Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kanizani Satana, Ndipo Iye Adzathawa!

Kanizani Satana, Ndipo Iye Adzathawa!

Kanizani Satana, Ndipo Iye Adzathawa!

“Mverani Mulungu; koma kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthawani inu.”​—YAKOBO 4:7.

1, 2. (a) Kodi mawu olembedwa mu Yesaya chaputala 14 amasonyeza khalidwe liti la Mdyerekezi? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

MDYEREKEZI ndiye chimake cha kudzitama. Kudzikuza kwake kumaoneka m’mawu amene analemba Yesaya, mneneri wa Mulungu. Zaka zoposa 100 Babulo asanakhale ulamuliro wamphamvu padziko lonse, Yesaya analemba mawu aulosi osonyeza anthu a Yehova akulankhula mawu otsutsa “mfumu ya ku Babulo.” Anati: “Iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu [mafumu a mzera wa Davide] . . . Ndidzafanana ndi Wam’mwambamwamba.” (Yesaya 14:3, 4, 12-15; Numeri 24:17) Kudzikuza kwa “mfumu ya ku Babulo” kunafanana ndi mzimu wa Satana, “mulungu wa nthawi ino ya pansi pano.” (2 Akorinto 4:4) Mzera wa mafumu a ku Babulo unatha mochititsa manyazi ndipo mofanana ndi zimenezi Satana naye adzakumana ndi zoopsa chifukwa cha kudzitama kwake.

2 Koma malinga ngati pali Mdyerekezi, tingamavutikebe ndi mafunso onga awa: Kodi Satana tizimuopa? N’chifukwa chiyani iye amasonkhezera anthu kuzunza Akristu? Kodi tingachite chiyani kuti Mdyerekezi asatichenjerere?

Kodi Mdyerekezi Tizimuopa?

3, 4. N’chifukwa chiyani Akristu odzozedwa pamodzi ndi anzawo samuopa Mdyerekezi?

3 Mawu otsatirawa, amene Yesu Kristu ananena, ndi olimbikitsa kwambiri kwa Akristu odzozedwa. Iye anati: “Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, Mdyerekezi adzaponya ena a inu m’nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.” (Chivumbulutso 2:10) Odzozedwa pamodzi ndi anzawo amene akuyembekeza kudzakhala padziko lapansi samuopa Mdyerekezi. Sikuti alibe mantha chifukwa chakuti ndi olimba mtima mwachibadwa. Koma n’chifukwa chakuti amaopa ndi kulemekeza Mulungu ndipo ‘amathawira ku mthunzi wa mapiko ake.’​—Salmo 34:9; 36:7.

4 Ophunzira a Yesu Kristu oyambirira analibe mantha ndipo anakhalabe okhulupirika mpaka imfa ngakhale anakumana ndi mavuto. Iwo sanaope zimene Satana Mdyerekezi akanatha kuwachita, chifukwa anadziwa kuti Yehova sataya anthu okhulupirika kwa Iye. Masiku anonso, ngakhale kuti Akristu odzozedwa ndi anzawo odzipereka amakumana ndi chizunzo choopsa, amalimbikira kuti asasiye kukhala okhulupirika kwa Mulungu. Ngakhale zili choncho, mtumwi Paulo anasonyeza kuti Mdyerekezi amatha kuchititsa imfa ya munthu. Kodi sitiyenera kuchita mantha chifukwa cha zimenezo?

5. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa lemba la Ahebri 2:14, 15?

5 Paulo ananena kuti Yesu ‘adalawa nawo mwazi ndi nyama’ kuti “mwa imfa [yake] akamuwononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa [“njira yochititsa imfa,” NW], ndiye Mdyerekezi; nakamasule iwo onse amene, chifukwa cha kuopa imfa, m’moyo wawo wonse adamangidwa ukapolo.” (Ahebri 2:14, 15) Chifukwa chokhala ndi “njira yochititsa imfa,” Satana analamulira Yudasi Isikariote ndipo kenako anagwiritsa ntchito atsogoleri a Ayuda ndiponso Aroma kupha Yesu. (Luka 22:3; Yohane 13:26, 27) Koma kudzera mu imfa yake yansembe, Yesu amamasula anthu ochimwa ku mphamvu ya Satana ndipo n’zotheka kuti ife tikhale ndi moyo wosatha.​—Yohane 3:16.

