Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Uthenga Wabwino Ufika M’matawuni Aang’ono ku Bolivia

Uthenga Wabwino Ufika M’matawuni Aang’ono ku Bolivia

Uthenga Wabwino Ufika M’matawuni Aang’ono ku Bolivia

ANTHU pafupifupi 20 tasonkhana pagombe, kuyembekeza mwachidwi ulendo wopita kumidzi imene ili kumene kumachokera mtsinje wa Beni. Tili m’munsi mwenimweni mwa mapiri a Andes, pamalo amene mtsinje wa Beni umalowera m’chigwa cha mtsinje wa Amazon. Amenewa ndi malo okongola kwambiri!

Komatu siife alendo oona malo ayi. Ena a ife ndi a konkuno, ndipo enanso ndi ochokera ku mizinda yakutali, omwe anabwera kudzakhala kuno ku Rurrenabaque, tawuni yaing’ono ndiponso yokongola, yamitengo ya maluwa, nyumba za madenga ofolera udzu, ndi misewu yomwe mumadutsa njinga za moto mwa apa ndi apo. Kodi n’chifukwa chiyani takonza ulendowu?

Maulendo okhala ngati amenewa akuchitika m’madera enanso ambiri a ku Bolivia. Mboni za Yehova zochokera m’mizinda ndiponso m’mayiko ena zimalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu m’matawuni ang’onoang’ono.​—Mateyu 24:14.

Dziko la Bolivia lili pakatikati pa South America. Bolivia ndi dziko lalikulu kuwirikiza kawiri dziko la France koma chiwerengero cha anthu ndi pafupifupi 10 peresenti chabe ya chiwerengero cha anthu a ku France. Anthu ambiri a m’dziko la Bolivia amakhala m’mizinda ndiponso m’matawuni a migodi, m’madera okwera kwambiri kapena m’zigwa zimene amachitamo ulimi. Komabe matawuni a m’zigwa za m’madera otentha amenewa, amakhala ndi zipululu zikuluzikulu pakati pa tawuni ina kukafika tawuni inanso.

M’zaka za m’ma 1950 ndi 1960, amishonale olimba mtima, Betty Jackson, Elsie Meynberg, Pamela Moseley, ndi Charlotte Tomschafsky, anatsogolera ntchito yolalikira m’matawuni ambiri aang’ono. Iwo anaphunzitsa choonadi cha Baibulo anthu oona mtima ndi kuthandiza kukhazikitsa mipingo ing’onoing’ono. M’zaka za m’ma 1980 ndi 1990, chiwerengero cha Mboni za Yehova, makamaka m’mizinda, chinakwera mowirikiza kasikisi. Tsopano m’dera lililonse muli mipingo. Mungapeze mipingo ya Mboni za Yehova m’maboma otukuka, okhala ndi maofesi m’nyumba zazitali zamakono kumene anthu amagwirako ntchito, nyumba zikuluzikulu zamakono kumene anthu amakhala, ndi masitolo akuluakulu kumene anthu amagulako zinthu. Komanso mipingo ina ili m’madera a kumidzi, kumene anthu amakhala m’nyumba za zidina, misika yake ndi yapanja, komanso amavala zovala zokongola za chikhalidwe chawo. Komabe, kodi tingachite chiyani kuti tithandize anthu ambiri a kumidzi amenewa kuti adziwe Yehova?

Kusiya Moyo Wabwino wa M’mizinda

M’zaka 20 zapitazo, anthu ambiri anasamuka kuchoka ku matawuni a migodi ndi kumidzi ya ku Bolivia n’kupita kumizinda. Choncho n’zodabwitsa kuona anthu akusamuka kuchoka ku mzinda kupita kumudzi. Midzi yambiri ili ndi telefoni imodzi yokha ndiponso magetsi amayaka maola owerengeka okha patsiku. Mboni zimene zimakhala m’matawuni aang’ono amenewa zimaonana ndi okhulupirira anzawo pa misonkhano ya pachaka basi, ndipo kupita ku misonkhano imeneyi kungakhale kodula, koopsa ndiponso kotopetsa. Sukulu za kumudzi zimangophunzitsa kulemba ndi kuwerenga basi. Koma, kodi n’chiyani chimalimbikitsa Mboni za Yehova zambiri kusamuka kuchoka m’mizinda n’kupita kumidzi?

