Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za M’buku Lachiwiri la Mbiri

Mfundo Zazikulu za M’buku Lachiwiri la Mbiri

Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za M’buku Lachiwiri la Mbiri

BUKU lachiwiri la Mbiri limayamba ndi ulamuliro wa Solomo monga mfumu ya Israyeli ndipo limamaliza ndi mawu a Mfumu Koresi wa Perisiya amene analankhula kwa Ayuda, omwe anali akapolo ku Babulo. Mawuwo amati: ‘[Yehova] anandilangiza ndim’mangire nyumba m’Yerusalemu, ndiwo ku Yuda. Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Yehova Mulungu wake akhale naye, akwereko [ku Yerusalemu].’ (2 Mbiri 36:23) Amene analemba buku limeneli ndi Ezara ndipo anamaliza kulilemba mu 460 B.C.E. Bukuli likufotokoza zimene zinachitika pa zaka 500​—kuyambira mu 1037 B.C.E. mpaka mu 537 B.C.E.

Lamulo limene Koresi anapereka linathandiza kuti Ayuda abwerere ku Yerusalemu ndi kuyambiranso kulambira Yehova kumeneko. Komabe, zaka zambiri zimene anakhala akapolo ku Babulo zinali ndi mavuto ake. Akapolo amene anabwerera kwawo sanali kudziwa mbiri ya mtundu wawo. Choncho, buku lachiwiri la Mbiri linawafotokozera bwino lomwe mwachidule zimene zinachitika pamene mafumu a mzera wa Davide anali kulamulira. Ifenso nkhani imeneyi ikutikhudza chifukwa imasonyeza madalitso amene munthu amapeza pomvera Mulungu woona komanso mavuto amene amabwera chifukwa cha kusamvera Mulungu.

MFUMU IMANGIRA YEHOVA NYUMBA

(2 Mbiri 1:1–9:31)

Yehova akupatsa Mfumu Solomo zimene mfumuyo inapempha kuchokera pansi pa mtima​—nzeru ndi kudziwa​—limodzi ndi chuma ndi ulemerero. Mfumuyo imangira Yehova nyumba yokongola ku Yerusalemu, ndipo anthu “akusekera ndi kukondwera m’mtima mwawo.” (2 Mbiri 7:10) Solomo ‘aposa mafumu onse a padziko lapansi, kunena za chuma ndi nzeru.’​—2 Mbiri 9:22.

Atalamulira Israyeli zaka 40, Solomo ‘agona pamodzi ndi makolo ake, ndipo Rehabiamu mwana wake akhala mfumu m’malo mwake.’ (2 Mbiri 9:31) Ezara sakufotokoza za kupatuka kwa Solomo kusiya kulambira koona. Zolakwa zokha zimene akutchula, zimene mfumu inachita, ndizo kugula kwake akavalo ambiri ku Igupto ndi ukwati wake ndi mwana wa Farao. Mwa kuchita zimenezi, wolemba mbiri ameneyu akufotokoza nkhani yake yonseyi m’njira yolimbikitsa kwambiri.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

2:14—N’chifukwa chiyani mbadwo wa mmisiri amene akutchulidwa pano ukusiyana ndi uja umene uli pa 1 Mafumu 7:14? Buku loyamba la Mafumu limanena kuti amayi a mmisiri ameneyu anali “mkazi wamasiye wa fuko la Nafitali” chifukwa chakuti anali atakwatiwa ndi mwamuna wa fuko limenelo. Koma mkaziyo anali wa fuko la Dani. Mwamuna wake atamwalira, mkaziyo anakwatiwa ndi mwamuna wa ku Turo, ndipo anabereka naye mmisiriyo.

2:18; 8:10—Mavesi amenewa amati chiwerengero cha akuluakulu amene anali oyang’anira ndi akapitawo a anthu ogwira ntchito chinali 3,600 ndiponso 250, pamene malinga ndi 1 Mafumu 5:16; 9:23, iwo anali 3,300 ndiponso 550. N’chifukwa chiyani pali kusiyana? Pali kusiyana mwina chifukwa cha mmene maguluwo anawagawira. Mwina buku lachiwiri la Mbiri likusiyanitsa akapitawo 3,600 amene sanali Aisrayeli ndi akapitawo 250 amene anali Aisrayeli, pamene buku loyamba la Mafumu likusiyanitsa akapitawo 3,300 ndi akapitawo aakulu 550. Mulimonsemo, onse amene anali akapitawo anali 3,850.

