Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ino Ndi Nthawi Yofunika Kuchitapo Kanthu Mwachangu

Ino Ndi Nthawi Yofunika Kuchitapo Kanthu Mwachangu

Ino Ndi Nthawi Yofunika Kuchitapo Kanthu Mwachangu

“Mukayikakayika kufikira liti?”​—1 MAFUMU 18:21.

1. N’chifukwa chiyani masiku athu ano ali osiyana kwambiri ndi kale?

KODI mumakhulupirira kuti Yehova ndiye Mulungu yekha woona? Ndiponso kodi mumakhulupirira kuti maulosi a m’Baibulo amanena kuti nthawi imene tikukhalayi ndi “masiku otsiriza” a dongosolo loipa la Satana? (2 Timoteo 3:1) Ngati mwayankha kuti mumakhulupirira, ndiye kuti mukuvomereza kuti lero, kuposa kalelonse, ndi nthawi yofunika kuchitapo kanthu mwachangu. Sizinachitikepo m’mbuyo monsemo kuti miyoyo yambiri choncho ikhale pachiswe ngati masiku ano.

2. Kodi chinali kuchitika n’chiyani mu ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi pamene Mfumu Ahabu inali kulamulira?

2 Zaka za m’ma 900 B.C.E., mtundu wa Israyeli unafunika kusankha pa nkhani yaikulu kwambiri. Nkhani yake inali yakuti: Kodi iwo adzatumikira ndani? Mfumu Ahabu, atasonkhezeredwa ndi mkazi wake wakunja, Yezebeli, analimbikitsa anthu kupembedza Baala mu ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi. Baala anali mulungu woona za kubereka ndipo anthu anali kukhulupirira kuti iye apatsa mvula ndi kubalitsa mbewu. N’kutheka kuti anthu ambiri opembedza Baala anali kupsompsona dzanja lawo kenako n’kukhala ngati akum’psompsonetsa dzanja lawolo kapena anali kugwadira fano la mulungu wawoyo. Pofuna kulimbikitsa Baala kuti adalitse mbewu ndi ziweto zawo, opembedza ake amakhala ndi mwambo wochita chiwerewere chosaneneka ndi mahule a pakachisi. Analinso ndi mwambo wodzitema ndi mipeni mpaka kuchucha magazi ambirimbiri.​—1 Mafumu 18:28.

3. Kodi kupembedza Baala kunakhudza bwanji anthu a Mulungu?

3 Aisrayeli ena pafupifupi 7,000 anakana kupembedza nawo mwa njira imeneyi ya mafano, chiwerewere, ndi chiwawa. (1 Mafumu 19:18) Iwo mokhulupirika anamamatira unansi wawo wa pangano ndi Yehova Mulungu, ndipo chifukwa cha zimenezi, anazunzidwa. Mwachitsanzo, Mfumukazi Yezebeli anapha aneneri a Yehova ambiri. (1 Mafumu 18:4, 13) Chifukwa cha mavuto amenewa, Aisrayeli ambiri anaphatikiza zipembedzo pofuna kukondweretsa Yehova ndi Baala. Koma Mwisrayeli akasiya Yehova n’kuyamba kupembedza mulungu wonama, umenewo unali kukhala mpatuko. Yehova analonjeza kuti adzawadalitsa Aisrayeliwo ngati iwo am’konda ndi kumvera malamulo ake. Ngakhale zili choncho, anawachenjeza kuti ngati iwo asiya kum’lambira iye yekha, adzawonongedwa.​—Deuteronomo 5:6-10; 28:15, 63.

4. Kodi Yesu ndi atumwi ake analosera kuti chidzachitika n’chiyani pakati pa Akristu, ndipo kodi zimenezi zakwaniritsidwa motani?

4 Ndi mmenenso zinthu zilili masiku ano m’Matchalitchi Achikristu. Anthu a matchalitchi amanena kuti ndi Akristu pamene zikondwerero zimene amachita, khalidwe lawo, ndi zimene amakhulupirira zimasemphana ndi ziphunzitso za Baibulo. Mofanana ndi Yezebeli, atsogoleri a Matchalitchi Achikristu amakhala patsogolo kuzunza Mboni za Yehova. Kuyambira kale n’kale, atsogoleri a Matchalitchi Achikristu achirikiza nkhondo ndipo aphetsa anthu awo mamiliyoni osawerengeka. Baibulo limanena kuti kugwirizana kwa zipembedzo ndi maboma a dziko mwa njira imeneyi n’kuchita chigololo chauzimu. (Chivumbulutso 18:2, 3) Ndiponso, Matchalitchi Achikristu nthawi zambiri alekerera chigololo chenicheni, ngakhale pakati pa atsogoleri ake. Yesu Kristu ndi atumwi ake analosera kuti kudzakhala mpatuko waukulu umenewu. (Mateyu 13:36-43; Machitidwe 20:29, 30; 2 Petro 2:1, 2) Kodi chidzachitikira anthu onse oposa wani biliyoni amene ali m’Matchalitchi Achikristu n’chiyani? Ndipo kodi olambira oona a Yehova ali ndi udindo wotani kwa anthu amenewa ndi ena onse amene chipembedzo chonyenga chawasocheretsa? Yankho lake timalipeza mwa kupenda nkhani yochititsa chidwi imene inachititsa kuti ‘awononge Baala m’Israyeli.’​—2 Mafumu 10:28.

