Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusonkhanitsa Zinthu za Kumwamba ndi za Padziko Lapansi

Kusonkhanitsa Zinthu za Kumwamba ndi za Padziko Lapansi

Kusonkhanitsa Zinthu za Kumwamba ndi za Padziko Lapansi

‘Kunam’komera . . . kusonkhanitsa pamodzi zonse mwa Kristu, za kumwamba, ndi za padziko.’​—AEFESO 1:9, 10.

1. Kodi ‘chom’komera’ Yehova n’chiyani chokhudza kumwamba ndi dziko lapansi?

YEHOVA, “Mulungu wa mtendere,” ali ndi cholinga chapamwamba. (Ahebri 13:20) Cholinga chakecho n’chobweretsa mtendere m’chilengedwe chonse. Yehova anauzira mtumwi Paulo kulemba kuti ‘chom’komera’ Iye n’chakuti ‘asonkhanitse pamodzi zonse mwa Kristu, za kumwamba, ndi za padziko.’ (Aefeso 1:9, 10) Kodi mawu akuti ‘kusonkhanitsa pamodzi’ m’vesili akutanthauzanji makamaka? Katswiri wina wamaphunziro a Baibulo, dzina lake J. B. Lightfoot, anati: “Mawuwa akusonyeza kugwirizana kwathunthu kwa chilengedwe chonse, chomwe sichidzakhalanso ndi zinthu zosiyana ndi zinzake ndiponso zogawanitsa, koma zonse zidzakhala zogwirizana mwa Kristu. Sikudzakhalanso uchimo ndi imfa, chisoni ndi kulephera ndiponso matenda.”

Zinthu “za Kumwamba”

2. Kodi zinthu “za kumwamba” zofunika kusonkhanitsidwa pamodzi ndani?

2 Mtumwi Petro anafotokoza mwachidule chiyembekezo chosangalatsa chomwe Akristu oona ali nacho pamene analemba kuti: “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) “Miyamba yatsopano” yolonjezedwa pa lembali ndi ulamuliro watsopano, womwe ndi Ufumu wa Mesiya. Zinthu “za kumwamba” zomwe Paulo anatchula m’kalata yomwe analembera Aefeso ziyenera kusonkhanitsidwa pamodzi “mwa Kristu.” Zinthu zimenezi ndi anthu owerengeka osankhidwa kukalamulira ndi Kristu kumwamba. (1 Petro 1:3, 4) Akristu odzozedwa okwanira 144,000 amenewa “ogulidwa kuchokera kudziko,” “anagulidwa mwa anthu” kuti akalamulire limodzi ndi Kristu mu Ufumu wake wa kumwamba.​—Chivumbulutso 5:9, 10; 14:3, 4; 2 Akorinto 1:21; Aefeso 1:11; 3:6.

3. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti odzozedwa ‘anakhazikitsidwa m’zakumwamba’ ngakhale pamene ali padziko lapansi pano?

3 Akristu odzozedwa amabadwanso mwa mzimu woyera kuti akhale ana auzimu a Yehova. (Yohane 1:12, 13; 3:5-7) Popeza kuti Yehova amawatenga kukhala “ana” ake, iwo amayamba kukhala abale a Yesu. (Aroma 8:15; Aefeso 1:5) Chifukwa cha zimenezi, ngakhale panthawi yomwe ali padziko lapansi pano, iwo amaonedwa kuti ‘anaukitsidwa, nakhazikitsidwa pamodzi m’zakumwamba mwa Kristu Yesu.’ (Aefeso 1:3; 2:6) Amakhala malo apamwamba amenewa chifukwa chakuti ‘anasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano, [umene ndi] chikole cha cholowa chawo’ chomwe anawasungira kumwamba. (Aefeso 1:13, 14; Akolose 1:5) Motero anthu amenewa ndiwo zinthu “za kumwamba,” omwe akufunika kusonkhanitsidwa mogwirizana ndi chiwerengero chomwe Yehova anafuna.

