Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Lemba la Salmo 102:26 limanena kuti dziko lapansi ndi kumwamba “zidzatha.” Kodi mawu amenewa akusonyeza kuti dziko lapansili lidzawonongedwa?

Popemphera kwa Yehova, wamasalmo anati: “Munakhazika dziko lapansi kalelo; ndipo zakumwamba ndizo ntchito ya manja anu. Zidzatha izi, koma Inu mukhala: inde, zidzatha zonse ngati chovala; mudzazisintha ngati malaya, ndipo zidzasinthika.” (Salmo 102:25, 26) Nkhani imene ikunenedwa m’salmo limeneli imasonyeza kuti mavesi amenewa sakunena za kuwonongedwa kwa dziko lapansi, koma akunena za umuyaya wa Mulungu. Nkhani ya m’salmoli imasonyezanso chifukwa chake mfundo yoona ndi yofunika imeneyi ili yolimbikitsa kwa atumiki a Mulungu.

Wamasalmoyo, mwina ali ku ukapolo ku Babulo, akuyamba ndi kufotokoza mavuto ake. Iye akudandaula kuti moyo wake ndi wosakhalitsa “ngati utsi.” Nkhawa yaikulu kwambiri yachititsa thupi lake tsembwe, ndipo ikuchititsa mafupa ake kumveka kuti ‘akunyeka ngati nkhuni.’ Watopa kwambiri, ndipo ‘akukhala ngati udzu womweta,’ ndiponso wasungulumwa “ngati kadzidzi wa kumabwinja.” Mavutowo amuthetsera njala yake yonse, ndipo masiku onse akungokhalira kulira. (Salmo 102:3-11) Ngakhale zili choncho, wamasalmoyo sanatayiretu chiyembekezo. Chifukwa chiyani? Chifukwa cha zimene Yehova walonjeza kuchitira Ziyoni, kapena kuti Yerusalemu.

Ngakhale kuti Ziyoni wawonongedwa, Yehova walonjeza kuti adzabwezeretsedwa. (Yesaya 66:8) Choncho, wamasalmoyo akunena modalira Yehova kuti: “Mudzauka, ndi kuchitira nsoni Ziyoni; popeza yafika nyengo yakum’chitira chifundo, nyengo yoikika. Pakuti Yehova anamanga Ziyoni.” (Salmo 102:13, 16) Kenaka wamasalmoyo akubwereranso ku nkhani ya kuvutika kwake. Iye akufotokoza kuti ngati Yerusalemu yemwe wawonongeka angabwezeretsedwe ndi mphamvu ya Mulungu, Yehova angathenso kumupulumutsa ku mavuto akewo. (Salmo 102:17, 20, 23) Ndipo palinso china chimene chikuchititsa wamasalmoyo kukhulupirira Yehova ndi mtima wake wonse. N’chiyani? Mfundo yoti Mulungu adzakhalako kwamuyaya.

Umuyaya wa Yehova ndi wosiyana kwambiri ndi kufupika kwa moyo wa wamasalmoyo. Iye akuuza Yehova kuti: “Zaka zanu zikhalira m’mibadwomibadwo.” (Salmo 102:24) Kenako wamasalmoyo akuti: “Munakhazika dziko lapansi kalelo; ndipo zakumwamba ndizo ntchito ya manja anu.”​—Salmo 102:25.

Komabe, ngakhale zaka zambiri zomwe dziko lapansi ndi kumwamba zakhalako sizingafanane ndi umuyaya wa Yehova. Wamasalmoyo akuwonjezera kuti: “Zidzatha izi [dziko lapansi ndi kumwamba], koma Inu mukhala.” (Salmo 102:26) Dziko lapansi ndi kumwamba zikhoza kuwonongeka. N’zoona kuti Yehova ananenapo kuti zidzakhala kosatha. (Salmo 119:90; Mlaliki 1:4) Koma zikhoza kuwonongedwa ngati Mulungu atafuna. Mosiyana ndi zimenezi, Mulungu sangafe. Zinthu zolengedwa zimakhala “ku nthawi za nthawi” kokha chifukwa choti Mulungu amaziyang’anira. (Salmo 148:6) Yehova atasiya kusamalira zinthu zolengedwa, “zidzatha zonse ngati chovala.” (Salmo 102:26) Mofanana ndi momwe munthu amakhalira nthawi yaitali kuposa malaya ake, momwemonso zolengedwa za Yehova zikhoza kukhala nthawi yochepa poyerekezera ndi iyeyo, ngati atafuna kutero. Komabe, tikudziwa kuchokera ku malemba ena kuti chimenecho si cholinga chake. Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti Yehova wakonza zoti dziko lapansili ndi kumwamba zidzakhale kosatha.​—Salmo 104:5.

N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova adzakhalapo mpaka kalekale kuti akwaniritse malonjezo ake onse. Kaya tikumane ndi mavuto otani, tikamuuza mavuto athuwo, tingakhale ndi chikhulupiriro kuti ‘amasamalira pemphero la iwo akusowa konse, osapeputsa pemphero lawo.’ (Salmo 102:17) Zoonadi, lonjezo la Yehova loti adzatichirikiza lopezeka mu Salmo 102 n’lodalirika kwambiri kuposa pansi pamene timapondapa.