Mmene Mulungu Ankakondera Anthu Ake Opulupudza

5. Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti anakonda anthu ake opulupudza?

5 Sikuti Yehova Mulungu amasangalala kulanga anthu amene akhala osakhulupirika kwa iye. Popeza kuti ndi Atate wachikondi, amafuna kuti oipa alape n’kubwerera kwa iye. (Ezekieli 18:32; 2 Petro 3:9) Umboni wa zimenezi n’ngwakuti Yehova anagwiritsa ntchito aneneri ambiri masiku a Ahabu ndi Yezebeli kuchenjeza anthu Ake za mavuto amene adzakumana nawo chifukwa chopembedza Baala. Mmodzi wa aneneriwo anali Eliya. Chitadutsa chilala choopsa chimene chinanenedweratu, Eliya anauza Mfumu Ahabu kusonkhanitsa Aisrayeli ndi aneneri a Baala pa phiri la Karimeli.​—1 Mafumu 18:1, 19.

6, 7. (a) Kodi Eliya anasonyeza bwanji gwero lenileni la mpatuko wa Israyeli? (b) Kodi aneneri a Baala anachita chiyani? (c) Kodi Eliya anachita chiyani?

6 Msonkhanowo unali pamalo pamene panali guwa la nsembe la Yehova limene ‘adaligumulalo,’ mwina pofuna kusangalatsa Yezebeli. (1 Mafumu 18:30) N’zomvetsa chisoni kuti Aisrayeli amene analipo sanali kudziwa kuti ndani pakati pa Yehova ndi Baala amene angathe kuwapatsa mvula imene anali kufuna kwambiri. Panali aneneri a Baala okwanira 450, pamene Eliya anali mneneri yekha woimira Yehova. Potchula vuto lawo, Eliya anafunsa anthuwo kuti: “Mukayikakayika kufikira liti?” Kenako mosapita m’mbali, anawapempha kuti iwo asankhe. Anati: “Ngati Yehova ndiye Mulungu, m’tsateni Iye; ngati Baala, mum’tsate iyeyo.” Pofuna kulimbikitsa Aisrayeli okayikakayikawo kuti azilambira Yehova yekha, Eliya ananena kuti achite mayeso oti aone kuti Mulungu woona ndani. Anati paphedwe ng’ombe ziwiri zamphongo azipereke nsembe, ina kwa Yehova ndi ina kwa Baala. Mulungu woona adzatentha ng’ombe yake ndi moto. Aneneri a Baala anakonza nsembe yawo, ndipo anayamba kufuula kwa maola ambiri kuti: “Baala, timvereni ife.” Eliya atayamba kuwaseka, iwo anadzitema ndi mipeni mpaka kuchucha magazi, ndipo anafuula mokwezadi mawu. Koma sanawayankhe.​—1 Mafumu 18:21, 26-29.

7 Ndiye zinali kwa Eliya tsopano. Poyamba, anakonza guwa la nsembe la Yehova ndipo anaikapo zidutswa za ng’ombe ija. Kenako, analamula kuti athire nsembeyo mbiya zinayi zazikulu za madzi. Anachita zimenezi katatu mpaka mchera umene unazungulira guwa la nsembelo unadzaza madzi. Pamenepo, Eliya anapemphera kuti: “Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isake ndi Israyeli, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israyeli, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mawu anu ndachita zonsezi. Ndimvereni Yehova, ndimvereni, kuti anthu awa adziwe kuti Inu Yehova ndinu Mulungu, ndi kuti Inu mwabwezanso mitima yawo.”​—1 Mafumu 18:30-37.