4:2-4—N’chifukwa chiyani anagwiritsa ntchito chizindikiro cha ng’ombe pomanga poika thawale lamkuwa? M’Malemba ng’ombe ndi chizindikiro cha mphamvu. (Ezekieli 1:10; Chivumbulutso 4:6, 7) M’pake kuti anagwiritsa ntchito chizindikiro cha ng’ombe chifukwa ng’ombe zonse 12 zamkuwa zinanyamula “thawale” lalikulu, lolemera matani 30. Kupanga ng’ombe kuti zigwire ntchito imeneyi sikunaswe lamulo lachiwiri, limene linaletsa kupanga mafano opembedza.​—Eksodo 20:4, 5.

4:5—Kodi m’thawale lamkuwa lonse munkalowa madzi ochuluka motani? Likadzaza lonse, thawalelo limatha kulowa madzi a mitsuko yaikulu zikwi zitatu, kapena pafupifupi malita 66,000. Koma kambiri, mumalowa madzi okwanira zigawo ziwiri mwa zitatu za kukula kwake. Lemba la 1 Mafumu 7:26 limati: “[M’thawalemo] analowamo madzi a mitsuko yaikulu zikwi ziwiri [malita 44,000].”

5:4, 5, 10—Kodi ndi zipangizo zotani za m’chihema zimene zinaikidwa m’kachisi wa Solomo? Chinthu chokha chimene chinali m’chihema chokumanako chimene anachisunga m’kachisi wa Solomo ndi Likasa. Atamanga kachisiyo, chihema anachitenga ku Gibeoni kubwera nacho ku Yerusalemu ndipo zikuoneka kuti anachisunga kumeneko.​—2 Mbiri 1:3, 4.

Zimene Tikuphunzirapo:

1:11, 12. Pempho la Solomo linasonyeza Yehova kuti zimene mfumuyo inafuna kwambiri mu mtima mwake ndi kupeza nzeru ndi kudziwa. Inde, mapemphero athu kwa Mulungu amavumbula zimene mtima wathu umakonda. Ndiye ndi bwino kuganizira mofatsa za zimene timanena m’mapemphero athuwo.

6:4. Chifukwa choyamikira kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova ndi ubwino wake, tiyenera kulemekeza Yehova​—kutanthauza, kum’tamanda ndi mtima wonse ndi chiyamiko.

6:18-21. Ngakhale kuti Mulungu sangakhale m’nyumba iliyonse, kachisiyo anali malo olambirirako Yehova. Masiku ano, Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova ndi malo olambirira Mulungu woona m’dera lililonse mmene zili.

6:19, 22, 32. Zinali zotheka aliyense kufika kwa Yehova​—kuyambira mfumu mpaka anthu otsika kwambiri pa mtunduwo​—ngakhalenso akunja amene anapemphera kwa Yehova ndi mtima wonse. *​—Salmo 65:2.

MAFUMU A MZERA WA DAVIDE

(2 Mbiri 10:1–36:23)

Ufumu umodzi wa Israyeli ugawika pawiri kukhala ufumu wa Israyeli wakumpoto wa mafuko khumi ndi ufumu wakumwera wa mafuko awiri, la Yuda ndi la Benjamini. Ansembe ndi Alevi mu Israyeli yense akhala okhulupirika pa pangano la Ufumu m’malo mokonda dziko lawo, ndipo akhala kumbali ya Rehabiamu, mwana wa Solomo. Kupitirira pang’ono zaka 30 kuchokera pamene anamalizidwa, kachisi afunkhidwa chuma chake.

