Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyenda M’njira ya Kuunika Komawalabe

Kuyenda M’njira ya Kuunika Komawalabe

Kuyenda M’njira ya Kuunika Komawalabe

“Mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kumkabe kuwala kufikira usana woti mbe.”​—MIYAMBO 4:18.

1, 2. Kodi anthu a Mulungu achitanji chifukwa cha kuunika kwauzimu komawalabe kochokera kwa Yehova?

KODI ndaninso wina kuposa Gwero la kuunika, Yehova Mulungu, amene angafotokoze bwino zimene dzuwa likamatuluka limachita pa mdima wa usiku? (Salmo 36:9) Mulungu anati: ‘Kuwala kwa mbandakucha kukafika malekezero a dziko lapansi, dziko limasandulika ngati dothi lonyata pansi pa chosindikizira, ndi zonse zibuka ngati chovala.’ (Yobu 38:12-14) Chifukwa cha kuunika kwa dzuwa komawalabe, zinthu padziko lapansi pano zimayamba kuoneka bwinobwino, ngati mmene dongo lofewa limasinthira wina akalisindikiza kapena kuti kulidinda ndi chidindo.

2 Yehova alinso Gwero la kuunika kwauzimu. (Salmo 43:3) Pamene dzikoli lili mumdima wandiweyani, Mulungu woona akupitiriza kuunikira anthu ake. Kodi chotsatirapo chake n’chiyani? Baibulo limayankha kuti: “Mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kumkabe kuwala kufikira usana woti mbe.” (Miyambo 4:18) Kuunika komawalabe kochokera kwa Yehova kukupitiriza kuwaunikira anthu ake njira. Kuunika kumeneku kukuwathandiza kukonza zinthu pa kayendetsedwe ka gulu lake, ziphunzitso, ndiponso makhalidwe.

Zinthu Zikonzeka M’gulu Chifukwa cha Kuunika

3. Kodi lemba la Yesaya 60:17 limalonjeza chiyani?

3 Yehova analosera kudzera mwa mneneri Yesaya kuti: “M’malo mwa mkuwa ndidzatenga golidi, ndi m’malo mwa chitsulo ndidzatenga siliva, ndi m’malo mwa mtengo ndidzatenga mkuwa, ndi m’malo mwa miyala ndidzatenga chitsulo.” (Yesaya 60:17) Kusinthitsa chinthu chotsika mtengo ndi chokwera mtengo kumasonyeza kuti zinthu zikupita patsogolo, ndipo umu ndi mmenenso zakhalira ndi Mboni za Yehova. Izo zaona kusintha kwa kayendetsedwe ka gulu lawo m’nyengo yonse ya “mathedwe a nthawi ya pansi pano,” kapena kuti “masiku otsiriza.”​—Mateyu 24:3; 2 Timoteo 3:1.

4. Kodi mu 1919 panakhazikitsidwa dongosolo lotani, ndipo linali lothandiza motani?

4 Chakumayambiriro kwa masiku otsiriza ano, mipingo ya Ophunzira Baibulo, dzina lomwe Mboni za Yehova zinkadziwika nalo panthawiyo, inkasankha akulu ndi madikoni awo mwa demokalase. Komabe, akulu ena analibe kwenikweni mtima wolalikira. Ena mwa iwo, kuwonjezera pa kusafuna kuchita nawo ntchito yolalikira, ankaletsanso anzawo kuchita ntchitoyi. Motero, mu 1919 mu mpingo uliwonse munakhazikitsidwa udindo watsopano, wa wotsogolera utumiki. Mpingo si umene unkasankha munthu paudindowu ayi, koma ankaikidwa ndi ofesi ya nthambi ya anthu a Mulungu mogwirizana ndi zomuyeneretsa munthuyo zotchulidwa m’Malemba. Zina mwa ntchito za wotsogolera utumiki zinali kukonza za ntchito yolalikira, kugawa magawo, ndi kulimbikitsa anthu kuchita utumiki wa kumunda. M’zaka zotsatira, anthu analimbikira kwambiri kugwira ntchito yolalikira za Ufumu.

