Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Chabwino Chidzagonjetsere Choipa

Mmene Chabwino Chidzagonjetsere Choipa

Mmene Chabwino Chidzagonjetsere Choipa

Mfumu Davide anali munthu wabwino. Anali munthu wokonda Mulungu, wokonda chilungamo, ndi wokonda anthu otsika. Komabe, mfumu yabwino yomweyi inachita chigololo ndi mkazi wa mmodzi wa anyamata ake apamtima. Ndipo pamene Davide anazindikira kuti mkaziyo, Bateseba, anali ndi pakati, anakonza zoti mwamuna wake aphedwe. Ndipo kenako pofuna kubisa zolakwa zake, anakwatira Bateseba.​—2 Samueli 11:1-27.

N’ZODZIWIKIRATU kuti anthu angathe kuchita zinthu zabwino. Koma, nanga n’chifukwa chiyani anthu omwewo akuchita zinthu zoipa kwambiri? Baibulo limatchula zinthu zazikuluzikulu zingapo zimene zimachititsa kuipa. Limafotokozanso za mmene Mulungu, kudzera mwa Kristu Yesu, adzachotsere kuipa konse.

Mtima Wofuna Kuchita Zoipa

Mfumu Davide iye mwiniyo anatchulapo chinthu chimodzi chimene chimachititsa kuipa. Ataona kuti zochita zake zoipa zaululika, anavomereza kulakwa kwake konse. Kenako, ndi mtima wachisoni analemba kuti: “Onani, ndinabadwa m’mphulupulu: ndipo mayi wanga anandilandira m’zoipa.” (Salmo 51:5) Sichinali cholinga cha Mulungu kuti amayi azibala ana oti n’kuchimwa. Komano, pamene Hava ndipo kenako Adamu anasankha kupandukira Mulungu, sakanathanso kubereka ana opanda uchimo. (Aroma 5:12) Pamene anthu opanda ungwiro anachuluka, zinayamba kuonekeratu kuti “ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake.”​—Genesis 8:21.

Kupanda kusamala, mtima wofuna kuchita zinthu zoipa umenewu ungatitengere ku “dama, . . . madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru,” ndi zinthu zina zoipa zimene Baibulo limazitcha “ntchito za thupi.” (Agalatiya 5:19-21) Mfumu Davide inagonjera thupi lake lofooka ndipo inachita chigololo, chimene kenako chinachititsa zachiwawa. (2 Samueli 12:1-12) Zinali zotheka ndithu kukana maganizo amenewa ofuna kuchita chiwerewere. Komano chifukwa chakuti anapitirizabe kumuganizira Bateseba, Davide anachita ndendende zimene wophunzira Yakobo analemba kuti: “Munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chim’kokera, nichimunyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.”​—Yakobo 1:14, 15.

Zinthu ngati kupha anthu ambirimbiri, kugwirira akazi, ndi chiwawa zotchulidwa m’nkhani yapitayo, zikusonyeza zimene zimachitika anthu akalola zilakolako zoipa kuwalamulira.

Zoipa Zingayambe Chifukwa Chosazindikira

Chifukwa chachiwiri chimene anthu amachitira zinthu zoipa timachipeza mu mbiri ya mtumwi Paulo. Pamene amamwalira, Paulo anali atadziwika bwino monga munthu wofatsa ndi wachikondi. Anali atadzipereka kutumikira abale ndi alongo ake achikristu modzimana. (1 Atesalonika 2:7-9) Komabe kumbuyoko, pamene anali kudziwika ndi dzina lakuti Saulo, ankachita kupumira m’mwamba poopseza ndi kupha anthu a gulu lomweli. (Machitidwe 9:1, 2) Kodi n’chifukwa chiyani Paulo anavomereza kuti Akristu oyambirira achitiridwe zinthu zoipa, ndiponso iye mwiniyo n’kuchita nawo zimenezo? Iye anati: “Popeza ndinazichita wosazindikira.” (1 Timoteo 1:13) N’zoona kuti Paulo anali ndi “changu cha kwa Mulungu, koma simonga mwa chidziwitso.”​—Aroma 10:2.

