Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzisangalala Nako Kusinkhasinkha

Muzisangalala Nako Kusinkhasinkha

Muzisangalala Nako Kusinkhasinkha

ANTHU ena akaganiza zosinkhasinkha amaona ngati n’chinthu chovuta kwambiri. Amaona ngati kusinkhasinkha ndi chintchito chachikulu chofunika khama kwambiri. Anthu oterowo angamadziimbenso mlandu chifukwa choti akhala akunyalanyaza kuchita zimenezi, makamaka akamawerenga za kufunika kwake. (Afilipi 4:8) Komabe, kuganizira zinthu zoona zomwe taphunzira zokhudza Yehova, makhalidwe ake abwino kwambiri, zinthu zodabwitsa zomwe wachita, zimene amafuna, ndi cholinga chake chabwino kwambiri, kukhoza kukhala kosangalatsa ndipo kuyenera kutero. Chifukwa chiyani?

Yehova Mulungu ndiye Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse ndipo ali m’kati mokwaniritsa cholinga chake chachikulu. (Yohane 5:17) Ngakhale zili choncho, iye amachita chidwi ndi zimene akuganiza wolambira wake aliyense. Wamasalmo Davide ankadziwa zimenezi ndipo mouziridwa analemba kuti: “Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa. Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali.”​—Salmo 139:1, 2.

Poyamba, munthu wina akhoza kuona ngati mawu a wamasalmo amenewa ndi osalimbikitsa. Akhoza kuganiza kuti: ‘Ngakhale kuti Mulungu ali “kutali,” amaona maganizo oipa aliwonse amene amabwera m’mutu mwanga.’ N’zoona kuti nthawi zina ndi bwino kumaganizira zimenezo. Zingatithandize kuyesetsa kuti tisamaganize zinthu zolakwika, ndipo ngati titaganiza zolakwika, zingatithandize kuti tilape kwa Mulungu, tili ndi chikhulupiriro kuti atikhululukira chifukwa cha chikhulupiriro chathu mwa nsembe ya dipo ya Yesu. (1 Yohane 1:8, 9; 2:1, 2) Komabe, tiyeneranso kukumbukira kuti Yehova amayang’anitsitsa olambira ake n’cholinga chabwino. Amakhala nafe chidwi tikamaganizira za iye moyamikira.

Koma mwina mungafunse kuti: “Kodi Yehova amaonadi maganizo abwino onse a olambira ake ambirimbiri?” Iye amaterodi. Yesu anasonyeza kuti Yehova amakhaladi nafe chidwi pamene ananena kuti Yehova amaona ngakhale timpheta ting’onoting’ono, ndipo kenaka anawonjezera kuti: “[Inu] muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.” (Luka 12:6, 7) Mpheta sizingaganizire za Yehova. Choncho ngati amasamala za mpheta, tangoganizirani mmene amasamalira za ifeyo ndi mmene amasangalalira ndi maganizo abwino a aliyense wa ife! Zoonadi, mofanana ndi Davide, tingapemphere mwachidaliro kuti: “Maganizo am’mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.”​—Salmo 19:14.

Umboni wina wosonyeza kuti Yehova amachitadi chidwi ndi zosinkhasinkha za olambira ake okhulupirika timaupeza m’mawu ouziridwa a mneneri Malaki. Ponena za nthawi yathu ino, iye ananeneratu kuti: ‘Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira [“ndi kuganizira,” NW] dzina lake.’ (Malaki 3:16) Ngati tikumbukira kuti Yehova ‘amatchera khutu’ tikamaganizira za iyeyo, tikhoza kusangalaladi nako kusinkhasinkha. Choncho, tiyeni tizichita mogwirizana ndi mawu a wamasalmo amene analemba kuti: “Ndidzalingalira ntchito yanu yonse, ndi kulingalirabe zimene munazichita Inu.”​—Salmo 77:12.