Ntchito Yosonkhanitsa Iyamba

4. Kodi ndi liti pamene ntchito yosonkhanitsa zinthu “za kumwamba” inayamba ndipo inayamba motani?

4 Mogwirizana ndi “makonzedwe” a Yehova, kapena kuti njira yake yosamalira zinthu, kusonkhanitsa zinthu “za kumwamba” kunafunika kuyamba ‘pamakwaniridwe a nyengozo.’ (Aefeso 1:10) Nthawi yoikidwa imeneyi inakwana pa Pentekoste wa mu 33 C.E. Tsiku limenelo, atumwi limodzi ndi kagulu ka ophunzira, ka amuna ndi akazi, analandira mzimu woyera. (Machitidwe 1:13-15; 2:1-4) Izi zinapereka umboni wakuti pangano latsopano layamba kugwira ntchito, ndipo pamenepa m’pamene panabadwira mpingo wachikristu ndiponso mtundu watsopano wa Israyeli wauzimu, womwe ndi “Israyeli wa Mulungu.”​—Agalatiya 6:16; Ahebri 9:15; 12:23, 24.

5. N’chifukwa chiyani Yehova analenga “mtundu” watsopano kuti ulowe m’malo mwa Israyeli wakuthupi?

5 Pangano la Chilamulo lomwe linapangidwa ndi Israyeli wakuthupi silinathe kutulutsa “ufumu . . . wa ansembe, ndi mtundu wopatulika” womwe ukanakatumikira kwamuyaya kumwamba. (Eksodo 19:5, 6) Yesu anauza atsogoleri a chipembedzo chachiyuda kuti: “Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.” (Mateyu 21:43) Anthu amenewo, omwe ndi Israyeli wauzimu, ali Akristu odzozedwa omwe analowetsedwa m’pangano latsopano. Mtumwi Petro analembera anthu amenewa kuti: “Inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwiniwake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani muturuke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa; inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu.” (1 Petro 2:9, 10) Aisrayeli akuthupi sanalinso m’pangano ndi Yehova. (Ahebri 8:7-13) Mogwirizana ndi zimene Yesu analosera, iwo analandidwa mwayi wokhala mbali ya Ufumu wa Mesiya ndipo mwayiwu unapatsidwa kwa anthu a 144,000 omwe amapanga Israyeli wauzimu.​—Chivumbulutso 7:4-8.

Alowetsedwa M’pangano la Ufumu

6, 7. Kodi Yesu anapanga pangano lapadera lotani ndi abale ake obadwa mwa mzimu, ndipo izi zili ndi tanthauzo lotani kwa iwo?

6 Usiku womwe Yesu anakhazikitsa mwambo wa Chikumbutso cha imfa yake, iye anauza atumwi ake okhulupirika kuti: “Inu ndinu amene munakhala ndi Ine chikhalire m’mayesero anga; ndipo Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira Ine, kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu Ufumu wanga; ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.” (Luka 22:28-30) Yesu pano anali kunena za pangano lapadera lomwe anapanga ndi abale ake obadwa mwa mzimu a 144,000, omwe adzakhale ‘okhulupirika kufikira imfa’ ndi kusonyeza kuti ndi ‘olakika.’​—Chivumbulutso 2:10; 3:21.

7 Anthu owerengeka amenewa amasiya kukhala ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi pano kwamuyaya monga anthu a thupi ndi mwazi. Adzalamulira ndi Kristu kumwamba, kukhala pa mipando yachifumu kuti aweruze anthu. (Chivumbulutso 20:4, 6) Tsopano tiyeni tione malemba ena amene amanena za odzozedwa basi, ndiponso amene amasonyeza chifukwa chake a “nkhosa zina” sadya mkate ndi kumwa vinyo pa Chikumbutso.​—Yohane 10:16.

8. Kodi odzozedwa amasonyeza chiyani mwa kudya mkate? (Onani bokosi patsamba 23.)

8 Odzozedwa amavutika mofanana ndi Kristu ndipo amalolera kufa imfa yofanana ndi yake. Monga mmodzi mwa anthu a m’gulu limeneli, Paulo anafotokoza kuti anali wokonzeka kutaya chilichonse n’cholinga choti ‘adziwonjezere Kristu . . . kuti am’zindikire Iye, ndi mphamvu ya kuuka kwake, ndi kuyanjana [naye] m’zowawa zake.’ Inde, Paulo anali wokonzeka kufa “imfa” yofanana ndi ya Yesu. (Afilipi 3:8, 10) Akristu odzozedwa ambiri apirira ali ndi matupi aumunthu mavuto oti angathe “kufa” nawo imfa yofanana ndi ya Yesu.​—2 Akorinto 4:10.

