Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mawu a pa Nthawi Yake Kodi Sali Abwino?”

“Mawu a pa Nthawi Yake Kodi Sali Abwino?”

“Mawu a pa Nthawi Yake Kodi Sali Abwino?”

PAMSONKHANO wa tsiku lonse wa Mboni za Yehova, Kim anayesetsa kumvetsera ndi kulemba notsi ukunso akusamalira mwana wake wamkazi wa zaka ziwiri ndi theka kuti akhazikike malo amodzi osavutavuta. Pamapeto pa msonkhanowo, mlongo wina wachikristu amene anakhala mu mzere womwewo anatembenukira Kim ndi kumuyamikira kwambiri chifukwa cha momwe iye ndi mwamuna wake anasamalira mwana wawo pamsonkhanopo. Mawu a mlongoyo anamufika pamtima kwambiri Kim moti mpaka pano, patatha zaka zingapo, iye akuti: “Ndikatopa kwambiri pa misonkhano, ndimaganizira zimene mlongo uja ananena. Mawu ake okoma mtima aja amandilimbikitsabe kupitiriza kuphunzitsa mwana wanga.” Zoonadi, mawu a panthawi yake angalimbikitse munthu. Baibulo limati: “Mawu a pa nthawi yake kodi sali abwino?”​—Miyambo 15:23.

Komabe, ena a ife zimativuta kuyamikira ena. Nthawi zina, kuzindikira kuperewera kwathu kungatichititse kuvutika kuyamikira ena. Mkristu wina anati: “Kwa ine, zili ngati ndaima pamatope. Ndikamayamikira ena, zimakhala ngati ndikuwanyamula ine n’kumatitimira.” Zinthu ngati manyazi, kudzikayikira, ndi kuopa kuti ena satimvetsa zingachititsenso kuti tizivutika kuyamikira ena. Kuwonjezera apo, ngati panthawi imene ifeyo tinali kukula sitinkayamikiridwa kwambiri kapena sitinkayamikiridwa n’komwe, zingamativute kuyamikira ena.

Komabe, kudziwa kuti kuyamikira ena kuli ndi ubwino wake kwa onse awiri, woyamikira ndi woyamikiridwayo, kungatichititse kuyesetsa kwambiri kuuza ena mawu owayamikira pa nthawi yoyenerera. (Miyambo 3:27) Koma kodi ubwino woyamikira ena ndi wotani? Tiyeni tione mfundo zingapo.

Ubwino Wake

Kuyamikira koyenerera kungachititse munthu woyamikiridwayo kusiya kudzikayikira. Elaine, mkazi wachikristu wapabanja, anati: “Ndimamva kuti anthu akundidalira ndi kundikhulupirira akamandiyamikira.” Zoonadi, kuyamikira munthu amene amadzikayikira kungamulimbikitse kuti athane ndi zopinga, ndipo pamapeto pake amasangalala. Makamaka achinyamata amapindula kwambiri tikawayamikira pamene achita zabwino. Wachinyamata wina amene ananena kuti nthawi zambiri amaganizira zinthu zosalimbikitsa, anati: “Nthawi zonse ndimayesetsa momwe ndingathere kukondweretsa Yehova, koma nthawi zina ndimaona kuti ngakhale ndiyesetse bwanji, sindikuchita zokwanira. Wina akandiyamikira, ndimamva bwino kwambiri.” Zimenezi zikugwirizana ndi mwambi wa m’Baibulo woti: “Mawu oyenera a pa nthawi yake akunga zipatso zagolidi m’nsengwa zasiliva.”​—Miyambo 25:11.

Kuyamikira munthu kungamulimbikitse. Munthu wina amene ali mu utumiki wa nthawi zonse anati: “Munthu akandiyamikira, zimandilimbikitsa kuti ndizigwira ntchito mwakhama ndi kuwongolera utumiki wanga.” Mayi wina amene ali ndi ana awiri anati ana ake akayamikiridwa ndi anthu ena a mumpingomo chifukwa choyankha pamisonkhano, zimawalimbikitsa kudzayankha kwambiri ulendo wina. Indedi, kuyamikira ana kungawalimbikitse kupita patsogolo pa moyo wawo wachikristu. Ndipotu, tonsefe timafuna kumva kuti timayamikiridwa ndipo ndife ofunika. Dziko lopanikizali nthawi zina limatichititsa kukhala otopa ndi opsinjika. Mkulu wina wachikristu anati: “Nthawi zina ndikafooka, anthu akandiyamikira zimakhala ngati mapemphero anga ayankhidwa.” Mofanana ndi zimenezo, Elaine anati: “Nthawi zina ndimaona kuti Yehova amandiuza kuti akusangalala nane kudzera mwa anthu ena.”

