Makonzedwe Okwaniritsira Cholinga cha Mulungu
Makonzedwe Okwaniritsira Cholinga cha Mulungu
‘[Mulungu] amachita zonse monga mwa uphungu wa chifuniro chake.’—AEFESO 1:11.
1. N’chifukwa chiyani mipingo yonse ya Mboni za Yehova idzasonkhane pa April 12, 2006?
LACHITATU madzulo, pa April 12, 2006, anthu pafupifupi 16 miliyoni adzasonkhana kuti achite mwambo wa Mgonero wa Ambuye. Kulikonse komwe adzasonkhaneko, kudzakhala tebulo lomwe padzakhale mkate wopanda chotupitsa, woimira thupi la Kristu, ndi vinyo wofiira, woimira mwazi wake womwe iye anakhetsa. Chakumapeto kwa nkhani yofotokoza tanthauzo la Chikumbutso cha imfa ya Yesu, zizindikiro zimenezi zidzaperekedwa kwa onse amene adzasonkhanewo. Adzayamba ndi kupereka mkate, ndipo kenako adzapereka vinyo. M’mipingo yowerengeka ya Mboni za Yehova, munthu mmodzi kapena angapo mwa anthu osonkhanawo adzadya mkate ndi kumwa vinyo. Koma m’malo ambiri palibe amene adzadye. N’chifukwa chiyani Akristu owerengeka okha, amene akuyembekezera kukakhala kumwamba, ndiwo amadya mkate ndi kumwa vinyo, pamene ambiri, amene akuyembekezera kudzakhala kwamuyaya padziko lapansi pano, satero?
2, 3. (a) Kodi Yehova analenga zinthu m’ndondomeko yotani mogwirizana ndi cholinga chake? (b) Kodi Yehova anali ndi cholinga chotani polenga dziko lapansi ndiponso anthu?
2 Yehova ndi Mulungu amene ali ndi cholinga. Pokwaniritsa cholinga chakecho, iye ‘amachita zonse monga mwa uphungu wa chifuniro chake.’ (Aefeso 1:11) Choyamba, analenga Mwana wake wobadwa yekha. (Yohane 1:1, 14; Chivumbulutso 3:14) Kenako, kudzera mwa Mwana wakeyo, Yehova analenga banja la ana auzimu. Ndiyeno analenga chilengedwe chomwe timaonachi, kuphatikizapo dziko lapansili. Analenganso munthu n’kumuika m’dzikomo.—Yobu 38:4, 7; Salmo 103:19-21; Yohane 1:2, 3; Akolose 1:15, 16.
3 Yehova sanalenge dziko lapansili n’cholinga choti pakhale poyeserera mmene anthu angamakhalire kuti kenako akawaphatikize ndi ana ake auzimu kumwamba, ngati mmene amaphunzitsira Matchalitchi Achikristu ambiri. Analilenga ndi cholinga choti “akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18) Mulungu analenga dziko lapansi kuti pakhale anthu ndiponso analenga anthu kuti akhale padziko lapansi. (Salmo 115:16) Dziko lonse lapansi linali loti lidzakhale paradaiso, lili ndi anthu olungama, oti azilimapo ndi kuliyang’anira. Anthu awiri oyambirira sanauzidwepo n’kamodzi komwe kuti m’kupita kwa nthawi adzapita kumwamba.—Genesis 1:26-28; 2:7, 8, 15.
Satana Ayesa Kulepheretsa Cholinga cha Yehova
4. Kodi kalamuliridwe ka Yehova kanatsutsidwa motani kumayambiriro kwenikweni kwa mbiri ya anthu?
4 Mwana wina wauzimu wa Mulungu anapanduka n’kukonza zoti alepheretse cholinga cha Yehova, ndipo kuchita zimenezi kunali kugwiritsa ntchito molakwika ufulu wosankha umene Mulungu anam’patsa. Iye anasokoneza mtendere womwe anthu onse okonda ulamuliro wa Yehova ndi Genesis 3:1-6) Iye sanakane kuti Yehova ali ndi mphamvu, koma anatsutsa mmene Iye amalamulirira ndipo mwakutero anatsutsa ufulu wolamulira umene Mulungu ali nawo. Motero, nkhani yaikulu ya ulamuliro wa Yehova inayamba padziko lapansi kumayambiriro kwenikweni kwa mbiri ya anthu.
kuugonjera amakhala nawo. Satana anapangitsa anthu awiri oyambirira kuyamba moyo wodziimira paokha, wosadalira Mulungu. (5. Kodi nkhani yachiwiri yomwe Satana anayambitsa inali yotani ndipo inakhudza ndani?
