Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Akristu Enieni Ndani?

Kodi Akristu Enieni Ndani?

Kodi Akristu Enieni Ndani?

“CHIKRISTU ndi kuphunzitsa ndi kuchita zinthu zimene Yesu Kristu mwiniwakeyo anaphunzitsa.” (On Being a Christian) Ndi mawu amenewo, Hans Küng, wamaphunziro apamwamba a zaumulungu wa ku Switzerland, ananena mfundo yodziwikiratu. Mfundo yake n’njakuti: Chikristu chenicheni chili ndi anthu okhawo amene, ndi mtima wonse, amachita zimene Yesu anaphunzitsa.

Nanga bwanji ngati anthu kapena mabungwe akunena okha kuti amatsatira Kristu koma sachita zimene Yesu anaphunzitsa? Yesu ananena kuti anthu ambiri adzanena kumene kuti ndi Akristu. Anati iwo adzatchula ntchito zawo zosiyanasiyana monga umboni wakuti amam’tumikira. Iwo adzati: “Kodi sitinanenera mawu m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa mizimu yoipa, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri?” Koma kodi Yesu adzati chiyani? Mawu ake ndi odabwitsa koma akusonyeza maganizo ake. Iye adzati: “Sindinakudziwani inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusayeruzika.”​—Mateyu 7:22, 23.

Chenjezo limeneli n’loopsa kwambiri kwa anthu “akuchita kusayeruzika” amene amati amatsatira Yesu. Tiyeni tikambirane mfundo ziwiri zofunika kwambiri zimene Yesu anapereka zoti ngati anthu azikwanitsa, ndiye kuti iye angawaone ngati Akristu enieni m’malo mowakana chifukwa chokhala akuchita kusayeruzika.

“Ngati Muli Nacho Chikondano Wina ndi Mnzake”

Mfundo imodzi yofunika imene Yesu anapereka ndi iyi: ‘Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.’​Yohane 13:34, 35.

Yesu amafuna kuti otsatira ake azikondana ndi chikondi chenicheni ndiponso azikonda anthu onse chimodzimodzi. Akristu ambiri paokhapaokha achita zimenezi kuchokera pamene Yesu anali padziko lapansi. Koma bwanji nanga za zipembedzo zochuluka zimene zimanena kuti zikuimira Kristu? Kodi mbiri yawo ikusonyeza kuti zili ndi chikondi? Ayi. Zipembedzo zimenezo zatsogolera nkhondo zambiri zimene zakhetsa magazi a anthu osalakwa.​—Chivumbulutso 18:24.

Ndipo zachita zimenezo mpaka makono ano. Mayiko onena kuti chipembedzo chawo n’Chikristu anatsogolera pa kupha anthu ambirimbiri pankhondo ziwiri za padziko lonse zimene zinachitika m’zaka za m’ma 1900. Si kale kwambiri pamene mu 1994 ku Rwanda, mamembala a matchalitchi omwe amati ndi achikristu anali patsogolo kuchita nkhanza zoopsa ndi kuyesa kupulula fuko la anzawo. Desmond Tutu, amene kale anali bishopu wamkulu wa Angilikani, analemba kuti: “Anthu amene anaukirana mwankhanza chonchi anali oti ndi a chipembedzo chimodzi. Ochuluka anali Akristu.”

“Ngati Mukhala Inu M’mawu Anga”

Yesu anatchula mfundo yachiwiri yofunika pa Chikristu chenicheni pamene ananena kuti: ‘Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.’​—Yohane 8:31, 32.

Yesu amafuna kuti otsatira ake akhale m’mawu ake, kutanthauza kumamatira ziphunzitso zake. Koma aphunzitsi a zipembedzo amene amati ndi otsatira a Kristu “atengera kwambiri mfundo za Agiriki,” anatero Küng, wamaphunziro apamwamba a zaumulungu. Mwa zina, iwo asiya ziphunzitso za Yesu n’kuyamba kuphunzitsa zinthu monga kusafa kwa mzimu, purigatoliyo, kulambira Mariya, ndi kukhazikitsa timagulu ta atsogoleri achipembedzo. Zinthu zimenezi zinachokera ku zipembedzo zachikunja ndi kwa anthu anzeru achikunja.​—1 Akorinto 1:19-21; 3:18-20.

