Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhala Atumiki Opita Patsogolo ndi Otha Kusintha

Kukhala Atumiki Opita Patsogolo ndi Otha Kusintha

Kukhala Atumiki Opita Patsogolo ndi Otha Kusintha

“Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti paliponse ndikapulumutse ena.”​—1 AKORINTO 9:22.

1, 2. (a) Kodi mtumwi Paulo anali mtumiki wogwira mtima m’njira ziti? (b) Kodi Paulo anafotokoza motani mmene iye ankaonera ntchito yomwe anapatsidwa?

ANALI munthu womasuka kwa anthu ophunzira kwambiri ndiponso kwa anthu wamba osoka mahema. Analankhula mogwira mtima kwa nduna zachiroma ndiponso kwa alimi a ku Frugiya. Zimene anali kulemba zinkawagwira mtima Agiriki okonda kusintha zinthu ndiponso Ayuda osafuna kusintha zinthu. Panalibe amene ankatsutsa mfundo zake chifukwa zinkakhala zofika pamtima. Aliyense amene ankalankhula naye, ankayesetsa kum’pezera mfundo yoti agwirizane nayo ndi cholinga chothandiza ena kukhulupirira Kristu.​—Machitidwe 20:21.

2 Munthu amene tikufotokozayu anali mtumwi Paulo, ndipo n’zosachita kufunsa kuti anali mtumiki wogwira mtima ndi wopita patsogolo. (1 Timoteo 1:12) Yesu anapatsa Paulo ntchito ‘yonyamula dzina la [Kristu] pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israyeli.’ (Machitidwe 9:15) Kodi iye ankaiona motani ntchito imeneyi? Anafotokoza yekha kuti: “Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti paliponse ndikapulumutse ena. Koma ndichita zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nawo.” (1 Akorinto 9:19-23) Kodi tingaphunzire zotani pa chitsanzo cha Paulo zomwe zingatithandize kukhala ogwira mtima kwambiri pantchito yathu yolalikira ndi kuphunzitsa?

Atasintha Anatha Kuchita Ntchito Yake Bwinobwino

3. Paulo asanatembenuke, kodi ankawaona motani Akristu?

3 Kodi m’mbuyo monsemo Paulo anali munthu woleza ndi wokoma mtima, woyenerera pantchito yomwe anapatsidwayi? Ayi, sanali wotero! Chifukwa chotsatira chipembedzo chake monyanyira, Saulo (dzina lakale la Paulo) anayamba kuzunza mwankhanza anthu otsatira Kristu. Ali wachinyamata anavomereza zoti Stefano aphedwe. Kenako, mopanda chifundo, Paulo anasakasaka Akristu. (Machitidwe 7:58; 8:1, 3; 1 Timoteo 1:13) Anapitiriza “kupumira pa akuphunzira a Ambuye kuopsa ndi kupha.” Posakhutira ndi kusakasaka okhulupirira mu Yerusalemu mokha, Paulo anayamba kufalitsa chidani chakechi kukafika kumpoto, ku Damasiko.​—Machitidwe 9:1, 2.

4. Kodi Paulo anafunika kusintha chiyani kuti athe kugwira ntchito yomwe anapatsidwa?

4 N’kutheka kuti chinthu chachikulu chomwe chinkachititsa Paulo kudana kwambiri ndi Chikristu chinali chikhulupiriro chake chakuti chipembedzo chatsopanochi chidzaipitsa Chiyuda mwa kulowetsamo anthu akunja ndiponso maganizo ena oipa. Ndipotu, Paulo anali “Mfarisi” dzina lotanthauza “munthu wopatulidwa.” (Machitidwe 23:6) Taganizirani mmene Paulo anamvera mumtima atauzidwa kuti Mulungu wam’sankha kuti alalikire anthu za Kristu. Anthu ake Akunjanso! (Machitidwe 22:14, 15; 26:16-18) Afarisi ankakana ngakhale kudya kumene ndi anthu amene iwo ankati ndi ochimwa. (Luka 7:36-39) Mosakayikira, inali ntchito kwa Paulo kuti asinthe maganizo ake n’kugwirizana ndi chifuniro cha Mulungu choti anthu onse apulumuke.​—Agalatiya 1:13-17.