9. Kodi mkate wa pa Chikumbutso umaimira thupi lotani?

9 Pokhazikitsa mwambo wa Mgonero wa Ambuye, Yesu anati: “Thupi langa ndi ili.” (Marko 14:22) Anali kunena za thupi lake lenileni, lomwe posapita nthawi yaitali linamenyedwa ndipo linakhala magazi okhaokha. Mkate wopanda chotupitsa ndi chizindikiro choyenerera cha thupi loterolo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti nthawi zina m’Baibulo chotupitsa chimasonyeza uchimo kapena kuipa. (Mateyu 16:4, 11, 12; 1 Akorinto 5:6-8) Yesu anali wangwiro, ndipo thupi lomwe anali nalo monga munthu linalibe uchimo. Anali kudzapereka thupi langwiro limeneli monga chiwombolo cha machimo. (Ahebri 7:26; 1 Yohane 2:2) Mwa kuchita zimenezi, Akristu onse okhulupirika, kaya oyembekezera kukakhala kumwamba kapena kudzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi pano, akanapindula kwambiri.​—Yohane 6:51.

10. Kodi anthu amene amamwa vinyo wa pa Chikumbutso amagawana ‘mwazi wa Kristu’ motani?

10 Ponenapo za vinyo amene Akristu odzozedwa amamwa pa Chikumbutso, Paulo analemba kuti: “Chikho cha dalitso chimene tidalitsa, sichiri chiyanjano cha mwazi wa Kristu kodi?” (1 Akorinto 10:16) Kodi anthu amene amamwa vinyowa, ‘amayanjana [kapena kuti kugawana] mwazi wa Kristu’ motani? Sikuti iwo amapereka nawo nsembe ya dipo ayi, chifukwa chakuti nawonso amafunikira kuwomboledwa. Chifukwa choti amakhulupirira kuti mwazi wa Kristu uli ndi mphamvu yowombola anthu, machimo awo amakhululukidwa ndipo amayesedwa olungama, oyenerera moyo wa kumwamba. (Aroma 5:8, 9; Tito 3:4-7) A kagulu ka 144,000, omwe adzalamulire ndi Kristu ‘amayeretsedwa,’ ndi kusambitsidwa kuchotsa machimo, n’kukhala “opatulika” chifukwa cha mphamvu ya mwazi womwe Kristu anakhetsa. (Ahebri 10:29; Danieli 7:18, 27; Aefeso 2:19) Inde, ndi mwazi wake womwe anakhetsa umene Kristu ‘anagulira Mulungu . . . anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse, ndipo adawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo adzachita ufumu padziko.’​—Chivumbulutso 5:9, 10.

11. Kodi odzozedwa amasonyeza chiyani akamamwa vinyo pa Chikumbutso?

11 Atayambitsa mwambo wa Chikumbutso cha imfa yake, Yesu anapatsa atumwi ake okhulupirika chikho cha vinyo, n’kunena kuti: “Mumwere ichi inu nonse, pakuti ichi ndicho mwazi wanga wa pangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.” (Mateyu 26:27, 28) Mofanana ndi mwazi wa ng’ombe ndi mbuzi womwe unkatsimikizira pangano la Chilamulo pakati pa Mulungu ndi mtundu wa Israyeli, mwazi wa Yesu nawonso unatsimikizira pangano latsopano limene Yehova anadzapanga ndi Israyeli wauzimu, kuyambira pa Pentekoste wa mu 33 C.E. (Eksodo 24:5-8; Luka 22:20; Ahebri 9:14, 15) Odzozedwa akamamwa vinyo amene amaimira “mwazi wa chipangano,” iwo amasonyeza kuti alowetsedwa m’pangano latsopano ndipo akupindula nalo.