5. Kodi zinthu zinakonzeka motani m’ma 1920?

5 Anthu onse m’mipingo analimbikitsidwanso kwambiri ndi pempho lakuti, “Lengezani, lengezani, lengezani Mfumu ndi ufumu wake,” lomwe linaperekedwa mu 1922 pamsonkhano wa Ophunzira Baibulo womwe unachitikira ku Cedar Point, Ohio, m’dziko la United States. Pofika mu 1927 utumiki wa kumunda unali kuchitika mwadongosolo moti anthu ankaona kuti Lamlungu ndi tsiku labwino la ulaliki wa kunyumba ndi nyumba. N’chifukwa chiyani anasankha tsiku limeneli? Chifukwa chakuti Lamlungu linali tsiku lomwe anthu ambiri sankapita kuntchito. Mboni za Yehova masiku ano zimasonyezanso mtima wofanana ndi umenewu chifukwa zimayesetsa kupita kunyumba za anthu panthawi yomwe anthuwo amapezeka panyumba kawirikawiri, monga Loweruka ndi Lamlungu ndiponso nthawi ya madzulo.

6. Mu 1931, kodi anthu anavomereza chigamulo chotani, ndipo zimenezi zinakhudza motani ntchito yolengeza za Ufumu?

6 Lamlungu masana pa July 26, 1931, ntchito yolengeza Ufumu inalimbikitsidwa kwambiri, pamene anthu anavomereza chigamulo, koyamba pamsonkhano womwe unachitikira ku Columbus, Ohio, ku United States, ndipo kenako anachivomereza padziko lonse. Mwa zina, chigamulocho chinati: “Ife ndife atumiki a Yehova Mulungu otumidwa kugwira ntchito m’dzina lake, ndipo, pomvera lamulo lake, lopereka umboni wonena za Yesu Kristu, ndi kudziwitsa anthu kuti Yehova ndi Mulungu woona ndi Wamphamvuyonse; motero ndife okondwa kuvomera ndi kulandira dzina loperekedwa ndi Ambuye Mulungu, ndipo tikufuna kuti tizidziwika ndi dzina lakuti Mboni za Yehova.” (Yesaya 43:10) Kunena zoona, dzina latsopanoli linafotokoza bwino ntchito yaikulu ya anthu onse a dzina limeneli. Inde, Yehova anali ndi ntchito yoti atumiki ake agwire. Ambiri anasangalala kulandira ntchitoyi!

7. Kodi mu 1932 panakhala kusintha kotani ndipo chifukwa chiyani?

7 Akulu ambiri anadzichepetsa, n’kumagwira mwakhama ntchito yolalikirayi. Komabe, m’madera ena, akulu ochita kusankhidwa mwa demokalase anayesetsa kukana zoti aliyense mu mpingo azichita utumiki wa kumunda. Koma sipanapite nthawi yaitali, zinthu zinakonzekanso. Mu 1932 mipingo inalangizidwa kudzera mu Nsanja ya Olonda kuti isiye kusankha mwa demokalase akulu ndi madikoni. M’malo mwake, izisankha komiti ya utumiki yokhala ndi amuna okonda zinthu zauzimu omwe anali kuchita nawo ntchito yolalikira kumunda. Motero, ntchito yoyang’anira mipingo inaikidwa m’manja mwa anthu odalirika omwe anali kuchita nawo utumiki, ndipotu zimenezi zinapititsa patsogolo ntchito yolalikira.

Zinanso Zikonzeka Chifukwa cha Kuunika Komawalabe

8. Kodi ndi kukonza zinthu kotani komwe kunachitika mu 1938?

8 Kuunika kunali “kumkabe kuwala.” Mu 1938 kuchita chisankho kunatheratu. Atumiki onse m’mipingo anali kuikidwa mogwirizana ndi zowayeneretsa zotchulidwa m’Malemba ndipo “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndiye anali kuyang’anira zimenezo. (Mateyu 24:45-47) Anthu pafupifupi m’mipingo yonse ya Mboni za Yehova anagwirizana nako kusintha kumeneku, ndipo ntchito yolalikira inapitiriza kubala zipatso.

9. Kodi ndi dongosolo lotani lomwe linakhazikitsidwa mu 1972, ndipo n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kunali kukonza zinthu?

9 Kuyambira pa October 1, 1972, panakhala kusintha kwinanso pankhani ya oyang’anira m’mipingo. M’mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse munakhazikitsidwa dongosolo loti mipingoyo iziyang’aniridwa ndi bungwe la akulu, ndipo dongosolo limeneli linalowa m’malo mwa dongosolo loti mpingo uziyang’aniridwa ndi mtumiki kapena woyang’anira mpingo mmodzi yekha. Dongosolo latsopanoli lalimbikitsa kwambiri amuna okhwima maganizo kuti ayenerere kutsogolera mumpingo. (1 Timoteo 3:1-7) Izi zachititsa kuti abale ambiri aphunzire mmene angagwirire ntchito za mumpingo. Abale amenewa athandiza kwambiri pankhani yoweta anthu ambiri atsopano amene aphunzira choonadi cha m’Baibulo!