Kuyamikiridwa kungachititse munthu kumva kuti sali yekha. Kuyamikira munthu mochokera pansi pa mtima kumasonyeza kuti tikumuganizira ndipo kumamuchititsa kumva kuti amakondedwa, ndi wotetezeka, ndipo ndi wofunika. Ndi umboni woti timakondadi Akristu anzathu ndipo timayamikira zimene amachita. Josie, mayi amene ali ndi ana, anati: “M’mbuyomu ndinafunika kusankha kukhalabe m’choonadi m’banja la anthu osiyana zipembedzo. Panthawi imeneyo, kuyamikiridwa ndi anthu okhwima mwauzimu kunandilimbikitsa kuti ndisafooke.” Zoonadi, “tili ziwalo wina ndi mnzake.”​—Aefeso 4:25.

Kufuna kuyamikira ena kumatithandiza kuona zabwino mwa ena. Kumatithandiza kuona makhalidwe abwino amene ena ali nawo, osati zofooka zawo. Mkulu wina wachikristu dzina lake David anati: “Kusangalala ndi zimene ena amachita kungatithandize kuwayamikira pafupipafupi.” Tikakumbukira mmene Yehova ndi Mwana wake amayamikirira anthu opanda ungwiro pafupipafupi zingatithandize kuyamikiranso ena pafupipafupi.​—Mateyu 25:21-23; 1 Akorinto 4:5.

Oyenera Kuwayamikira

Yehova Mulungu, popeza ndi amene analenga zonse, ndi amene ali woyenera kwambiri kutamandidwa kuposa wina aliyense. (Chivumbulutso 4:11) Ngakhale kuti safunikira ifeyo kuti azidzidalira kapena kuti timulimbikitse, tikamatamanda Yehova chifukwa cha zochita zake zodabwitsa ndi kukoma mtima ndi chikondi chake, amatiyandikira ndipo timakhala naye pa ubwenzi. Kutamanda Mulungu kumatithandizanso ifeyo kunyadira moyenerera zinthu zimene tachita bwino ndipo kumatichititsa kuzindikira kuti zinthu zikutiyendera bwino chifukwa cha Yehova. (Yeremiya 9:23, 24) Yehova wapereka mwayi kwa anthu onse oyenerera wodzakhala ndi moyo wosatha, ndipo chimenecho ndi chifukwa chinanso chomutamandira. (Chivumbulutso 21:3, 4) Kalelo, Mfumu Davide inali yofunitsitsa ‘kulemekeza dzina la Mulungu’ ndi ‘kum’bukitsa ndi kum’yamika.’ (Salmo 69:30) Tiyeni nafenso tikhale ndi cholinga chomwecho.

Olambira anzathu ndi ofunika kuwayamikira. Tikamawayamikira, timakhala tikuchita zinthu mogwirizana ndi lamulo la Mulungu loti, “tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino.” (Ahebri 10:24) Mtumwi Paulo ndiye chitsanzo chabwino pankhaniyi. Iye analembera kalata ku mpingo wa ku Roma kuti: “Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Kristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idamveka pa dziko lonse lapansi.” (Aroma 1:8) Mofanana ndi zimenezo, mtumwi Yohane anayamikira Mkristu mnzake Gayo chifukwa cha chitsanzo chake chabwino kwambiri cha ‘kuyenda m’choonadi.’​—3 Yohane 1-4.

Masiku ano, tili ndi mpata wabwino woyamikira Akristu anzathu akasonyeza chitsanzo chabwino cha makhalidwe achikristu, akakamba nkhani imene anaikonzera bwino, kapena akapereka yankho logwira mtima pa misonkhano. Kapena mwana akayesetsa kuwerenga malemba pa misonkhano yampingo, tikhozanso kumuyamikira. Elaine, amene tamutchula kale uja, anati: “Tonsefe tili ndi mphatso zosiyanasiyana. Tikamayamikira zomwe wina wachita, timakhala tikuyamikira mphatso zosiyanasiyana zimene anthu a Mulungu ali nazo.”

M’banja

Nanga bwanji kuyamikira anthu a m’banja mwathu? Pamafunika nthawi, khama, ndiponso chikondi kuti mwamuna ndi mkazi apezere banja lawo zosowa zauzimu, zosowa za pamoyo wawo ndiponso kumathandizana maganizo. Choncho amafunika kuuzana mawu oyamikirana ndiponso kumva ana awo akuwayamikira. (Aefeso 5:33) Mwachitsanzo, ponena za mkazi wangwiro, Mawu a Mulungu amati: “Anake adzanyamuka, nadzamutcha wodala; mwamuna wake nam’tama.”​—Miyambo 31:10, 28.

