Umboni Wakale Kwambiri Woti Mabuku a M’Baibulo ndi Ovomerezeka
Umboni Wakale Kwambiri Woti Mabuku a M’Baibulo ndi Ovomerezeka
“MZERE uliwonse umaoneka kuti anaulemba makamaka n’cholinga chokopa anthu omwe ali ndi chidwi ndi mbiri ya Akristu oyambirira.” Umu ndi mmene mpukutu winawake wakale kwambiri unafotokozedwera. Kodi mukuganiza kuti mpukutuwu ndi uti?
N’kutheka kuti munamvapo kale kapena kuti simunamvepo za mpukutu wa Muratori. Kaya munamvapo nkhani yake kapena ayi, koma mwina mukudabwa kuti, ‘N’chiyani chinapangitsa mpukutu wa Muratori kukhala wapadera chonchi?’ Mpukutuwu uli ndi mndandanda wa mabuku ovomerezeka a Malemba Achigiriki Achikristu, ndipo umenewu ndi mndandanda wakale kwambiri womwe ulipo panopa.
Mwina kwa inuyo sinkhani yaikulu kuti ndi mabuku ati kwenikweni amene ali m’Baibulo. Koma, kodi mungadabwe kumva kuti nthawi inayake, anthu ena ankakayikira za mabuku oyenerera kukhala m’Baibulo? Mpukutu kapena kuti mndandanda wa mabuku ovomerezeka wa Muratori uli ndi mabuku omwe anthu ankaona kuti ndi ouziridwa. Mwina mukudziwa kuti, nkhani zopezeka m’Baibulo n’zofunika kwambiri. Ndiye kodi mpukutuwu umasonyeza zotani pankhani ya mabuku omwe tsopano ali m’Malemba Achigiriki Achikristu? Poyamba, tiyeni tioneko za mbiri ya mpukutuwu.
Mmene Unapezekera
Mpukutu wa Muratori ndi mbali ya mpukutu wolemba pamanja wa masamba 76 a zikopa, ndipo tsamba lililonse n’la masentimita 27 m’litali ndi masentimita 17 m’lifupi mwake. Ludovico Antonio Muratori (1672-1750), Mtaliyana wolemba mbiri wotchuka kwambiri, anapeza mpukutuwu mu laibulale ya Ambrosian, mu mzinda wa Milan, ku Italy. Muratori anafalitsa zomwe anapezazo mu 1740, ndipo n’chifukwa chake umatchedwa mpukutu wa Muratori. Zikuoneka kuti mpukutu wolemba pamanjawo unalembedwa zaka zoposa 1,200 zapitazo m’nyumba ina yakale ya amonke ya Bobbio, kufupi ndi tawuni ya Piacenza, kumpoto kwa dziko la Italy. Malemba a pamanjawo anapita nawo ku laibulale ya Ambrosian kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1600.
Mpukutu wa Muratori uli ndi mizere 85 ya mawu a pamasamba 10 ndi 11 a mpukutu wolemba pamanja uja. Malemba a pamanjawo ali m’Chilatini, ndipo zikuoneka kuti mlembi amene anawakopera sanali wosamala kwenikweni. Komabe zina mwa zimene anaphonyetsa zinatulukiridwa mwa
kufananitsa zomwe iye anakoperazo ndi zimene zili m’zolemba pamanja zina zinayi zomwe zinalembedwa zaka za m’ma 1000 ndi 1100.Kodi Unalembedwa Liti?
Komabe, n’kutheka kuti mukufuna kudziwa kuti ndi liti pamene mpukutu wa Muratori unalembedwa koyamba. Zikuoneka kuti mpukutu woyambirira unalembedwa m’Chigiriki zaka zambirimbiri mpukutu wa Muratori usanapangidwe, womwe unamasuliridwa m’Chilatini kuchokera m’Chigiriki. Taonani njira yothandiza kudziwa nthawi yomwe mpukutu woyambirirawo unalembedwa. Mpukutuwo umatchula za buku lina lomwe si la m’Baibulo, buku la Shepherd, ndipo umati munthu wina dzina lake Hermas walemba bukuli “posachedwapa, masiku athu ano, mu mzinda wa Roma.” Akatswiri amaphunziro amati Hermas anatsiriza kulemba buku lake lakuti Shepherd pakati pa 140 ndi 155 C.E. Motero, mungathe kuona chifukwa chake anthu amanena kuti mpukutu woyambirira wa Chigiriki unalembedwa pakati pa 170 ndi 200 C.E., ndipo mpukutu wa Muratori wa Chilatini anaumasulira kuchokera ku mpukutu umenewo.
Zikuoneka kuti mwina unalembedwera ku Roma chifukwa umatchula mzindawu mwachindunji kapena umangotchula zinthu zina zokhudza mzindawu. Koma panopa anthu sanagwirizane chimodzi kuti ndi ndani makamaka amene anaulemba. Ena amaganiza kuti ndi Clement wa ku Alesandriya, pamene ena amati ndi Melito wa ku Sarde, ndipo ena amaganiza kuti ndi Polycrates wa ku Efeso. Koma, akatswiri ambiri amaphunziro, amaganiza kuti analemba ndi Hippolytus, wolemba mabuku a Chigiriki wotchuka kwambiri yemwe ankakhala ku Roma panthawi yomwe ikuoneka kuti ndi pamene mpukutu wa Muratori unalembedwa. Ngakhale kuti mwina simungachite chidwi kwenikweni ndi zimenezi, n’kutheka kuti mukufuna kudziwa bwino zimene zili mu mpukutuwu zomwe zikuchititsa kuti ukhale wofunika kwambiri.
