaka, zomwe zikanachititsa kuti misonkhano ya Chitchaina izichitika madzulo kwambiri patsiku Lamlungu. Zimenezi zikanachititsa kuti ambiri mwa anthu osamukira m’deralo, omwe amagwira ntchito za m’malesitilanti, asamafike kumisonkhano. Akulu m’mipingo inayo anakoma mtima, ndi kusintha nthawi ya misonkhano yawo n’cholinga choti misonkhano ya Chitchaina izichitika koyambirira patsiku Lamlungu.

17. Kodi tiyenera kumva bwanji ena akaganiza zosamuka kuti akathandize gulu la chinenero china?

17 Oyang’anira achikondi amayamikira abale ndi alongo oyenerera ndi aluso amene akufuna kusamuka kuti akathandize magulu a zinenero zina. N’kutheka kuti kuchoka kwa aphunzitsi aluso a Baibulo amenewa kungabweretse mavuto ena mumpingo wawo, koma oyang’anirawo amamva ngati mmene akulu ku Lustra ndi ku Ikoniyo anamvera. Akulu amenewa sanalepheretse Timoteo kuyenda ndi Paulo, ngakhale kuti Timoteo ankathandiza kwambiri m’mipingo yawo. (Machitidwe 16:1-4) Kuwonjezera apo, anthu amene amatsogolera pantchito yolalikira sabwerera m’mbuyo ndi maganizo, miyambo, kapena chikhalidwe cha alendowo zomwe ndi zosiyana ndi zawo. Koma amaphunzira zinthu zosiyanasiyana ndi kuyesetsa kupeza njira zokhalira bwino ndi anthuwo n’cholinga cholalikira uthenga wabwino.​—1 Akorinto 9:22, 23.

18. Kodi ndi khomo la ntchito yaikulu liti limene latsegukira onse?

18 Mogwirizana ndi ulosi, uthenga wabwino ukulalikidwa ‘m’manenedwe onse a amitundu.’ N’zotheka kwambiri kuti pakhale kuwonjezeka chifukwa cha anthu ambiri amene ali m’munda wa anthu olankhula zinenero zina. Ofalitsa ambiri aluso alowa “khomo lalikulu ndi lochititsa” limeneli. (1 Akorinto 16:9) Komabe, pakufunika zambiri kuti tithe kugwira ntchito m’magawo amenewa, monga momwe nkhani yotsatirayi isonyezere.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 14 Onani nkhani yakuti “Tadalitsidwa Kwambiri Chifukwa Chodzimana Zinthu Zochepa,” mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 2004, masamba 24 mpaka 28 kuti mupeze zitsanzo zina.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi tingatsanzire motani Yehova posonyeza kuti sitisankha aliyense?

• Kodi tiziwaona motani anthu amene salankhula chinenero chathu m’gawo lathu?

• N’chifukwa chiyani zimathandiza kulalikira anthu m’chinenero chawo?

• Kodi tingasonyeze motani kuwaganizira anthu ochokera kumayiko ena amene tikukhala nawo?

[Mafunso]

[Mapu/​Chithunzi patsamba 23]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Roma

KRETE

ASIYA

FRUGIYA

PAMFULIYA

PONTO

KAPADOKIYA

MESOPOTAMIYA

MEDIYA

PARTHIA

ELAMU

ARABIYA

LIBIYA

IGUPTO

YUDEYA

Yerusalemu

[Nyanja]

Nyanja ya Mediterranean

Nyanja Yakuda

Nyanja Yofiira

Nyanja ya Perisiya

[Chithunzi]

Pa Pentekoste wa mu 33 C.E., anthu ochokera m’zigawo 15 za Ufumu wa Roma ndiponso ochokera m’madera ena anamva uthenga wabwino m’zinenero zawo

[Zithunzi patsamba 24]

Anthu ambiri ochokera kumayiko ena amalabadira choonadi cha m’Baibulo

[Chithunzi patsamba 25]

Chikwangwani cha Nyumba ya Ufumu cha zinenero zisanu