Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse”

“Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse”

“Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse”

KALI pamwambapa ndi kabuku kamene kanatuluka pa Misonkhano Yachigawo ya Mboni za Yehova ya 2004 ndi 2005 yakuti “Yendani ndi Mulungu.” Mtundu wake wina ndi wa kabuku ka masamba 32 kamene kali ndi uthenga wachidule m’zinenero 29, kuyambira Chiafirikana mpaka Chizulu. Zotsatirazi zikusonyeza zimene zingachitike pamene kabuku kameneka kagwiritsidwa ntchito.

• Atalandira kabuku kameneka pamsonkhano, banja lina la Mboni linapita kukaona malo a boma atatu oteteza zachilengedwe. Ali kumeneko anakumana ndi anthu a ku India, Netherlands, Pakistan, ndi Philippines. Mbale anati: “Ngakhale kuti anthu onsewa analankhula Chingelezi, anachita chidwi ataona uthengawo m’chinenero chawo, si nanga anali kutali kwambiri ndi kwawo. Iwo anazindikira kuti ntchito yathu ikuchitika padziko lonse lapansi komanso kuti ndife ogwirizana.”

• Mboni ina inasonyeza mnzake kuntchito kabuku kameneka. Mnzakeyo amachokera ku India. Anasangalala kuona zinenero zonse zimene zilimo ndipo anawerenga uthengawo m’chinenero chake. Chifukwa cha zimenezi, anakambirana zambiri zokhudza Baibulo. Mnzakenso wina kuntchito komweko wa ku Philippines anadabwa kupeza chinenero chakwawo m’kabukuko ndipo anafuna kudziwa zambiri zokhudza Mboni za Yehova.

• Ku Canada, mayi wina wa ku Nepal anavomera kuti aziphunzira Baibulo ndi Mboni pafoni koma sanafune kuitana mlongo kunyumba kwake. Koma pamene Mboniyo inauza mayi ameneyo za kabuku kamene muli chinenero cha Chinepali, mayiyo mosangalala anapempha mlongoyo kupita kunyumba kwake. Anafuna kudzionera yekha uthengawo m’chinenero chakwawo! Kuyambira nthawi imeneyo, akhala akuphunzirira Baibulo kunyumba kwa mayiyo.