5. Kodi mu utumiki wathu tingam’tsanzire motani Paulo?

5 Nafenso tingafunike kuchita zomwezo. Pamene tikukumana ndi anthu ambiri osiyanasiyana m’munda wathu wapadziko lonse ndiponso wa zinenero zambiri, tikufunika kupenda mtima wathu ndi kupewa tsankho la mtundu uliwonse. (Aefeso 4:22-24) Kaya tikudziwa kapena ayi, zimene timachita m’moyo wathu zimatengera chikhalidwe ndiponso maphunziro athu. Izi zingatipangitse kukhala ndi maganizo kapena mtima watsankho ndiponso waliuma. Kuti tithe kupeza ndi kuthandiza anthu onga nkhosa, tiyenera kuthetsa maganizo oterewa. (Aroma 15:7) Izi n’zimene Paulo anachita. Anavomera ntchito yofutukula utumiki wake, yomwe inafunika khama ndi kudzipereka. Chifukwa cha chikondi, iye anaphunzira luso lophunzitsa lomwe ifeyo tiyenera kutengera. Zoonadi, tikalingalira mmene ‘mtumwi wa anthu amitunduyu’ anachitira utumiki wake timaona kuti anali munthu watcheru, wotha kusintha, ndiponso waluso polalikira ndi kuphunzitsa. *​—Aroma 11:13.

Zimene Anachita Monga Mtumiki Wopita Patsogolo

6. Kodi Paulo anali watcheru motani ndi komwe omvera ake anali kuchokera, ndipo zotsatira zake zinali zotani?

6 Paulo anali watcheru ndi zikhulupiriro za omvera ake ndiponso komwe iwo anali kuchokera. Pamene ankalankhula kwa Mfumu Agripa Yachiwiri, Paulo anavomereza kuti mfumuyo inali ‘kudziwa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda.’ Kenako anagwiritsa ntchito mwaluso zinthu zimene ankadziwa pa zikhulupiriro za Agripa ndipo anafotokozera mfumuyo zinthu zomwe inali kuzidziwa kwambiri. Mfundo zimene Paulo anapatsa mfumuyi zinali zomveka ndiponso sankakayika polankhula, moti Agripa anati: “Ndi kundikopa pang’ono ufuna kundiyesera Mkristu.”​—Machitidwe 26:2, 3, 27, 28.

7. Kodi Paulo anasonyeza motani kuti anali wotha kusintha pamene anali kulalikira khamu lina ku Lustra?

7 Paulo analinso wotha kusintha. Taonani mmene anasinthira pamene ankayesa kulepheretsa gulu lina mumzinda wa Lustra limene linkafuna kulambira Pauloyo ndi Barnaba ngati milungu. Akuti anthu amenewa, omwe ankalankhula Chilukaoniya, anali ena mwa anthu osaphunzira ndiponso okhulupirira za malodza. Malinga ndi Machitidwe 14:14-18, Paulo anatchula zinthu zachilengedwe monga umboni wa mphamvu za Mulungu woona. Mfundo zake zinali zosavuta kuzitsatira, ndipo zikuoneka kuti ‘zinaletsa makamuwo kuti asapereke nsembe’ kwa Paulo ndi Barnaba.

8. Kodi Paulo anasonyeza motani kuti anali wotha kusintha ngakhale kuti nthawi zina ankakwiya ndi zinthu zina?

8 N’zoona kuti Paulo sanali wangwiro, ndipo nthawi zina ankakwiya ndi zinthu zina. Mwachitsanzo, nthawi ina anthu atam’chita chipongwe, Paulo anakalipira Myuda wina dzina lake Hananiya. Koma atauzidwa kuti wanyoza mkulu wa ansembe mosadziwa, iye anapepesa mwamsangamsanga. (Machitidwe 23:1-5) Ali ku Atene, poyamba “anavutidwa mtima pamene anaona [kuti] mudzi wonse wadzala ndi mafano.” Komatu, m’mawu ake pa Phiri la Mars, Paulo sanasonyeze mkwiyo uliwonse. M’malo mwake, iye analankhula ndi anthu a ku Atene pa bwalo lawo, ndipo anapereka mfundo zomwe nawonso anali kuzidziwa pamene anatchula za guwa lawo la nsembe lomwe linalembedwa kuti, “Kwa Mulungu Wosadziwika,” n’kunenanso mawu a mmodzi mwa anthu awo olemba ndakatulo.​—Machitidwe 17:16-28.