Pa mafumu 19 omwe anabwera pambuyo pa Rehabiamu, 5 anali okhulupirika, 3 anayamba bwino koma anakhala osakhulupirika, ndipo mfumu imodzi inasiya njira yake yoipa. Olamulira ena onse anachita zoipa pamaso pa Yehova. * Ntchito za mafumu asanu amene anakhulupirira Yehova zikufotokozedwa. Nkhani yakuti Hezekiya anayambitsanso ntchito za pakachisi ndi yakuti Yosiya anakonza phwando lalikulu la Paskha ziyenera kuti zinawalimbikitsa kwambiri Ayuda amene anafuna kukayambiranso kulambira Yehova ku Yerusalemu.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

13:5—Kodi mawu akuti “pangano la mchere” amatanthauza chiyani? Popeza kuti mchere uli ndi mphamvu yoteteza zinthu, unakhala chizindikiro cha zinthu zachikhalire ndi zosasinthika. Choncho, “pangano la mchere” likutanthauza pangano losasweka.

14:2-5; 15:17—Kodi Mfumu Asa anachotsa “misanje” yonse? Zikuoneka kuti sanatero. N’kutheka kuti Asa anangochotsa misanje imene anthu analambirirapo milungu yonyenga koma sanachotse imene analambirirapo Yehova. N’kuthekanso kuti misanjeyo inamangidwanso chakumapeto kwa ulamuliro wa Asa. Misanje imeneyi anaichotsa Yehosafati mwana wake. Ndipotu, misanje sinatheretu, ngakhale mu ulamuliro wa Yehosafati.​—2 Mbiri 17:5, 6; 20:31-33.

15:9; 34:6—Kodi fuko la Simeoni linakhala mbali iti pamene ufumu wa Israyeli unagawika? Popeza kuti fuko la Simeoni linalandira monga cholowa chawo mizinda yosiyanasiyana m’dera la Yuda, malo awo anali mu ufumu wa Yuda ndi Benjamini. (Yoswa 19:1) Koma pa zachipembedzo ndi zandale, fuko limeneli linali kumbali ya ufumu wakumpoto. (1 Mafumu 11:30-33; 12:20-24) N’chifukwa chake, Simeoni anawerengeredwa pamodzi ndi ufumu wa mafuko khumi.

35:3—Kodi pamene Yosiya anabweretsa Likasa lopatulika m’kachisi analichotsa kuti? Baibulo silinena ngati papitapo mmodzi wa mafumu oipa analichotsa Likasa m’kachisimo kapena ngati Yosiya anangolitenga n’kukalisunga kwinakwake pamene ntchito yaikulu yokonza kachisi inayamba. Nthawi yokha imene Likasa linatchulidwa atadutsa masiku a Solomo ndi pamene Yosiya analibweretsa m’kachisimo.

Zimene Tikuphunzirapo:

13:13-18; 14:11, 12; 32:9-23. Tikuphunzirapo mfundo yofunika kwambiri yakuti tizidalira Yehova.

16:1-5, 7; 18:1-3, 28-32; 21:4-6; 22:10-12; 28:16-22. Kugwirizana ndi akunja kapena anthu osakhulupirira kuli ndi mavuto ake oopsa. Ndi bwino kupeweratu kugwirizana ndi dziko pamene tikufunikadi kutero.​—Yohane 17:14, 16; Yakobo 4:4.

16:7-12; 26:16-21; 32:25, 26. Chifukwa chodzikuza, Mfumu Asa sanachite bwino zaka zomalizira za moyo wake. Uziya anagwa chifukwa cha mzimu wodzikuza. Hezekiya sanachite mwanzeru ndipo zikuoneka kuti ananyada pamene anaonetsa nthumwi za Babulo chuma chake. (Yesaya 39:1-7) Baibulo limachenjeza kuti: “Kunyada kutsogolera [ku] kuwonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera [ku] kupunthwa.”​—Miyambo 16:18.

16:9. Yehova amathandiza anthu amene mtima wawo uli wangwiro kulinga kwa iye, ndipo iye mofunitsitsa amafuna kugwiritsa ntchito mphamvu zake kuwathandiza.

18:12, 13, 23, 24, 27. Mofanana ndi Mikaya, tiyenera kukhala olimba mtima polankhula za Yehova ndi zolinga zake.

19:1-3. Yehova amafunafuna zabwino mwa ife ngakhale tikam’kwiyitsa.

20:1-28. Tili ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzatilola kuti tim’peze tikatembenukira kwa iye kuti atitsogolere.​—Miyambo 15:29.

