Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kulalikira Am’nsinga Mamasulidwe”

“Kulalikira Am’nsinga Mamasulidwe”

“Kulalikira Am’nsinga Mamasulidwe”

PACHIYAMBI pa utumiki wake, Yesu analengeza kuti ina mwa ntchito yake inali “kulalikira am’nsinga mamasulidwe.” (Luka 4:18) Potengera chitsanzo cha Mbuye wawo, Akristu oona amalalikira uthenga wabwino wa Ufumu kwa “anthu onse,” kuwamasula ku ukapolo wauzimu ndi kuwathandiza kuti akhale ndi moyo wabwino.​—1 Timoteo 2:4.

Masiku ano, ntchito imeneyi ikuphatikizapo kulalikira kwa anthu am’nsinga zenizeni, amene atsekeredwa m’ndende pa milandu yosiyanasiyana ndipo akufuna kumasulidwa mwauzimu. Musangalala ndi nkhani yolimbikitsa yotsatirayi yonena za ntchito ya Mboni za Yehova yolalikira m’ndende za ku Ukraine ndiponso m’mayiko ena ku Ulaya.

Kusiya Moyo wa Mankhwala Osokoneza Bongo N’kukhala Akristu

Pa zaka 38 za moyo wa Serhii, * iye wakhala zaka 20 m’ndende. Ngakhale sukulu anamalizira kundende komweko. Iye anati: “Ndinatsekeredwa m’ndende kalekale chifukwa cha kupha munthu, ndipo mpaka pano sindinamalize chilango changa. M’ndende ndinali wankhanza, ndipo akaidi anzanga ankandiopa.” Kodi izi zinam’patsa ufulu? Ayi. Kwa zaka zambiri, Serhii anali kapolo wa mankhwala osokoneza bongo, mowa, ndi fodya.

Kenako, mkaidi mnzake anam’fotokozera choonadi cha m’Baibulo. Anakhala ngati wam’tsegula maso. M’miyezi yochepa chabe, iye anasiya zinthu zoipa zimene ankakonda zija, n’kuyamba kulalikira uthenga wabwino, ndipo anabatizidwa. Tikunena pano Serhii ali ndi zochita zambiri kundende, ndipo akutumikira monga mtumiki wa Yehova wa nthawi zonse. Wathandiza zigawenga zisanu ndi ziwiri kuti zisinthe moyo wawo, n’kukhala abale ake mwauzimu. Anthu asanu ndi mmodzi mwa amenewa anatuluka m’ndende, koma Serhii sanatuluke. Sikuti iye n’ngokhumudwa ndi zimenezi chifukwa akusangala kuthandiza ena kuti amasuke ku ukapolo wauzimu.​—Machitidwe 20:35.

Mmodzi mwa anthu amene anaphunzitsidwa ndi Serhii kundende ndi Victor, yemwe kale ankagulitsa ndiponso ankakonda kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Atatuluka m’ndende, Victor anapitiriza kuchita bwino mwauzimu ndipo anaphunzira ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki ku Ukraine. Panopa ndi mpainiya wapadera ku Moldova. Victor anati: “Ndinayamba kusuta ndili ndi zaka 8, kumwa kwambiri mowa ndili ndi zaka 12, ndipo ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndili ndi zaka 14. Ndinkafuna kusintha moyo wanga, koma zonse zimene ndinkachita sizinathandize. Ndiyeno mu 1995, pamene ndinali kukonzekera ndi mkazi wanga kuti tisamuke kulekana ndi anthu oipa amene tinkacheza nawo, munthu wamisala anabaya mpaka kupha mkazi wanga. Moyo wanga unafika pomvetsa chisoni kwambiri. Ndinkadzifunsa nthawi zonse mafunso monga akuti, ‘Kodi mkazi wanga ali kuti tsopano? Kodi munthu amapita kuti akamwalira?’ Koma sindinapeze mayankho ake. Pofuna kuiwala mavuto, ndinkagwiritsa ntchito kwambiri mankhwala osokoneza bongo. Ndinamangidwa chifukwa chogulitsa mankhwala osokoneza bongo ndipo anandilamula kukhala m’ndende zaka zisanu. Kundendeko, Serhii anandithandiza kupeza mayankho a mafunso aja. Ndinali n’tayesapo kambirimbiri kuti ndisiye mankhwala osokoneza bongo, koma ulendo uwu ndinatha kusiya chifukwa choti Baibulo linandithandiza. Mawu a Mulungu ndi amphamvu!”​—Ahebri 4:12.