6, 7. Kodi Satana amachititsa imfa m’njira yotani?

6 Kodi Mdyerekezi amachititsa imfa m’njira yotani? Kuchokera pamene Satana anayamba ntchito zake zoipa, anthu amafa chifukwa cha mabodza ake ndi utsogoleri wake. Zili choncho chifukwa chakuti Adamu anachimwa ndipo anapatsira anthu onse uchimo ndi imfa. (Aroma 5:12) Ndiponso, atumiki a Satana padziko lapansi azunza olambira Yehova, nthawi zina mpaka kuwapha, ngati zimene anachita kwa Yesu Kristu.

7 Ngakhale zili choncho, tisaganize kuti Mdyerekezi angachititse imfa ya munthu aliyense amene iye akufuna kupha. Mulungu amateteza anthu Ake ndipo sangalole Satana kufafaniza kotheratu olambira onse oona padziko lapansi. (Aroma 14:8) N’zoona kuti Yehova amalola anthu ake onse kuzunzidwa, ndipo amalola ena kufa chifukwa cha zochita za Mdyerekezi. Koma Malemba amapereka chiyembekezo chabwino kwambiri chakuti anthu amene ali mu “buku la chikumbutso” la Mulungu adzauka kwa akufa, ndipo Mdyerekezi sangathe m’pang’ono pomwe kuletsa kuti anthuwa adzapezenso moyo!​—Malaki 3:16; Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.

N’chifukwa Chiyani Satana Amatizunza?

8. N’chifukwa chiyani Mdyerekezi amabweretsa chizunzo kwa atumiki a Mulungu?

8 Ngati ndife atumiki okhulupirika a Mulungu, pali chifukwa chimodzi chachikulu chimene Mdyerekezi amatizunzira. Cholinga chake n’chakuti ife titaye chikhulupiriro chathu. Ife tili ndi ubwenzi wabwino kwambiri ndi Atate wathu wa kumwamba, ndipo Satana akufuna kuwononga ubwenzi wathuwo. Zimenezi siziyenera kutidabwitsa ayi. Mu Edene, Yehova analosera kuti padzakhala udani pakati pa “mkazi” wake wophiphiritsa ndi “njoka” ndiponso pakati pa “mbewu” zawo. (Genesis 3:14, 15) Malemba amati Mdyerekezi ndiye “njoka yokalambayo” ndipo amanena kuti panopa kam’tsalira kanthawi ndipo ali ndi udani waukulu. (Chivumbulutso 12:9, 12) Pamene udani pakati pa “mbewu” ziwirizo ukupitirira, anthu amene akutumikira Yehova mokhulupirika ayembekeze kuzunzidwa. (2 Timoteo 3:12) Kodi mukudziwa chifukwa chachikulu chimene Satana amabweretsera chizunzo?

9, 10. Kodi Mdyerekezi wabutsa nkhani yotani, ndipo khalidwe la anthu likukhudzana bwanji ndi nkhaniyo?

9 Mdyerekezi wabutsa nkhani yoti ndani ayenera kulamulira chilengedwe chonse. Nkhani inanso n’njakuti iye amakayikira ngati anthufe tingakhale okhulupirika kwa Mlengi wathu. Satana anazunza munthu wolungama Yobu. N’chifukwa chiyani anatero? Anafuna kuti Yobu asiye kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Panthawi imeneyo, mkazi wa Yobu pamodzi ndi anzake a Yobu atatu ‘otonthoza mtima olemetsa’ anatumikira Mdyerekezi. Malinga ndi zimene buku la Yobu limanena, Mdyerekezi anatsutsa Mulungu, ndipo anati munthu aliyense sangakhale wokhulupirika kwa Iye ngati angalole Satana kuyesa munthuyo. Koma Yobu anakhalabe wokhulupirika, ndipo Satana anapezeka wabodza. (Yobu 1:8–2:9; 16:2; 27:5; 31:6) Mdyerekezi amazunza Mboni za Yehova masiku ano pofuna kuwononga kukhulupirika kwawo kuti asonyeze kuti zonena zake n’zoona.

