Chuma Chenicheni Chidzakhala M’dziko Latsopano la Mulungu
Chuma Chenicheni Chidzakhala M’dziko Latsopano la Mulungu
DAVID, * ndi bambo wachikristu wokwatira, yemwenso ali ndi ana. Iyeyu anasamukira ku United States ndipo panthawiyo ankangoona kuti palibe cholakwika potero. Sanasangalale kuti anasiya mkazi ndi ana ake, komano ankaona kuti kumene akupitako akapanga ndalama zambiri zomwe zidzatukule moyo wa banja lakelo. Motero achibale ake atamuitana ku New York iye anavomera ndipo posakhalitsa anapeza ntchito kumeneko.
Koma David atakhala kumeneko kwa kanthawi, zinthu zinam’sinthira. Anapezeka kuti ali ndi nthawi yochepa yochitira zinthu zauzimu. Panthawi ina, iye anangotsala pang’ono kutaya chikhulupiriro chake mwa Mulungu. Pamene anachita zosayenera m’pamene anazindikira
kuti anali atalowerera kwambiri. Mwapang’onopang’ono iye anayamba kuiwala zinthu zimene zinali zofunika kwambiri kwa iye chifukwa chofunitsitsa chuma. Anafunikira kusintha.Monga David, chaka chilichonse pali anthu ambiri omwe amasamuka kwawo pofuna kupeza bwino. Koma nthawi zambiri anthuwa amataya zinthu zomwe zili zofunika kwambiri pa moyo wawo wauzimu. N’chifukwa chake anthu ena amadzifunsa kuti, ‘Kodi Mkristu angathe kukhala wandalama komanso n’kukhala wolemera kwa Mulungu?’ Olemba mabuku ndiponso abusa ambiri otchuka amati n’zotheka. Koma monga mmene David ndi anthu enanso anaonera, m’povuta kukhala ndi zinthu ziwiri zonsezi nthawi imodzi.—Luka 18:24.
Ndalama Si Zoipa
Tikudziwa kuti ndalama zimapangidwa ndi anthu ndipo monga zinthu zambiri zopangidwa ndi anthu, ndalamazo pazokha si zoipa ayi. Ndalama ndi chinthu chothandiza posinthitsana zinthu basi. Motero, tikazigwiritsa ntchito bwino, ndalama zingatithandize kwambiri. Mwachitsanzo, Baibulo limavomereza kuti “ndalama zichinjiriza” makamaka ku mavuto obwera chifukwa cha umphawi. (Mlaliki 7:12) Koma zikuoneka kuti pali anthu ena amene amaona kuti “chilichonse chimatheka ndi ndalama.”—Mlaliki 10:19, New International Version.
Malemba amaletsa khalidwe la ulesi ndipo amalimbikitsa khalidwe lolimbikira ntchito. Tiyenera kusamalira mabanja athu, ndipo ngati tingathe tiyeneranso ‘kuchereza wosowa.’ (Aefeso 4:28; 1 Timoteo 5:8) Ndiponsotu, Baibulo sililimbikitsa kuti tizikhala anthu osasangalala, koma limalimbikitsa kuti tizisangalala ndi zinthu zomwe tili nazo. Limatiuza kuti ‘tizilandira gawo lathu’ ndi kusangalala ndi ntchito ya manja athu. (Mlaliki 5:18-20) Kwenikweni, m’Baibulo muli zitsanzo zosiyanasiyana za amuna ndi akazi okhulupirika amene anali olemera.
Anthu Okhulupirika Amene Anali Olemera
Abrahamu, anali mtumiki wokhulupirika wa Mulungu ndipo iyeyu anali ndi ng’ombe, nkhosa, siliva ndi golidi wambirimbiri, komanso anali ndi antchito mahandiredi angapo. (Genesis 12:5; 13:2, 6, 7) Yobu, yemwe anali munthu wolungama, nayenso anali ndi zinthu zambiri monga ziweto, antchito, golidi ndiponso siliva. (Yobu 1:3; 42:11, 12) Ngakhale titatengera pa moyo wa masiku ano, anthu amenewa anali olemera ndithu. Komatu analinso olemera kwa Mulungu.