Zigawenga Zoopsa Zisintha

Vasyl sanagwiritsepo ntchito mankhwala osokoneza bongo, koma panthawi ina anamangidwa. Iye anafotokoza kuti: “Ndinkakonda kwambiri masewera a nkhonya. Ndinaphunzira pandekha kumenya munthu popanda kum’siyira mabala.” Vasyl ankachita zachiwawa zakezo pofwamba anthu. “Ndinatsekeredwa m’ndende maulendo atatu, ndipo izi zinachititsa kuti mkazi wanga andisudzule. Pachilango changa chomaliza cha zaka zisanu, ndinawerenga mabuku a Mboni za Yehova. Izi zinandilimbikitsa kuwerenga Baibulo, koma ndinkakondabe nkhonya.

“Pambuyo powerenga Baibulo kwa miyezi isanu ndi umodzi, zinazake zinasintha mumtima mwangamu. Ndikapambana nkhonya, sindinkasangalalanso ngati kale. Motero ndinayamba kuganizira za moyo wanga pogwiritsa ntchito lemba la Yesaya 2:4 ndipo ndinazindikira kuti ngati sindisintha, ndidzakhala m’ndende moyo wanga wonse. Motero ndinataya zinthu zonse zimene ndinkagwiritsa ntchito pankhonya n’kuyamba kusintha makhalidwe anga. Sikuti zinali zophweka kuchita zimenezi, koma m’kupita kwa nthawi, kusinkhasinkha zimene ndinaphunzira ndi kupemphera kunandithandiza kusiya makhalidwe oipa. Nthawi zina ndinkachita kulira popempha Yehova kuti andipatse mphamvu zolimbanirana ndi vuto langa. Mapeto ake zinthu zinayenda bwino.

“Nditatuluka m’ndende, ndinabwererana ndi banja langa. Panopa ndimagwira ntchito pa mgodi wa malasha. Izi zimandipatsa mpata wokwanira wolalikira limodzi ndi mkazi wanga ndiponso wogwira ntchito zanga mu mpingo.”

Mykola ndi anzake anaba m’mabanki angapo ku Ukraine. Chifukwa cha zimenezi anatsekeredwa m’ndende zaka khumi. Asanamangidwe, anapitapo kamodzi kokha kutchalitchi, pokakonzekera kudzaba m’tchalitchimo. Sanathe kukabako, koma ulendo umene anapita ku tchalitchiwo unachititsa Mykola kukhulupirira kuti nkhani zonse za m’Baibulo n’zosasangalatsa, ndipo zimanena za ansembe a chipembedzo cha Orthodox, makandulo, ndiponso tchuthi za chipembedzo. Iye anati: “Sindikudziwa kuti n’chiyani kwenikweni chinandichititsa, koma ndinayamba kuwerenga Baibulo. Ndinachita chidwi kuona kuti ndi losiyana kwambiri ndi mmene ndinkaliganizira!” Anapempha kuti aziphunzira naye Baibulo ndipo anabatizidwa mu 1999. Mutamuona panopa, zingakuvuteni kukhulupirira kuti panthawi ina, mtumiki wothandiza wodzichepetsa ameneyu anali chigawenga choopsa choba m’mabanki ndi mfuti.

Vladimir anapatsidwa chilango choti aphedwe. Ali m’kati modikirira kunyongedwa, iye anapemphera kwa Mulungu ndi kumulonjeza kuti adzam’tumikira akapanda kuphedwa. Kenako, malamulo anasintha, ndipo chilango chophedwa chinachepetsedwa n’kukhala chilango chokhala m’ndende moyo wonse. Pofuna kukwaniritsa lonjezo lake, Vladimir anayamba kufunafuna chipembedzo choona. Anayamba kosi kudzera m’makalata ndipo analandira dipuloma kuchokera ku tchalitchi cha Adventist, komabe sanakhutire ndi zimenezi.