5 Nkhani yaikulu ya ulamuliro wachilengedwe chonseyi inadzagwirizana ndi nkhani ina yachiwiri yomwe inaonekera m’masiku a Yobu. Satana anakayikira cholinga chimene zolengedwa za Yehova zimakhala nacho pogonjera ndi kutumikira Yehovayo. Satana anasonyeza kuti zolengedwa zimenezi zimatero chifukwa cha dyera ndipo anati ngati zitayesedwa, zingathe kupandukira Mulungu. (Yobu 1:7-11; 2:4, 5) Ngakhale kuti nkhaniyi inatchulidwa chifukwa cha munthu wotumikira Yehova, inakhudzanso ana auzimu a Mulungu, ngakhalenso Mwana wobadwa yekha wa Yehova.
6. Kodi Yehova anasonyeza motani kuti amachita zinthu mogwirizana ndi cholinga chake ndiponso dzina lake?
6 Mogwirizana ndi cholinga chake ndiponso tanthauzo la dzina lake, Yehova anadzipanga kukhala Mneneri ndiponso Mpulumutsi. * Anauza Satana kuti: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:15) Kudzera mwa Mbewu ya ‘mkazi’ wake, kapena kuti mbali ya kumwamba ya gulu lake, Yehova adzatha kuyankha zimene Satana anatsutsa ndi kupatsa mbadwa za Adamu chiyembekezo chodzapulumuka ndi kudzakhala ndi moyo.—Aroma 5:21; Agalatiya 4:26, 31.
“Chinsinsi cha Chifuniro Chake”
7. Kudzera mwa mtumwi Paulo, kodi Yehova anasonyeza kuti ali ndi cholinga chotani?
7 M’kalata yomwe mtumwi Paulo analembera Akristu a ku Efeso, iye anafotokozamo bwino kwambiri mmene Yehova amachitira zinthu kuti akwaniritse cholinga chake. Paulo analemba kuti: “Anatizindikiritsa ife chinsinsi [chopatulika, NW] cha chifuniro chake, monga kunam’komera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa Iye, kuti pa makonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Kristu, za kumwamba, ndi za padziko.” (Aefeso 1:9, 10) Cholinga chaulemerero cha Yehova n’chakuti zinthu zonse za m’chilengedwe zikhale zogwirizana ndiponso zogonjera ulamuliro wake chifukwa chomukonda. (Chivumbulutso 4:11) Zikadzatero, dzina lake lidzayeretsedwa, zidzaoneka kuti Satana ndi wabodza, ndipo chifuniro cha Mulungu chidzachitika “Kumwamba” ndi “pansi pano.”—Mateyu 6:10.
8. Kodi mawu omasuliridwa kuti “makonzedwe” amatanthauza chiyani?
8 ‘Chom’komera,’ kapena kuti cholinga cha Yehova, chidzakwaniritsidwa mwa “makonzedwe.” Paulo anagwiritsa ntchito mawu amene kwenikweni amatanthauza “kusamalira zinthu panyumba.” Mawu amenewo sanena za boma, monga * Njira yabwino kwambiri imene Yehova anayendetsera zinthu pokwaniritsira cholinga chake inaphatikizapo “chinsinsi chopatulika” chomwe anachiulula pang’onopang’ono m’kupita kwa nthawi.—Aefeso 1:10; 3:9, NW, mawu a m’munsi.
Ufumu wa Mesiya ayi, koma za njira yosamalira zinthu.9. Kodi mwapang’onopang’ono Yehova anaulula motani chinsinsi cha chifuniro chake?
