Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mtengo Wokondwerera Chaka Chatsopano, Kodi Ndi Mwambo wa ku Russia Kapena Wachikristu?

Mtengo Wokondwerera Chaka Chatsopano, Kodi Ndi Mwambo wa ku Russia Kapena Wachikristu?

Mtengo Wokondwerera Chaka Chatsopano, Kodi Ndi Mwambo wa ku Russia Kapena Wachikristu?

“KUCHIYAMBI kwa zaka za m’ma 1830, anthu ankaonabe nkhani ya mtengo wosayoyola masamba monga ‘maganizo a ku Germany ongosangalatsa anthu.’ Pa mapeto a zaka khumi zimenezo, ‘unakhala mwambo’ m’nyumba za anthu olemera ku St. Petersburg. . . . Mu ma 1800, anali atsogoleri achipembedzo ndi anthu wamba okha amene sanatsatire mwambo woika mtengo wosayoyola masamba m’nyumba zawo. . . .

“Zaka za m’ma 1800 zisanafike, anthu sanakonde kwambiri . . . mtengowo. Malinga ndi mwambo wa ku Russia, amauona kukhala woimira imfa ndiponso ‘dziko la mizimu,’ mofanana ndi mwambo woika mtengowo padenga la nyumba zomwera mowa. Zimenezi sizinagwirizane ndi kusintha kwa maganizo a anthu kumene kunachitika pakati pa zaka za m’ma 1800. . . . N’zomveka kuti m’kupita kwa nthawi, mwambo wachilendowu unatanthauza zofanana ndi zimene mtengo wa pa Khirisimasi wa kumayiko a Kumadzulo umatanthauza, ndipo unagwirizana ndi nkhani ya Khirisimasi. . . .

“Kusintha mtengowu kukhala chizindikiro cha Chikristu ku Russia kunali ndi zopinga zake. A Tchalitchi cha Orthodox anatsutsa zimenezi. Atsogoleri achipembedzo anaona kuti mwambo watsopanowu unali wa ‘ziwanda,’ wachikunja, sunali wokhudzana ndi kubadwa kwa Mpulumutsi, ndiponso unali mwambo wochokera ku mayiko a Kumadzulo.”​—Anatero Pulofesa Yelena V. Dushechkina, katswiri wa zachinenero pa yunivesite ya St. Petersburg State University.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Photograph: Nikolai Rakhmanov