Mtumwi Paulo anatchula Abrahamu kuti “kholo la onse akukhulupira.” Abrahamu sankaumira kapena kukondetsa chuma chake. (Aroma 4:11; Genesis 13:9; 18:1-8) Chimodzimodzinso Yobu. Mulungu ananena kuti Yobu anali “wangwiro ndi woongoka.” (Yobu 1:8) Yobu anali wokonzeka nthawi zonse kuthandiza osauka ndi ozunzika. (Yobu 29:12-16) Abrahamu ndi Yobu ankakhulupirira Mulungu osati chuma chawocho.—Genesis 14:22-24; Yobu 1:21, 22; Aroma 4:9-12.
Chitsanzo china ndi cha Mfumu Solomo. 1 Mafumu 3:4-14) Kwa nthawi yaitali pa moyo wake, iye anali wokhulupirika. Koma cha kumapeto kwa moyo wake, “mtima wake sunakhala wangwiro ndi Yehova.” (1 Mafumu 11:1-8) Kwenikweni, nkhani yake yomvetsa chisoniyi imasonyeza mavuto ena ofala a chuma. Tatiyeni tionepo ena mwa mavutowa.
Atalowa mpando wachifumu wa Mulungu ku Yerusalemu, anadalitsidwa popatsidwa nzeru zochokera kwa Mulungu komanso chuma ndi ulemerero wochuluka. (Mavuto a Chuma
Vuto lalikulu kwambiri ndilo kuyamba kukonda ndalama ndiponso zinthu zimene ndalamazo zimagula. Chifukwa cha chuma, anthu ena amakhala ndi mtima wosakhutira. Kumayambiriro kwa ulamuliro wake, Solomo anaona kuti anthu ena anali ndi mtima wotere. Iye analemba kuti: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.” (Mlaliki 5:10) Pambuyo pake, Yesu ndiponso Paulo anachenjeza Akristu za chikondi chosocheretsa munthuchi.—Marko 4:18, 19; 2 Timoteo 3:2.
Tikayamba kukonda kwambiri ndalama n’kufika posiya kuziona ngati chinthu chongotithandiza pa zinthu zina ndi zina chabe, zimakhala zosavuta kuti tigwe m’ziyeso zosiyanasiyana, monga kunama, kuba, ndiponso chinyengo. Yudase Isikariote, yemwe anali mmodzi wa atumwi a Kristu, anapereka mbuye wakeyu ndi marupiya atheka mazana atatu. (Marko 14:11; Yohane 12:6) Anthu ena achita kufika pokonda kwambiri ndalama moti Mulungu amamuponyera kutali. (1 Timoteo 6:10) Motero Akristu nthawi zonse ayenera kuganizira moona mtima zifukwa zenizeni zimene akufunira kukhala ndi ndalama zambiri.—Ahebri 13:5.
Kufuna ndalama kumabweretsanso mavuto ena osaonekera kwambiri. Vuto loyamba n’lakuti munthu akakhala ndi chuma chambiri amayamba kudzidalira kwambiri. Vuto limeneli lili m’gulu la zinthu zimene Yesu anazitcha kuti “chinyengo cha chuma.” (Mateyu 13:22) Yakobo nayenso anachenjeza Akristu kuti asamaiwale Mulungu ngakhale pa nkhani za malonda amene iwo akuganizira kuchita. (Yakobo 4:13-16) Popeza kuti ndalama zimaoneka kuti zimatipatsa ufulu winawake, anthu amene ali ndi ndalama nthawi zonse ayenera kuchenjera kuti asayambe kudalira ndalama zawozo kusiya Mulungu.—Miyambo 30:7-9; Machitidwe 8:18-24.
Chachiwiri n’chakuti, monga anaonera David amene tam’tchula koyambirira uja, kufunafuna ndalama nthawi zambiri kumawonongetsa mphamvu ndiponso nthawi yambiri ya munthu moti pang’onopang’ono amatalikirana ndi zinthu zauzimu. (Luka 12:13-21) Anthu olemera, amakhalanso pa chiyeso chofuna kuti chuma chawo azingosangalala nacho basi kapena azichitira zakumtima kwawo.