Posachedwapa Luis anatiuza kuti: “Ndinali ndi mwayi wopeza ntchito mu mzinda wa La Paz. Koma makolo anga ankandiuza nthawi zonse kuti ntchito yopanga ophunzira ndi yopindulitsa kwambiri. Choncho ndinachita kosi yaifupi ya luso la zomangamanga. Pamene ndinadzachita tchuthi kuno ku Rurrenabaque, ndinaona kuti anthu ali ndi chidwi chomvetsera uthenga wabwino. Nditaona kuti kuli abale owerengeka okha, ndinaganiza zoti ndibwere kudzathandiza. Panopo ndili ndi maphunziro a Baibulo a panyumba okwanira 12. Mwachitsanzo, ndimaphunzira ndi mwamuna wina wachinyamata limodzi ndi mkazi wake amene ali ndi ana anayi. Mwamunayu ankamwa mowa kwambiri ndiponso ankatchova juga, koma anasiya kuchita zonsezi ndipo wayamba kuuza anzake zimene akuphunzira ponena za Yehova. Nthawi zonse amakonzekera phunziro lake. Akapita ku nkhalango kukadula mitengo kwa masiku atatu kapena anayi amadandaula kwambiri chifukwa safuna kuphonya zinthu zachikristu. Ndikamaona banja lonselo litapezeka pa misonkhano yachikristu, ndimadziwa kuti ndinachita bwino kudzipereka kubwera kuno.”

Juana alibe banja koma ali ndi mwana. Iye anati: “Ndinkagwira ntchito ya m’nyumba ku La Paz. Pamene mwana wanga wamwamuna anali wamng’ono, ndinayamba utumiki wa nthawi zonse mu mzinda. Nditabwera kudzacheza kuno ku Rurrenabaque, ndinazindikira kuti ndingachite zambiri ngati nditasamukirako. Choncho ndinabwera, n’kupeza ntchito ya m’nyumba. Poyamba, zinali zovuta kupirira kutentha ndiponso zolumaluma. Koma takhala kuno zaka seveni tsopano. Ndimatha kuchititsa maphunziro a Baibulo ambiri mlungu uliwonse, ndipo ophunzira ambiri amasonyeza kuyamikira mwa kubwera ku misonkhano.” Juana ndi mwana wake wamwamuna ali pagulu la anthu aja amene akukwera bwato kupita kumene mtsinje wa Beni ukuchokera. Tiyeni tipitire limodzi.

Kulowera Kumene Mtsinje Ukuchokera

Injini ikulira ndipo tikuyamba ulendo kudutsa pakati pa mapiri. Mbalame za mtundu wa zinkhwe zikulira kukhala ngati zikudandaula potiona. Madzi a matope omwe akuchokera kumapiri akuvunduka pamene woyendetsa bwatolo akuliwongolera bwinobwino. Tikufika pa kamudzi kenakake dzuwa litakwera ndithu. Pamenepo tikukumana ndi mkulu wa Mpingo wa Rurrenabaque, ndipo akutionetsa kumene tikalalikire.

Anthu a m’mudziwo akutilandira bwino, ena akutilandirira pamithunzi ya mitengo, pamene ena akutilandirira m’nyumba za nsungwi zofoleredwa ndi masamba a mtengo wa mgwalangwa. Posakhalitsa tikukumana ndi banja lachinyamata, limene likusasantha nzimbe ndi chosasanthira cha matabwa. Madzi a nzimbewo akugwera m’mbiya ya mkuwa. Kenako, amawawiritsa mpaka atasanduka akuda ngati uchi ndiyeno n’kukagulitsa m’tawuni. Banjali likutilowetsa m’nyumba ndipo likutifunsa mafunso ambiri a Baibulo.

