“Tapeza Ife Mesiya”
“Tapeza Ife Mesiya”
“TAPEZA ife Mesiya.” “Iye amene Mose analembera za Iye m’chilamulo, ndi aneneri, tam’peza.” Mawu achisangalalo amenewa ananenedwa ndi Ayuda awiri okhulupirika, zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Mesiya amene anali kumuyembekezera kwa nthawi yaitali anali atafika. Anthuwa anali ndi chikhulupiriro chonse kuti sangakhalenso wina ayi.—Yohane 1:35-45.
Tikaganizira mmene zinalili zinthu m’nthawiyo pankhani ya chikhalidwe ndi chipembedzo, zimachititsa chidwi kwambiri kuona kuti anthuwa anali ndi chikhulupiriro choterechi. Anthu angapo omwe anaganiziridwa kuti adzamasula anthu anali atabwera, modzionetsera komanso ndi malonjezo ambirimbiri, koma mosapita nthawi anthu ankakhumudwa, iwo atalephera kupulumutsa Ayuda mu ukapolo wa Aroma.—Machitidwe 5:34-37.
Koma Ayuda awiriwa, Andreya ndi Filipo, sanakayikire m’pang’ono pomwe zoti apeza Mesiya weniweni. M’malo mwake, m’zaka zotsatira, chikhulupiriro chawo chinakula pamene ankadzionera okha ntchito zamphamvu zomwe munthu ameneyu ankachita pokwaniritsa maulosi onena za Mesiya.
Kodi n’chifukwa chiyani anthu awiriwa komanso ena ambiri anam’khulupirira, osam’kayikira n’komwe kuti mwina ndi Mesiya wachinyengo kapena kamberembere woti angowakhumudwitsa? Kodi ndi zinthu zotani zomwe zinatsimikizira kuti iye analidi Mesiya?
Mbiri imasonyeza kuti Andreya ndi Filipo anazindikira kuti Yesu wa ku Nazarete, yemwe anali Yohane 1:45) Wolemba mbiri wina panthawi imeneyo, yemwe anali katswiri pantchito yake, dzina lake Luka, anafotokoza kuti kubwera kwa Mesiya kumeneku kunachitika ‘m’chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberiyo Kaisara.’ (Luka 3:1-3) Chaka chakhumi ndi chisanu cha ulamuliro wa Tiberiyo chimenechi chinayamba mu September wa mu 28 C.E. n’kudzatha mu September wa mu 29 C.E. Luka anafotokozanso kuti panthawiyo, Ayuda “anali kuyembekezera” kufika kwa Mesiya. (Luka 3:15) N’chifukwa chiyani anthu anali kumuyembekezera pa nthawi imeneyi? Tiona zimenezi bwino lino.
wopala matabwa, ndiye anali Mesiya wolonjezedwa amene anthu anakhala akumuyembekezera kwa nthawi yaitali. (Zoyenereza Mesiya
Popeza kuti udindo wa Mesiya unali waukulu, mungasangalale kudziwa kuti Mlengi wathu, Yehova, anapereka maumboni osiyanasiyana pofuna kuthandiza anthu atcheru ndi okhulupirika kuzindikira Mesiya wolonjezedwa. Chifukwa chiyani anatero? Pochita zimenezi anathandiza anthu atcheru kuti asadzapusitsidwe ndi anthu achinyengo ngati mmene zinachitikira ndi anthu ambiri.
Kazembe wa dziko akamakayamba ntchito yake m’dziko lina amafunika kupereka kwa akuluakulu a dzikolo makalata otsimikizira kuti iye ndiyedi kazembe wovomerezedwa ndi dziko lake. N’chimodzimodzinso ndi Mesiya. Yehova anali atalemberatu kalekale zinthu zimene Mesiya adzakwaniritse. Motero, pamene ‘Mtumiki Wamkuluyu,’ anaonekera zinakhala ngati ali ndi makalata otsimikizira kuti ndiyedi Mesiya.—Ahebri 12:2, NW.