9. Kodi Paulo anasonyeza motani luso polankhula ndi anthu osiyanasiyana?

9 Pofuna kuthandiza anthu osiyanasiyana omwe anali kumumvetsera, Paulo anasonyeza kuti anali waluso kwambiri. Ankaganizira chikhalidwe cha anthu ndiponso zinthu zowazungulira zomwe zakhudza maganizo a omvera akewo. Polembera kalata Akristu a ku Roma, iye ankadziwa bwino kuti iwo ankakhala mu likulu la ufumu wamphamvu kwambiri panthawiyo. Mfundo yaikulu m’kalata yomwe Paulo analembera Akristu a ku Roma inali yakuti mphamvu yoipa ya uchimo wa Adamu imagonja kwa mphamvu yowombola ya Kristu. Analankhula mawu owafika pamtima Akristu a ku Roma ndiponso anthu ena mu Roma.​—Aroma 1:4; 5:14, 15.

10, 11. Kodi Paulo ankagwirizanitsa motani mafanizo ake ndi omvera ake? (Onaninso mawu a m’munsi.)

10 Kodi Paulo anatani pamene anafuna kufotokozera omvera ake mfundo zakuya za choonadi cha m’Baibulo? Mtumwiyu anali katswiri pankhani yogwiritsa ntchito mafanizo odziwika bwino ndi osavuta kumva, n’cholinga chomveketsa bwino mfundo zovuta kumva za m’Malemba. Mwachitsanzo, Paulo ankadziwa kuti nkhani ya ukapolo womwe unkachitika mu ufumu wonse wa Roma sinali yachilendo kwa anthu a ku Roma. Ndipo n’kutheka kuti ambiri mwa anthu amene anali kuwalembera kalatawo anali akapolo. Motero Paulo anapereka fanizo la ukapolo pogogomezera mfundo yake yaikulu yokhudza ufulu wa munthu, wogonjera uchimo kapena chilungamo.​—Aroma 6:16-20.

11 Buku lina limati: “Kwa Aroma, mbuye ankatha kumasula kapolo wake popanda kumuikira malire alionse paufulu wake, kapena kapolo ankatha kugula ufulu wake mwa kulipira mbuye wake. Kapolo ankathanso kukhala mfulu pakakonzedwa zoti kapoloyo akhale wa mulungu.” Kapolo amene wamasulidwa ankatha kupitiriza kugwirira mbuye wake ntchito ndi kumalipidwa. Zikuoneka kuti Paulo anafanizira ndi mchitidwe umenewu pamene analemba za ufulu wa aliyense payekha wosankha mbuye woti amumvere, kaya uchimo kapena chilungamo. Akristu ku Roma anali atamasulidwa ku uchimo ndipo tsopano anali akapolo a Mulungu. Anali ndi ufulu wotumikira Mulungu, komabe akanatha kusankha kutumikira uchimo, mbuye wawo wakale, ngati afuna kutero. Fanizo losavuta koma lodziwika bwino limeneli linatha kuchititsa Akristu amenewo ku Roma kuganizaganiza kuti, ‘Kodi ndikutumikira mbuye uti?’ *

Zimene Tikuphunzira pa Chitsanzo cha Paulo

12, 13. (a) Kodi masiku ano pakufunika kuchita khama lotani kuti tithe kuwafika pamtima anthu osiyanasiyana amene timawalalikira? (b) Kodi inu mwaona kuti ndi chiyani chimene chingakuthandizeni kuwalalikira mogwira mtima anthu ochokera kosiyanasiyana?

12 Mofanana ndi Paulo, tiyenera kukhala atcheru, otha kusintha, ndiponso aluso n’cholinga choti tiwafike pamtima omvera athu osiyanasiyana. Kuti tithandize omvera athu kumvetsa uthenga wabwino, si zokwanira kungolankhula ndi anthu mwachizolowezi, kupereka uthenga womwe takonzekera, kapena kugawira mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Timayesetsa kuzindikira mavuto ndiponso nkhawa za anthu, zimene amakonda ndi zimene amadana nazo, ndiponso malingaliro olakwika amene angakhale nawo. Ngakhale kuti pamafunika kuganiza mozama ndiponso khama kuti tithe kuchita zimenezi, ofalitsa Ufumu padziko lonse akusangalala kuchita zimenezi. Mwachitsanzo, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko la Hungary inati: “Abale amalemekeza miyambo ndi chikhalidwe cha anthu a kumayiko ena ndipo sayembekezera alendowo kuti iwo atengere miyambo ya kuno.” Mboni kwina kulikonse zimayesetsa kuchita chimodzimodzi.

