Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Armagedo Ndi Chiyambi cha Moyo Wosangalatsa

Armagedo Ndi Chiyambi cha Moyo Wosangalatsa

Armagedo Ndi Chiyambi cha Moyo Wosangalatsa

MAWU oti “Armagedo” amachokera ku mawu achihebri akuti “Har–​Magedon” kapena kuti “Phiri la Megido.” Mawuwa amapezeka pa Chivumbulutso 16:16, pamene pamati: “Anawasonkhanitsira ku malo otchedwa m’Chihebri Harmagedo.” Kodi ndani adzasonkhanitsidwa ku Armagedo, ndipo chifukwa chiyani? Pa Chivumbulutso 16:14, timawerenga kuti: ‘Mafumu a dziko lonse’ anawasonkhanitsa pamodzi ‘ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.’ Mosakayikira, mawu amenewa amabutsa mafunso ena owonjezereka ochititsa chidwi. Kodi “mafumu” amenewa akuchitira kuti nkhondo? Kodi n’chifukwa chiyani akuchita nkhondoyo ndipo akumenyana ndi ndani? Kodi mafumu amenewa adzagwiritsa ntchito zida zoopsa zopululutsa anthu ochuluka, monga momwe amanenera anthu ambiri? Kodi padzakhala anthu opulumuka Armagedo? Tiyeni tilole Baibulo lipereke mayankho.

Kodi kutchula “Phiri la Megido” kukutanthauza kuti Armagedo idzachitikira pa phiri linalake ku Middle East? Ayi. Choyamba, ku malo amene Megido wakale anali, kulibe phiri loterolo, ndipo kumapezeka chabe chitunda chotalika mamita 20 kuposa chigwa chomwe chili pafupi ndi chitundachi. Ndiponso, malo a dera la Megido ndi ochepa kwambiri kuti “mafumu [onse] a dziko, ndi magulu a nkhondo awo” asonkhanepo. (Chivumbulutso 19:19) Komabe, Megido anali malo kumene nkhondo zina zoopsa kwambiri m’mbiri ya ku Middle East zinachitikira. Chotero, dzina loti Armagedo limaimira nkhondo yoopsa kwambiri yokhala ndi wopambana mmodzi yekha.​—Onani bokosi lakuti “Megido Ndi Chizindikiro Choyenera,” patsamba 5.

Armagedo singakhale nkhondo ya mayiko a padziko lapansi okha, chifukwa lemba la Chivumbulutso 16:14 limati “mafumu a dziko lonse” adzakhala gulu limodzi pa “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.” Mu ulosi wake wouziridwa, Yeremiya anati “akuphedwa a Yehova” adzangoti mbwee “kuchokera ku malekezero ena a dziko lapansi kumka ku malekezero ena a dziko lapansi.” (Yeremiya 25:33) Chotero, Armagedo si nkhondo ya anthu imene idzachitikira pa malo ena ake ku Middle East. Ndi nkhondo ya Yehova, ndipo idzachitika padziko lonse.

Koma onani kuti pa lemba la Chivumbulutso 16:16, Armagedo imatchedwa kuti “malo.” Mu Baibulo, “malo” angaimire mmene zinthu zilili kapena zochitika. Pamenepa chochitika n’chakuti dziko lonse lidzagwirizana potsutsana ndi Yehova. (Chivumbulutso 12:6, 14) Pa Armagedo, mayiko onse a dziko lapansi adzagwirizana kutsutsana ndi “magulu ankhondo okhala m’Mwamba” otsogozedwa ndi mkulu wa asilikali yemwe ndi “Mfumu ya mafumu, ndi Mbuye wa ambuye,” Yesu Kristu.​—Chivumbulutso 19:14, 16.

Nanga bwanji zimene anthu amanena kuti, Armagedo ndi nkhondo ya zida zoopsa zopululutsa anthu ambiri kapena kugundana kwa zinthu za kumwamba? Kodi Mulungu wachikondi angalole kuti anthu ndiponso mudzi wawo, dziko lapansi ziwonongeke mwa njira yoopsa imeneyi? Ayi. Iye amanena momvekera bwino kuti sanalenge dziko lapansi “mwachabe,” koma “analiumba akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18; Salmo 96:10) Pa Armagedo, Yehova sadzawononga dziko lathu lapansili ndi moto. M’malo mwake, ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’​—Chivumbulutso 11:18.