10 Kudziwa kuti Mdyerekezi amatibweretsera chizunzo poyesetsa kuti tisiye kukhala okhulupirika kwa Mulungu, kumatithandiza kukhala olimba mtima ndi olimbikira. (Deuteronomo 31:6) Mulungu wathu ndiye Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, ndipo amatithandiza kukhalabe okhulupirika. Ndiyetu tiyeni nthawi zonse tiyesetse kukondweretsa mtima wa Yehova mwa kukhala okhulupirika. Ndipo tikatero, tidzam’patsa yankho loti apereke kwa Satana Mdyerekezi, mkulu wa otonza.​—Miyambo 27:11.

“Mutipulumutse kwa Woipayo”

11. Kodi pempho lakuti “Musatitengere kokatiyesa,” limatanthauza chiyani?

11 Kukhala wokhulupirika si nkhani yamasewera, chifukwa kumafuna kupemphera kwambiri. Ndipo pemphero la chitsanzo limathandiza kwambiri pa nkhani imeneyi. Mwa zina, Yesu ananena kuti: “Musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.” (Mateyu 6:13) Sikuti Yehova amatiyesa kuti tichimwe. (Yakobo 1:13) Ngakhale zili choncho, Malemba nthawi zina amanena ngati kuti iye ndi amene akuchita kapena kuchititsa zinazake, pamene kwenikweni, iye amangolola zinthuzo. (Rute 1:20, 21) Ndiye tikamapemphera malinga ndi zimene Yesu ananena, timakhala tikupempha Yehova kuti asatisiye pamene tikuyesedwa. Ndipotu iye sangatisiye, chifukwa Malemba amatilonjeza kuti: “Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.”​—1 Akorinto 10:13.

12. N’chifukwa chiyani timapemphera kuti: “Mutipulumutse kwa woipayo”?

12 Atanena za kuyesedwa m’pemphero la chitsanzo, Yesu moyenerera anati: “Mutipulumutse kwa woipayo.” Pamenepa, Mabaibulo ena amanena kuti: “Mutipulumutse ku zoipa” (King James Version; Revised Standard Version) kapena “Mutiteteze ku zoipa.” (Contemporary English Version) Komabe, Malemba akamatchula mawu akuti ‘kupulumutsa,’ amakhala makamaka akunena za anthu, ndipo Uthenga Wabwino wa Mateyu umanena za Mdyerekezi kuti ndiye “woyesayo,” munthu wauzimu. (Mateyu 4:3, 11) Choncho tifunika kupemphera kuti Mulungu atipulumutse kwa “woipayo,” Satana Mdyerekezi. Iyeyu amayesa kutinyengerera kuti tichimwire Mulungu. (1 Atesalonika 3:5) Tikamapemphera kuti, “Mutipulumutse kwa woipayo,” timakhala tikupempha Atate wathu wa kumwamba kuti atitsogolere ndi kutithandiza kotero kuti Mdyerekezi asatichenjerere.

Mdyerekezi Asakuchenjerereni

13, 14. N’chifukwa chiyani Akorinto anafunikira kusintha zochita zawo kwa munthu amene anali wachiwerewere mu mpingo?

13 Polimbikitsa Akristu a ku Korinto kuti azikhululuka, Paulo analemba kuti: “Amene mum’khululukira kanthu, inenso nditero naye; pakuti chimene ndakhululukira inenso, ngati ndakhululukira kanthu, ndachichita chifukwa cha inu, pamaso pa Kristu; kuti asatichenjerere Satana; pakuti sitikhala osadziwa machenjerero ake.” (2 Akorinto 2:10, 11) Mdyerekezi angatichenjerere m’njira zambiri. Koma n’chifukwa chiyani Paulo ananena mawu amene tawagwirawa?

