Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Angelo Ndani?

Kodi Angelo Ndani?

Kodi Angelo Ndani?

MFUMU ya ufumu wamphamvu kwambiri sinakhulupirire zimene inali kuona. Amuna atatu omwe anawalamula kuti aphedwe m’ng’anjo ya moto anali atapulumutsidwa ku imfa yochititsa manthayo. Kodi ndani anawapulumutsa? Mfumuyi inauza anthu opulumukawo kuti: “Alemekezedwe [Mulungu wanu], amene anatuma mthenga wake, napulumutsa atumiki ake om’khulupirira iye.” (Danieli 3:28) Mfumu ya Babuloyi, imene inakhalapo zaka zoposa 2000 zapitazo, inadzionera yokha mngelo atapulumutsa anthu. Anthu ambiri kalelo ankakhulupirira angelo. Masiku ano anthu ambiri amakhulupirira kuti angelo alipo, komanso amadziwa kuti angelowo amakhudza moyo wawo m’njira inayake. Kodi angelo ndani, ndipo kodi anakhalako bwanji?

Baibulo limanena kuti, angelo ndi mizimu monga Mulungu. (Salmo 104:4; Yohane 4:24) Angelo alipo ambiri kwabasi moti amatha kukwana mamiliyoni ambirimbiri. (Chivumbulutso 5:11) Ndiponso angelo onse ali ndi “mphamvu zolimba.” (Salmo 103:20) Ngakhale kuti angelo ali ndi umunthu ndiponso anapatsidwa mwayi wosankha zinthu, iwo sanawalenge ngati anthu. Ndipotu, Mulungu analenga angelo kalekale anthu asanakhaleko, ngakhale dziko lapansili asanalilenge. Baibulo limati, pamene Mulungu ‘anaika maziko a dziko lapansi, nyenyezi za m’mawa [kapena kuti angelo] zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe.’ (Yobu 38:4, 7) Popeza kuti Mulungu ndiye analenga angelo, iwo amatchedwa ana a Mulungu.

Kodi Mulungu analenga angelo n’cholinga chotani? Kodi ndi ntchito yotani, ngati ilipo n’komwe, imene angelo akhala akugwira pamoyo wa anthu? Kodi angelo amakhudza moyo wathu panopa? Popeza kuti angelo anawalenga ndi ufulu wosankha zochita, kodi pali angelo ena amene anatsatira Satana Mdyerekezi n’kudzipanga kukhala adani a Mulungu? Baibulo lili ndi mayankho oona a mafunso amenewa.