Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anakondweretsa Mtima wa Makolo Awo

Anakondweretsa Mtima wa Makolo Awo

Anakondweretsa Mtima wa Makolo Awo

“MWANANGA, mtima wako ukakhala wanzeru, mtima wanga wa inedi udzakondwa.” (Miyambo 23:15) Zoonadi, makolo achikristu amakondwera ana awo akapeza nzeru za Mulungu. Loweruka pa September 10, 2005, anthu okwana 6,859, ochokera m’mayiko osiyanasiyana anasonkhana pa mwambo wokondwerera kumaliza maphunziro kwa kalasi ya nambala 119 ya Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo. Onse anali ndi chimwemwe chachikulu mu mtima, makamaka makolo a anthu 56 omaliza maphunzirowo.

David Walker, yemwe wakhala m’banja la Beteli la ku United States kwa zaka zambiri, anatsegulira pulogalamuyo ndi pemphero lochokera pansi pa mtima. Kenaka tcheyamani wa patsikulo, David Splane wa m’Bungwe Lotsogolera Mboni za Yehova, anayamba mwambowo ndi kuuza makolo a omaliza maphunzirowo kuti: “Tikukuthokozani kwambiri. Makhalidwe amene mwaphunzitsa ana anu ndiwo amene awachititsa kufuna kukhala amishonale.” Mwina makolowo anali ndi nkhawa, poganizira kuti posachedwa ana awowo akatumikira ku madera akutali. Komabe, Mbale Splane anawakhazika mtima pansi powauza kuti: “Musadere nkhawa za ana anu. Yehova awasamalira bwino kwambiri kuposa mmene inuyo mukanachitira.” Kenako anati: “Tangoganizirani zinthu zabwino zomwe ana anu akachite. Anthu amene akuvutika akalimbikitsidwa kwa nthawi yoyamba m’miyoyo yawo.”

Mmene Angapitirizire Kukondweretsa Ena

Tcheyamani anaitana anthu anayi kuti alankhulepo. Poyamba, Ralph Walls wa mu Komiti ya Nthambi ya United States analankhula pa mutu wakuti “Khalanibe Maso.” Iye anagogomezera kuti kukhala wakhungu mwauzimu n’koipa kwambiri kuposa khungu lenileni. Mpingo wa Akristu oyambirira wa ku Laodikaya unasiya kuona zinthu mwauzimu. Akristu a mumpingo umenewo amene anali akhungu anathandizidwa, koma nthawi zonse ndi bwino kupeweratu khungu loterolo mwakukhalabe maso mwauzimu. (Chivumbulutso 3:14-18) Wokamba nkhaniyo anati: “Khalanibe maso, ndipo onani amuna amene akutsogolera zinthu monga mmene Yehova amawaonera.” Omaliza maphunzirowo sayenera kuda nkhawa kwambiri ngati mumpingo muli mavuto. Ambuye Yesu Kristu akudziwa bwino zonsezo. Adzaonetsetsa kuti zinthu zakonzeka panthawi yake.

Kenaka, Samuel Herd wa m’Bungwe Lotsogolera anakamba nkhani yoyankha funso lakuti “Kodi Mwakonzeka?” Monga momwe munthu wapaulendo amatengera zovala zoti azikavala, chimodzimodzinso omaliza maphunzirowo ayenera nthawi zonse kuvala makhalidwe a munthu watsopano. Ayenera kukhala achifundo ngati Yesu. Munthu wakhate atamuuza Yesu kuti: “Ngati mufuna mukhoza kundikonza,” iye anati: “Ndifuna; khala wokonzedwa.” (Marko 1:40-42) Kenaka wokamba nkhaniyo anati: “Ngati mukufunadi kuthandiza anthu, mudzapeza njira yowathandizira.” Lemba la Afilipi 2:3 limauza Akristu kuti “yense ayese anzake om’posa iye mwini.” Mbale Herd anati: “Kukhala wodzichepetsa n’kofunika kwambiri kuposa kungokhala wodziwa zinthu. Anthu amene mukakumane nawo mu utumiki komanso abale ndi alongo anu mu mpingo adzapindula ndi zinthu zimene mukudziwa kokha ngati muli odzichepetsa.” Iye anamaliza n’kunena kuti ngati omaliza maphunzirowo apitirizabe kuvala chikondi monga Akristu, ndiye kuti ali okonzeka kupita ku utumiki wawo, ndipo n’zosakayikitsa kuti zinthu zikawayendera bwino.​—Akolose 3:14.