Tikupitirizabe ulendo wathu wopita kumene mtsinje ukuchokera, uku tikulalikira mudzi uliwonse. Anthu ambiri akusangalala kumva zimene Baibulo limanena zoti matenda ndi imfa sizidzakhalaponso. (Yesaya 25:8; 33:24) Kumalo amenewa, munthu amavutika kupeza chithandizo cha kuchipatala akadwala, ndipo mabanja ambiri akudziwa mmene imfa ya mwana imapwetekera. Anthuwa amakhala movutika chifukwa amangokhalira kulima ndi kuwedza nsomba zakudya basi. N’chifukwa chake, anthu ambiri akusangalala kwambiri ndi lonjezo la Mulungu limene limapezeka pa Salmo 72 lonena za boma limene lidzathetsa umphawi. Komabe, kodi mukuganiza kuti anthu achidwi amene akukhala m’midzi ya kutali imeneyi angakwanitse kufika ku misonkhano yachikristu? Funso limenelo linadetsa nkhawa Eric ndi Vicky, atumiki a nthawi zonse a ku Santa Rosa, mtunda woyenda maola atatu pagalimoto ndipo tawuniyi ili m’chigwa cha mtsinje wa Amazon.

Kodi Anthu Achidwiwo Angabwere Kumisonkhano?

Eric ndi Vicky anabwera ku Bolivia kuchokera ku California, m’dziko la United States, zaka 12 zapitazo. Woyang’anira woyendayenda anauza Eric ndi Vicky maganizo oti asamukire ku Santa Rosa. “Tawuniyi ili ndi matelefoni awiri okha ndiponso kulibe Intaneti,” anatero Vicky. “Kuli zinyama zambiri. Kawirikawiri timaona ng’ona, nthiwatiwa, ndi njoka zikuluzikulu tikamapita ku madera ozungulira tawuniyi pa njinga zathu zamoto. Komabe, zosangalatsa kuposa zinyamazo ndi anthu. Timaphunzira Baibulo ndi banja lina lachinyamata la a Vaca, amene ali ndi ana aang’onoang’ono anayi. Amakhala pamtunda wa makilomita pafupifupi 26 kunja kwa tawuniyo. Bambo wa pa banjapo anali chidakwa koma tsopano anasintha. Mlungu uliwonse amabwera ndi banja lake lonse komanso ndi mchemwali wake ku Nyumba ya Ufumu. Amakweza mkazi ndi mwana wake pa keliyala ya njinga yake yaikulu. Ndipo mwana wake wina wa zaka nayini amakwezanso mlongo wake wamng’ono panjinga ina, ndiponso mwana wake wina wa zaka eyiti amapalasa yekha njinga. Amapalasa njingayi kwa maola atatu kuti akafike ku Nyumba ya Ufumu.” Banjali limakondadi Yehova, ndipo limayesetsa kuchita chilichonse kuti lithe kusonkhana ndi mpingo.

M’miyezi 18 yokha imene takhala ku Santa Rosa, anthu atatu ayenerera ubatizo ndipo anthu pafupifupi 25 amabwera ku Nyumba ya Ufumu yatsopano ku Santa Rosa. Ngakhale kuti anthu ochuluka akufuna kuphunzira Baibulo, ambiri ali ndi zopinga zazikulu zimene zingawalepheretse kutumikira Yehova.

Vuto Lolembetsa Maukwati

Marina ndi mwamuna wake Osni, omwe ndi amishonale, ndipo akutumikira ku tawuni ina yaing’ono pafupi ndi malire a Bolivia ndi Brazil, analongosola kuti anthu ambiri kuno amaona kuti ukwati ungathe nthawi ina iliyonse. Amuna amasinthasintha akazi kwambiri ndipo nawonso akazi amachita chimodzimodzi. “Limeneli ndi vuto limene likulepheretsa anthu kupita patsogolo mwauzimu,” anatero Osni. “Ndipo anthu akafuna kukhala Akristu oona, zimavuta ndiponso zimafuna ndalama zambiri. Ena amathetsa zibwenzi zawo zakale ndiyeno n’kukwatira kapena kukwatiwa mwa lamulo. Komabe, podziwa kuti Malemba amanena kuti tiyenera kulembetsa ukwati, ena amagwira ntchito molimbika kuti apeze ndalama zofunikira kuti akadule mtchato.”​—Aroma 13:1, 2; Ahebri 13:4.