10. Kodi ndi dongosolo lotani lomwe linakhazikitsidwa mu 1976?

10 Mamembala a Bungwe Lolamulira anagawidwa m’makomiti asanu ndi imodzi, ndipo kuyambira pa January 1, 1976, ntchito zonse za gululi ndiponso za m’mipingo padziko lonse zinayamba kuyang’aniridwa ndi makomiti amenewa. Kunena zoona, kukhala ndi ‘aphungu ochuluka’ otsogolera mbali zonse za ntchito ya Ufumu kwakhala kopindulitsa kwambiri.​—Miyambo 15:22; 24:6.

11. Kodi ndi kukonza zinthu kotani komwe kunayamba mu 1992, ndipo n’chifukwa chiyani?

11 M’chaka cha 1992 panakhala kukonza zinthu kwinanso. Zimene zinachitika m’chaka chimenechi n’zofanana ndi zimene zinachitika Aisrayeli ndi anthu ena atabwerera kwawo kuchokera kudziko la eni ku Babulo. Nthawi imeneyo, panalibe Alevi okwanira ogwira ntchito za pakachisi. Chifukwa cha zimenezo, Anetini, omwe sanali Aisrayeli, anawonjezeredwa ntchito zomwe anali kugwira pothandiza Alevi. Mofanana ndi zimenezi, pofuna kuthandiza kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru pantchito ya padziko lonse yomwe ikumka nichuluka, mu 1992 ena mwa anthu a “nkhosa zina” anapatsidwa maudindo owonjezera a utumiki. Anaikidwa kuti azithandiza m’makomiti a Bungwe Lolamulira.​—Yohane 10:16.

12. Kodi Yehova watiikira motani mtendere ngati akapitawo?

12 Kodi zotsatira za zinthu zonsezi zakhala zotani? Yehova anati: “Ndidzakuikira akapitawo a mtendere, ndi oyang’anira ntchito a chilungamo.” (Yesaya 60:17) Lero, pakati pa atumiki a Yehova pali “mtendere,” ndipo kukonda “chilungamo” ndiko kwakhala “oyang’anira ntchito” zawo, zomwe zikutanthuza kuti kukonda chilungamo ndiko kumawalimbikitsa kutumikira Mulungu. Iwo ndi okonzeka bwino kugwira ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira.​—Mateyu 24:14; 28:19, 20.

Yehova Aunikira Njira Pankhani ya Ziphunzitso

13. M’ma 1920, kodi Yehova anawaunikira motani njira anthu ake pankhani ya ziphunzitso?

13 Yehova wawaunikiranso anthu ake njira pang’onopang’ono pankhani ya ziphunzitso. Chitsanzo cha zimenezi ndi lemba la Chivumbulutso 12:1-9. Lembali limatchula mbali zophiphiritsa zitatu, “mkazi” amene ali ndi pakati ndipo akubala mwana, “chinjoka,” ndiponso “mwana wamwamuna.” Kodi mukudziwa kuti mbali iliyonse yotchulidwa pamenepa imaimira ndani? Matanthauzo ake anafotokozedwa m’nkhani yakuti “Kubadwa kwa Ufumu,” yomwe inatuluka mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 1925. Nkhaniyi inathandiza anthu a Mulungu kumvetsetsa maulosi onena za kubadwa kwa Ufumu, mfundo zimene zinasonyeza bwino kuti pali magulu awiri akuluakulu, omwe ndi gulu la Yehova ndi gulu la Satana. Kenako, cha m’ma 1927 ndi 1928, anthu a Mulungu anazindikira kuti kukondwerera Khirisimasi ndiponso masiku a kubadwa kumasemphana ndi malemba, motero iwo anasiya kuchita zikondwerero zimenezi.