Maulosi ambirimbiri m’Baibulo, omwe analembedwa zaka zambiri Mesiya asanaonekere, anali ndi zinthu zomuyenereza zimene anafunikira kuzikwaniritsa. Maulosiwo ananena mwatsatanetsatane mmene Mesiya adzafikire, za utumiki wake, kuzunzidwa kwake ndi anthu, ndiponso mmene adzafere. Mungakonde kudziwa kuti maulosi odalirika amenewo ananenanso za kuuka kwake, kukwezedwa kwake n’kukhala pa dzanja lamanja la Mulungu, ndipo pomaliza ananenanso za madalitso omwe ulamuliro wa Ufumu wake udzabweretse. Motero, maulosi a m’Baibulowo anapereka chizindikiro chapadera chomwe chikanangozindikiritsa munthu mmodzi yekha basi.
N’zoona kuti, Yesu atakhala Mesiya mu 29 C.E., sikuti maulosi onse onena za Mesiya anakwaniritsidwa nthawi yomweyo ayi. Mwachitsanzo, panthawiyo anali asanaphedwe ndi kuukitsidwa. Komabe, Andreya, Filipo, limodzi ndi anthu ena ambiri anakhulupirira Yesu chifukwa cha zinthu zomwe ankaphunzitsa ndi kuchita. Iwo anaona umboni wokwanira, wotsimikizira kuti iye analidi Mesiya. N’kutheka kuti nanunso mukanakhalapo nthawi imeneyo n’kudzionera nokha maumboni amenewo, mulibe maganizo alionse osuliza, mukanakhutira kuti Yesu ndiyedi Mesiya.
Umboni Wosiyanasiyana
Kodi n’chiyani chikanakuthandizani kuti mufike pomukhulupirira? Kwa zaka zambirimbiri, aneneri a m’Baibulo anafotokoza zinthu zomwe Mesiya anafunikira kudzachita, zomwe zikanam’dziwikitsa bwino kwambiri. Pamene aneneriwo anali kufotokoza zinthu zimenezi, pang’ono ndi pang’ono anthu anakhala ndi chithunzithunzi cha Mesiya. Henry H. Halley anati: “Tiyerekeze kuti anthu angapo ochokera m’mayiko osiyanasiyana, amene sanaonanepo kapena kulankhulana mwanjira ina iliyonse, aliyense wa iwo akulowa m’chipinda chinachake, n’kumasiyamo mwala wosemedwa bwinobwino ndipo miyalayo ikalumikizidwa ikupanga munthu wooneka bwino kwambiri, kodi tingafotokoze kuti zimenezi zatheka chonchi motani, popanda kunena kuti munthu winawake anafotokozera aliyense wa anthuwo zofunika kuchita?” Kenako anafunsa kuti: “Kodi tingafotokoze bwanji umboni wosiyanasiyana wodabwitsawu wa moyo ndi ntchito ya Yesu womwe unalembedwa ndi anthu osiyanasiyana, m’nthawi zosiyanasiyana, ndipo anaulemba zaka zambirimbiri Yesuyo asanabwere, popanda kunena kuti ntchito yolembayo inayang’aniridwa ndi Winawake Wauzimu?” Ndiyeno, Halley anafotokoza kuti “ichi ndi chozizwitsa chachikulu kwambiri!”
‘Chozizwitsachi’ chinayambira m’buku loyambirira la m’Baibulo. Kuwonjezera pa ulosi Genesis 3:15; 22:15-18) Chizindikiro china chinasonyeza kuti Mesiya adzachokera m’fuko la Yuda. (Genesis 49:10) Mulungu anauza Aisrayeli kudzera mwa Mose kuti Mesiya adzakhala mneneri ndi mpulumutsi wamkulu kuposanso Mose.—Deuteronomo 18:18.
woyambirira wa m’Baibulo womwe unasonyeza udindo wa Mesiya, wolemba buku la Genesis anati Mesiya adzabadwira mu mzera wa Abrahamu. (M’masiku a Mfumu Davide, ulosi unasonyeza kuti Mesiya adzalowa ufumu wa Davide ndipo ufumu wake “udzakhazikika ku nthawi zonse.” (2 Samueli 7:13-16) Buku la Mika linanena kuti Mesiya adzabadwira mu mzinda womwe Davide ankachokera, mzinda wa Betelehemu. (Mika 5:2) Yesaya analosera kuti Iye adzabadwa kwa namwali. (Yesaya 7:14) Mneneri Malaki analosera kuti kubwera Kwake kudzalengezedwa ndi munthu wina wofanana ndi Eliya.—Malaki 4:5, 6.