Kodi Armagedo Idzachitika liti?

Kwa zaka zambiri, funso lofunika kwambiri limene layambitsa maganizo osiyanasiyana n’lakuti, Kodi Armagedo idzachitika liti? Kupenda buku la Chivumbulutso mogwirizana ndi mbali zina za Baibulo kungatithandize kuona nthawi ya nkhondo yofunika kwambiri imeneyi. Lemba la Chivumbulutso limasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa Armagedo ndi kubwera kwa Yesu monga mbala. Yesu anagwiritsanso ntchito fanizoli pofotokoza kubwera kwake kudzaweruza dongosolo la zinthu lilipoli.​—Mateyu 24:43, 44; 1 Atesalonika 5:2.

Kuyambira mu 1914 takhala tili m’masiku otsiriza a dongosolo lino la zinthu, monga momwe maulosi a m’Baibulo amene akwaniritsidwa amasonyezera. * Chimene chidzasonyeza chigawo chomaliza cha masiku otsiriza ndi nthawi imene Yesu anaitcha kuti chisautso chachikulu. Baibulo silinena utali wa nthawi ya chisautso chimenechi, koma mavuto amene chidzabweretsa adzakhala aakulu kwambiri kuposa alionse amene dziko lakumanapo nawo. Chisautso chachikulu chimenechi chidzatha pa Armagedo.​—Mateyu 24:21, 29.

Popeza kuti Armagedo ndi ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse,’ palibe chimene anthu angachite kuti aichedwetse. Yehova ali ndi nthawi ‘yoikika’ pamene nkhondoyi idzayamba ndipo sidzachedwa.​—Habakuku 2:3.

Mulungu Wachilungamo Amenya Nkhondo Yolungama

Koma, n’chifukwa chiyani Mulungu angachite nkhondo padziko lonse? Armagedo ndi yogwirizana kwambiri ndi chilungamo, limodzi la makhalidwe a Mulungu aakulu kwambiri. Baibulo limati: “Yehova akonda chiweruzo,” kapena kuti chilungamo. (Salmo 37:28) Iye waona zinthu zonse zopanda chilungamo zimene zachitika m’mbiri ya anthu. Mwachionekere, iye amakwiya ndi zimenezi, ndipo n’chilungamo kutero. N’chifukwa chake, waika Mwana wake kuti achite nkhondo yolungama kuti awononge dongosolo ili lonse loipa.

Ndi Yehova yekha amene angathe kuchita nkhondo yachilungamo imene idzawononga anthu okhawo ofunika kuwonongedwa. Pankhondo imeneyi anthu a mtima wabwino adzapulumutsidwa mosasamala kanthu za kumene angakhale padziko lapansi. (Mateyu 24:40, 41; Chivumbulutso 7:9, 10, 13, 14) Ndipo iye yekha ndi amene ali ndi mphamvu yolamulira dziko lonse lapansi, chifukwa ndi chilengedwe chake.​—Chivumbulutso 4:11.

Kodi Yehova adzagwiritsa ntchito chiyani powononga adani ake? Ife sitikudziwa. Zimene tikudziwa n’zoti iye ali nazo zida zowonongeratu mitundu yoipa. (Yobu 38:22, 23; Zefaniya 1:15-18) Koma olambira a Mulungu padziko lapansi sadzachita nawo nkhondo imeneyi. Masomphenya a m’Chivumbulutso chaputala 19 amasonyeza kuti ndi ankhondo akumwamba okha limodzi ndi Yesu Kristu omwe adzachita nawo nkhondoyi. Atumiki a Yehova a padziko lapansi pano sadzachita nawo nkhondoyi.​—2 Mbiri 20:15, 17.

Mulungu Wanzeru Apereka Machenjezo Okwanira

Nanga bwanji opulumuka? N’zoona, palibe amene akufuna kudzawonongedwa pa Armagedo. Mtumwi Petro anati: ‘Ambuye . . . safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’ (2 Petro 3:9) Ndipo mtumwi Paulo anati Mulungu “afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.”​—1 Timoteo 2:4.

