Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

N’chifukwa chiyani tchimo loyamba, kusamvera kwa Adamu, tingaliyerekezere ndi matenda otengera kwa makolo?

Lili ngati matenda chifukwa Adamu anapatsira uchimo kwa ana ake. Chotero tinabadwa ndi chilema cha uchimo, monga momwe ana ena amatengera nthenda kuchokera kwa makolo awo.​—8/15, tsamba 5. 

Kodi chiwawa masiku ano chikuchuluka chifukwa chiyani makamaka?

Satana akufuna kuti tisamagwirizane ndi Yehova mwa kuika zachiwawa m’mitima yathu. Amachita zimenezi kudzera m’mafilimu, nyimbo, ndi masewera a pakompyuta amene amalimbikitsa osewerawo kuchitira anzawo nkhanza zosaneneka kapena kuwapha. Chiwawa cha pa TV, m’mabuku ndi m’mafilimu chapangitsa anthu kuchita zachiwawa zambiri.​—9/1, tsamba 29.

Kodi Pontiyo Pilato anali ndani?

Iye anali Mroma wochokera ku banja lodziwikako ndipo akuoneka kuti anali msilikali. Tiberiyo, mfumu ya Roma, anasankha Pilato kukhala bwanamkubwa wa chigawo cha Yudeya m’chaka cha 26 C.E. Panthawi yozenga mlandu wa Yesu, Pilato anamva milandu imene atsogoleri achiyuda anamuimba. Kuti asangalatse anthu, anavomereza kuti Yesu aphedwe.​—9/15, masamba 10-12.

Kodi “chizindikiro” chotchulidwa pa Mateyu 24:3 n’chiyani?

Chizindikiro chimenechi chili ndi mbali zingapo. Chimaphatikizapo nkhondo, njala, mliri, ndi zivomezi, ndipo chidzathandiza otsatira a Yesu kuzindikira kukhalapo kwake ndiponso “mathedwe a nthawi ya pansi pano.”​—10/1, masamba 4-5.

M’nthawi ya atumwi, kodi Ayuda ankakhala m’madera ati kunja kwa Palesitina?

M’nthawi ya atumwi, madera aakulu amene Ayuda ankakhala anali Suriya, Asiyamina, Babulo, ndi Igupto ndipo Ayuda ena ochepa ankakhala m’mbali za Ulaya za Ufumu wa Roma.​—10/15, tsamba 12.

Kodi Mkristu angakhale ndi chikumbumtima chabwino ngati avomera ntchito yogwiritsa ntchito zida?

Zili kwa munthu kuvomera kapena kukana ntchito yomwe imafuna kuti munthu azinyamula mfuti kapena chida china chilichonse. Komabe, ntchito yofunika kunyamula chida imaika munthu pangozi yokhala ndi mlandu wa mwazi ngati patafunika kugwiritsa ntchito chidacho. Ndipo munthuyo amadziika pangozi yovulazidwa kapena kuphedwa ndi anthu ena pofuna kudziteteza. Mkristu wotero sangayenerere kutumikira pambali iliyonse yapadera mumpingo. (1 Timoteo 3:3, 10)​—11/1, tsamba 31.

Popeza kuti liwu loti “Armagedo” limachokera ku liwu loti “Phiri la Megido,” kodi nkhondo ya Armagedo idzachitikira pa phiri linalake ku Middle East?

Ayi. Kulibe phiri la Megido, kuli chabe chitunda chotalika kuposa chigwa chomwe chili pafupi ku Israyeli. Malo amenewa ndi ochepa kwambiri kuti “mafumu [onse] a dziko, ndi magulu a nkhondo awo” asonkhanepo. Nkhondo yaikulu ya Mulungu idzachitika padziko lonse lapansi, ndipo idzathetsa nkhondo zonse. (Chivumbulutso 16:14, 16; 19:19; Salmo 46:8, 9)​—12/1, masamba 4-7.