Mfundo inanso yofotokoza bwino za Mesiya imapezeka m’buku la Danieli. Potchula chaka chenicheni chimene Mesiya adzaonekere, ulosiwo unati: ‘Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kum’manga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto.’—Danieli 9:25.
Mfumu Aritasasta ya Perisiya inatulutsa “lamulo” lomanganso Yerusalemu m’chaka cha 20 cha ulamuliro wake. Iye anayamba kulamulira mu 474 B.C.E., motero chaka cha 20 cha ulamuliro wake chinali chaka cha 455 B.C.E. (Nehemiya 2:1-8) Motero, kuchokera nthawi yomwe panatuluka lamulo lokamanganso Yerusalemu, kudzafika pa kuonekera kwa Mesiya, panayenera kudutsa masabata 69 (7 kuphatikizapo 62) aulosi. N’zosachita kufunsa kuti m’masabata 69 enieni muli masiku 483 okha, kapena kuti nthawi yosakwana n’komwe zaka ziwiri. Koma tikatsatira kuwerengera masiku kwa ulosi, “tsiku limodzi ngati chaka chimodzi,” zikusonyeza kuti Mesiya anadzaonekera patatha zaka 483, m’chaka cha 29 C.E.—Ezekieli 4:6. *
Ngakhale kuti anthu angapo odzitcha Mesiya anaonekera panthawi zosiyanasiyana, Yesu wa ku Nazarete anaonekera padzikoli monga Mesiya m’chaka cha 29 C.E. (Luka 3:1, 2) Chaka chomwecho, Yesu anabwera kwa Yohane Mbatizi ndi kubatizidwa m’madzi. Pambuyo pake, Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera n’kukhala Mesiya. Kenako, posonyeza Yesu kwa Andreya ndi wophunzira wake wina, Yohane, amene analoseredwa kuti adzakhala ngati Eliya ndiponso kalambulabwalo wa Yesu, anatcha Yesuyo, “Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi.”—Yohane 1:29; Luka 1:13-17; 3:21-23.
Banja Lobadwiramo Mesiya
Maulosi ouziridwa anasonyeza kuti Mesiya adzachokera m’mabanja enaake achiyuda. Motero m’pomveka kuti Mlengi wanzeru akonze zoti Mesiya abwere panthawi yoti akaundula a mabanjawo anali alipo kuti makolo ake athe kudziwika bwinobwino.
Buku lina lofotokoza za m’Baibulo, lomwe analemba McClintock ndi Strong limati: “N’zosakayikitsa kwenikweni kuti akaundula a mafuko ndi mabanja achiyuda anawonongedwa pamene Yerusalemu ankawonongedwa [mu 70 C.E.]; sanawonongedwe chakachi chisanakwane.” Pali umboni wokwanira wosonyeza kuti Mateyu ndi Luka analemba mabuku awo a Uthenga Wabwino chisanakwane chaka cha 70 C.E. Motero, n’kutheka kuti pamene ankalemba za makolo a Mateyu 1:1-16; Luka 3:23-38) Ndipo n’zodziwikiratu kuti pankhani yofunikira kwambiri ngati imeneyi, anthu ambiri a m’nthawi yawo akanafuna kutsimikizira okha za makolo a Yesu.
Yesu, iwo ankagwiritsa ntchito akaundula amenewo. (Kodi Zinangochitika Mwamwayi Kuti Zinakwaniritsidwa mwa Yesu?