Kuti akwaniritse cholinga chimenechi, Yehova mwanzeru wachititsa kuti “uthenga . . . wabwino wa Ufumu” ulalikidwe padziko lonse, m’zinenero zambiri. Kulikonse kumene anthu ali akupatsidwa mwayi woti adzapulumuke. (Mateyu 24:14; Salmo 37:34; Afilipi 2:12) Anthu amene amamvera uthenga wabwino angadzapulumuke Armagedo ndi kukhala kosatha ndi moyo wangwiro mu paradaiso padziko lapansi. (Ezekieli 18:23, 32; Zefaniya 2:3; Aroma 10:13) Kodi izi si zimene anthu akuyembekezera kwa Mulungu amene ndi chikondi?​—1 Yohane 4:8.

Zingatheke Bwanji Kuti Mulungu Wachikondi Amenye Nkhondo?

Anthu ambiri amadabwa chifukwa chimene Mulungu amene iyeyo ndiye chikondi angawonongere anthu ambiri. Zimenezi tingaziyerekeze ndi nyumba imene ili ndi makoswe ambiri. Kodi simukuvomereza kuti mwininyumba wosamala kwambiri ayenera kuteteza thanzi ndi moyo wa banja lake mwa kuwononga makoswewo?

Mofananamo, chifukwa chakuti Yehova amakonda kwambiri anthu, nkhondo ya Armagedo iyenera kuchitika. Cholinga cha Mulungu ndicho kupanga dziko lapansi kukhala paradaiso ndiponso kuti anthu akhale angwiro ndi amtendere, opanda “wakuwaopsa.” (Mika 4:3, 4; Chivumbulutso 21:4) Kodi n’chiyani chidzachitikira anthu amene amasokoneza mtendere ndi chitetezo cha anzawo? Chifukwa cha ubwino wa anthu olungama, Mulungu afunika kuwononga anthu onga makoswewo, amene ali oipa kwambiri moti sangasinthe.​—2 Atesalonika 1:8, 9; Chivumbulutso 21:8.

Mavuto ndiponso nkhondo zambiri masiku ano zimachitika chifukwa cha ulamuliro wa anthu wopanda ungwiro komanso dyera lokonda kwambiri dziko lawo. (Mlaliki 8:9) Chifukwa chofuna kupitiriza ndi ulamuliro wawo, maboma a anthu amanyalanyaziratu Ufumu wokhazikitsidwa ndi Mulungu. Palibe chimene chikusonyeza kuti maboma a anthu adzasiyira Mulungu ndi Kristu ulamuliro wawo. (Salmo 2:1-9) Chotero, maboma amenewa afunika kuchotsedwapo kuti pakhale ulamuliro wolungama wa Ufumu wa Yehova wolamulidwa ndi Kristu. (Danieli 2:44) Armagedo ifunika kuchitika kotero kuti nkhani ya amene ali woyenera kulamulira dziko lonse ndiponso anthu ithetsedweretu.

Yehova adzachita nkhondo ya Armagedo n’cholinga chopindulitsa anthu. Pamene zinthu zikuipiraipirabe padziko lapansi, ndi ulamuliro wangwiro wa Mulungu wokha umene ungakhutiritse zofuna za anthu. Mtendere weniweni ndi moyo wabwino udzakhalako kudzera mu Ufumu wake wokha. Kodi zinthu padziko lapansi zingakhale bwanji ngati Mulungu angasiyiretu osachitapo kanthu? Kodi chidani, chiwawa ndi nkhondo sizingapitirizebe kuvutitsa anthu monga momwe zakhala zikuchitira zaka zonsezi pamene anthu akhala akulamulira? Nkhondo ya Armagedo n’chimodzi mwa zinthu zabwino kwambiri chimene chidzapindulitsa anthu.​—Luka 18:7, 8; 2 Petro 3:13.

Nkhondo Yothetsa Nkhondo Zonse

Armagedo idzachita chinthu chimene palibe nkhondo ina iliyonse inachitapo. Ndicho kuthetsa nkhondo zonse. Kodi pali munthu amene salakalaka tsiku limene sikudzakhalanso nkhondo? Koma kuyesayesa konse kwa anthu kuthetsa nkhondo kwalephera. Kulephera mobwerezabwereza kwa anthu kuthetsa nkhondo kumangosonyezeratu mmene mawu a Yeremiya alili oona. Iye anati: “Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Kunena za zimene Yehova adzachita, Baibulo limalonjeza kuti: “Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magareta ndi moto.”​—Salmo 46:8, 9.

