Kodi Nyengo ya Tchuthi Idzakwaniritsa Zokhumba Zanu Zonse?
Kodi Nyengo ya Tchuthi Idzakwaniritsa Zokhumba Zanu Zonse?
Buku lakuti Peter the Great—His Life and World limati: “Peter [Wamkulu] analamula kuti pa January 1, mu matchalitchi onse muchitike mapemphero apadera pokondwerera Chaka Chatsopano. Komanso, analamula kuti anthu agwiritse ntchito nthambi za mitengo yosayoyola masamba pokongoletsa mphuthu za m’kati mwa nyumba, ndipo analamula nzika zonse za ku Moscow kuti ‘zisonyeze kusangalala kwawo mwa kukuwirana mawu ofunirana’ zabwino pa tsiku lokondwerera Chaka Chatsopano.”
KODI inuyo mukuyembekezera zotani panthawi yomwe anthu ambiri amati ndi nyengo ya tchuthi? Padziko lonse lapansi, anthu amati nkhani yaikulu panyengoyi ndi ya Khirisimasi, tsiku limene kwa nthawi yaitali anthu amati ndi limene Kristu anabadwa. Koma panyengoyi anthu amakondwereranso Chaka Chatsopano. Motero tchuthi chimenechi chimakhala chachitali kwambiri. Panthawiyi, makolo ndi ana omwe amatha kukhala patchuthi, motero imaoneka kuti ndi nthawi yabwino kwambiri yoti mabanja akhale pansi ndi kucheza. Koma ena amatchula nyengo imeneyi kuti “nyengo ya Khirisimasi,” chifukwa chakuti panyengo imeneyi iwo amafuna kulemekeza Kristu. Mwina nanunso mumaona kuti imeneyi ndiyo nkhani yofunika kwambiri panyengoyi.
Kaya cholinga chake ndicho kulemekeza Kristu, kucheza ndi banja lawo, kapena zonse ziwirizi, amuna, akazi, ndi ana ambiri sagona tulo kuyembekezera nthawi imeneyi. Nanga bwanji chaka chino? Kodi nthawi imeneyi ikhalanso yapadera kwa mabanja, ndipo kodi ndi nthawi yapadera kwa Mulungu? Ngati banja lanu lidzakhala pansi n’kumacheza, kodi mudzakhutira ndi zimenezo, kapena mudzakhumudwa?
Ambiri amene amayembekezera zochitika zachipembedzo panyengoyi, amaona kuti nthawi zambiri anthu saganizira za Kristu m’pang’ono pomwe akamakondwerera Khirisimasi ndi Chaka Chatsopano. M’malo mwake, nyengo ya tchuthiyi imangokhala nthawi yolandira mphatso, nthawi yochita mapwando omwe pangachitike zinthu zosalemekeza Kristu, kapena kungokhala nthawi yoti banja ligwirizanenso. Nthawi zambiri phwando loterolo limasokonekera chifukwa wina kapena anthu angapo paphwandopo amadya ndi kumwa kwambiri, zomwe zimayambitsa mikangano imene kawirikawiri imathera m’ziwawa. N’kutheka kuti inu mwaonapo zoterezo, kapenanso zakuchitikirani.
Ngati ndi choncho, mwina mukuona kuti zinthu sizinasinthe kwenikweni kuchokera panthawi ya Mfumu Peter Wamkulu ya ku Russia, yomwe taifotokoza poyamba paja. Pokhumudwa ndi zimene zafala masiku ano, anthu ambiri amalakalaka nyengo ya tchuthiyi itakhala nthawi yoganizira mozama pa zinthu zauzimu ndiponso yoti mabanja akhalire limodzi ndi kusangalala bwinobwino. Ndipo ena afika mpaka polimbikitsa kuti zinthu zisinthe, ndipo amati, nyengoyi imakhalapo chifukwa cha Yesu. Koma kodi n’zotheka kusintha? Ndipo kodi zimenezi zingaperekedi ulemu kwa Kristu? Kodi pali zifukwa zosinthira maganizo anu panyengo ya tchuthiyi?
Kuti mumve mayankho ogwira mtima a mafunsowa, tiyeni tiione nkhaniyi monga momwe amaionera anthu a m’dziko lina, amene ayenera kukhala ndi chifukwa chapadera choyamikirira nyengo imeneyi.