Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Timafunikira Mesiya?

Kodi Timafunikira Mesiya?

Kodi Timafunikira Mesiya?

N’KUTHEKA kuti inu muli ndi funso lakuti, “Kodi timafunikira Mesiya?” M’pomveka ndithu kufuna kudziwa ngati zochita za Mesiya zingakhudzedi moyo wanu.

Anthu ena amene mwina simungatsutse zonena zawo angathe kukutsimikizirani kuti yankho la funso limeneli n’lachidziwikire ndiponso n’lotsimikizirika. Iwo angakuuzeni kuti: Mumafunikiradi Mesiya, ngati mmene zilili ndi munthu wina aliyense. Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, katswiri wina wa malamulo a Ayuda anafotokoza motere za Mesiya: “Ngakhale malonjezo a Mulungu atachuluka chotani, onsewo ndi ‘Inde’ mwa Khristu.” Pamenepa, iye anasonyeza udindo wofunika kwambiri wa Mesiya pa cholinga cha Mlengi wathu chodalitsa mitundu yonse ya dziko lapansi. (2 Akorinto 1:20, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Udindo wa Mesiyayu ndi waukulu kwambiri moti m’maulosi a m’Baibulo, nkhani yaikulu ndi ya kufika kwake ndiponso moyo wake. M’buku lina lomwe lawerengedwa ndi anthu mamiliyoni ambiri m’zaka 70 zapitazi, Henry H. Halley anati: “Chipangano Chakale chinalembedwa kuti chichititse anthu kuyembekezera ndiponso kukonzekera Kubwera kwa [Mesiya].” Koma kodi kubwera kwakeko n’kofunika? N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala nako ndi chidwi?

Kwenikweni, mawu oti “Mesiya” amatanthauza “Wodzozedwa” ndipo ndi ofanana ndi mawu otchuka akuti “Kristu.” Ameneyu, yemwe buku la Encyclopædia Britannica, 1970 Edition, limamutcha “muwomboli wamkulu koposa,” anafunika kubwera chifukwa cha kusalingalira bwino kwa anthu awiri oyambirira, Adamu ndi Hava. Iwo analengedwa angwiro, ndipo anali ndi chiyembekezo chosangalatsa kwambiri chokhala m’Paradaiso kwamuyaya, koma anataya mwayi umenewo. Mngelo wina wopanduka, amene anadzadziwika ndi dzina loti Satana Mdyerekezi, anawauza kuti Mlengi wawo anali kukhwimitsa zinthu kwambiri ndipo anati iwo angamakhale moyo wabwino atamadzisankhira okha chabwino ndi choipa.​—Genesis 3:1-5.

Hava ananyengeka n’kukhulupirira bodza limenelo. Zikuoneka kuti Adamu anaona kuti ubwenzi ndi mkazi wake unali wofunika kwambiri kuposa kukhala wokhulupirika kwa Mulungu, motero anagwirizana ndi kupanduka komwe Mdyerekezi anayambitsa. (Genesis 3:6; 1 Timoteo 2:14) Zochita zawo zinawatayitsa chiyembekezo chokhala kwamuyaya m’paradaiso. Kuwonjezera pamenepo, iwo anasiyira mbadwa zawo, zomwe panthawiyi zinali zisanabadwe, uchimo ndi imfa, yomwe inabwera chifukwa cha uchimowo.​—Aroma 5:12.

Nthawi yomweyo, Mlengi wathu, Yehova, anakonza njira yodzathetsera zotsatirapo zoipa zimene kupandukako kunayambitsa. Kuyanjananso ndi anthu kukanatheka mwa mfundo ya zamalamulo yomwe pambuyo pake inadzaikidwa m’Chilamulo cha Mose. Mfundoyi mwa zina inkafuna moyo kulipa moyo. (Deuteronomo 19:21; 1 Yohane 3:8) Mfundo imeneyi inafunika kukwaniritsidwa kuti mbadwa zovutika za Adamu ndi Hava zidzapeze moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi, monga momwe Mlengi ankafunira poyamba. Pamenepa m’pamene panafunikira Mesiya.

Popereka chigamulo kwa Mdyerekezi, Yehova Mulungu anafotokoza izi mu ulosi woyambirira wa m’Baibulo: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:15) Katswiri wina wa maphunziro a Baibulo ananena kuti “nkhani ya malonjezo a m’Malemba onena za Mesiya imayambira pa mawu [amenewa].” Katswiri winanso anafotokoza kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito Mesiya “kuthetsa mavuto onse amene anayamba chifukwa cha kuchimwa kwa anthu oyambirira,” ndiponso kuti adalitse anthu.​—Ahebri 2:14, 15.

Komabe, mwina mukudziwa inu kuti anthu panopa akuvutika kwambiri. Alibe chiyembekezo chilichonse. Motero, buku lakuti The World Book Encyclopedia limati “Ayuda ambiri akuyembekezerabe kubwera kwa Mesiya” ndipo akuyembekezera kuti akadzabwera “adzathetsa zoipa ndi kugonjetsa adani a anthu.” Koma Baibulo limati Mesiya anabwera kale. Kodi pali chifukwa chokhulupirira zimene Baibulo limanenazi? Nkhani yotsatirayi iyankha funso limeneli.