Marina akusimba zimene Norberto anakumana nazo. “Norberto anakhala ndi akazi ambirimbiri asanayambe kukhalira limodzi ndi mzimayi wina yemwe anali wowotcha buledi. Mzimayiyu ndi wamng’ono kwa Norberto ndi zaka 35 ndipo ali ndi mwana wamwamuna amene Norberto anamupeza. Norberto anafuna kuti akhale chitsanzo chabwino cha mwanayo, pamene akukula. Choncho pamene wa Mboni anafika kumene amawotchera bulediko, n’kuwafunsa ngati angafune kuyamba kuphunzira Baibulo, Norberto anavomera, ngakhale kuti anali wosatha kuwerenga ndiponso anali ndi zaka zoposa 70. Norberto ndi mzimayiyo ataphunzira zimene Yehova amafuna, anakwatirana mwa lamulo ndipo kenako onse anabatizidwa. Mnyamatayo tsopano ndi Mkristu wodalirika, zimene bambo wake womupeza aja ankayembekezera. Norberto anaphunzira kuwerenga, ndipo wakambapo nkhani pa misonkhano ya mpingo. Mosasamala kanthu kuti ndi wofooka, chifukwa cha msinkhu wake, Norberto ndi mtumiki wokangalika wa uthenga wabwino.”

Mzimu wa Yehova Unawapatsa Mphamvu

Yesu anauza otsatira ake oyambirira kuti: “Mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga . . . kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Ndi zolimbikitsa kwambiri kuona mzimu wa Mulungu ukulimbikitsa amuna ndi akazi achikristu kusamukira ku malo akutali. Mwachitsanzo, m’chaka cha 2004 Akristu pafupifupi 30 okangalika analola kukachita utumiki wa upainiya wapadera kwa nthawi yochepa kumagawo akutali. Amayamikira chitsanzo cha anthu 180 ochokera m’mayiko ena amene anabwera ku Bolivia kudzakhala apainiya, oyang’anira madera, odzipereka kutumikira pa Beteli kapenanso amishonale. Ofalitsa Ufumu okwana 17,000 a ku Bolivia akuchititsa maphunziro a Baibulo pafupifupi 22,000 m’nyumba za anthu achidwi.

Abalewa amasangalala kwambiri podziwa kuti mzimu wa Yehova ukuwatsogolera. Mwachitsanzo, Robert ndi Kathy anali okondwa kukachita umishonale ku Camiri, tawuni yaing’ono yomwe ili m’mapiri okongola m’mphepete mwa mtsinje. “Zikuoneka kuti tinabwera panthawi yake,” anatero Robert. “M’zaka ziwiri zokha, anthu okwana pafupifupi 40 akhala ofalitsa uthenga wabwino.”

Chidakwa Ndiponso Wotchova Juga Amvetsera

Anthu ambiri a m’matawuni amachita chidwi ndi kusintha makhalidwe kumene anthu amene aphunzira Baibulo amachita. Mwachitsanzo, tsiku lina pafupifupi zaka zinayi zapitazo, munthu wina dzina lake Ariel yemwe anali chidakwa amagona chifukwa cha matsire. Ngakhale kuti anali wotchuka chifukwa cha juga, iye ankada nkhawa ndi ngongole yambiri yomwe anali nayo, ukwati wake womwe unali utavuta, ndiponso ana ake aakazi omwe sankatha kuwasamalira. Munthu wina wa Mboni za Yehova yemwe anali kulalikira nyumba ndi nyumba, atafika pakhomo pake, Ariel anasiya kuganizira za mavuto akewo. Ariel anamvetsera mwachidwi pamene mbaleyo ankafotokoza Malemba. Posapita nthawi Ariel anapita kukagonanso, tsopano n’kumakawerenga za moyo wa banja wachimwemwe, Paradaiso, ndi kutumikira Mulungu. Kenako anavomera kuphunzira Baibulo.