8. Kodi Mulungu analiyankha motani pemphero la Eliya, nanga mneneriyo anachita chiyani?

8 Mulungu woona anayankha mwa kutentha nsembeyo ndi guwa lake ndi moto wochokera kumwamba. Mpaka motowo unaphwetsa madzi omwe anali mu mchera wozungulira guwa la nsembe! Muganiza Aisrayeli anatani? ‘Anagwa nkhope zawo pansi, nati, Yehova ndiye Mulungu [woona], Yehova ndiye Mulungu [woona].’ Zitatero, Eliya sanazengerezenso. Analamula Aisrayeli kuti: “Gwirani aneneri a Baala, asapulumuke ndi mmodzi yense.” Aneneri onse a Baala okwanira 450 anawaphera m’munsi mwa phiri la Karimeli.​—1 Mafumu 18:30-42.

9. Kodi olambira oona anayesedwabe motani?

9 Tsiku losaiwalika limenelo, Yehova anavumbitsa mvula kwa nthawi yoyamba patadutsa zaka zitatu ndi theka. (Yakobo 5:17, 18) Kaya Aisrayeli anali kukambirana zotani pamene anali kubwerera kwawo, Yehova anali atatsimikiza kuti iye ndiye Mulungu woona. Koma olambira Baala sanasiyirepo msanga. Yezebeli anapitiriza chiwembu chake chozunza atumiki a Yehova. (1 Mafumu 19:1, 2; 21:11-16) Choncho, anthu a Mulungu anayesedwanso pa kukhulupirika kwawo. Kodi iwo adzakhala akulambirabe Yehova yekha likadzafika tsiku lopereka chiweruzo pa olambira Baala?

Chitanipo Kanthu Mwachangu Panopo

10. (a) Nthawi zamakono, kodi Akristu odzozedwa akhala akuchita chiyani? (b) Kodi kumvera lamulo lopezeka pa Chivumbulutso 18:4 kumatanthauza chiyani?

10 Nthawi zamakono, Akristu odzozedwa akhala akuchita ntchito yonga ya Eliya. Mwa kugwiritsa ntchito mawu apakamwa ndi olembedwa, iwo akhala akuchenjeza anthu amitundu yonse, amene ali m’Matchalitchi Achikristu ndi amene ali kunja, za kuipa kwa chipembedzo chonyenga. Ndipo anthu mamiliyoni achitapo kanthu mwachangu kuchoka m’chipembedzo chonyenga. Apereka moyo wawo kwa Yehova ndipo abatizidwa kukhala ophunzira a Yesu Kristu. Inde, iwo alabadira zimene Mulungu walamula zofuna changu zokhudzana ndi chipembedzo chonyenga. Iye akuti: “Tulukani mmenemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake.”​—Chivumbulutso 18:4.

11. Kodi chofunika n’chiyani kuti anthu ayanjidwe ndi Yehova?

11 Anthu ena mamiliyoni ambiri akukayikakayika kuti atani, ngakhale kuti amachita chidwi ndi uthenga wa m’Baibulo umene Mboni za Yehova zimafalitsa. Ena a iwo amabwera nthawi zina pamisonkhano yachikristu, monga pa mwambo wa Mgonero wa Ambuye kapena pamsonkhano wachigawo. Tikuwalimbikitsa onsewo kuganizira mofatsa zimene Eliya ananena kuti: “Mukayikakayika kufikira liti?” (1 Mafumu 18:21) M’malo mozengereza, afunikira kuchitapo kanthu mwachangu panopo ndi kulimbikira kuti adzipereke ndi kubatizidwa kukhala olambira Yehova. Mpata umene ali nawo woti apeze moyo wosatha watsala pang’ono kutha!​—2 Atesalonika 1:6-9.

12. Kodi Akristu ena obatizidwa ali poopsa motani, ndipo ayenera kuchita chiyani?

12 N’zomvetsa chisoni kuti Akristu ena obatizidwa ayamba kusakhazikika pa kulambira kwawo ngakhale kusiya kumene. (Ahebri 10:23-25; 13:15, 16) Ena changu chawo chazilala chifukwa cha kuopa kuzunzidwa, nkhawa yopeza zofunika pa moyo, kufunafuna chuma kuti alemere, kapena kufuna kusangalala kuti akhutiritse dyera lawo. Yesu anachenjeza kuti otsatira ake ena adzakhumudwa, kutsamwa, ndi kukodwa mu msampha ndi zinthu zimenezi. (Mateyu 10:28-33; 13:20-22; Luka 12:22-31; 21:34-36) M’malo ‘mokayikakayika,’ titero kunena kwake, anthu amenewo ayenera ‘kuchita changu, natembenuke mtima’ mwa kuonetsetsa kuti akukwaniritsa kudzipereka kwawo kwa Mulungu.​—Chivumbulutso 3:15-19.