Ananso amafunika kumawayamikira. N’zomvetsa chisoni kuti makolo ambiri amalimbikira kuuza ana awo zomwe anawo amafunika kuchita koma nthawi zambiri sawayamikira akayesetsa kukhala aulemu ndi omvera. (Luka 3:22) Ngati mwana akuyamikiridwa panthawi imene ali wamng’ono kwambiri, zimamuchititsa kumva kuti ndi wofunika ndiponso wotetezeka.

N’zoona kuti pamafunika khama kuti tiyamikire ena, koma timapindula kwambiri chifukwa chochita zimenezi. Ndipotu, ngati timayesetsa kuyamikira anthu oyenera kuwayamikira, m’pamenenso timakhala achimwemwe kwambiri.​—Machitidwe 20:35.

Khalani ndi Mtima Woyenera Akakuyamikirani Ndiponso Mukamayamikira Ena

Komabe, ena akayamikiridwa zingawaike pachiyeso. (Miyambo 27:21) Mwachitsanzo, kuyamikiridwa kungachititse anthu amene amakonda kunyada kudziona ngati ndi apamwamba kuposa ena. (Miyambo 16:18) Choncho m’pofunika kusamala. Mtumwi Paulo anapereka malangizo osapita m’mbali otsatirawa: “Ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.” (Aroma 12:3) Pofuna kuthandiza ena kuti asagwe mu msampha wodzikweza, mwina ndi bwino osamagogomezera zinthu monga nzeru kapena kukongola kwawo. M’malo mwake, tiziyamikira ena chifukwa cha zochita zawo zabwino.

Tikamakhala ndi maganizo oyenera poyamikira anthu ena ndiponso ena akamatiyamikira, tingapindule. Zingatichititse kuvomereza kuti zabwino zonse zomwe tachita zatheka chifukwa chothandizidwa ndi Yehova. Kuyamikiridwa kungatilimbikitsenso kupitiriza kusonyeza khalidwe labwino.

Kuyamikira ena moona mtima ndi mphatso imene tonsefe tingapereke. Tikayamikira munthu, zingamulimbikitse kwambiri kuposa momwe tinali kuganizira.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 18]

Kalata Imene Inamufika Pamtima

Woyang’anira woyendayenda wina akukumbukira bwino tsiku linalake lomwe iye ndi mkazi wake anafika komwe anali kukhala kuchokera mu utumiki kunja kukuzizira kwambiri. Iye anati: “Mkazi wanga anali atazizidwa ndiponso atakhumudwa, ndipo anandiuza kuti akuona kuti sangathe kupitiriza ntchito imeneyi. Mkazi wangayo anati, ‘Zingakhale bwino kwambiri titati tizichita utumiki wa nthawi zonse mu mpingo winawake, kukhala malo amodzi, n’kumachititsa maphunziro a Baibulo athuathu.’ Sindinaganize chochita panthawi imeneyo, ndipo ndinati tipitiriza mpaka mlungu umenewo uthe kenako adzandiuze momwe akumvera. Ngati adzaonebe kuti akufuna kusiya, ndidzalemekeza maganizo ake. Tsiku lomwelo, tinaima pa positi ofesi n’kupeza kalata yochokera ku ofesi ya nthambi yopita kwa mkazi wangayo. M’kalatayo munali mawu omuyamikira kwambiri chifukwa cha ntchito yomwe anali kugwira mu utumiki wa kumunda ndiponso chifukwa cha kupirira kwake, ndipo anamuuza kuti akudziwa kuti n’zovuta kumagona m’nyumba yosiyana mlungu uliwonse. Mawu omuyamikira amenewo anamukhudza mtima kwambiri moti kuyambira tsiku limenelo sananeneponso zoti akufuna kusiya ntchito yoyendayenda. Ndipotu, nthawi zingapo anandilimbikitsa ineyo kuti ndipitirize pamene ndinaganiza zosiya.” Banja limeneli linakhala mu ntchito yoyendayenda kwa zaka pafupifupi 40.

[Chithunzi patsamba 17]

Kodi ndani ayenera kuyamikiridwa mu mpingo wanu?

[Chithunzi patsamba 19]

Ana amamva bwino tikamawasamalira mwachikondi ndi kuwayamikira