Mark Noumair, mmodzi mwa alangizi a Sukulu ya Gileadi, anachititsa anthu chidwi ndi mutu wa nkhani yake wakuti: “Kodi Mudzapitirizabe Kumva Chonchi?” Nkhaniyo inali yonena za ubwino wa Yehova. Lemba la Salmo 103:2 limati: “Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi.” Aisrayeli anasonyeza kuti sanayamikire mana amene ankadya kuti akhale ndi moyo, ndipo anawatcha “mkate wachabe.” (Numeri 21:5) Pamene nthawi inali kupita, ubwino wa manawo sunasinthe, koma iwo anasiya kuwayamikira. Mlangiziyo anati: “Mukaiwala zochita za Yehova n’kuyamba kuona utumiki wanu waumishonale ngati ntchito wamba, zingakulepheretseni kuyamikira utumiki umene Yehova wakupatsani.” Lemba la Salmo 103:4 limati Yehova ‘amaveka korona wa chifundo.’ Omaliza maphunzirowo adzaona chifundo cha Mulungu m’mipingo yawo yatsopano.

Mlangizi wina wa Sukulu ya Gileadi, Lawrence Bowen, anakamba nkhani yakuti “Kodi Madalitso Adzakupezani?” Iye anafotokoza kuti anthu a m’kalasi ya nambala 119 ya Gileadi achita khama kwambiri kuphunzira zimene ayenera kuchita kuti zinthu zikawayendere bwino monga amishonale. Koma tsopano ayenera kumamatira Yehova ndi ntchito imene wawapatsa. Pa Chivumbulutso 14:1-4; anthu a m’gulu la 144,000 akufotokozedwa kuti ndi “amene atsata Mwanawankhosa kuli konse amukako.” Onse m’gulu limenelo amamatira Yehova ndi Mwana wake mokhulupirika, kaya akumane ndi ziyeso zotani, ndipo amakwanitsa cholinga chawo. Wokamba nkhaniyo anati, “Kaya tikumane ndi zotani, nafenso mokhulupirika timamatire Yehova ndi ntchito imene watipatsa.” Akachita zimenezo, omaliza maphunzirowo adzaona kuti madalitso a Yehova ‘adzawapeza.’​—Deuteronomo 28:2.

Kubala Zipatso mu Utumiki Wawo

Loweruka ndi Lamlungu lililonse pa nthawi yomwe anali pasukulu, ophunzirawo ankalowa mu utumiki wakumunda. Pamene Wallace Liverance, wosunga kaundula wa sukuluyo analankhula nawo pa mwambowu, zinaonekeratu kuti ophunzirawo anachita bwino kwambiri mu utumiki wawo. Analalikira uthenga wabwino m’zilankhulo zosachepera teni ndipo anayambitsa maphunziro a Baibulo angapo. Mwamuna wina ndi mkazi wake a m’kalasili anayambitsa phunziro la Baibulo ndi munthu winawake wachitchaina. Atamuyendera kawiri, anamufunsa kuti afotokoze mmene amamvera pophunzira za Yehova. Iye anatsegula Baibulo lake n’kuwapempha iwowo kuti awerenge Yohane 17:3. Anawauza kuti akuona kuti ali pa njira yopita ku moyo.

Anthony Morris wa m’Bungwe Lotsogolera kenako anafunsa mafunso abale atatu amene ali m’Komiti ya Nthambi ku Côte d’Ivoire, Dominican Republic, ndi ku Ecuador. Abale amenewa anawatsimikizira omaliza maphunzirowo kuti Makomiti a Nthambiwa akuwadikirira mwachidwi ndipo adzawathandiza kuti azolowerane ndi moyo wa kumalo kwatsopanoko.