Ndiponso aphunzitsi a zipembedzo anayambitsa chiphunzitso chosamvetsetseka cha Utatu, kuika Yesu pamalo amene ngakhale mwiniwakeyo sananene. Mwa kuchita zimenezi, anasokoneza anthu kuti asiye kupembedza Yehova, Atate wake, amene Yesuyo nthawi zonse anawauza kuti azim’pembedza. (Mateyu 5:16; 6:9; Yohane 14:28; 20:17) Hans Küng analemba kuti: “Yesu akamalankhula za Mulungu, amakhala akunena za Mulungu wa makolo akale monga Abrahamu, Isake, ndi Yakobo: Yahweh . . . Kwa iye ameneyu ndiye Mulungu yekha, osatinso wina ayi.” Kodi ndi anthu angati masiku ano amene amadziwa kuti Mulungu wa Yesu ndiponso Atate wake ndi Yahweh, kapena kuti Yehova, malinga ndi mmene dzina lakelo limalembedwera nthawi zambiri m’Chichewa?

Chinanso, atsogoleri a zipembedzo akaniratu kutsatira lamulo la Yesu la kusalowerera ndale. M’masiku a Yesu, Galileya “ndiye anali chimake cha mzimu wokonda fuko ndi dziko lako,” anatero munthu wina wolemba nkhani, dzina lake Trevor Morrow. Ayuda ambiri okonda dziko lawo anamenya nkhondo kuti apeze ufulu wa ndale ndi wa chipembedzo. Kodi Yesu analangiza ophunzira ake kuchita nkhondo ngati zimenezo? Ayi. M’malo mwake, anawauza kuti: “Simuli a dziko lapansi.” (Yohane 15:19; 17:14) Koma atsogoleri a matchalitchi, m’malo mwakuti asalowerere ndale, anakhazikitsa zimene munthu winawake wa ku Ireland wolemba nkhani, dzina lake Hubert Butler, anatcha “mfundo za tchalitchi zolimbikitsa nkhondo ndi ndale.” Iye analemba kuti: “Nthawi zambiri, Chikristu chikamalimbikitsa ndale chimalimbikitsanso nkhondo, ndipo akuluakulu a boma akakambirana ndi atsogoleri a zipembedzo n’kugwirizana, zimachitika kuti pofuna kukhala ndi mwayi wapadera, Tchalitchi chimadalitsa asilikali a boma.”

Aphunzitsi Onama Amakana Yesu

Mtumwi Paulo anachenjezapo zoti anthu adzapatuka pa Chikristu chenicheni. Ananena kuti iye atamwalira, “mimbulu yosautsa” pakati pa anthu amene amati ndi Akristu ‘idzalankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.’ (Machitidwe 20:29, 30) Iwo ‘adzavomereza kuti adziwa Mulungu,’ pamene ‘ndi ntchito zawo adzam’kana Iye.’ (Tito 1:16) Mtumwi Petro nayenso anachenjeza kuti aphunzitsi onama “adzalowa nayo mseri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula.” Anati chifukwa cha khalidwe lawo loipa, anthu ‘adzanenera njira ya choonadi zamwano.’ (2 Petro 2:1, 2) Katswiri winawake wa Chigiriki, dzina lake W. E. Vine, ananena kuti kukana Kristu mwanjira imeneyi kumatanthauza “kukana Atate ndi Mwanayo, mwa kuyambitsa mpatuko ndi kufalitsa ziphunzitso zoipa.”

Kodi Yesu amamva bwanji ngati anthu amene amanena okha kuti ndi ophunzira ake alephera dala ‘kukhala m’mawu ake’ ndi kukwanitsa zofunika zina zimene iye ananena? Iye anachenjeza kuti: “Yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzam’kana iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.” (Mateyu 10:33) Apatu sakunena kuti Yesu amakana munthu amene walakwa pamene akuyesetsa ndi mtima wonse kukhala wokhulupirika ayi. Titenge chitsanzo cha mtumwi Petro. Iye anakana Yesu katatu koma analapa ndipo anakhululukidwa. (Mateyu 26:69-75) Amene Yesu amakana, ndi anthu kapena mabungwe amene ndi mimbulu yovala zikopa za nkhosa. Inde, anthu amene amakhala ngati akutsatira Kristu koma mwadala akulimbikira kukana ziphunzitso zake. Za aphunzitsi onama ngati amenewo, Yesu anati: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo.”​—Mateyu 7:15-20.