Mapeto Odzidzimutsa a Chipembedzo Chonyenga

13. Fotokozani mmene zinthu zinalili mu Israyeli nthawi imene Yehu anadzozedwa kukhala mfumu.

13 Chifukwa chimene anthu ayenera kuchitirapo kanthu mwachangu panopo ndi zimene zinachitika mu Israyeli patadutsa zaka pafupifupi 18 kuchokera pamene nkhani yakuti kodi Mulungu woona ndani inathetsedwa pa phiri la Karimeli. Tsiku la Yehova loweruza olambira Baala linafika modzidzimutsa panthawi imene Elisa anali mneneri. Iye ndiye anatenga malo a Eliya. Nthawi imeneyo amene anali kulamulira Israyeli ndi Yoramu mwana wa Mfumu Ahabu, ndipo Yezebeli anali adakali moyo monga mayi wa mfumu. Mwachinsinsi, Elisa anatuma mnyamata wake kukadzoza Yehu, mkulu wa asilikali a Israyeli, kukhala mfumu. Apo n’kuti Yehu ali tsidya lina la Yordano kum’mawa, ku Ramoti Gileadi, kutsogolera nkhondo pakati pa Israyeli ndi adani ake. Mfumu Yoramu anali ku Yezreeli kuchigwa, pafupi ndi Megido, kumene anali kudikirira kuti mabala ake amene anam’pweteka kunkhondo apole.​—2 Mafumu 8:29–9:4.

14, 15. Kodi Yehu anapatsidwa ntchito yanji, ndipo anatani?

14 Nazi zimene Yehova analamula Yehu kuchita: ‘Kantha nyumba ya Ahabu mbuye wako, kuti ndibwezere chilango cha mwazi wa atumiki anga aneneri, ndi mwazi wa atumiki onse a Yehova, dzanja la Yezebeli. Popeza nyumba yonse ya Ahabu idzawonongeka . . . Agalu adzamudya Yezebeli pa dera la Yezreeli, wopanda wina wakumuika.”​—2 Mafumu 9:7-10.

15 Yehu anali munthu wachangu kwambiri. Iye msangamsanga anakwera galeta lake n’kulikutumula liwiro kupita ku Yezreeli. Kumeneko, mlonda anazindikira Yehu chifukwa cha mmene anayendetsera galeta lakelo ndipo anauza Mfumu Yoramu. Yoramu atamva zimenezo, anakwera galeta lake napita kukakumana ndi mkulu wa asilikali akeyo. Atakumana, Yoramu anafunsa Yehuyo kuti: “Mtendere kodi, Yehu?” Koma Yehu anayankha kuti: “Ngwanji mtendere pokhala chachuluka chigololo ndi nyanga zake za mayi wako Yezebeli?” Ndiye, Mfumu Yoramu isanathawe, Yehu anakoka uta wake ndi kupha Yoramu ndi muvi umene unapyoza pamtima pake.​—2 Mafumu 9:20-24.

16. (a) Kodi nduna za Yezebeli za m’bwalo la mfumu mosayembekezera zinayang’anizana ndi nkhani yotani? (b) Kodi mawu a Yehova okhudza Yezebeli anakwaniritsidwa bwanji?

16 Popanda kuzengereza, Yehu analikumba liwiro pagaleta lake kupita ku mzindawo. Yezebeli anali atadzikongoletsa koopsa, ndipo akusuzumira pansi ali pazenera, analandira Yehu ndi mawu omuopseza. Koma Yehu anachita ngati sakumva, ndipo anaitana oti amuthandize. Anati: “Ali ndi ine ndani? Ndani?” Apa adindo a Yezebeli anafunika kuchita chamuna. Nduna ziwiri kapena zitatu za m’bwalo la mfumu zinatulutsa mitu yawo pazenera. Pamenepo, iwo anafunika kuonetsa kuti ali mbali ya ndani. Yehu analamula kuti: “M’gwetsereni pansi.” Ndunazo zinam’ponyera pansi Yezebeli mumsewu, ndipo akavalo ndi galeta la Yehu anam’pondaponda. Ndi mmenetu anathera Yezebeli wolimbikitsa kulambira Baala mu Israyeli. Ndipo m’pake kuti zinatero! Ataganiza zoti akamuike, anapeza agalu atamudya minofu yonse, ndendende ndi mmene ulosi unanenera.​—2 Mafumu 9:30-37.