14. Kodi ndi ziphunzitso za choonadi zotani zomwe zinafotokozedwa bwino m’zaka za m’ma 1930?

14 M’ma 1930 panakhala kuunika kwinanso pa ziphunzitso zitatu za choonadi. Kwa zaka zambiri, Ophunzira Baibulo ankadziwa kuti “khamu lalikulu” lotchulidwa pa Chivumbulutso 7:9-17 linali gulu lina osati la a 144,000, omwe adzalamulire limodzi ndi Kristu monga mafumu ndi ansembe. (Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1-5) Komabe sizinali kudziwika bwinobwino kuti khamu lalikulu ndi ndani kwenikweni. Monga mmene kuunika komawalabe kwa m’mawa kumaunikira bwino zinthu zomwe sizinali kuoneka bwino, mu 1935 zinadziwika kuti khamu lalikulu ndi anthu amene adzapulumuke ‘chisautso chachikulu,’ oyembekezera kudzakhala kwamuyaya padziko lapansi pano. Kenako, m’kati mwa chaka chomwecho anthu a Mulungu anathandizidwanso kumvetsetsa bwino nkhani ina yomwe inakhudza ana opita ku sukulu a Mboni za Yehova m’mayiko ambiri. Padziko lonse lapansi, m’nthawi imeneyo, ambiri ankakonda kuchita zinthu zosonyeza kukonda kwambiri dziko lawo. Mboni zinazindikira kuti kuchitira sawatcha mbendera sunali mwambo chabe. Chaka chotsatira, mfundo inanso ya chiphunzitso cha choonadi, yoti Kristu anafera pamtengo, osati pamtanda, inafotokozedwa.​—Machitidwe 10:39.

15. Kodi ndi liti pamene mfundo ya kupatulika kwa magazi inafotokozedwa bwino ndipo zinatero motani?

15 Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itangotha, asilikali ambiri ovulala ankaikidwa magazi. Nthawi imeneyi panakhala kuunikira kwinanso pankhani ya kupatulika kwa magazi. Nsanja ya Olonda ya July 1, 1945 inalimbikitsa “onse olambira Yehova amene akufuna moyo wosatha m’dziko lake latsopano lachilungamo kuona kuti magazi ndi opatulika ndi kutsatira mfundo zolungama za Mulungu pankhani yofunika imeneyi.”

16. Kodi Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures linatulutsidwa liti, ndipo lili ndi zinthu ziwiri zofunika ziti?

16 M’chaka cha 1946 panaoneka kuti pakufunika Baibulo lomasuliridwa mwatsopano pogwiritsa ntchito maphunziro amakono ndiponso losaipitsidwa ndi ziphunzitso zochokera m’miyambo ya Matchalitchi Achikristu. Ntchito yomasulira Baibulo loterolo inayamba mu December 1947. Mu 1950 Baibulo la New World Translation of the Christian Greek Scriptures linatulutsidwa m’Chingelezi. Malemba Achihebri m’Chingelezi anasindikizidwa m’mavoliyumu asanu omwe anali kutulutsidwa pang’onopang’ono kuyambira mu 1953. Voliyumu yomaliza inatulutsidwa mu 1960, patangopitirira pang’ono zaka 12 kuchokera pamene ntchito yomasuliraliyo inayamba. Baibulo lathunthu m’voliyumu imodzi, la New World Translation of the Holy Scriptures linatulutsidwa mu 1961. Panopa Baibuloli likupezeka m’zinenero zambiri, ndipo lili ndi zinthu zina zofunika kwambiri. Linabwezeretsa dzina la Mulungu, lakuti Yehova. Komanso, popeza kuti linamasuliridwa motsatira liwu ndi liwu m’mabuku oyambirira, Baibuloli likutithandiza kupitiriza kumvetsetsa choonadi cha Mulungu.

17. Kodi ndi kuunika kowonjezeka kotani komwe kunawala mu 1962?

17 Kumveketsa bwino za “maulamuliro a akulu” otchulidwa pa Aroma 13:1 ndiponso kuti Mkristu ayenera kuwamvera mpaka pati kunachitika mu 1962. Kuphunzira mozama chaputala 13 cha buku la Aroma ndiponso Malemba monga Tito 3:1, 2 ndi 1 Petro 2:13, 17 kunatithandiza kumvetsa bwino kuti mawu akuti “maulamuliro a akulu” sanena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu, koma amanena za maboma olamulira a anthu.

18. Kodi mfundo zina za choonadi zomwe zinafotokozedwa bwino m’ma 1980 ndi ziti?

18 Zaka zotsatira, njira ya olungama inapitiriza kumawalabe. Mu 1985 panakhala kuunikira tanthauzo la kuyesedwa wolungama kaamba ka moyo ndiponso kuyesedwa wolungama monga bwenzi la Mulungu. (Aroma 5:18; Yakobo 2:23) Tanthauzo la Chaka Choliza Lipenga cha Akristu linafotokozedwa mwatsatanetsatane mu 1987.