12. Kodi odzozedwa amabatizidwa motani mu imfa ya Kristu?

12 Pali chinthu chinanso chimene odzozedwa amakumbutsidwa. Yesu anauza ophunzira ake okhulupirika kuti: “Chikho chimene ndimwera Ine mudzamwera; ndipo ubatizo umene ndibatizidwa nawo Ine, mudzabatizidwa nawo.” (Marko 10:38, 39) Panthawi ina mtumwi Paulo anadzafotokoza kuti Akristu ‘amabatizidwa mu imfa [ya Kristu].’ (Aroma 6:3) Odzozedwa amakhala moyo wodzipereka. Imfa yawo ndi imfa yansembe chifukwa chakuti amasiya chiyembekezo chilichonse chodzakhala kwamuyaya padziko lapansi pano. Ubatizo wa mu imfa ya Kristu wa Akristu odzozedwa amenewa umamalizika akamwalira ali okhulupirika ndi kuukitsidwa ngati anthu auzimu kuti ‘akachite ufumu’ ndi Kristu kumwamba.​—2 Timoteo 2:10-12; Aroma 6:5; 1 Akorinto 15:42-44, 50.

Kudya Mkate ndi Kumwa Vinyo

13. N’chifukwa chiyani anthu amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi sadya mkate ndi kumwa vinyo wa pa Chikumbutso, koma n’chifukwa chiyani amakhala nawo pa mwambowu?

13 Popeza kuti kudya mkate ndi kumwa vinyo amene amaperekedwa pa Chikumbutso kumakhudza zinthu zonsezi, n’zoonekeratu kuti sikoyenera kuti anthu amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi adye ndi kumwa nawo. Anthu amenewa amazindikira kuti iwo si odzozedwa, omwe amapanga thupi la Kristu, komanso sali nawo m’pangano latsopano lomwe Yehova anapanga ndi anthu omwe akalamulire ndi Yesu Kristu. Popeza kuti “chikho” chimaimira pangano latsopano, okhawo amene ali m’pangano latsopanolo ndiwo amadya mkate ndi kumwa vinyo. Anthu amene akuyembekezera moyo wosatha padziko lapansi pano panthawi yomwe anthu adzakhale angwiro mu ulamuliro wa Ufumu, sabatizidwa mu imfa ya Yesu kapenanso kuitanidwa kukalamulira naye kumwamba. Atati adye mkate ndi kumwa vinyo, angasonyeze kuti ali m’gulu lomwe iwo mulibemo. Motero, iwo sadya mkate kapena kumwa vinyo, ngakhale kuti amakhalapo ndi kuonerera mwambo wa Chikumbutsowu mwaulemu. Iwo amayamikira zonse zimene Yehova wawachitira kudzera mwa Mwana wake, kuphatikizapo kuwakhululukira machimo pogwiritsa ntchito mwazi womwe Kristu anakhetsa.

14. Kodi odzozedwa amalimbikitsidwa motani mwauzimu akamadya mkate ndi kumwa vinyo?

14 Kusindikiza chizindikiro pa Mkristu womaliza mwa Akristu ochepa oitanidwa kukalamulira ndi Kristu kumwamba kuli pafupi kuchitika. Kufikira atamaliza moyo wawo wodzipereka padziko lapansi pano, odzozedwa amalimbikitsidwa mwauzimu akamadya ndi kumwa zizindikiro za pa Chikumbutso. Iwo amamva kuti ndi ogwirizana ndi abale ndi alongo awo monga anthu omwe amapanga thupi la Kristu. Akamadya mkate ndi kumwa vinyo amakumbutsidwa za udindo womwe ali nawo wokhala okhulupirika mpaka imfa.​—2 Petro 1:10, 11.

Kusonkhanitsa Zinthu “za Padziko” Lapansi

15. Kodi ndani amene asonkhanitsidwa kuti akhale ku mbali imodzi ndi Akristu odzozedwa?

15 Kuyambira m’katikati mwa zaka za m’ma 1930, gulu lomwe likumka likula la “nkhosa zina,” omwe si a “kagulu ka nkhosa” ndipo akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi kwamuyaya, lakhala likuthandiza odzozedwa. (Yohane 10:16; Luka 12:32; Zekariya 8:23) Iwo tsopano akhala anzawo okhulupirika a abale a Kristu, ndipo akuwathandiza kwambiri pantchito yolalikira “uthenga uwu wabwino wa Ufumu” kuti ukhale umboni kwa anthu a mitundu yonse. (Mateyu 24:14; 25:40) Pochita zimenezi, iwo ali ndi mwayi woti Kristu akadzabwera kudzaweruza mitundu ya anthu, iwo adzaweruzidwe monga “nkhosa” zake, zomwe zili “kudzanja lake lamanja,” kusonyeza kuti ndi anthu amene amawayanja. (Mateyu 25:33-36, 46) Mwa kukhulupirira mwazi wa Kristu, iwo adzakhala “khamu lalikulu,” lomwe lidzapulumuke ‘chisautso chachikulu.’​—Chivumbulutso 7:9-14.