Pamene mayiko akugwiritsa ntchito zida zawo zoopsa kwambiri pomenyana ndiponso akufuna kuwononga chilengedwe, Mlengi wa dziko adzachitapo kanthu, pa nkhondo ya Armagedo ya m’Baibulo. (Chivumbulutso 11:18) Chotero, nkhondo imeneyi idzachita zimene anthu amene akhala oopa Mulungu m’mbiri yonse ya anthu akhala akuziyembekezera. Idzatsimikizira kuti ulamuliro woyenera pa zolengedwa zonse ndi wa Mwini dziko, Yehova Mulungu.

Chotero, anthu amene amakonda chilungamo saopa Armagedo. M’malo mwake, Armagedo imawapatsa chiyembekezo. Nkhondo ya Armagedo idzachotsa katangale yense ndi kuipa konse padziko lapansi. Ndipo idzachititsa kuti pakhale dongosolo latsopano lolungama lolamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu wa Mesiya. (Yesaya 11:4, 5) M’malo mokhala tsoka loopsa la mapeto a zonse, Armagedo idzakhala chizindikiro cha chiyambi chosangalatsa cha anthu olungama, amene adzakhala kosatha m’paradaiso padziko lapansi.​—Salmo 37:29.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Onani buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, mutu 11, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 5]

MEGIDO NDI CHIZINDIKIRO CHOYENERA

Mzinda wakale wa Megido unali pamalo abwino kwambiri, oyang’anizana ndi mbali ya kumadzulo ya chigwa cha chonde cha Yezreeli, kumpoto kwa Israyeli. Mzindawu umayang’anira njira zimene zinadutsa mu mzindawu zimene amalonda ndi asilikali ochokera madera osiyanasiyana amadutsamo. Chotero, Megido anakhala malo ankhondo zoopsa kwambiri. Pulofesa Graham Davies, mu buku lake lakuti Cities of the Biblical World​—Megiddo analemba kuti: “Mzinda wa Megido . . . unali wosavuta kufikamo kwa amalonda ndi anthu ochokera madera osiyanasiyana. Koma panthawi imodzimodziyo, ngati unali ndi mphamvu zokwanira, unkatha kuletsa kapena kulola anthu kudutsa m’njirazo ndipo mwa kutero unkakhala ndi mphamvu pa ntchito za malonda ndi nkhondo. Chotero, n’zosadabwitsa kuti anali . . . malo amene ankalimbanirana ndipo amene analanda malowa anali kuwateteza kwambiri.”

Mbiri yaitali ya Megido inayamba zaka zoposa 3,500 zapitazo pamene wolamulira wa Igupto Thutmose Wachitatu anagonjetsa olamulira achikanani mu mzindawu. Mbiri imeneyi inapitiriza kwa zaka zambiri mpaka mu 1918 pamene Kazembe Edmund Allenby wa ku Britain anagonjetseratu asilikali a dziko la Turkey. Kunali ku Megido kumene Mulungu anathandiza Woweruza Baraki kugonjetseratu Mfumu Yabini ya ku Kanani. (Oweruza 4:12-24; 5:19, 20) Kufupi ndi mzindawu, Woweruza Gideoni anagonjetsa Amidyani kotheratu. (Oweruza 7:1-22) Kunalinso ku mzinda umenewu kumene Mfumu Ahaziya ndi Mfumu Yosiya anaphedwera.​—2 Mafumu 9:27; 23:29, 30.

Chotero, n’koyenera kuti dzina la Armagedo likutengedwa kuchokera pa dzina la malo amenewa, chifukwa n’kumene nkhondo zambiri zoopsa zinachitikira. Dzinali ndi chizindikiro choyenera cha nkhondo ya Mulungu yogonjetseratu anthu onse otsutsana naye.

[Mawu a Chithunzi]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

[Zithunzi patsamba 7]

Padziko lonse lapansi, anthu akuchenjezedwa ndi kupatsidwa mwayi wopulumuka Armagedo

[Chithunzi patsamba 7]

Armagedo idzakhala chizindikiro cha chiyambi chosangalatsa