N’zotheka kuti chinthu china chimene chinasokoneza Solomo mwauzimu n’chakuti analola moyo wapamwamba kumuiwalitsa zinthu zauzimu. (Luka 21:34) Iye ankadziwa bwinobwino lamulo la Mulungu lonena mosapita m’mbali kuti n’kulakwa kukwatirana ndi anthu amitundu. Koma iye anatenga akazi akunja pafupifupi 1,000. (Deuteronomo 7:3) Pofuna kusangalatsa akazi ake akunjawo, iye anayamba kuchita zinthu zophatikiza chipembedzo. Monga tanena kale, mtima wa Solomo unakhota motero anasiya kulambira Yehova m’njira yowongoka.
N’zoonekeratu kuti zitsanzo zimenezi zikugwirizana ndi malangizo a Yesu akuti: “Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.” (Mateyu 6:24) Motero, kodi Mkristu angalimbane bwanji ndi mavuto a zachuma amene anthu ambiri akukumana nawo masiku ano? Komanso funso lofunika kwambiri n’lakuti kodi tingayembekeze zotani m’tsogolo?
Chuma Chenicheni Chili M’tsogolo
Mosiyana ndi makolo akale monga Abrahamu ndi Yobu ndiponso mtundu wa Israyeli, otsatira a Yesu ali ndi udindo ‘wophunzitsa anthu a mitundu yonse.’ (Mateyu 28:19, 20) Kuti tikwaniritse udindo umenewu pamafunika kuti tisawononge nthawi yathu ndiponso khama lathu pochita zinthu zakuthupi. Motero, chinthu chofunika kwambiri kuti zinthu zitiyendere bwino ndicho kuchita zimene Yesu anatiuza, zoti: “Koma muthange mwafuna Ufumu [wa Mulungu] ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mateyu 6:33.
David anangotsala pang’ono kutaya banja lake,
chikhulupiriro chake ndiponso ubwenzi wake ndi Mulungu, koma mapeto ake iye anakonza moyo wake. Monga Yesu analonjezera, David atasintha moyo wake n’kuyamba kulimbikira kwambiri zinthu monga kuwerenga Baibulo, kupemphera, ndiponso kulalikira, zinthu zina zonsezo zinayambanso kumuyendera bwino. Mpaka anafika poyambanso kugwirizana kwambiri ndi mkazi wake komanso ana ake. Anayambanso kukhala wosangalala ndiponso wokhutira. Panopa amalimbikirabe ntchito yake koma si kuti anachoka muumphawi n’kufika pokhala ndi chuma chadzaoneni ayi. Komabe, anaphunzira zambiri pa mavuto amene anakumana nawo.David akuona kuti analakwitsa kusamukira ku United States, ndipo akutsimikiza kuti sadzalolanso kuti ndalama zizimulamulira. Iyeyu wadziwa kuti ndalama sungagulire zinthu zomwe zili zofunika kwambiri pamoyo, monga banja ndiponso anzako okukonda, komanso ubwenzi wabwino ndi Mulungu. (Miyambo 17:17; 24:27; Yesaya 55:1, 2) Inde, khalidwe labwino n’lofunika kwambiri kuposa chuma. (Miyambo 19:1; 22:1) David pamodzi ndi anthu a m’banja mwake onse n’ngotsimikiza kuika zinthu zofunika patsogolo.—Afilipi 1:10.
Anthu ayesa umu ndi umu kuchita zinthu zothandiza kuti anthufe tikhale achuma komanso amakhalidwe abwino, koma akanika. Mulungu analonjeza kuti Ufumu wake udzatipatsa zinthu zonse zofunikira kuti tikhale ndi moyo wabwino. (Salmo 72:16; Yesaya 65:21-23) Yesu anaphunzitsa kuti tikamakonda zinthu zauzimu m’pamene timakhaladi moyo wabwino. (Mateyu 5:3) Motero, kaya ndife olemera kapena osauka, njira yabwino kwambiri yokonzekera dziko latsopano la Mulungu lomwe likubwerali ndiyo kulimbikira kwambiri kuchita zinthu zauzimu. (1 Timoteo 6:17-19) Dziko limenelo lidzakhala lachuma chadzaoneni chakuthupi komanso chauzimu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 Dzinali talisintha.
[Zithunzi patsamba 5]
Yobu anakhulupirira Mulungu osati chuma chake
[Zithunzi patsamba 7]
Ndalama sungagulire zinthu zomwe zili zofunikira kwambiri pamoyo