9 Kudzera m’mapangano osiyanasiyana, Yehova anali kuulula pang’onopang’ono mmene cholinga chake pankhani ya Mbewu yolonjezedwa mu Edene chidzakwaniritsidwire. Pangano lomwe anachita ndi Abrahamu linasonyeza kuti Mbewu yolonjezedwa idzabwera padziko lapansi kudzera mumzera wa Abrahamu ndipo “mitundu yonse ya dziko lapansi” idzadzidalitsa mwa Mbewu imeneyo. Panganoli linasonyezanso kuti anthu ena adzagwirizana ndi mbali yoyamba ya mbewuyo. (Genesis 22:17, 18) Pangano la Chilamulo lomwe anapanga ndi Israyeli wakuthupi linasonyeza cholinga cha Yehova chokhala ndi “ufumu . . . wa ansembe.” (Eksodo 19:5, 6) Pangano lomwe anapanga ndi Davide linasonyeza kuti Mbewuyo idzakhala Mfumu ku nthawi zonse. (2 Samueli 7:12, 13; Salmo 89:3, 4) Pangano la Chilamulo litafikitsa Ayuda kwa Mesiya, Yehova anasonyezanso mbali zina za kukwaniritsidwa kwa cholinga chake. (Agalatiya 3:19, 24) Anthu amene anali kudzagwirizana ndi mbali yoyamba ya mbewuyo adzapanga “ufumu . . . wa ansembe” womwe unaloseredwa kale ndipo adzalowetsedwa ‘m’pangano latsopano’ monga “Israyeli” watsopano, wauzimu.—Yeremiya 31:31-34; Ahebri 8:7-9. *
10, 11. (a) Kodi Yehova anaulula motani Mbewu yomwe inaloseredwa? (b) N’chifukwa chiyani Mwana wobadwa yekha wa Mulungu anabwera padziko lapansi?
Luka 1:32, 33) Apa zinadziwika bwino kuti Mbewu yolonjezedwayo ndani.—Agalatiya 3:16; 4:4.
10 Mogwirizana ndi makonzedwe a cholinga cha Mulungu, nthawi inakwana yoti Mbewu yomwe inaloseredwa ionekere padziko lapansi. Yehova anatumiza mngelo Gabrieli kukafotokozera Mariya kuti adzabala mwana wamwamuna amene adzamutche dzina loti Yesu. Mngeloyo anafotokoza kuti: “Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzam’patsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake: ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo ku nthawi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha.” (11 Mwana wobadwa yekha wa Yehova anali kudzabwera padziko lapansi ndi kudzayesedwa mpaka imfa. Zochita za Yesu ndi zimene zikanathandiza kuti papezeke yankho logwira mtima pa zimene Satana anatsutsa zija. Kodi adzakhalabe wokhulupirika kwa Atate wake? Izi zinakhudza chinsinsi chopatulika. Patapita zaka zingapo mtumwi Paulo anadzafotokoza udindo wa Yesu kuti: “Chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu n’chachikulu: Iye amene anaonekera m’thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m’dziko lapansi, wolandiridwa m’ulemerero.” (1 Timoteo 3:16) Inde, chifukwa chokhala wokhulupirika kwambiri mpaka imfa, Yesu anapereka yankho lotsimikizirika pa zimene Satana anatsutsa zija. Komabe mbali zina za chinsinsi chopatulika chija zinali zisanadziwikebe.
“Chinsinsi cha Ufumu wa Mulungu”
12, 13. (a) Kodi mbali imodzi ya “chinsinsi cha Ufumu wa Mulungu” ndi yotani? (b) Kodi Yehova anafunika kuchitanji kuti asankhe kagulu ka anthu owerengeka opita kumwamba?
12 Nthawi ina paulendo wake wolalikira ku Galileya, Yesu anasonyeza kuti chinsinsi chopatulikacho chinali chogwirizana kwambiri ndi boma lake la Ufumu wa Mesiya. Anauza ophunzira ake kuti: “Kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba [“Ufumu wa Mulungu,” Marko 4:11].” (Mateyu 13:11) Mbali imodzi ya chinsinsicho inali yoti Yehova adzasankha “kagulu ka nkhosa” ka anthu 144,000 kuti agwirizane ndi Mwana wake monga mbali ya mbewu, ndi kukalamulira naye limodzi kumwamba.—Luka 12:32; Chivumbulutso 14:1, 4.