20:17. Kuti ‘tipenye chipulumutso cha Yehova,’ tikufunika ‘kuchirimika’ mwa kuchirikiza mwachangu Ufumu wa Mulungu. M’malo mochita zinthu mwa ife tokha, tiyenera ‘kuima,’ kutanthauza kuika chidaliro chathu chonse mwa Yehova.

24:17-19; 25:14. Kupembedza mafano kunali msampha kwa Yoasi ndi mwana wake Amaziya. Masiku ano, kupembedza mafano kungakhalenso kokopa, makamaka ngati kukuchitika m’njira zovuta kuzizindikira monga kusirira kapena kukonda dziko.​—Akolose 3:5; Chivumbulutso 13:4.

32:6, 7Ifenso tiyenera kukhala olimba mtima pamene ‘tavala zida zonse za Mulungu” ndi kumenya nkhondo yauzimu.​—Aefeso 6:11-18.

33:2-9, 12, 13, 15, 16. Munthu amasonyeza kuti walapa zenizeni mwa kusiya njira yake yoipa ndi kuyesetsa kuchita chabwino. Ngakhale munthu amene wachita zoipa ngati Mfumu Manase angachitidwe chifundo ndi Yehova ngati walapa zenizeni.

34:1-3. Mavuto alionse amene tinakumana nawo tili ana sayenera kutilepheretsa kum’dziwa Mulungu ndi kum’tumikira. Mwina amene analimbikitsa Yosiya ali mwana anali agogo ake olapa, a Manase. Chilimbikitso chilichonse chimene Yosiya analandira chinathandiza patapita nthawi. Ifenso zimenezi zingatichitikire.

36:15-17. Yehova ali wachifundo ndi woleza mtima. Koma chifundo chake ndi kuleza mtima kwake zili ndi malire. Kuti anthu adzapulumuke pamene Yehova awononga dziko loipa lino, iwo afunika kulabadira ntchito yolalikira Ufumu.

36:17, 22, 23. Nthawi zonse mawu a Yehova amakhala oona.​—1 Mafumu 9:7, 8; Yeremiya 25:9-11.

Anakhudzidwa Mtima ndi Buku

Lemba la 2 Mbiri 34:33 limati: “Yosiya nachotsa zonyansa zonse m’mayiko onse okhala a ana a Israyeli, natumikiritsa onse opezeka m’Israyeli, inde kutumikira Yehova Mulungu wawo.” Kodi chinalimbikitsa Yosiya kuchita zimenezi n’chiyani? Pamene Safani, mlembi, anabweretsa kwa Mfumu Yosiya buku la Chilamulo cha Yehova limene anali atangolipeza kumene, mfumuyo inam’pempha kuti aliwerenge mokweza. Zimene Yosiya anamva zinam’khudza mtima kwambiri moti analimbikitsa kulambira koyera moyo wake wonse.

Ngati tiwerenga Mawu a Mulungu ndi kuwasinkhasinkha, akhoza kutikhudza mtima kwambiri. Kodi kusinkhasinkha nkhani za mafumu a mzera wa Davide si kotilimbikitsa kutengera zitsanzo za mafumu amene anakhulupirira Yehova ndi kupewa khalidwe la amene sanam’khulupirire? Buku lachiwiri la Mbiri limatilimbikitsa kulambira Mulungu yekha woona ndi kukhala okhulupirika kwa iye. Ndithudi, uthenga wake uli wamoyo ndiponso wamphamvu.​—Ahebri 4:12.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Za mafunso okhudza kuperekedwa kwa kachisi ndi mfundo zina zimene pemphero la Solomo panthawi imeneyo likutiphunzitsa, onani Nsanja ya Olonda ya July 1, 2005, masamba 28 mpaka 31.

^ ndime 1 Ngati mukufuna kuona mndandanda wa mafumu a Yuda malinga ndi nthawi imene analamulira, onani Nsanja ya Olonda ya August 1, 2005, tsamba 12.

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi mumadziwa chifukwa chake ng’ombe zinali chizindikiro choyenera kuikapo thawale lamkuwa?

[Zithunzi patsamba 21]

Ngakhale anali ochepa amene anam’thandiza ali mwana, Yosiya anakula n’kukhala wokhulupirika kwa Yehova