17. Kodi chiweruzo cha Mulungu pa Yezebeli chiyenera kulimbitsa chikhulupiriro chathu pa zochitika ziti za m’tsogolo?

17 Ndi mmenenso adzathera modzidzimutsa mkazi wachigololo wophiphiritsa, dzina lake ‘Babulo Wamkulu.’ Mkazi wachigololo ameneyu akuimira zipembedzo zonyenga za dziko la Satana, zimene gwero lawo ndi mzinda wamakedzana wa Babulo. Chipembedzo chonyenga chitathetsedwa, Yehova Mulungu adzatembenukira anthu amene amapanga mbali yotsala ya dziko la Satana. Awanso adzawonongedwa, kukonzekera dziko latsopano lolungama.​—Chivumbulutso 17:3-6; 19:19-21; 21:1-4.

18. Kodi chinachitika n’chiyani kwa olambira Baala mu Israyeli Yezebeli atamwalira?

18 Yezebeli atamwalira, Mfumu Yehu sanazengereze kupha mbadwa zonse za Ahabu ndi akuluakulu amene anali kumbali yake. (2 Mafumu 10:11) Koma munatsalabe Aisrayeli ambiri olambira Baala m’dzikomo. Pa amenewa, Yehu anachitapo kanthu mwachamuna kusonyeza ‘changu chake cha kwa Yehova.’ (2 Mafumu 10:16) Ponamizira kukhala wolambira Baala, Yehu anakonza phwando lalikulu kukachisi wa Baala amene anamangidwa ndi Ahabu ku Samariya. Olambira Baala onse mu Israyeli anafika kuphwando limeneli. Atawatsekera m’kati, onse anaphedwa ndi anyamata a Yehu. Pomaliza nkhani imeneyi, Baibulo limati: “Momwemo Yehu anawononga Baala m’Israyeli.”​—2 Mafumu 10:18-28.

19. Kodi ndi zinthu zosangalatsa zotani zimene likuyembekezera “khamu lalikulu” la anthu okhulupirika olambira Yehova?

19 Kulambira Baala kunathetsedwa mu Israyeli. Zipembedzo zonyenga za dziko lino zidzathanso chimodzimodzi modzidzimutsa moti anthu adzangoti kukamwa yasa! kudabwa. Kodi inu mudzakhala mbali ya ndani tsiku lalikulu limenelo lopereka chiweruzo? Chitanipo kanthu mwachangu panopo, kuti kapena mungadzapeze mwayi wokhala pakati pa “khamu lalikulu” la anthu opulumuka “chisautso chachikulu.” Ndiye mudzati mukakumbukira, mudzasangalala ndipo mudzatamanda Mulungu chifukwa choweruza “mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake.” Mutagwirizana ndi olambira anzanu oona, mudzavomerezana ndi mawu osangalatsa oimbidwa kumwamba akuti: “Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.”​—Chivumbulutso 7:9, 10, 14; 19:1, 2, 6.

Mafunso Ofuna Kusinkhasinkha

• Kodi zinatheka bwanji kuti Israyeli wakale apezeke ndi mlandu wolambira Baala?

• Kodi Baibulo linalosera za mpatuko waukulu uti, ndipo ulosi umenewo wakwaniritsidwa motani?

• Kodi Yehu anathetsa bwanji kulambira Baala?

• Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipulumuke tsiku la Mulungu lopereka chiweruzo?

[Mafunso]

[Mapu patsamba 25]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Soko

Afeki

Helikati

Yokineamu

Megido

Taanaki

Dotana

SAMARIYA

Eni-doro

Sunemu

Ofira

Yezreeli

Ibleamu (Gati-rimoni)

Tiriza

Betesemesi

Betiseani (Betisani)

Yabesi-gileadi?

Abelemehola

Betaribeli

Ramoti-gileadi

Pamwamba pa Mapiri

Phiri la Karimeli

Phiri la Tabori

More

Phiri la Giliboa

[Nyanja]

Nyanja ya Mediterranean

Nyanja ya Galileya

[Mtsinje]

Mtsinje ya Yordano

[Kasupe ndi Chitsime]

Chitsime cha Harodi

[Mawu a Chithunzi]

Based on maps copyrighted by Pictorial Archive (Near Eastern History) Est. and Survey of Israel

[Zithunzi patsamba 26]

Kulalikira za Ufumu nthawi zonse ndi kupezeka pa misonkhano yachikristu n’zofunika kwambiri pa kulambira koona

[Chithunzi pamasamba 28, 29]

Mofanana ndi Yehu, onse amene akufuna kupulumuka tsiku la Yehova ayenera kuchitapo kanthu mwachangu