Kenaka, Leonard Pearson wa m’banja la Beteli la United States analankhula ndi anthu atatu a m’Makomiti a Nthambi, ochokera ku Democratic Republic of Congo, Papua New Guinea, ndi Uganda. Abalewa analimbikitsa omaliza maphunzirowo kuti azilimbikira kwambiri utumiki wa kumunda. Mwamuna wina ndi mkazi wake omwe ndi amishonale ndipo akhala zaka zoposa 21 ku Congo athandiza anthu oposa 60 kufika podzipereka ndi kubatizidwa. Panopa banja limeneli likuchititsa maphunziro a Baibulo 30, ndipo ophunzira awo 22 amapita ku misonkhano. Poona kututa kwauzimu kwakukulu kumeneku, ino ndi nthawi yabwino kwambiri kukhala mmishonale.

Kuchitira Umboni Mwachangu

Gerrit Lösch wa m’Bungwe Lotsogolera anakamba nkhani yomaliza. Mutu wake unali wakuti “Kulankhula za Mulungu ndi Kuchitira Umboni za Yesu M’tsiku la Ambuye.” Mawu akuti “mboni” ndi “umboni” amapezeka nthawi 19 m’buku la Chivumbulutso. Choncho, Yehova akusonyeza mosapita m’mbali ntchito imene akufuna kuti anthu ake azichita. Kodi umboni umenewu tikuyenera kuupereka liti? Mu “tsiku la Ambuye.” (Chivumbulutso 1:9, 10) Tsiku limenelo linayamba mu 1914, likadalipobe panopa, ndipo lipitirira mpaka m’tsogolo. Malinga ndi lemba la Chivumbulutso 14:6, 7; angelo nawonso akuthandizapo pa ntchito yolankhula za Mulungu. Lemba la Chivumbulutso 22:17 limasonyeza kuti udindo wotsogolera ntchito yochitira umboni za Yesu unapatsidwa kwa otsalira a Akristu odzozedwa. Koma tonsefe tiyenera kugwiritsa ntchito mwayi wapadera umene tili nawo panopa. M’vesi 20, Yesu anati: “Ndidza msanga.” Mbale Lösch analimbikitsa onse amene analipo kuti: “Itanani anthu n’kuwauza kuti, ‘Bwerani mudzatenge madzi amoyo aulere.’ Yesu akubwera msanga. Kodi takonzeka?”

Fred Rusk, amene anali mlangizi wa Sukulu ya Gileadi kwa zaka 11, anamaliza pulogalamuyo ndi pemphero lothokoza Yehova limene linakhudza mitima ya onse amene analipo. Anali mapeto abwino a tsiku limeneli, lomwe linali losangalatsa kwambiri.

[Bokosi patsamba 13]

ZIWERENGERO ZOKHUDZA OPHUNZIRAWO

Chiwerengero cha mayiko kumene ophunzira anachokera: 10

Chiwerengero cha mayiko kumene anawatumiza: 25

Chiwerengero cha ophunzira: 56

Avereji ya zaka zakubadwa: 32.5

Avereji ya zaka zimene akhala m’choonadi: 16.4

Avereji ya zaka zimene akhala mu utumiki wa nthawi zonse: 12.1

[Chithunzi patsamba 15]

Kalasi la Nambala 119 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

Pa m’ndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mayina tawandandalika kuyambira kumanzere kupita kumanja mumzera uliwonse.

(1) Helgesen, S.; Daugaard, H.; Pierluissi, A.; Joseph, I.; Racanelli, C. (2) Byrge, T.; Butler, D.; Freedlun, J.; Nuñez, K.; Pavageau, C.; Doumen, T. (3) Camacho, O.; Lindqvist, L.; Broomer, A.; Wessels, E.; Burton, J.; Woodhouse, O.; Doumen, A. (4) Tirion, A.; Connally, L.; Fournier, C.; Gil, A.; Johnsson, K.; Hamilton, L. (5) Byrd, D.; Scribner, I.; Camacho, B.; Laschinski, H.; Hallahan, M.; Libuda, O. (6) Joseph, A.; Lindqvist, M.; Helgesen, C.; Nuñez, D.; Scribner, S.; Fournier, J. (7) Pierluissi, F.; Pavageau, T.; Broomer, C.; Racanelli, P.; Butler, T.; Woodhouse, M.; Libuda, J. (8) Laschinski, M.; Freedlun, S.; Burton, I.; Tirion, M.; Byrd, M.; Byrge, J. (9) Wessels, T.; Hallahan, D.; Connally, S.; Gil, D.; Daugaard, P.; Hamilton, S.; Johnsson, T.