Zomwe Zili mu Mpukutuwu
Mpukutuwu uli ndi zinthu zinanso kuwonjezera pa mndandanda wa mabuku a Malemba Achigiriki Achikristu. Uli ndi ndemanga zonena za mabuku ndi anthu amene analemba mabukuwo. Mutati mwawerenga mpukutuwu, mukhoza kuona kuti ulibe mizere yoyamba ya malemba apamanjawo, ndipo umaonekanso ngati unathera m’malere. Umayamba ndi kutchula Uthenga Wabwino wa Luka, ndipo umanena kuti amene analemba buku la m’Baibulo limeneli anali dokotala. (Akolose 4:14) Umanena kuti, buku lomwe Luka analemba ndi lachitatu pa mabuku a Uthenga Wabwino, motero mungathe kuona kuti mbali yoyambirira yomwe inasowayo iyenera kuti inanena za Mauthenga Abwino a Mateyu ndi Marko. Ngati umu ndi momwe inu mukuonera, ndiye kuti mukugwirizana ndi zomwe mpukutu wa Muratori umanena, chifukwa umati Uthenga Wabwino wachinayi ndi wa Yohane.
Mpukutuwu umavomereza kuti buku la Machitidwe a Atumwi analemba ndi Luka, kulembera ‘Teofilo wabwino.’ (Luka 1:3; Machitidwe 1:1) Ndiyeno uli ndi mndandanda wa makalata a mtumwi Paulo opita kwa Akorinto (awiri), kwa Aefeso, kwa Afilipi, kwa Akolose, kwa Agalatiya, kwa Atesalonika (awiri), kwa Aroma, kwa Filemoni, kwa Tito, ndi kwa Timoteo (awiri). Umanenanso za kalata ya Yuda ndiponso makalata awiri a Yohane kuti ndi mabuku ouziridwa. Kalata yoyamba ya mtumwi Yohane inatchulidwa chakoyambirira limodzi ndi Uthenga Wabwino womwe iye analemba. Buku lomaliza pamndandanda wa mabuku omwe anali kuonedwa kuti ndi ouziridwawu ndi buku la Chivumbulutso.
N’zochititsa chidwi kuti mpukutuwu umatchula za buku lina la Chivumbulutso cha Petro koma umati anthu ena ankaona kuti Akristu sayenera kuliwerenga. Wolemba mpukutuwu anachenjeza kuti mabuku achinyengo anali atayamba kale kufalitsidwa m’masiku amenewo. Mpukutu wa Muratori umafotokoza kuti mabuku amenewa sayenera kuvomerezedwa, chifukwa “si bwino kusakaniza ndulu ndi uchi.” Mpukutuwu umatchulanso mabuku ena amene sanaikidwe m’gulu la malemba oyera. Mwina sanaikidwe chifukwa chakuti analembedwa atumwi onse atafa, ngati mmene zinalili ndi buku lakuti Shepherd la Hermas, kapena chifukwa chakuti analembedwa n’cholinga cholimbikitsa ziphunzitso zabodza.
Mwina mwaona kuti pa zimene tatchulazi, mndandanda wa mabuku ovomerezeka a m’Baibulowu ulibe kalata yopita kwa Ahebri, makalata awiri a Petro, ndiponso kalata ya Yakobo. Komabe, Dr. Geoffrey Mark Hahneman atatchula za luso la munthu amene anakopera malembawa, ananena kuti “m’pomveka kuganiza kuti mpukutuwu unali ndi mbali zina zotchula mabuku ena zomwe zinasowa, ndipo n’kutheka kuti ena mwa mabukuwo ndi Yakobo ndi Ahebri (ndiponso 1 Petro).”—The Muratorian Fragment and the Development of the Canon.
Motero mpukutu wa Muratori umavomereza kuti m’zaka za m’ma 100 C.E., anthu anali atayamba kale kuona ambiri mwa mabuku amene tsopano ali m’Malemba Achigiriki Achikristu kuti ndi ovomerezeka. Inde, kuvomerezeka kwa mabuku a m’Baibulo, kuti ndi oyenerera kukhala mbali ya mabuku a Baibulolo, sikukudalira kuti atchulidwe pamndandanda winawake wakale. Zimene zili m’mabuku a m’Baibulowo ndizo zimapereka umboni wakuti mabukuwo ndi ouziridwa ndi mzimu woyera. Mabuku onsewo amatsimikizira kuti analembedwa ndi Yehova Mulungu ndipo nkhani zake n’zogwirizana kwambiri. Kugwirizana kwa nkhani za m’mabuku onse 66 ovomerezeka a m’Baibulo ndi umboni wakuti Baibulo lonse ndi logwirizana ndiponso kuti lili ndi nkhani zonse zofunika. Ndiyetu mungapindule kwambiri ngati mutalivomereza ndi kulitsatira monga Mawu a Yehova a choonadi chouziridwa, lomwe lasungidwa mpaka masiku athu ano.—1 Atesalonika 2:13; 2 Timoteo 3:16, 17.
[Chithunzi patsamba 13]
Ludovico Antonio Muratori
[Chithunzi patsamba 14]
Laibulale ya Ambrosian
[Chithunzi patsamba 15]
Mpukutu wa Muratori
[Mawu a Chithunzi]
Diritti Biblioteca Ambrosiana. Vietata la riproduzione. Aut. No. F 157 / 05
[Mawu a Chithunzi patsamba 13]
Fragments: Diritti Biblioteca Ambrosiana. Vietata la riproduzione. Aut. No. F 157 / 05; Muratori, based on line art: © 2005 Brown Brothers