14 Paulo anali atadzudzula Akorinto chifukwa chakuti iwo analola munthu wachiwerewere kukhalabe mu mpingo. Satana ayenera kuti anasangalala kwambiri, chifukwa mbiri ya mpingowo inaipa chifukwa cholekerera “chigololo chotere chonga sichimveka mwa amitundu.” Patapita nthawi, munthu wolakwayo anachotsedwa mu mpingo. (1 Akorinto 5:1-5, 11-13) Munthuyo analapa pambuyo pake. Akorintowo akanakana kukhululuka ndi kum’bwezeretsa munthuyo, Mdyerekezi akanawachenjerera mwa njira ina. Njira yake iti? Iwo akanakhala ouma mtima ndi opanda chifundo, ngati Satana mwini wakeyo. Munthu wolapayo akanakhala kuti ‘wamizidwa ndi chisoni chochuluka’ n’kusiyiratu kulambira, akulu makamaka akanakhala ndi mlandu ndithu kwa Yehova, Mulungu wachifundo. (2 Akorinto 2:7; Yakobo 2:13; 3:1) Kunena zoona, Mkristu woona aliyense safuna kutsanzira Satana mwa kukhala wankhanza, wouma mtima, ndi wopanda chifundo.

Kutetezedwa ndi Zida za Mulungu

15. Kodi tili pankhondo yotani, ndipo tiyenera kuchita chiyani kuti tipambane?

15 Kuti tipulumutsidwe kwa Mdyerekezi, tiyenera kumenya nkhondo yauzimu yolimbana ndi makamu a mizimu yoipa. Popeza kuti adani athuwo ali ndi mphamvu kwambiri, tiyenera kuvala “zida zonse za Mulungu” kuti tipambane nkhondoyo. (Aefeso 6:11-18) Zida zakezo zikuphatikizapo “chapachifuwa cha chilungamo.” (Aefeso 6:14) Mfumu Sauli ya Israyeli wakale sinamvere Mulungu ndipo mzimu woyera unaichokera. (1 Samueli 15:22, 23) Koma tikamachita chilungamo ndi kuvala zida zonse zauzimu, tidzakhala ndi mzimu woyera wa Mulungu. Tidzatetezekanso kwa Satana ndi angelo ake oipa, kapena kuti ziwanda zake.​—Miyambo 18:10.

16. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhalebe otetezeka ku makamu a mizimu yoipa?

16 Zina mwa zinthu zimene tiyenera kuchita kuti tikhalebe otetezeka ku makamu a mizimu yoipa, ndizo kuwerenga ndi kuphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse. Inde, kugwiritsa ntchito bwino zofalitsa zimene amapereka “mdindo wokhulupirika.” (Luka 12:42) Tikatero, tidzakhala tikumalowetsa zinthu zabwino zauzimu m’maganizo mwathu. Zimenezi zikugwirizana ndi langizo la Paulo lakuti: “Abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.”​—Afilipi 4:8.

17. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhala alaliki ogwira mtima a uthenga wabwino?

17 Yehova amatithandiza ‘kudziveka mapazi athu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere.’ (Aefeso 6:15) Kutenga nawo mbali m’misonkhano yachikristu nthawi zonse, kumatithandiza kukonzekera kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Tikamathandiza ena kudziwa choonadi cha Mulungu ndi kupeza ufulu wauzimu, timasangalala kwambiri. (Yohane 8:32) ‘Lupanga la Mzimu, limene lili Mawu a Mulungu,’ limathandiza kwambiri kupherera ziphunzitso zonama ndi ‘kupasula malinga.’ (Aefeso 6:17; 2 Akorinto 10:4, 5) Kugwiritsa ntchito mwaluso Baibulo, lomwe lili Mawu a Mulungu olembedwa, kumatithandiza kuphunzitsa choonadi ndipo kumatiteteza kuti Mdyerekezi asatigonjetse ndi machenjera ake.

18. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti ‘tichirimike pokana machenjerero a Mdyerekezi’?