Mofanana ndi Paulo, anthu ambiri oona mtima akhala akuchita zinthu zoipa chifukwa chosadziwa molondola chifuniro cha Mulungu. Zili monga mmene Yesu anachenjezera otsatira ake kuti: “Ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.” (Yohane 16:2) Mboni za Yehova za masiku ano zaona ndi maso awo mawu a Yesu amenewa akukwaniritsidwa. M’mayiko ambiri, zazunzidwa ndi kuphedwa ndi anthu amene pochita zimenezi, amati akutumikira Mulungu. N’zachionekere kuti changu cholakwika chotere sichikondweretsa Mulungu.​—1 Atesalonika 1:6.

Woyambitsa Kuipa

Yesu anatchulapo chifukwa chachikulu chimene chapangitsa kuti kuipa kukhalepo. Polankhula ndi atsogoleri achipembedzo amene anali ndi cholinga chofuna kumupha, iye anati: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi.” (Yohane 8:44) Anali Satana amene, chifukwa chodzikonda, ananyenga Adamu ndi Hava kuti apandukire Mulungu. N’kupanduka kumeneku komwe kunabweretsa uchimo, ndipo kenaka imfa kwa mtundu wonse wa anthu.

Mtima wa Satana wofuna kupha anthu unaonekeranso bwino ndi mmene anachitira zinthu ndi Yobu. Pamene Yehova anamulola kuyesa chikhulupiriro cha Yobu, Satana sanakondwere ndi kulanda kokha katundu wa Yobu. Iye anaphetsanso ana ake onse teni. (Yobu 1:9-19) Pa zaka za posachedwapa, anthu akumana ndi zinthu zoipa zochuluka chifukwa cha kupanda ungwiro kwawo, kusazindikira, ndiponso chifukwa chakuti Satana wakhala akulowerera kwambiri mu zochita za anthu. Baibulo limanena kuti Satana ‘anaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.’ Ulosi womwewu umanena molondola kuti kuponyedwa pansi kwa Satana kunali kudzayambitsa “tsoka” losaneneka padziko lapansi. Ngakhale kuti Satana alibe mphamvu youmiriza anthu kuchita zinthu zoipa, iye ndi katswiri, “wonyenga wa dziko lonse.”​—Chivumbulutso 12:9, 12.

Kuthetsa Mtima Wofuna Kuchita Zoipa

Kuti kuipa kutheretu pakati pa anthu, chibadwa chawo chofuna kuchita zoipa, kusazindikira zinthu molondola, ndi zochita za Satana ziyenera kuchotsedwa. Choyamba, kodi ndi motani mmene chibadwa cha anthu chofuna kuchita tchimo chingachotsedwere mumtima mwawo?

Palibe dokotala aliyense kapena mankhwala alionse amene angachotse chibadwa cha anthu chofuna kuchita zoipa. Komabe, Yehova Mulungu wapereka mankhwala othetsa machimo achibadwa ndiponso kupanda ungwiro kwa onse amene akufuna. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Mwazi wa Yesu . . . utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.” (1 Yohane 1:7) Pamene munthu wangwiroyo, Yesu, mwakufuna kwake anapereka moyo wake, “anasenza machimo athu mwini yekha m’thupi mwake [pamtengo], kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo.” (1 Petro 2:24) Imfa ya nsembe ya Yesu, inali kudzachotsa mavuto obwera chifukwa cha kuchimwa kwa Adamu. Paulo analemba kuti Kristu Yesu anakhala “chiwombolo m’malo mwa onse.” (1 Timoteo 2:6) Inde, imfa ya Kristu inatsegula njira yakuti mtundu wonse wa anthu upatsidwenso ungwiro umene Adamu anataya.

Koma mwina mungafune kudziwa kuti, ‘Ngatidi imfa ya Yesu imene inachitika zaka 2,000 zapitazo inachititsa kuti anthu akhale angwiro, n’chifukwa chiyani kuipa ndi imfa zikupitirirabe?’ Kupeza yankho la funso limeneli kungatithandize kuthetsa chifukwa chachiwiri choyambitsa kuipa, chomwe ndi kusazindikira chifuniro cha Mulungu.

Munthu Angayambe Kuchita Zabwino Akadziwa Zolondola

Kudziwa zolondola ponena za zimene Yehova ndi Yesu panopa akuchita pofuna kuthetseratu kuipa zingathandize munthu woona mtima kupewa kulekerera zoipa mosazindikira, ndiponso kupewa kukhala ‘wotsutsana ndi Mulungu.’ (Machitidwe 5:38, 39) Yehova Mulungu ndi wofunitsitsa kutikhululukira zoipa zonse zimene tinachita tisanazindikire. Poyankhula ku Atene, mtumwi Paulo anati: “Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima; chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa iye kwa akufa.”​—Machitidwe 17:30, 31.