Nthawi imene amishonale ankafika ku Camiri, mkazi wa Ariel, Arminda, anali akuphunzira Baibulo, koma anali ndi chidwi chochepa. “Ndichita chilichonse kuti asiye kumwa mowa,” anatero mkaziyo. “Koma ndikukayikira ngati zingatheke. Ameneyu n’ngosatheka.” Komabe Arminda anasangalala kuphunzira Baibulo kuposa mmene ankaganizira poyamba. Chitangotha chaka chimodzi, anabatizidwa ndiponso anali kulakira kwa achibale ake. Posapita nthawi, abale ake ambiri ndithu anapereka moyo wawo kwa Yehova.

Ariel anavutika kuti asiye kumwa mowa, kusuta fodya ndiponso kutchova juga. Nthawi yosinthira zinthu inafika pamene anaitanira anzake onse ku Chikumbutso cha imfa ya Yesu. Iye anaganiza izi: “Anzanga amene sabwera ku Chikumbutso, ndisiya kucheza nawo. Koma amene abwere ndiyamba kuphunzira nawo Baibulo.” Chifukwa cha zimenezo anayamba maphunziro atatu a Baibulo. Ariel asanakhale Mboni, ankaphunzira Baibulo ndi mbale wake amene anapita patsogolo ndipo anabatizidwa tsiku limodzi ndi Ariel. Arminda anati: “Ariel wasintha kwambiri ngati kuti si yemwe uja tinkamudziwa.”

Robert anapereka lipoti lakuti: “Titawerenga komaliza, tinapeza kuti anthu 24 a m’banja la Ariel amabwera ku misonkhano mokhazikika. Anthu okwanira 10 anali obatizidwa pamene anthu ena eyiti ndi ofalitsa osabatizidwa. Anthu ena amene anaona kusintha khalidwe kwa anthu amenewa anayambanso kuphunzira Baibulo ndipo amabwera ku misonkhano ya mpingo. Chiwerengero cha osonkhana chinakwera kuchokera pa anthu 100 kufika pa 190. Ine ndi Kathy tikuchititsa maphunziro a Baibulo okwana 30 ndipo onse amafika pa misonkhano. Ndife osangalala kuti tikutumikira kuno.”

Zimene zikuchitika m’matawuni aang’ono ku Bolivia ndi mbali yochepa chabe ya ntchito yosonkhanitsa yomwe ikuchitika padziko lonse imene inanenedweratu m’chaputala 7 cha buku la Chivumbulutso, chimene chimanena za kusonkhanitsa anthu “tsiku la Ambuye.” Anthuwa ndi amene adzapulumuke chisautso chachikulu. (Chivumbulutso 1:10; 7:9-14) Chiyambire m’mbiri ya anthu sizinachitikepo kuti anthu ambirimbiri ochokera m’mitundu yonse agwirizane pa kulambira Mulungu woona yekha. Umenewu ndi umboni wosangalatsa wakuti malonjezo a Mulungu atsala pang’ono kukwaniritsidwa.

[Chithunzi patsamba 9]

Betty Jackson

[Chithunzi patsamba 9]

Elsie Meynberg

[Chithunzi patsamba 9]

Pamela Moseley

[Chithunzi patsamba 9]

Charlotte Tomaschafsky, waima kudzanja lamanjayo

[Chithunzi patsamba 10]

Mlungu uliwonse banja la a Vaca limapalasa njinga kwa maola atatu kupita ku Nyumba ya Ufumu

[Chithunzi patsamba 10]

Eric ndi Vicky anabwera kudzatumikira kumene kumafunika ofalitsa Ufumu ambiri

[Chithunzi patsamba 11]

Anthu a m’midzi yapafupi ndi mtsinje wa Beni akumvetsera uthenga wabwino mwachidwi

[Chithunzi patsamba 12]

Robert ndi Kathy akuchita umishonale ku Camiri