13 Chifukwa choti anthu analengedwa kuti akhale padziko lapansi, panafunika kuti Yehova apange ‘chilengedwe chatsopano’ kuti anthu ena athe kupita kumwamba. (2 Akorinto 5:17) Polankhula monga mmodzi wa anthu osankhidwa kukhala ndi chiyembekezo chapadera chodzapita kumwambachi, mtumwi Petro analemba kuti: “Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Kristu; kuti tilandire cholowa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira m’Mwamba inu.”—1 Petro 1:3, 4.
14. (a) Kodi anthu amene sanali Ayuda analowetsedwa motani mu “chinsinsi cha Ufumu wa Mulungu”? (b) N’chifukwa chiyani ifeyo tikutha kumvetsetsa zinthu “zakuya za Mulungu” zimenezi?
14 Mbali ina ya chinsinsi chopatulika yokhudzana ndi boma lam’tsogolo la Ufumu inali chifuniro cha Mulungu choti pa anthu owerengeka odzaitanidwa kukalamulira ndi Kristu kumwamba pakhalenso anthu ena amene sanali Ayuda. Paulo anafotokoza mbali imeneyi ya “makonzedwe” a Yehova, kapena kuti njira yosamalira zinthu pokwaniritsa cholinga chake, kuti: ‘[Chinsinsi] chimenechi sanachizindikiritsa ana a anthu m’mibadwo ina, monga anachivumbulutsa tsopano kwa atumwi ndi aneneri ake oyera mwa Mzimu, kuti amitundu ali olowa nyumba pamodzi ndi ife, ndi ziwalo zinzathu za thupilo, ndi olandira nafe pamodzi palonjezano mwa Kristu Yesu, mwa Uthenga Wabwino.’ (Aefeso 3:5, 6) ‘Atumwi . . . oyera’ ndiwo anazindikiritsidwa mbali imeneyi ya chinsinsi chopatulika. N’chimodzimodzimodzinso ndi masiku ano; mzimu woyera ukadapanda kutithandiza, sitikanatha kumvetsetsa zinthu “zakuya za Mulungu” zimenezi.—1 Akorinto 2:10; 4:1; Akolose 1:26, 27.
15, 16. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anasankha olamulira anzake a Kristu kuchokera mwa anthu?
15 Anthu “zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi” amene anaoneka ataimirira ndi Chivumbulutso 14:1-4) Yehova anasankha woyamba mwa ana ake akumwamba kuti akhale mbali yoyamba ya mbewu yomwe inalonjezedwa mu Edene, komano n’chifukwa chiyani anasankha anzake a Kristu kuchokera mwa anthu? Mtumwi Paulo anafotokoza kuti anthu owerengeka amenewa ‘anaitanidwa monga mwa kutsimikiza mtima’ kwa Yehova, “umo kunakomera chifuniro chake.”—Aroma 8:17, 28-30; Aefeso 1:5, 11; 2 Timoteo 1:9.
“Mwanawankhosa” m’phiri la Ziyoni kumwamba akutchedwa “ogulidwa kuchokera kudziko,” amene “anagulidwa mwa anthu zipatso zoundukula kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa,” Kristu Yesu. (16 Cholinga cha Yehova n’choti ayeretse dzina lake lalikulu ndi loyera ndi kutsimikizira kuti iye ndiye woyenera kulamulira m’chilengedwe chonse. Mwa “makonzedwe,” kapena kuti njira yake yosamalira zinthu, yomwe ndi yanzeru zakuya kwambiri, Yehova anatumiza padziko lapansi Mwana wake woyamba kubadwa, pomwe anadzayesedwa mpaka imfa. Komanso, Yehova anaona kuti boma la Ufumu wa Mesiya la Mwana wake lidzakhalenso ndi anthu omwe adzakhalire kumbuyo ulamuliro Wake mpaka imfa.—Aefeso 1:8-12; Chivumbulutso 2:10, 11.
17. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kusangalala kuti Kristu limodzi ndi anzake amene adzalamulire naye anakhalapo anthu?