18 Paulo anayamba nkhani yake yofotokoza zida zathu zauzimu ndi mawu akuti: “Tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m’kulimba kwa mphamvu yake. Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.” (Aefeso 6:10, 11) Liwu lachigiriki limene analimasulira kuti “kuchirimika” limanena za msilikali amene waima nji, osasunthika pamalo ake. Ifetu timaima nji pankhondo yathu yauzimu, ngakhale kuti Satana amagwiritsa ntchito machenjera amitundumitundu pofuna kusokoneza umodzi wathu, kuwononga ziphunzitso zathu kapenanso kukhulupirika kwathu kwa Mulungu. Koma mpaka pano Mdyerekezi sanapambane kuchita zimenezi, ndipo sadzapambana! *

Kanizani Mdyerekezi, Ndipo Iye Adzathawa

19. Kodi njira imodzi imene tingalimbanirane ndi Mdyerekezi ndi iti?

19 Tingathe kupambana nkhondo yathu yauzimu yolimbana ndi Mdyerekezi ndiponso makamu a mizimu yoipa amene iye akuwatsogolera. Palibe chifukwa chonjenjemerera ndi mantha poopa Satana, pakuti mtumwi Yakobo analemba kuti: “Mverani Mulungu; koma kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthawani inu.” (Yakobo 4:7) Njira imodzi imene tingalimbanirane ndi Satana ndi mizimu yoipa imene ikugwirizana naye ndiyo kupeweratu zamizimu kapena zamatsenga ndiponso anthu amene amachita zinthu zimenezo. Malemba amasonyeza bwino kuti atumiki a Yehova amakaniratu malaulo kapena kukhulupirira nyenyezi, kuombeza maula, ndi kukhulupirira mizimu. Ngati timachita khama ndiponso ndife olimba pa zinthu zauzimu, sitiyenera kuchita mantha kuti winawake atilodza.​—Numeri 23:23; Deuteronomo 18:10-12; Yesaya 47:12-15; Machitidwe 19:18-20.

20. Kodi tingam’kanize bwanji Mdyerekezi?

20 ‘Timakaniza Mdyerekezi’ ngati nthawi zonse timatsatira makhalidwe ndiponso choonadi cha m’Baibulo ndi kum’tsutsa zolimba Mdyerekeziyo. Dziko limagwirizana ndi Satana chifukwa chakuti iye ndiye mulungu wa dzikoli. (2 Akorinto 4:4) N’chifukwa chake ife timakana makhalidwe a dzikoli monga kudzikuza, kudzikonda, chiwerewere, chiwawa, ndi kukonda chuma. Tikudziwa kuti Mdyerekezi anathawa pamene Yesu anam’kaniza mwa kugwiritsa ntchito Malemba pamene anali kuyesedwa m’chipululu. (Mateyu 4:4, 7, 10, 11) Ifenso Satana adzatilephera ‘n’kutithawa’ ngati titagonjera Yehova m’zinthu zonse ndi kum’dalira mwa mapemphero. (Aefeso 6:18) Popeza kuti Yehova Mulungu ndi Mwana wake wokondedwa ali nafe, palibe amene angativulaze kosatha, ngakhale Mdyerekezi weniweniyo!​—Salmo 91:9-11.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Kuti mudziwe zambiri zokhudza zida zauzimu za Mulungu, onani Nsanja ya Olonda ya May 15, 1992, masamba 21 mpaka 23.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi Satana Mdyerekezi tizimuopa?

• N’chifukwa chiyani Satana amabweretsa chizunzo pa Akristu?

• N’chifukwa chiyani timapemphera kuti Mulungu atipulumutse kwa “woipayo”?

• Kodi chofunika n’chiyani kuti tipambane nkhondo yauzimu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 26]

Ophunzira a Kristu oyambirira analibe mantha ndipo anakhalabe okhulupirika mpaka imfa

[Chithunzi patsamba 27]

Mdyerekezi sangalepheretse kuuka kwa anthu amene Yehova akuwakumbukira

[Chithunzi patsamba 28]

Kodi mumapemphera kuti Mulungu akupulumutseni kwa “woipayo”?

[Chithunzi patsamba 29]

Kodi mwavala “zida zonse za Mulungu”?