Atumwi Atamwalira, Panabuka Mpatuko

Kodi Akristu onyenga anayamba liti kum’kana Kristu? Anayamba pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Yesu anamwalira. Iye mwiniwakeyo anachenjeza zoti Satana Mdyerekezi mofulumira adzafesa “namsongole” wambiri, kapena kuti Akristu onyenga, pakati pa “mbewu zabwino” zimene Yesu anafesa pa utumiki wake, zimene ndi Akristu enieni. (Mateyu 13:24, 25, 37-39) Mtumwi Paulo anachenjeza zoti aphunzitsi onyenga analipo masiku akewo. Iye anati chifukwa chachikulu chimene iwo anapatukira kusiya ziphunzitso za Yesu Kristu chinali chakuti analibe “chikondi [chenicheni] cha choonadi.”​—2 Atesalonika 2:10.

Nthawi yonse imene atumwi a Yesu Kristu anali moyo, analetsa mpatukowo. Koma atumwi atamwalira, atsogoleri a chipembedzo pogwiritsa ntchito ‘mphamvu yonse, ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama; ndi chinyengo chonse cha chosalungama’ kuti asocheretse ena, anapatutsa anthu ambirimbiri kusiya choonadi chimene Yesu ndi atumwi ake anaphunzitsa. (2 Atesalonika 2:3, 6-12) Munthu winawake wa ku England wofufuza nzeru zapamwamba, dzina lake Bertrand Russell, analemba kuti patapita nthawi mpingo woyamba wachikristu unasintha n’kukhala chipembedzo chimene “Yesu, ndi Paulo yemwe, angadabwe nacho.”

Chikristu Chenicheni Chiyambiranso

Mfundo yake n’njomveka. Kuchokera nthawi imene atumwi anamwalira, zambiri zimene zachitika m’dzina la Chikristu sizigwirizana ndi ziphunzitso za Kristu. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti Yesu sanasunge lonjezo lake lakuti adzakhala ndi otsatira ake “masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.” (Mateyu 28:20) Ndife otsimikiza kuti chinenereni mawu amenewo, pakhala anthu okhulupirika amene ‘akuphunzitsa ndi kuchita zinthu zimene Yesu Kristu mwiniwakeyo anaphunzitsa.’ Yesu Kristu wasunga lonjezo lake lakuti adzathandiza anthuwo pamene iwo akuyesetsa kuonetsa chikondi chimene n’chizindikiro cha Akristu oona ndi kukhalabe okhulupirika pa choonadi chimene iye anaphunzitsa.

Chinanso, Yesu analonjeza kuti m’masiku otsiriza a dzikoli, iye adzasonkhanitsa pamodzi ophunzira ake okhulupirika mu mpingo wachikristu wosavuta kuuzindikira, umene adzagwiritsa ntchito kuchita chifuniro chake. (Mateyu 24:14, 45-47) Panopo iye akugwiritsa ntchito mpingowo kusonkhanitsa pamodzi “khamu lalikulu” la amuna, akazi, ndi ana “ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe,” ndipo akuwagwirizanitsa pansi pa utsogoleri wake kukhala “gulu limodzi, mbusa mmodzi.”​—Chivumbulutso 7:9, 14-17; Yohane 10:16; Aefeso 4:11-16.

Ndiye, pewani mabungwe kapena magulu alionse amene aipitsa dzina la Kristu ndi kuwononga mbiri yabwino ya Chikristu pa zaka 2,000 zapitazo. Ngati simutero, “mungalandireko ya miliri yake” pamene Mulungu adzawalanga posachedwa m’tsogolo muno, malinga ndi zimene Yesu Kristu anauza mtumwi Yohane. (Chivumbulutso 1:1; 18:4, 5) Onetsetsani kuti muli pakati pa anthu amene mneneri Mika ananena za iwo pamene anati “masiku otsiriza,” olambira oona amene ndi anthu otsatira Chikristu choona, adzamvera malangizo a Mulungu ndipo adzayenda “m’mabande ake” a kulambira koyera kumene kudzayambiranso. (Mika 4:1-4) Ofalitsa magazini ino ndi okonzeka kukuthandizani kuwadziwa olambira oona amenewo.

[Zithunzi patsamba 5]

N’chifukwa chiyani Akristu enieni samenya nkhondo?

[Mawu a Chithunzi]

Soldiers, left: U.S. National Archives photo; flamethrower, right: U.S. Army Photo

[Zithunzi patsamba 7]

Mawu akuti ‘mukhale nacho chikondano wina ndi mnzake’ ndipo ‘mukhale inu m’mawu anga’ ndiwo mfundo zazikulu zimene Yesu anapereka zofunika kwa Akristu enieni