“Kodi Kansalu Kapepoka Kamatanthauza Chiyani?”
“Kodi Kansalu Kapepoka Kamatanthauza Chiyani?”
“MASIKU angapo apitawo, munthu wina wa Mboni za Yehova anandipatsa magazini ya Nsanja ya Olonda,” analemba motero mwamuna wina wogwira ntchito ku unduna wa zachilungamo mu mzinda wa Seoul, m’dziko la Korea. Anapitiriza kuti: “M’magaziniyo, ndinaphunziramo nkhani yonena za mmene Mboni za Yehova zinazunzidwira mu ulamuliro wa chipani cha Nazi ndiponso wa Chikomyunizimu. Koma ndili ndi funso. Pachikuto cha magaziniyi pali chithunzi cha Mboni za Yehova zitavala malaya omwe kumanzere kwake anasokererako kansalu kapepo. Kodi kansalu kapepoka kamatanthauza chiyani?”
Panthawi ya ulamuliro wa chipani cha Nazi ku Germany, Mboni za Yehova zinakana kunena mawu otamanda Hitler, ndiponso sizinkalowa nawo m’ndale ngakhalenso kupita nawo ku nkhondo. Choncho Mbonizi zinazunzidwa mwankhaza ndi a Nazi, ndipo zina zokwana 12,000 zinamangidwa n’kuikidwa m’ndende zozunzirako anthu komwe zinakhalako nthawi zosiyanasiyana. Mboni zokwana pafupifupi 2,000 zinafa, ndipo zambiri mwa izo zinachita kunyongedwa.
Kodi kansalu kapepo komwe ankasokerera pa zovala za akaidi kankatanthauza chiyani? Buku lakuti Anatomy of the SS State linafotokoza kuti: “Magulu osiyanasiyana a akaidi m’makampu a [Nazi] ankakhala ndi zizindikiro, ndipo mchitidwewu unayambika nkhondo isanayambe. Pachovala cha mkaidi aliyense, ankasokererapo kansalu kamakona atatu, ndipo mtundu wa kansaluko unkakhala wogwirizana ndi gulu limene mkaidiyo ali: pamalaya a akaidi a zandale, ankasokererapo kansalu kofiira; Mboni za Yehova, kansalu kapepo; akaidi omwe anamangidwa chifukwa cha makhalidwe ena oipa, kansalu kakuda; zigawenga, kansalu kobiriwira; anthu ogonana amuna kapena akazi okhaokha, kansalu kapinki; alendo m’dzikolo, kansalu kabluu. Pamwamba pa kansalu kamtundu womwe ankasokerera pamalaya a akaidi achiyuda, ankasokererapo kansalu kena kachikasu kamakonanso atatu ndipo tinsaluto ankatisokerera moti tizioneka ngati Nyenyezi ya Davide.”
Pulofesa John K. Roth m’buku lake lakuti Holocaust Politics analemba kuti: “Ngati m’tsogolomu anthu angamakumbukirebe tanthauzo la kachizindikiro kapepo kameneka, zingatithandize kuti tisadzaonenso tsoka lina. Kachizindikiro kameneka kangatithandize kuti tisaiwale udindo wathu woteteza khalidwe labwino kwambiri lofunika kwa anthu.” Mboni za Yehova zinatulutsa vidiyo yakuti Jehovah’s Witnesses Stand Firm Against Nazi Assault imene zinapata nayo mphoto. Bwanji osapempha wa Mboni za Yehova kuti akonze zoti muonere vidiyoyi?