16. Kodi zinthu “za padziko” lapansi zidzaphatikizapo ndani, ndipo kodi onsewa adzakhala ndi mwayi wotani woti akhale “ana a Mulungu”?

16 Akadzangomaliza kusindikiza chizindikiro a 144,000, kudzawomba “mphepo” zowononga dongosolo loipa la Satana la padziko lapansi pano. (Chivumbulutso 7:1-4) Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu ndi ansembe anzake achifumu, khamu lalikulu lidzalandira khwimbi la anthu oukitsidwa. (Chivumbulutso 20:12, 13) Anthu amenewa adzakhala ndi mwayi wokhala padziko lapansi kwamuyaya molamulidwa ndi Mfumu Yaumesiya, Kristu Yesu. Pamapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000, zinthu zonse “za padziko” zidzayesedwa komaliza. Amene adzakhale okhulupirika adzakhala “ana a Mulungu” a padziko lapansi.​—Aefeso 1:10; Aroma 8:21; Chivumbulutso 20:7, 8.

17. Kodi cholinga cha Yehova chidzakwaniritsidwa motani?

17 Motero, mwa “makonzedwe,” kapena kuti njira yake yosamalira zinthu, yomwe ndi yanzeru zakuya, Yehova adzakhala atakwaniritsa cholinga chake ‘chosonkhanitsa pamodzi zonse mwa Kristu, za kumwamba, ndi za padziko.’ Zolengedwa zonse zanzeru, kumwamba ndi padziko lapansi, zidzakhala zitasonkhanitsidwa pamodzi mumtendere wa m’chilengedwe chonse, n’kumagonjera mosangalala ulamuliro wangwiro wa Yehova, yemwe ndi wamkulu pokwaniritsa zolinga zake.

18. Kodi odzozedwa ndiponso anzawo adzapindula motani mwa kupezeka pa mwambo wa Chikumbutso?

18 Zidzakhala zolimbikitsatu kwambiri kwa anthu owerengeka odzozedwa ndiponso anzawo mamiliyoni ambirimbiri a nkhosa zina kusonkhana pa April 12, 2006! Adzachita mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Kristu, mogwirizana ndi mmene Yesu analamulira, kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” (Luka 22:19) Onse odzapezekapo ayenera kukumbukira zimene Yehova wawachitira kudzera mwa Mwana wake wokondedwa, Kristu Yesu.

Kubwereza

• Kodi cholinga cha Yehova cha zinthu za kumwamba ndi za padziko lapansi n’chiyani?

• Kodi zinthu “za kumwamba” ndani, ndipo zasonkhanitsidwa motani?

• Kodi zinthu “za padziko” lapansi ndani, ndipo zili ndi chiyembekezo chotani?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 23]

“Thupi la Kristu”

Pa 1 Akorinto 10:16, 17, Paulo, pofotokoza kufunika kwa mkate kwa abale odzozedwa ndi mzimu a Kristu, anatchula “thupi” mwapadera. Anati: “Mkate umene tinyema suli chiyanjano cha thupi la Kristu kodi? Pakuti mkate ndiwo umodzi, chotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse titengako ku mkate umodzi.” Akristu odzozedwa akamadya mkate wa pa Chikumbutso, amalengeza kuti ndi amodzi mumpingo wa odzozedwa, womwe uli ngati thupi ndipo Kristu ndiye Mutu wake.​—Mateyu 23:10; 1 Akorinto 12:12, 13, 18.

[Zithunzi patsamba 23]

Kodi n’chifukwa chiyani odzozedwa okha ndiwo amadya mkate ndi kumwa vinyo?

[Chithunzi patsamba 25]

Mwa makonzedwe a Yehova, zolengedwa zonse za kumwamba ndi za padziko lapansi zidzagwirizana