Koma atawerenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! m’nyumba yowerengera mabuku pandende yawo, Vladimir analembera kalata ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Ukraine, ndi kupempha kuti akamuchezere. Abale ochokera m’dera lomwe muli ndendeyo atakamuchezera, iye n’kuti akunena kuti ndi Mboni ndipo anali kulalikira m’ndendemo. Anathandizidwa kuti ayenerere kukhala wofalitsa Ufumu. Pamene nkhani ino inali kulembedwa, n’kuti Vladimir ndi anzake asanu ndi awiri m’ndendemo akuyembekezera kubatizidwa. Koma ali ndi chothetsa nzeru. Popeza kuti akaidi amene anapatsidwa chilango chokhala m’ndende moyo wonse amatsekeredwa m’maselo mogwirizana ndi zipembedzo zawo, Vladimir ndi akaidi amene ali nawo m’selo mwake onse ndi achipembedzo chimodzi. Motero, kodi angathe kumalalikira kwa ndani? Amalalikira uthenga wabwino kwa olondera ndende ndiponso kudzera m’makalata.

Nazar anasamuka ku Ukraine kupita ku Czech Republic, komwe anakagwirizana ndi gulu la mbava. Izi zinachititsa kuti atsekeredwe m’ndende zaka zitatu ndi theka. Ali m’ndende, Nazar anavomera kumacheza ndi Mboni za Yehova zomwe zinkabwera ku ndendeyo kuchokera mu mzinda wa Karlovy Vary. Mwanjira imeneyi, anaphunzira choonadi, ndiponso anasintha kwambiri. Ataona zimenezi, mmodzi wa alonda a pandendepo anauza akaidi amene ankakhala m’selo imodzi ndi Nazar kuti: “Nonse mutakhala ngati Myukireniya ameneyu, ine ndikhoza kupeza ntchito ina.” Wina anati: “Mboni za Yehovazi ndi akatswiri enieni. Munthu pobwera kundende amakhala ali chigawenga, koma potuluka amakhala ali munthu waulemu wake.” Pano tsopano Nazar ali kunyumba. Anaphunzira ukalipentala, anakwatira, ndipo onse ndi mkazi wake ndi atumiki a nthawi zonse. Iye amayamikira kwambiri maulendo amene Mboni zimachita okacheza ku ndende kuja!

Akuluakulu Akuyamikira

Sikuti ndi akaidi okha omwe akuyamikira ntchito imene Mboni za Yehova zikuchita. Miroslaw Kowalski, mneneri wa ndende ina ku Poland, anati: “Timayamikira kwambiri kubwera kwawo. Moyo wa m’mbuyomu wa akaidi ena ndi womvetsa chisoni kwambiri. Mwinamwake sankaonedwa ngati anthu. . . . Thandizo [la Mboni za Yehova] ndi lamtengo wapatali kwambiri chifukwa chakuti tili ndi antchito ndiponso aphunzitsi ochepa.”

Woyang’anira ndende ina ku Poland analembera kalata ofesi ya nthambi, ndi kupempha Mboni kuti ziwonjezere ntchito yawo pa ndende yake. Chifukwa chiyani? Anafotokoza kuti: “Oimira Watchtower akamabwera pafupipafupi mwina akaidi angathandizidwe kuphunzira makhalidwe abwino aumunthu, ndi kuthetsa uchinyama.”

Nyuzipepala ina ya ku Ukraine inalemba nkhani ya mkaidi wina amene anadwala nthenda yovutika maganizo ndipo ankafuna kudzipha koma kenako anathandizidwa ndi Mboni za Yehova. “Tikunena pano, munthuyu akuchira vuto lakelo,” inatero nkhaniyo. Amatsatira pulogalamu ya pa ndendeyo ndipo ndi chitsanzo kwa akaidi ena.”

Phindu Lake Ngakhale Kunja kwa Ndende

Phindu la ntchito imene Mboni za Yehova zikuchita sikuti limangothera kundende kokha ayi. Akaidi amapindulabe pambuyo potuluka m’ndende. Akristu awiri, Brigitte ndi Renate, akhala akuthandiza anthu mwanjirayi kwa zaka zingapo. Pofotokoza za Akristu awiriwa, nyuzipepala ina ya ku Germany, yotchedwa Main-Echo Aschaffenburg, inati: “Amayang’anira akaidi kwa miyezi mwina itatu mpaka isanu pambuyo poti atuluka m’ndende, ndi kuwalimbikitsa kupeza chochita pamoyo. . . . Amadziwika kuboma monga antchito odzipereka oyang’anira anthu amene angotuluka kumene kundende. . . . Komanso amathandizana kwambiri ndi ogwira ntchito kundende.” Anthu ambiri apereka moyo wawo kwa Yehova chifukwa chothandizidwa mwamtunduwu.