17 Yehova anasonyeza chikondi chake chachikulu kwa mbadwa za Adamu mwa kulola Mwana wake kubwera padziko lapansi komanso mwa kusankha anthu okalamulira limodzi ndi Mwana wakeyo m’boma la Ufumu kuchokera mwa anthu. Kodi anthu ena amene akhala okhulupirika kwa Yehova, kungoyambira pa Abele, adzapindula bwanji ndi zimenezi? Popeza kuti anthu opanda ungwiro amabadwa ali akapolo a uchimo ndi imfa, iwo anafunikira kuchiritsidwa mwauzimu ndi mwakuthupi kuti afike pokhala angwiro, mogwirizana ndi cholinga chomwe Yehova anali nacho poyambirira pamene analenga anthu. (Aroma 5:12) Onse oyembekezera moyo wosatha padziko lapansi amalimbikitsidwa kwambiri kudziwa kuti Mfumu yawo idzakhala yachikondi ndiponso yokoma mtima monga momwe inachitira ndi ophunzira ake panthawi ya utumiki wake padziko lapansi. (Mateyu 11:28, 29; Ahebri 2:17, 18; 4:15; 7:25, 26) Komanso n’zowalimbikitsa kudziwa kuti anzake a Kristu omwe adzakhale mafumu ndi ansembe kumwamba, adzakhala amene kale anali amuna ndi akazi achikhulupiriro omwe nawonso analimbana ndi zofooka ndiponso mavuto m’moyo monga momwe ifeyo tikuchitira!—Aroma 7:21-25.
Cholinga cha Yehova N’chosalephereka
18, 19. N’chifukwa chiyani tikumvetsetsa mawu a Paulo omwe ali pa Aefeso 1:8-11, ndipo m’nkhani yotsatirayi tiona zotani?
18 Tamvetsetsa tsopano tanthauzo la mawu a pa Aefeso 1:8-11, omwe Paulo ananena kwa Akristu odzozedwa. Iye ananena kuti Yehova anawazindikiritsa “chinsinsi cha chifuniro chake,” kuti ‘anayesedwa [olandira, NW] cholowa,’ ndi Kristu ndiponso kuti ‘anawakonzeratu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye wakuchita zonse monga mwa uphungu wa chifuniro chake.’ Tazindikira kuti zimenezi zikugwirizana ndi “makonzedwe” apamwamba a Yehova pofuna kukwaniritsa cholinga chake. Izi zikutithandizanso kumvetsetsa chifukwa chimene Akristu owerengeka okha ofika pa mwambo wa Mgonero wa Ambuye ndiwo amadya mkate ndi kumwa vinyo.
19 M’nkhani yotsatirayi, tiona kuti Chikumbutso cha imfa ya Kristu chimatanthauza chiyani kwa Akristu amene akuyembekezera kupita kumwamba. Tionanso kuti n’chifukwa chiyani anthu ambiri amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi pano kwamuyaya ayenera kukhala ndi chidwi chachikulu ndi tanthauzo la Chikumbutso.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Dzina la Mulungu limatanthauza “Amachititsa Kukhala.” Yehova angathe kukhala chilichonse chomwe chingafunike kuti akwaniritse cholinga chake.—Eksodo 3:14.
^ ndime 8 Mawu a Paulo akusonyeza kuti “makonzedwe” amenewa anali kugwira ntchito m’nthawi yake, koma Malemba amasonyeza kuti nthawi imeneyo Ufumu wa Mesiya unali usanakhazikitsidwe mpaka mu 1914.
^ ndime 9 Kuti mumve mwatsatanetsatane za mapangano amenewa, okhudza kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Mulungu, onani Nsanja ya Olonda ya February 1, 1989, masamba 10 mpaka 15.
Kubwereza
• N’chifukwa chiyani Yehova analenga dziko lapansi ndi kuikapo anthu?
• N’chifukwa chiyani Mwana wobadwa yekha wa Yehova anafunika kuti ayesedwe padziko lapansi?
• N’chifukwa chiyani Yehova anasankha olamulira anzake a Kristu kuchokera mwa anthu?
[Mafunso]