13 M’dziko lina la kum’mawa kwa Asia, anthu amadera nkhawa za umoyo wawo, kulera ana, ndi maphunziro. M’dziko limeneli, ofalitsa Ufumu amayesetsa kukambirana ndi anthu nkhani zimenezi m’malo mokambirana nawo za kuipiraipira kwa zinthu padziko lonse kapena za mavuto ena akuluakulu. N’chimodzimodzi ndi zimene ofalitsa mu mzinda wina waukulu ku United States akuchita. Iwo anaona kuti anthu a m’dera linalake m’gawo lawo amada nkhawa ndi nkhani monga za ziphuphu, kuchuluka kwa galimoto m’misewu, ndiponso umbanda. Mbonizo zakhala zikugwiritsa ntchito bwino nkhani zimenezi monga poyambira kukambirana ndi anthuwo za m’Baibulo. Aphunzitsi ogwira mtima a Baibulo amaonetsetsa kuti pa mutu uliwonse umene asankha, iwo alankhule zolimbikitsa. Amaonetsetsanso kuti akutsindika phindu lomwe anthu amapeza panopo pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo ndiponso chiyembekezo chabwino cha zinthu za m’tsogolo chimene Mulungu amapereka.​—Yesaya 48:17, 18; 52:7.

14. Fotokozani njira zimene tingagwirizanitsire uthenga wathu ndi mavuto osiyanasiyana a anthu ndiponso moyo wawo.

14 Ndi bwinonso kumasinthasintha njira zimene timalalikirira, chifukwa chikhalidwe, maphunziro, ndiponso zipembedzo za anthu zimakhala zosiyana kwambiri. Mmene tingalankhulire ndi anthu amene amakhulupirira kuti kuli Mlengi koma sakhulupirira Baibulo zingasiyane ndi mmene tingalankhulire ndi anthu amene amakhulupirira kuti kulibe Mulungu. Polankhula ndi munthu amene amaona kuti mabuku onse a zipembedzo amangothandiza kufalitsa maganizo oipa a anthu, tingasiyanitse ndi mmene timalankhulira ndi munthu amene amavomereza zimene Baibulo limaphunzitsa. Pamafunikanso kusintha tikamalankhula ndi anthu amene maphunziro awo ndi osiyanasiyana. Aphunzitsi aluso amagwiritsa ntchito mfundo ndiponso mafanizo oyenererana ndi mmene zinthu zilili panthawiyo.​—1 Yohane 5:20.

Kuthandiza Atumiki Atsopano

15, 16. Kodi n’chifukwa chiyani pakufunika kuphunzitsa atumiki atsopano?

15 Panali zinthu zinanso zimene Paulo ankafuna kuwongolera kuwonjezera pa njira zimene iye ankagwiritsa ntchito pophunzitsa. Anaona kufunika kophunzitsa ndi kukonzekeretsa mbadwo wachinyamata, monga Timoteo ndi Tito, kuti akhale aphunzitsi ogwira mtima. (2 Timoteo 2:2; 3:10, 14; Tito 1:4) N’chimodzimodzinso masiku ano. Pali kufunika kophunzitsa ndi kuphunzitsidwa.

16 Mu 1914, padziko lonse panali ofalitsa Ufumu pafupifupi 5,000. Masiku ano, anthu atsopano pafupifupi 5,000 amabatizidwa mlungu uliwonse! (Yesaya 54:2, 3; Machitidwe 11:21) Atsopano akayamba kugwirizana ndi mpingo wachikristu n’kukhala ndi mtima wofuna kuchita nawo utumiki, amafunikira kuphunzitsidwa ndi kulangizidwa. (Luka 6:40) Pophunzitsa ndi kulangiza ophunzira, tikufunika kugwiritsa ntchito njira zimene Mbuye wathu, Yesu, ankagwiritsa ntchito. *

17, 18. Kodi tingawathandize motani atsopano kuti azilankhula molimba mtima akakhala mu utumiki?