Paulo anadziwa kuti Yesu waukitsidwa kwa akufa, popeza kuti Yesu woukitsidwa mwiniyo analankhula ndi Paulo ndipo anamuleketsa kuzunza Akristu. (Machitidwe 9:3-7) Pamene Paulo anangoti wauzidwa zinthu zolondola ponena za chifuniro cha Mulungu, anasintha ndi kukhala munthu wabwino kwambiri wotsanzira Kristu. (1 Akorinto 11:1; Akolose 3:9, 10) Ndiponso, Paulo analalikira mwakhama “uthenga uwu wabwino wa Ufumu.” (Mateyu 24:14) Kwa zaka 2,000 kuchokera pamene Yesu anafa ndi kuukitsidwa, Kristu wasankha anthu amene, monga Paulo, adzalamulira naye pamodzi mu Ufumu wake.​—Chivumbulutso 5:9, 10.

Kwa zaka zoposa 100, Mboni za Yehova zakhala zikukwaniritsa lamulo la Yesu lakuti: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Onse amene akumvera uthenga umenewu ali ndi mwayi wokhala ndi moyo kosatha padziko lapansi lolamulidwa ndi boma la kumwamba la Kristu. Yesu anati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Chinthu chabwino kwambiri chimene munthu angachitire mnzake ndicho kumuthandiza kudziwa zimenezi.

Onse amene avomereza uthenga wabwino wa Ufumu umenewu amakhala anthu a “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso” ngakhale kuti m’dzikoli mwadzaza zoipa. (Agalatiya 5:22, 23) Motsanzira Yesu, ‘samabwezera munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa.’ (Aroma 12:17) Payekhapayekha, amayesetsa ‘ndi chabwino kugonjetsa choipa.’​—Aroma 12:21; Mateyu 5:44.

Kugonjetseratu Kuipa

Paokha anthu sangagonjetseretu woyambitsa kuipa, Satana Mdyerekezi. Komabe, posachedwapa Yehova adzagwiritsa ntchito Yesu kuphwanya mutu wa Satana. (Genesis 3:15; Aroma 16: 20) Yehova adzalamulanso Kristu Yesu kuti ‘adzaphwanye ndi kutha’ maulamuliro andale onse, amene ambiri a iwo achititsa zoipa zambiri m’mbiri yonse ya anthu. (Danieli 2:44; Mlaliki 8:9) Mu tsiku lopereka chiweruzo limene likubweralo, onse “osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu . . . adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha.”​—2 Atesalonika 1:8, 9; Zefaniya 1:14-18.

Pambuyo pakuti Satana ndi onse omutsatira achotsedwa, Yesu adzathandiza opulumukawo kukonzanso dziko lapansi kuti libwerere mwakale. Adzachita zimenezi iye ali kumwamba. Kristu adzaukitsanso onse amene ali oyenerera kupatsidwa mwayi wodzakhala padziko lapansi, lomwe lidzakhale litakonzedwanso. (Luka 23:32, 39-43; Yohane 5:26-29) Potero, iye adzachotseratu zotsatirapo zina za kuipa kumene anthu akumana nako.

Yehova sadzaumiriza anthu kuti amvere uthenga wabwino wa Yesu. Komabe, iye akupatsa anthu mwayi wakuti azindikire zinthu molondola kuti apeze moyo. M’pofunika kuti mugwiritse ntchito mwayi umenewu panopa! (Zefaniya 2:2, 3) Ngati mutachita zimenezo, mungadziwe bwino mmene mungathanirane ndi mavuto alionse amene mumakumana nawo panopa. Mungazindikirenso mmene Yesu adzagonjetsere kuipa konse.​—Chivumbulutso 19:11-16; 20:1-3, 10; 21:3, 4.

[Chithunzi patsamba 5]

Paulo analekerera zoipa chifukwa chakuti samazindikira zinthu molondola

[Chithunzi patsamba 7]

Chinthu chabwino kwambiri chimene munthu angachitire mnzake ndicho kumuthandiza kudziwa Mulungu molondola