Komabe, kodi zingatheke kuti unali mwayi chabe kuti Yesu anakwaniritsa maulosi onena za Mesiya? Katswiri wina wa maphunziro atafunsidwa za nkhaniyi anayankha kuti: “Sizingatheke kungochitika mwamwayi. N’zovuta kwambiri kuti zichitike choncho. Munthu wina anachita masamu ndipo anapeza kuti mwayi woti maulosi eyiti okha akwaniritsidwe n’ngochepa kwambiri, moti zingakhale ngati kufufuza chinthu chinachake pa zinthu zinzake mabiliyoni okwanira mamiliyoni wani handiredi.” Potithandiza kumvetsa kuvuta kwakeko, iye anati: “Mutatenga ndalama za siliva zokwanira nambala tatchula ija mukhoza kuziyala masentimita 60 kuchokera pansi m’dziko lonse la Texas [lomwe kukula kwake ndi kuposa makolomita 690,000]. Mutati muike chizindikiro ndalama imodzi, ndiyeno n’kuuza munthu woti mwam’manga m’maso kuti ayendeyende m’dziko lonselo penapake n’kutola ndalama imodzi, kodi pangakhale mwayi wotani wotola ndalama mwaiika chizindikiro ija?” Kenako ananena kuti “mmenemu ndi mmene zingakhalire zovuta kuti winawake akwaniritse maulosi eyiti chabe onena za [Mesiya].”
Koma, pazaka zitatu ndi theka za utumiki wake, Yesu sikuti anangokwaniritsa maulosi eyiti okha, koma anakwaniritsanso maulosi ambirimbiri a m’Baibulo. Kuchuluka kwa maumboni kotereku, kunachititsa katswiri wa maphunziro uja kunena kuti: “Yesu, ndipo ndi Yesu yekha amene anakwanitsa zimenezo.”
‘Kudza’ kwa Mesiya
N’zoonekeratu kuti Mesiya anabwera mu 29 C.E. ndipo anali Yesu wa ku Nazarete. Umu ndi mmene anabwerera Muwomboli, wodzichepetsa amene anavutika. Panthawiyo sanabwere ngati Mfumu yolakika kuti adzapasule goli lozunza la Aroma ayi, ndipo zikuoneka kuti izi n’zimene Ayuda ambiri ngakhalenso anthu omutsatira ankayembekezera. (Yesaya, chaputala 53; Zekariya 9:9; Machitidwe 1:6-8) Koma, ulosi umanena kuti pakubwera kwake kwam’tsogolo adzakhala ndi mphamvu ndiponso ulamuliro waukulu.—Danieli 2:44; 7:13, 14.
Kuphunzira maulosi a m’Baibulo mosamala kwambiri kwathandiza anthu oganiza bwino padziko lonse kukhulupirira kuti Mesiya anabwera koyamba zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, ndiponso kuti adzabweranso. Maumboni akusonyeza kuti kubweranso kwake kumene kunanenedwa kale, komwe ndi chiyambi cha “kufika” kapena kuti kukhalapo kwake, kunachitika mu 1914. * (Mateyu 24:3-14) Chaka chimenecho, Yesu mosaonekera kwa anthu, analongedwa ufumu kumwamba monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Posachedwapa adzachitapo kanthu kuti athetse mavuto a padziko pano omwe anayamba chifukwa cha kupanduka komwe kunachitika mu Edene. Ulamuliro wake wa za 1,000 womwe udzatsatirepo udzadalitsa anthu onse okhulupirira kuti iye ndiye Mbewu yolonjezedwa, Mesiya, amene “achotsa tchimo lake la dziko lapansi.”—Yohane 1:29; Chivumbulutso 21:3, 4.
Mboni za Yehova zidzakhala zokondwa kukambirana nanu umboni umenewo ndi kukusonyezani m’Baibulo mmene inuyo ndi okondedwa anu adzakhalire mu ulamuliro wa Mesiya.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 17 Kuti mumvetse bwino lemba la Danieli 9:25, onani buku la Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, masamba 899 mpaka 904. Bukuli limafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
^ ndime 27 Kuti mumve tsatanetsatane wa nkhaniyi, onani mutu 10 ndi 11 m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Zithunzi pamasamba 6, 7]
Mu 455 B.C.E., “lamulo lakukonzanso. . .Yerusalemu”
Mu 29 C.E., Mesiya anabwera
Zaka 483 (masabata 69 aulosi)—Danieli 9:25
Mu 1914, Mesiya analongedwa ufumu kumwamba
Posachedwapa Mesiya adzathetsa kuipa n’kupanga dziko kukhala paradaiso