17 Sikuti Yesu anangopeza gulu la anthu ndi kuuza atumwi kuti ayambe kulankhula ayi. Choyamba, iye anatsindika kufunika kwa ntchito yolalikira ndipo analimbikitsa atumwiwo kuti azipempherera utumiki wawo. Kenako, anachita zinthu zikuluzikulu zitatu zowathandiza: anapatsa aliyense mnzake woyenda naye, gawo lokalalikiramo, ndiponso anawauza uthenga woti akalalikire. (Mateyu 9:35-38; 10:5-7; Marko 6:7; Luka 9:2, 6) Nafenso tingachite chimodzimodzi. Kaya tikuthandiza mwana wathu, wophunzira watsopano, kapena munthu wina amene wakhala nthawi yaitali osalalikira, tiyenera kuyesetsa kum’thandiza mwanjira imeneyi.

18 Atsopano akufunika kuwathandiza kwambiri kuti azilankhula molimba mtima akamalalikira uthenga wa Ufumu. Kodi mungawathandize kukonzekera ndi kuyesera ulaliki wosavuta ndi wogwira mtima? M’munda, aphunzitseni kudzera mu chitsanzo chanu pamene mukulalikira pa nyumba zingapo zoyambirira. Mungatsanzire zimene Gideoni anachita. Iye anauza ankhondo anzake kuti: “Mundipenyerere ine, ndi kuchita momwemo.” (Oweruza 7:17) Kenako m’patseni watsopanoyo mwayi woti nayenso alalikire. Yamikirani anthu atsopano chifukwa cha khama lawo, ndipo ngati m’poyenera, alangizeni mwachidule mmene angawongolerere.

19. Kodi mwatsimikiza kuchita zotani pamene mukuyesetsa ‘kukwaniritsa utumiki wanu’?

19 Kuti ‘tikwaniritse utumiki wathu,’ ndife otsimikiza mtima kukhala otha kusintha kwambiri njira zolalikirira, ndiponso tikufuna kuphunzitsa atumiki atsopano kuti azichita chimodzimodzi. Tikaona kufunika kwa cholinga chathu, chomwe ndi kudziwitsa anthu za Mulungu zimene zingawathandize kudzapulumuka, tikuona kuti tiyenera kuchita khama kukhala ‘zonse kwa anthu onse, kuti paliponse tikapulumutse ena.’​—2 Timoteo 4:5; 1 Akorinto 9:22.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Kuti muone zitsanzo za makhalidwe amenewa mu utumiki wa Paulo, werengani Machitidwe 13:9, 16-42; 17:2-4; 18:1-4; 19:11-20; 20:34; Aroma 10:11-15; 2 Akorinto 6:11-13.

^ ndime 11 Mofanana ndi zimenezi, pofotokoza za ubale watsopano wa pakati pa Mulungu ndi “ana” ake odzozedwa ndi mzimu, Paulo anagwiritsa ntchito mfundo ya zamalamulo yomwe inali yodziwika kwa anthu a mu Ufumu wa Roma omwe anawerenga kalata yake. (Aroma 8:14-17) Buku lakuti St. Paul at Rome limati: “Aroma, pachikhalidwe chawo, ankatha kutenga mwana wa wina n’kumulera kukhala wawo, ndipo umenewu ndiwo unali mchitidwe wofala m’mabanja a Aroma.”

^ ndime 16 Panopa, m’mipingo yonse ya Mboni za Yehova muli dongosolo la Apainiya Athandiza Ena. Cholinga chake ndi choti anthu ongoyamba kumene utumiki athandizidwe ndi luso la atumiki a nthawi zonse ndiponso maphunziro amene atumiki amenewa anachita.

Kodi Mukukumbukira?

• Mu utumiki wathu, kodi tingatsanzire Paulo m’njira ziti?

• Kodi tingafunike kusintha motani maganizo athu?

• Kodi tingatani kuti uthenga wathu uzikhala wolimbikitsa?

• Kodi atumiki atsopano amafunikira chiyani kuti azilankhula molimba mtima?

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 29]

Mtumwi Paulo anali watcheru, wotha kusintha, ndiponso waluso polalikira ndi kuphunzitsa

[Mawu Otsindika patsamba 31]

Yesu anachita zinthu zikuluzikulu zitatu zothandiza ophunzira ake: anapatsa aliyense mnzake woyenda naye, gawo lokalalikiramo, ndiponso anawauza uthenga woti akalalikire

[Zithunzi patsamba 28]

Chifukwa chotha kusintha, Paulo analalikira anthu osiyanasiyanya

[Chithunzi patsamba 30]

Atumiki ogwira mtima amaganizira za chikhalidwe cha omvera awo

[Chithunzi patsamba 31]

Atumiki opita patsogolo amathandiza anthu atsopano kukonzekera utumiki