19. Kodi Yehova wawaunikira motani mwauzimu anthu ake m’zaka zaposachedwazi?

19 Mu 1995 tinamvetsa bwino nkhani ya kulekanitsa “nkhosa” ndi “mbuzi.” M’chaka cha 1998 anafotokoza bwino kwambiri masomphenya a Ezekieli onena za kachisi, omwe panopa ayamba kale kukwaniritsidwa. Mu 1999 anatifotokozera bwino kuti ndi liti pamene ‘chonyansa cha kupululutsa chidzaime m’malo oyera’ ndiponso kuti chidzaima motani. (Mateyu 24:15, 16; 25:32) Ndipo m’chaka cha 2002 tinamvetsanso bwino tanthauzo la kulambira Mulungu “mumzimu ndi m’choonadi.”​—Yohane 4:24.

20. Kodi ndi mbali zinanso ziti zimene zakonzeka pakati pa anthu a Mulungu?

20 Kuwonjezera pa kukonza zinthu m’gulu ndiponso kumveketsa bwino ziphunzitso, pakhalanso kukonza zinthu pankhani ya makhalidwe a Akristu. Mwachitsanzo, mu 1973 tinazindikira kuti kugwiritsa ntchito fodya ‘kumadetsa thupi’ ndipo tizikuona kuti ndi tchimo lalikulu. (2 Akorinto 7:1) Zaka khumi pambuyo pake, Nsanja ya Olonda ya July 15, 1983 inamveketsa bwino mmene timaonera kugwiritsa ntchito zida zankhondo. Izi ndi zina mwa zitsanzo chabe za kuunika komawalabe m’nthawi yathu ino.

Pitirizani Kuyenda M’njira ya Kuunika Komawalabe

21. Kodi ndi maganizo otani amene angatithandize kupitiriza kuyenda m’njira ya kuunika komawalabe?

21 “Nthawi zina zinthu zikasintha, kumakhala kovuta kuti munthu uvomereze ndi kugwirizana ndi kusinthako,” anatero mbale wina amene wakhala mkulu kwa nthawi yaitali. Kodi n’chiyani chimene cham’thandiza kuvomereza zinthu zambiri zimene waona zikusintha m’zaka 48 zomwe wakhala akulengeza Ufumu? Iye anayankha kuti: “Chinsinsi chake chagona pa kukhala ndi maganizo abwino. Kukana kuti zinthu zasintha n’kutsalira, pamene gulu likupita patsogolo. Ndikaona kuti zikundivuta kuvomereza kuti zinthu zasintha, ndimaganizira zimene Petro anauza Yesu kuti: ‘Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha.’ Kenako ndimadzifunsa kuti, ‘Kodi ndipita kuti, kumdima wadzikoli?’ Izi zimandithandiza kusasiyana ndi gulu la Mulungu ngakhale pang’ono.”​—Yohane 6:68.

22. Kodi timapindula motani tikamayenda m’kuunika?

22 Kunena zoona dzikoli lili mumdima wandiweyani. Pamene Yehova akupitiriza kuunikira anthu ake, kusiyana komwe kulipo pakati pa iwo ndi dzikoli kukukulirakulira. Kodi kuunika kumeneku kumatithandiza motani? Kuunikira dzenje mumsewu sikuti kumachotsa dzenjelo. Nakonso kuunika kwa m’Mawu a Mulungu sikuchotsa mbuna. Komabe, kuunika kumeneku kumatithandiza kupewa mbunazo ndipo timapitiriza kuyenda m’kuunika komawalabe. Ndiyetu, tiyeni tipitirize kulabadira mawu a Yehova aulosi, “monga nyali younikira m’malo amdima.”​—2 Petro 1:19.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi Yehova wathandiza anthu ake kukonza zinthu zotani m’gulu lake?

• Kuunika komawalabe kwabweretsa kusintha kotani pankhani ya ziphunzitso?

• Kodi inuyo mwaona kusintha kotani, ndipo n’chiyani chakuthandizani kuvomereza kusintha kumeneko?

• N’chifukwa chiyani mukufuna kupitiriza kuyenda m’njira ya kuunika komawalabe?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 27]

Msonkhano wa mu 1922, womwe unachitikira ku Cedar Point, Ohio, unapatsa Ophunzira Baibulo nyonga zogwirira ntchito ya Mulungu

[Chithunzi patsamba 29]

Baibulo la “New World Translation of the Christian Greek Scriptures” lomwe linatulutsidwa mu 1950 ndi N. H. Knorr

[Mawu a Chithunzi patsamba 26]

© 2003 BiblePlaces.com