Ngakhale akuluakulu a ndende apindula ndi ntchito ya Mboni za Yehova yophunzitsa anthu Baibulo. Mwachitsanzo, Roman anali ndi udindo waukulu ku usilikali ndiponso anali katswiri wa zamaganizo pa ndende ina ku Ukraine. Mboni zitafika kunyumba kwake, iye anavomera kuphunzira Baibulo. Kenako anamva kuti Mboni siziloledwa kulankhula ndi akaidi a pandende yomwe iye ankagwira ntchito. Motero anapempha woyang’anira ndendeyo kuti amulole kuti azigwiritsa ntchito Baibulo pantchito yake yothandiza akaidiwo. Pempho lake linavomerezedwa ndipo akaidi pafupifupi khumi anasonyeza chidwi. Roman nthawi zonse anali kukambirana ndi akaidiwo zimene iye anali kuphunzira m’Baibulo, ndipo zotsatira zake zinali zosangalatsa kwambiri. Pambuyo potuluka m’ndende, ena mwa iwo anapitiriza kuphunzira n’kukhala Akristu obatizidwa. Poona mphamvu ya Mawu a Mulungu, Roman anayamba kuikira mtima kwambiri paphunziro lija. Anasiya ntchito yausilikali n’kupitiriza ntchito yake yophunzitsa Baibulo. Panopa amagwirira limodzi ntchito yolalikira ndi munthu wina amene kale anali mkaidi.

Mkaidi wina analemba kuti: “Baibulo, mabuku ofotokoza za m’Baibulo, ndi phunziro la Baibulo ndizo zimatithandiza ife kuno.” Mawu amenewa akufotokoza bwino kufunika kwa mabuku ofotokoza za m’Baibulo m’ndende zina. Mpingo wina ku Ukraine unafotokoza za ntchito yophunzitsa Baibulo pa ndende ina ya m’gawo lake. Unati: “Akuluakulu pa ndendeyi amayamikira kwambiri mabuku amene timawapatsa. Timawapatsa magazini 60 pa magazini alionse a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amene atuluka.” Mpingo wina unalemba kuti: “Timayang’anira ndende ina yomwe ili ndi zipinda zing’onozing’ono zowerengera mabuku zokwana 20. Tinapereka mabuku athu akuluakulu oti aike ku chipinda chilichonse. Mabuku onse anakwana makatoni 20.” M’ndende ina, alonda amasunga magazini athu mu nyumba yawo yowerengeramo mabuku n’cholinga choti akaidi aziwerenga magazini athu alionse.

Mu 2002 ofesi ya nthambi ku Ukraine inakhazikitsa Dipatimenti Yoona za ku Ndende. Panopo, dipatimentiyi yalankhula ndi ndende pafupifupi 120 ndipo yapeza mipingo yoti iziyang’anira ndendezi. Mwezi uliwonse amalandira kalata pafupifupi 50 zochokera kwa akaidi, ndipo zambiri zimakhala zopempha mabuku kapena phunziro la Baibulo. Nthambi imawatumizira mabuku, magazini, ndi mabulosha mpaka abale a m’dera lomwe kuli ndendezo atayamba kuonana ndi akaidiwo.

Mtumwi Paulo analembera Akristu anzake kuti: “Kumbukirani am’nsinga.” (Ahebri 13:3) Apa anali kunena za anthu amene anamangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Lerolino, Mboni za Yehova zimakumbukira anthu omangidwa, zimayendera ndende, ndi “kulalikira am’nsinga mamasulidwe.”​—Luka 4:18.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Tasintha mayina ena.

[Chithunzi patsamba 9]

Mpanda wa ndende ku L’viv, Ukraine

[Chithunzi patsamba 10]

Mykola

[Chithunzi patsamba 10]

Vasyl ndi mkazi wake, Iryna

[Chithunzi patsamba 10]

Victor